Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/1 tsamba 31
  • Ufulu Wauzimu m’Colombia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufulu Wauzimu m’Colombia
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Malamulo aku United States ndi Mboni za Yehova
    Galamukani!—1988
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Colombia
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Ufulu wa Chipembedzo Umatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Chifukwa Chimene Nthanthi Ya Zaumulungu Yonena za Ufulu Siiri Yankho
    Galamukani!—1988
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/1 tsamba 31

Lipoti la Olengeza Ufumu

Ufulu Wauzimu m’Colombia

KUYAMBIRA panthaŵi yakugonjetsa kwa Aspanya, Chikatolika chakhala chiri chipembedzo chotsendereza mu South America. M’Colombia chakhala chiri chipembedzo Chaboma chalamulo kwanthaŵi yaitali. Kwazaka 105 zapitazo, Vatican inali ndi pangano ndi boma la Colombia limene linatetezera tchalitchicho ndi kuchipatsa mwaŵi wapadera m’nkhani zamaphunziro ndi ukwati.

Mu December 1990 anthu aku Colombia anasankha bungwe loti lilembe mpambo watsopano wamalamulo, umene unamalizidwa chapakati pa 1991. Mpambo watsopano wamalamulo umasintha mkhalidwe wazipembedzo m’Colombia. Tsopano zipembedzo zonse ziri ndi ufulu wofanana pamaso pa lamulo, ndipo malangizo achipembedzo sangathe kukakamizidwa pa ana m’masukulu a anthu onse. Panganolo ndi Vatican liyenera kupendedwanso mogwirizana ndi masinthidwe ampambo wamalamulo amenewa.

Ufulu wachipembedzo wokulirapo umenewu udzachepetsa chisonkhezero cha Tchalitchi cha Katolika, kukupangitsa kukhala kosavutirapo kwa anthu owona mtima kupeza chidziŵitso cha Baibulo ndi kupeza ufulu wauzimu.

Zikumayembekezera ufulu wauzimu umenewu, Mboni za Yehova 51,000 m’dzikolo zakhala zikupanga makonzedwe akusamalira othaŵa auzimu. Ofesi yawo yanthambi yatsopano limodzi ndi nyumba zake zowonjezeredwa, imene imaphatikizapo makina osindikizira otulutsa mawonekedwe onse achinthu othamanga kwambiri, iri pafupi kumalizidwa. Apainiya apadera akanthaŵi atumizidwa m’matawuni aang’ono kufunafuna nkhosa zotaika za Yehova ndipo achita ntchito yakuphunzitsa Baibulo yabwino kwambiri. M’matawuni 63, lirilonse lokhala ndi nzika pafupifupi 10,000, mipingo yatsopano 47 ndi timagulu yapangidwa.

Pamene mzimu wa Yehova upitirizabe kusonkhezera anthu owona mtima, achichepere ambiri nawonso akulabadira. Bukhu lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza latsimikizira kukhala chithandizo chopindulitsa kwa ponse paŵiri achichepere ndi makolo awo. Popita kunyumba ndi nyumba, Mboni ina inakumana ndi mwamuna amene anali ataŵerenga mbali za bukhuli, kope limene mnansi wake anambwereka. Mwamunayo anachita chidwi kwambiri ndi nzeru yothandiza imene bukhuli linasonyeza pofotokoza mavuto a banja. Mutu 4, “Kodi Nchifukwa Ninji Amayi ndi Atate Analekana?” unamchititsa chidwi mwapadera, popeza kuti iye ndi mkazi wake anatsala nenene kulekana. Iye anati bukhulo linampulumutsa kutsoka lalikulu. Tsopano mwamunayo ndi banja lake akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo akufika pamisonkhano yonse yampingo. Iwo akuthokoza kwambiri nzeru yothandiza imene Yehova akugaŵira kudzera m’Baibulo ndi gulu lake.

Chokumana nacho chimenechi chikufotokoza mwafanizo ufulu wauzimu umene ukuchitika m’Colombia pamene Mboni za Yehova zikuthandiza anjala mwauzimu kuphunzira zifuno zabwino kwambiri za Yehova ndi dziko lake latsopano, zimene tsopano zayandikira.​—2 Petro 3:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena