Kodi Ndani Amene Amabadwanso?
KODI anthu onse abwino amapita kumwamba? Ambiri amaganiza choncho, koma Yesu Kristu sanavomereze. Polankhula kwa wolamulira Wachiyuda Nikodemo, amene anadza kwa iye mtseri pa usiku, Yesu anati: “Kulibe munthu anakwera kumwamba.”—Yohane 3:13.
Chikhalirechobe, Yesu anasonyeza kwa Nikodemo kuti nthaŵi ikafika pamene anthu ena akakhala ndi mwaŵi wakuloŵa Ufumu wakumwamba. Pamfundo imeneyi Yesu anati: “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mzimu, sakhoza kuloŵa ufumu wa Mulungu. Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwamzimu, chikhala mzimu. Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, uyenera kubadwa mwatsopano.” Komatu Nikodemo anadabwa mmene munthu aliyense angabadwirenso.—Yohane 3:1-9.
Mwinamwake inunso mukudabwa zimene Yesu anatanthauza. Kodi mawu ake angagwire ntchito kuzochitika za kutembenuka kwamwadzidzidzi zonenedwa ndi ochuluka amene amalingalira kuti adzazidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu?
Kutengeka Maganizo ndi Malingaliro
Ena amanena kuti kuti mutsimikizire kuti kaya munthuyo wabadwanso, chimene chiri kanthu ndicho kumva mphamvu ya mzimu. Komabe mtima wathu ndi maganizo zingatisocheretse, makamaka ngati zisonkhezeredwa ndi kutengeka maganizo kwamphamvu.—Yeremiya 17:9.
William Sargant, wofufuza ziyambukiro zakutengeka maganizo pa malingaliro, akutchula kufunika kwa “kukhala maso motsutsana ndi zikhulupiriro zopezeka m’mikhalidwe yakunyanyuka maganizo pamene maubongo athu angatisocheretse.” Mogwirizana ndi kunena kwa Sargant, chitsanzo chimodzi ndicho chiyambukiro cha kulalikira za kutsitsimulidwa ndi ziwopsezo za chilango cha moto wa helo. Kodi ndani amene sakafuna kubadwanso kuti apite kumwamba ngati kulephera kutero kunali kuvutika kwamuyaya m’chizunzo? Sargant akunena kuti mutapsinjika maganizo kwambiri chotero, “kulingalira kumalekeka, kompyuta ya nthaŵi zonse yaubongo imasiya kugwira ntchito kwakanthaŵi, ndipo malingaliro atsopano ndi zikhulupiriro zimavomerezedwa mosaŵiringula.”—The Mind Possessed.
Chotero, pamenepa, kodi ndi motani mmene munthu angadziŵire ngati chikhulupiriro pankhani yakubadwanso chakhala “chovomerezedwa popanda kuŵiringula?” Njira yanzeru yowona ndiyo yakutsogozedwa ndi chirichonse chimene mzimu woyera wa Mulungu unachititsa olemba Baibulo kuchilemba. Akristu akulimbikitsidwa kulambira Mulungu ‘ndi mphamvu yawo yakulingalira’ ndipo afunikira kutsimikizira kuti zimene akuzikhulupirira nzowona.—Aroma 12:1, 2; 1 Atesalonika 5:21.
Kubadwanso kumatsegula umodzi wa mwaŵi waukulu koposa woperekedwa kwa anthu. Kumagwirizanitsidwa ndi chochitika chabwino kwambiri m’kuchitidwa kwa chifuno cha Mulungu. Ngakhale kuti zonsezi ziri zowona, mafunso onga awa amabuka: Kodi ndani amene amabadwanso? Kodi kumeneku kumachitika motani? Kodi nziyembekezo zotani zomwe zaperekedwa kwa anthu otero? Ndipo kodi ndiwo okha amene adzapulumuka?
[Chithunzi patsamba 3]
Nikodemo anadabwa mmene munthu aliyense angabadwirenso