Lipoti la Olengeza Ufumu
Kukhutiritsa Anjala Mwauzimu—Pa Sukulu
“ACHIMWEMWE ali awo ozindikira chosoŵa chawo chauzimu,” anatero Yesu mu Ulaliki wake wa pa Phiri. (Mateyu 5:3, NW) Ana asukulu ochuluka nganjala yofuna kudziŵa Mulungu ndi zifuno zake zodabwitsa. Iwo amafuna mayankho amafunso onena za moyo ndipo afuna kudziŵa mmene ayenera kukhalira ndi moyo kuti alandire chiyanjo cha Mulungu ndi kukhala achimwemwe. Izi zinawoneka pa sukulu ina ku British Virgin Islands. Mmodzi wa Mboni za Yehova kumeneko akusimba kuti:
◻ “Ndinafika pamsonkhano wa makolo ndi aphunzitsi ku sukulu yakwathu, ndipo zambiri zinanenedwa ponena za mankhwala oledzeretsa, kumwa, kupalana ubwenzi, kuwonerera TV, magiredi, ndi nkhani zina, chotero ndinasankha kumka ndi bukhu la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza ndi kukalipereka kwa mphunzitsi wamkulu wachikazi. Atatha kupenda bukhulo, ananena kuti ndilo limene anawo anafunikiradi ndipo anapempha ngati sukulu ikakhoza kupeza kope la aliyense wa ophunzira 120. Nkhaniyo inakambitsiridwa ndi akulu ampingo, ndipo akuluwo anasankha kupanga chopereka cha mabukhuwo kusukulu. Pamene tinawauza zimenezi, aphunzitsi anapempha kuti tipereke mabukhuwo ku gulu la ophunzira onsewo. Mboni ziŵiri zinapita, ndipo chipinda chinali chodzala ndi ophunzira, akumawayembekezera. Abalewo analankhula kwa theka la ola, ndipo zokumana nazo zosonyeza mmene bukhulo lathandizira achichepere ndi akulu omwe zinaŵerengedwa m’magazini a Watch Tower Society. Pamenepo mabukhu anaperekedwa kwa ophunzira okhala ndi chikhumbowo.”
Chiri chisangalalo kudziŵa kuti sukulu inasankha kugwiritsira ntchito bukhulo monga mbali ya maphunziro anthaŵi zonse a giredi lachinayi ndi lachisanu. Ilo lidzayankhadi mafunso ambiri amene ophunzira amenewa ali nawo onena za moyo ndi mtsogolo.
Kukhutiritsa a Njala Mwauzimu—M’Papua New Guinea
Chokumana nacho chotsatirachi chinalandiridwa kuchokera kwa woyang’anira woyendayenda. Chikufotokoza mwafanizo mmene anthu aliri anjala mwauzimu m’dzikolo ndi mmene mabukhu athu ofotokoza Baibulo aliri ogwira mtima m’kukhutiritsa njala yawo.
◻ “Pamene ndinali wosakhoza kuchezera mudzi wa Kamberatoro,” anatero woyang’anirayo, “Ndinathera nthaŵi yanga ndikugwira ntchito ndi mpingo waung’ono mu Vanimo. Kumeneko kuli okondwerera ochuluka. Anthu ambiri a ku Bewani analandira mabukhu. Mwamuna wina anandipempha kufika ndi kukachezetsa mudziwu, ndipo ankandipatsa malo ogona. Anthu ambiri ngozoloŵerana ndi mabukhu athu. Nthaŵi iriyonse imene tinapita kutawuni ya Vanimo, mabukhu amatithera mosasamala kanthu kuti tanyamula mabokosi atatu amabukhu. Bukhu Langa Lankhani za Baibulo likulingaliridwa kukhala golidi wamtego wake. Anthu akulifunafuna. Mabukhu amene ndinatenga anagaŵiridwa mofulumira kwambiri. Pamene tinasonyeza anthu mabukhu athu, ena ankafunsa kuti: ‘Kodi bukhu lachikasu liri kuti?’ Mwamuna wina anawodetsa asanu ndi limodzi. Anandipatsa dzina lake ndi keyala nandipempha kukalengeza pa wailesi pamene ndikawalandira. Kuchitira kuti iye anyamuke kumudzi kwawo kudzawatenga.” Woyang’anira woyendayendayo akuwonjezera kuti: “Ndinapeza kuti anthu ambiri mu Vanimo analandira mabukhu a Mankind’s Search for God ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.”
Izi zikufotokoza mwafanizo mmene anthu owona mtima aliri anjala ya chakudya chauzimu chopezedwa mu Baibulo ndi m’mabukhu amene Yehova wawagaŵira kudzera mwa “kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Mboni za Yehova nzachimwemwe chotani nanga kukhala zokhoza kuthandiza anthu anjala ya chowonadi amenewa!
[Chithunzi patsamba 19]
Kuchitira umboni m’Papua New Guinea