“Monga Mkango Wobuma”
KODI mumakhulupirira kuti Satana aliko? Lerolino, ambiri samatero. Kukuwonekera ngati kuti amawona chikhulupiriro chotero kukhala “chosemphana ndi sayansi.” Ngakhale kalelo mu 1911, Encyclopædia Britannica inati: “Sayansi yafotokoza kwambiri zochitika zambiri za chilengedwe ndi moyo wa munthu kotero kuti palibiretu mpata wotsala wakukhulupirira kukhalako kwa wotchedwa Satana.” Aphunzitsi azaumulungu amaganiza kuti Satana ali kokha chizindikiro, nthano, The World Book Encyclopedia imati: “Aphunzitsi azaumulungu amakono ambiri amalingalira Mdyerekezi kukhala chizindikiro cha mphamvu ya choipa, cha mikhalidwe yoipitsitsa yachibadwidwe cha anthu.”
Komabe, kodi maumboni akuti bwanji? Ngati mukhulupirira Baibulo, muyenera kukhulupirira kuti Satana ali weniweni. Sikokha kuti Yesu anakhulupirira kuti iye aliko koma anamutcha iye ‘wolamulira wa dziko.’ (Yohane 14:30) Mtumwi Paulo anatcha Satana kukhala “Mulungu wanthaŵi ino yapansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Ndipo mtumwi Yohane wokalambayo anati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.
Ngati inu simukuvomerezana ndi Yohane, talingalirani mbiri yaposachedwapa. Talingalirani timagulu ta onyonga ndi kugwiritsidwa ntchito kwa chizunzo kochitidwa ndi maboma. Kumbukirani nkhondo ndi kuphana zimene mbadwo wathu wawona. Ndipo bwanji za mitu yankhani za maupandu yowonekera pa manyuzipepa—kuchita mbanda kopululutsa, kugwirira zigololo, kupha kotsatizanatsatizana, kuchitira nkhanza ana mwakuwagona, kungotchulapo zochepekera chabe? Kodi wina ndani amene angakhale mulungu wadziko lino kusiyapo Satana?
Mtumwi Petro anachenjeza kuti: “Dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Ngati mkango unali kuyendayenda m’chitaganya chanu, kodi inu mukalankhula za kukhalako kwake kapena za kusakhalako kwake? Kapena kodi mukathaŵira pobisala?
Ndithudi Satana aliko. Iye ngwankhalwe ndi wolusa, ndipo ngwamphamvu kwambiri kutiposa ife. Chotero thaŵirani kumalo otetezereka kwa Uyo amene alidi wamphamvupo. “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” (Miyambo 18:10) Bisalani mwa Yehova Mulungu, ndipo dziŵani kuti posachedwapa anthu onse adzawonjoledwa kuchisonkhezero cha woipayo, Satana. Umenewu udzakhala mpumulo wosangalatsa chotani nanga!—Chivumbulutso 20:1-3.