Msonkhano Waukulu wa Zipembedzo za Dziko—Kodi Idzapambana?
ATSOGOLERI azipembedzo mazana ambiri anasonkhana pa Msonkhano Waukulu wachiŵiri wa Zipembedzo za Dziko wochitidwa ku Chicago, Illinois, U.S.A., m’chilimwe cha 1993. Abuddha, Akristu, Ahindu, Ayuda, ndi Asilamu onsewo analipo. Opembedza ufiti ndi milungu yachikazi nawonso analipo. Anakambitsirana za mbali yawo pa kuthetsa nkhondo. Tcheyamani wa msonkhano waukulu anavomereza kuti “magawo aŵiri mwa atatu a nkhondo zazikulu m’dziko lerolino ngosonkhezeredwa ndi chipembedzo.”
Zaka Zana Zapitazo
Kodi msonkhano waukuluwo unali wachipambano? Onani zimene zinachitika zaka zana zapitazo pa Msonkhano Waukulu woyamba wa Zipembedzo za Dziko. Nawonso unachitidwira m’Chicago, m’chilimwe cha 1893, ndipo magulu achipembedzo oposa 40 anali ndi owaimira. Bungwe la Msonkhano waukulu wa Zipembedzo za Dziko likuvomereza kuti awo amene analipo mu 1893 “anakhulupirira kuti umenewo ukakhala msonkhano woyamba mumpambo wa misonkhano ya kuloŵana chikhulupiriro kwa mitundu yonse kumene kukachirikiza kumvana, mtendere ndi chitukuko. Uwo sunakhale wotero. Kusalekerera kwachipembedzo ndi chiwawa zakhala mbali ya nkhondo kwa zaka 100 zapitazo, ndipo zikupitirizabe lerolino.” Kodi nchifukwa ninji pali kulepheraku? Chifukwa chakuti lingaliro lonse la kuloŵana chikhulupiriro lili losavomerezedwa ndi Mulungu. Baibulo limati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.”—2 Akorinto 6:14-17.
Moyenerera, kope la Zion’s Watch Tower la September 1893 linafotokoza kupanda chichirikizo cha m’Malemba kwa Msonkhano waukulu wa Zipembedzo za Dziko pamene moseka linati: “Ofukula m’mabwinja afukula mipembe yadothi yowotchedwa m’mabwinja a Babulo ndi mizinda ina yakale, koma pali ina imene sinapezedwebe. . . . Sanapeze uliwonse wonena za Mose ndi Yoswa kukhala atasonkhanitsa ‘Msonkhano waukulu wa Zipembedzo,’ wa Amoabu ndi Aamoni, ndi Aedomu . . . Sanapeze uliwonse umene umafotokoza za Samueli wokalamba wojintcha kukhala atatumidwa ku Gati ndi Ekroni kuitana oimira ansembe a Dagoni kuti adze ku Silo kudzachita msonkhano ndi ansembe a Yehova . . . Sanapeze uliwonse umene umafotokoza za Eliya wokalamba womanga lamba lachikopa kukhala atapereka lingaliro la kuchita ‘msonkhano’ ndi ansembe a Baala ndi Moloki wa kukambitsirana kwa mlungu umodzi kwa malamulo a zikhulupiriro zawo zosiyanasiyana, ndi cholinga cha kuchirikiza kulemekezana pachipembedzo cha wina ndi mnzake.”
Ufumu wa Mulungu —Chiyembekezo Chokha
Msonkhano waukulu wa Zipembedzo za Dziko sudzapambana. Manyuzipepala ndi nthumwi anagwiritsira ntchito mawu onga akuti “chipwirikiti,” “msokonezo,” ndi “misala” ponena za msonkhano waukuluwo. Malinga ndi kunena kwa lipoti lina, ngakhale apolisi anaphatikizidwa m’kutontholetsa ziwawa ziŵiri zochititsidwa ndi magaŵano a ndale zadziko. M’chikalata cha 1952, msonkhano waukulu unalemba pampambo mawu awa monga china cha zifuno zake: “Kukhazikitsa Msonkhano waukulu wa Dziko wa Zipembedzo wachikhalire woti ugwire ntchito limodzi ndi gulu la MITUNDU YOGWIRIZANA m’kupeza mtendere wa dziko ndi kumvetsetsana pakati pa anthu onse.” Mosiyana ndi zimenezo, Yesu ananena kuti Ufumu wake sunali mbali ya dzikoli. Baibulo limasonyeza Ufumu wa Mulungu kukhala chothetsera chokha cha mavuto a mtundu wa anthu.—Danieli 2:44; Yohane 18:36.