Mboni Za Yehova—Gulu la Dzinalo
PA OCTOBER 6, 1990, khamu la anthu pafupifupi 5,000 limene linasonkhana m’Nyumba Yamsonkhano ya Mboni za Yehova mu Jersey City, New Jersey, ku U.S.A., pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society linali pafupi kuwona zodabwitsa. Tcheyamani, John E. Barr, anadziŵitsa omvetserawo za kutulutsidwa kwa vidiyo ya mphindi 55 yotchedwa Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Imeneyi inali vidiyo yoyamba kupangidwa ndi Sosaite, koma osati yomalizira.
Vidiyo imeneyi imasonyeza mmene anthu a Yehova aliri olinganizidwa kuchitira umboni dzina la Mulungu ndi kufalitsa “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Kwakukulukulu imasonyeza malikulu ku Brooklyn, New York, ndi malo a Watchtower Farms. Makope ake Achingelezi oposa 500,000 apangidwa, ndipo tsopano iripo (kapena idzakhalapo posachedwapa) m’zinenero zina 26.a
Kodi Yawayambukira Motani Anthu?
Kodi anthu amene saali Mboni za Yehova ayambukiridwa motani ndi vidiyo imeneyi? Mwinibizinensi wina analemba kuti:
“Ndinapeza tepi imeneyi kukhala yabwino koposa. Ndinachita chidwi kwambiri ndi mawonekedwe abwino kwambiri a zithunzithunzi ndi mmene zinajambulidwira mwaukatswiri. Ndinaiŵala kuti inali tepi ndi kuiyesa kukhala kanema yeniyeni. Tepi imeneyi iyenera kukhala yothandiza kwambiri kufotokoza chifuno cha malikulu anu ku New York. Ndikuthokozani pantchito yabwino imeneyi.”—J.J.
Amene amaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova apindula mwakuwonerera vidiyo imeneyi. Otsatiraŵa akufotokoza chifukwa chake:
“Ndimaphunzira Baibulo ndi mnyamata wazaka 20 zakubadwa amene amaphunzira payunivesiti. Iye anali wakuda nkhaŵa ponena za mkhalidwe wa dziko womaipaipirabe. Koma pamene anawonerera tepi imeneyi ndi kuwona abale onse abwino achichepere a pa Beteli, okhala ndi chifuno chenicheni m’moyo, kaimidwe kake kamaganizo kanasinthiratu. Iye anafika pa Tsiku la Msonkhano Wapadera ndipo anapempha kuphunzira Baibulo kaŵiri pamlungu. Wophunzira Baibulo wina, mphunzitsi wa pasukulu yasekondale, anabwereka vidiyo imeneyi kukasonyeza achibale ake. Iwo analingalira kuti Mboni za Yehova zinali chabe kagulu kakang’ono kosatchuka ndi kosalimba. Koma anadabwa atawona ukulu wa ntchito yathu ya padziko lonse ndi chipambano chimene tikupeza, Yehova ayamikike.”—J. B.
“Ndiribe mawu ofotokozera chimwemwe chimene ndinakhala nacho pamene mkazi amene ndimaphunzira naye Baibulo analira ndi chimwemwe ndi chiyamiko atawonerera vidiyo imeneyi. Akumagwetsa misozi, iye anati: ‘Kodi ndani angalephere kuwona kuti ili ndilo gulu la Mulungu wowona, Yehova? Sindinadziŵe konse kuti pali anthu otero.’ Ndiyeno anati: ‘Ndifuna kubatizidwa.’”—C. D.
“Tapeza chipambano chachikulu mwakusonyeza vidiyo imeneyi kwa ophunzira Baibulo. Usiku wathawu mwamuna wa phunziro lina la mkazi wanga anabwera kudzacheza. Iye anali wotsutsa kwambiri. Anawonerera vidiyoyo. Pambuyo pake anafunsa mafunso ndipo anachokapo ndi Baibulo ndi bukhu lophunzirira Baibulo la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Kalelo iye anatentha mabuku onse ofotokoza Baibulo a mkazi wake!”—D. H.
Achichepere nawonso apeza vidiyo imeneyi kukhala yochititsa chidwi, monga momwe ndemanga zotsatira zikusonyezera:
“Ndiri ndi zaka zisanu ndi chimodzi ndi theka. Ndinakondwera ndi mbali yosonyeza Mabaibulo ndi mabokosi oyenda mofulumira.”—K. W.
“Ana athu aang’ono ananena kuti njabwino koposa programu iriyonse imene anaiwonerera pa TV.”—R. C.
“Atawonerera vidiyo imeneyi kachiŵiri, mwana wathu wamwamuna wazaka zisanu, amene anachita chidwi kwambiri kufikira pomalizira, anafunsa kuti, ‘Kodi sitingawonerere imeneyi masiku onse?’ Mwana wathu wamkazi wazaka zitatu analoŵerapo ndi mawu akuti ‘Ndifuna kupita ku Beteli ndikapange mabuku!’”—M. E.
“Ana anga, Robin ndi Shannan, azaka 12 ndi 9 zakubadwa, amawonerera tepi imeneyi mobwerezabwereza. Pambuyo powonerera tepi imeneyi, mwana wanga wamkazi wamng’ono koposa anati, ‘Ndimakonda kupita muutumiki wakumunda. Kumandisangalatsa kwambiri.’ Tikhulupirira kuti vidiyo imeneyi yayambukira moyo wa banja lathu mwachindunji. Nkotsitsimula chotani nanga kutsegula programu pa wailesi yakanema imene mumapenyerera ndi chikumbumtima chabwino!”—N. B.
“Ndiri ndi zaka zakubadwa 131/2. Vidiyo yatsopano imeneyi inandichititsa kuzindikira mmene ndimatengera mosasamala zogaŵira za Yehova zabwino kwambiri. Uli mwaŵi wapadera kukhala mmodzi wa anthu a Mulungu.”—K. W.
“Ndiri ndi zaka 16 zakubadwa, ndipo vidiyo imeneyi yandithandiza kumvetsetsa kuti ntchito imene ikuchitidwayi njapadziko lonse.”—A. M.
“Ana athu ananena kuti maprogramu anthaŵi yonse pa TV samawasangalatsanso chifukwa chakuwona mmene kusanguluka kwenikweni kwateokratiki kungakhalire. Yakulitsanso chikhumbo chawo cha kuloŵa utumiki wanthaŵi yonse.”—L. M.
Ngakhale amene akhala Mboni za Yehova kwa zaka zambiri asonkhezeredwa ndi zimene awona.
“Ngati vidiyo imeneyi iri ndi chiyambukiro chotero pa ife monga anthu a Yehova, bwanji mmene idzayambukirira ena? Pamene ndipeza vuto kuchita ndi dongosolo lino, ndimawombola ola limodzi panthaŵi yanga ndi kuyendera Beteli patepi imeneyi ndikumapuma m’chipinda changa chochezera!”—K. B.
“Nditawona mmene ntchitoyo imachitidwira mosamalitsa ndi molongosoka, ndinachita ngati ndidzapita m’chipinda changa kukakupatira mabuku anga ofotokoza Baibulo.”—L. P.
Tikulimbikitsani inunso kupeza nthaŵi yakuwonerera vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Idzakupatsani kapenyedwe kosiyana ka moyo ndi kukuthandizani kukhala ndi chidaliro cha mtsogolo mosungika.
[Mawu a M’munsi]
a Chinenero cha manja cha ku Amereka, Arabic, Basque, Cantonese, Catalan, Croatian, Czech (Bohemian), Danish, Dutch, Finnish, French, German, Greek, Hungarian, Italian, Japanese, Korean, Mandarin, Norwegian, Polish, Portuguese (Brazil), Portuguese (Europe), Romanian, Slovak, Spanish, Swedish.