Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Mateyu 28:17 amatanthauza kuti atumwi ena anapitirizabe kukaikira nthaŵi yaitali Yesu woukitsidwayo atawonekera kwa iwo?
Ayi, sitifunikira kutsimikizira motero ponena za Mateyu 28:16, 17, pamene pamati: “Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira. Ndipo pamene anamuwona Iye, anamlambira; koma ena anakaika.”
Nthaŵi yaikulu pasadakhale Yesu anayesa kuthandiza ophunzira ake kuzindikira “kuti kuyenera iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.” (Mateyu 16:21) Komabe, kumangidwa kwake ndi kuphedwa kunasiya ophunzirawo ali othedwa nzeru ndi osokonezeka maganizo. Chiukiriro chake chinawonekera kukhala chitadza monga chodabwitsa. Ndipo pamene iye anadziwonetsa iye mwini mumpangidwe waumunthu, poyamba ena ‘sanakhulupirire chifukwa cha chimwemwe.’ (Luka 24:36-41) Komabe, kuwonekerawonekera kwake pambuyo pa chiukiriro, kunathandiza otsatira ake apafupi kuvomereza chiukiriro chake; ngakhale mtumwi Tomasi anakhutiritsidwa kuti Yesu anali ataukitsidwa.—Yohane 20:24-29.
Pambuyo pa zimenezo atumwi okhulupirika 11 “anamuka ku Galileya.” (Mateyu 28:16; Yohane 21:1) Ali kumeneko, Yesu “anawoneka panthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu.” (1 Akorinto 15:6) Muli mkati mwazochitika zimenezi kuti Mateyu 28:17 akutchula kuti “ena anakaika.” Chotero awo amene anali kukaikabe angakhale analidi pakati pa otsatira 500 amenewo.
Tamverani ndemanga yokondweretsa pamfundoyi imene C. T. Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, anapereka:
“Sitingathe kuyerekezera bwino lomwe kuti awo amene anakaikira anali ena a atumwi khumi ndi mmodzi, chifukwa chakuti iwo anali okhutiritsidwa kotheratu, ndipo anali atanena motero iwo eni papitapo. Tiganiza kuti, awo amene anakaikira, ayenera kukhala mwa ‘abale mazana asanu’ amene anapezeka pa msonkhano wolinganizidwa umenewu, amene sanawonane naye poyamba kuyambira chiukiriro chake, ndi ena amene, mwinamwake tingayerekezere kuti anali ofookerapo m’chikhulupiriro, osati atumwi ndi mabwenzi apadera amene anali atacheza ndi kulankhula ndi Yesu pambuyo pachiukiriro chake. Mawu akutiwo ‘ena anakaika’ ali umboni wakusabisa mawu kwacholembedwa cha wolemba Uthenga Wabwino. Ndiponso, amatisonyeza kuti, otsatira a Ambuye sanali ongovomera zonse, koma mmalo mwake anafuna kusefa ndi kupima maumboni operekedwa, ndipo changu chosonyezedwa ndi nyonga, ndi mzimu wakudzimana wa amene anakhulupirira umatipatsa umboni wochuluka wakuwona mtima kwa zikhutiro zawo zonena za chiukiriro cha Ambuye wathu, zimene iwo ndi ife timazindikira kukhala mfungulo yeniyeni ya chikhulupiriro chathu mwa iye. Ngati Kristu sanaukitsidwe chikhulupiriro chathu chiri chabe ndipo ife tikali chikhalirebe m’machimo athu.—1 Akor. 15:17.”—Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence, May 1, 1901, tsamba 152.
Ndiponso, tinganene kuti njira imene Mateyu akutchulira mfundoyi imatipatsa umboni wakudalirika ndi kuwona kwa Baibulo. Ngati munthu anali kupeka chochitika, iye akakhoterera kupereka maumboni amene akapangitsa nkhani yake yopekedwayo kuwonekera kukhala yokhulupiririka; mwachiwonekere iye akalingalira kuti maumboni osiidwa kapena yowonekera kukhala mipata akapereka chikaikiro pankhani yake yopekayo. Bwanji za Mateyu?
Iye sanalingalire kukhala wokakamizika kupereka malongosoledwe atsatanetsatane a mawu ake akuti: “ena anakaika.” Zolembedwa za Marko, Luka ndi Yohane sizimanena kanthu za mfundoyi, chotero mawu a Mateyu atawonedwa mwa iwo okha angawonekere kukhala akusonya kwa atumwi 11, amene iye anali mmodzi wawo. Komabe, Mateyu ananena mawu achidulewo popanda kupereka malongosoledwe aliwonse. Zaka 14 pambuyo pake, mtumwi Paulo analemba bukhu la Akorinto Woyamba. Mothandizidwa ndi umboni umene anaupereka pa 1 Akorinto 15:6, tingatsimikizire kuti awo amene anakaikira sanali atumwi koma ophunzira ku Galileya kwa amene Yesu anali asanawonekereko. Chotero, mawu a Mateyu akuti “ena anakaika” ngowona; moyenerera amamvekera kukhala operekedwa ndi wolemba wowona mtima wosimba chochitika chowona popanda kuyesa kufotokoza umboni wopezeka uliwonse.