Mboni za Yehova Padziko Lonse—Colombia
COLOMBIA ndi dziko lapadera la ku South America. Nyanja zazikulu zamchere ziŵiri za Atlantic ndi Pacific zimakhudza gombe la dziko la volcano limeneli. Kutentha kwa magombe otsika a kumalo otentha ndi zigwa kumasiyana ndi kuzizira kwa kumalo okwera, a mapiri okutidwa ndi chipale chofeŵa a Andes.a
Ngakhale kuti Colombia ngwotchuka chifukwa cha golidi ndi ma emerald, anthuwo ndiwo chuma chake chamtengo koposa. Lerolino, Yehova akudzaza nyumba yake yauzimu ndi ulemerero. Olambira okongola, ofunika akuthamangiramo m’mbali zonse za dziko lapansi, kuphatikizapo Colombia.—Hagai 2:7.
Akuluakulu Amalonda Anachita Chidwi
Sande, November 1, 1992, linali deti la kupatuliridwa kwa ofesi yanthambi yatsopano ya Watch Tower Society ndi nyumba yosindikizira pa Facatativá, makilomita 42 kumpoto koma chakumadzulo kwa Bogotá. Maulendo oyendera nthambiyo akhala ndi chiyambukiro chachikulu pa alendo. Pamene anabwerera ku fakitale kumene amagwira ntchito, mlendo wina motenthedwa maganizo anasonkhezera amanijala ake kupita ndi kukaona gulu limene lili ‘chozizwitsa cha kugwira bwino ntchito, dongosolo, ndi mzimu wantchito wosonyezedwa ndi antchito.’ Mkati mwa ulendo wawo woyendera wotsatira, akuluakuluwo anasonyeza chikondwerero chachikulu ndipo anafunsa mafunso ambiri.
Akuluakulu ameneŵa anafuna kutumiza oyang’anira, olangiza, ndi akapitawo awo—kwenikweni, antchito awo onse—pa ulendo wodzayendera. Mlungu uliwonse, anandandalika antchito 15 kufikira 25 kudzayendera kufikira gulu lonse la antchito 1,300 litaona kugwira bwino kwa gulu koteroko.
Mazana a antchito awo anayendera malo a nthambiyo ndi kuona vidiyo ya Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Atachita chidwi ndi ukulu wa gululo ndi kufalikira padziko lonse kwa ntchito yolalikira Ufumu, iwo anadabwa ndi kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga limene limagwiritsiridwa ntchito ndi Sosaite. Pamene anali kuchoka, ambiri anamvedwa akunena kuti akumva ngati kuti ‘akuchoka m’Paradaiso kubwerera ku dziko la msokonezo.’
Choonadi Chifikira a Mitundu Yonse
Mitundu yonse ya anthu ikufikiridwa ndi mbiri yabwino. (1 Timoteo 2:3, 4, NW) Mwachitsanzo, yemwe kale anali wolemba nyimbo ndi mtsogoleri wa gulu loimba la roko la heavy-metal analandira choonadi cha Baibulo, anapanga masinthidwe m’moyo wake, ndipo posakhalitsa anakhala mpainiya wokhazikika. Pambuyo pake anaikidwa kukhala mtumiki wotumikira. Anthu angapo omwe anali ziŵalo za magulu opandukira aphunzira kuika chidaliro ndi chiyembekezo chawo mu Ufumu wa Yehova. Iwo tsopano ali odziloŵetsa mokangalika m’kulalikira uthenga wa dziko latsopano lamtendere.
Omwerekera ndi ogulitsa mankhwala oledzeretsa atembenukiranso ku choonadi. Mwamuna wina wachichepere amene tsopano ndi Mboni anakhala akusamalira munda wa mankhwala oledzeretsa ndi laboratory ya cocaine m’nkhalango kwa zaka zisanu asanamasuke ku moyo wa mtundu umenewo. Iye wapeza chimwemwe m’kuphunzira ndi kuchita malamulo a mkhalidwe a Baibulo. M’nyumba yandende akupha anthu mwachiwembu oweruzidwa osonkhezeredwa ndi phunziro loona mtima la Baibulo akupemphera moona mtima kuti Yehova awakhululukire machimo awo ndi kuwalandira monga atumiki ake.
Ndi mmene zilili kuti anthu a mitundu yonse akulandira uthenga wa Ufumu. Mu Colombia, limodzinso ndi kwina konse, Yehova akudzazadi nyumba yake ndi ulemerero.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.
[Bokosi patsamba 8]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1993
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 60,854
KUGAŴA: Mboni 1 kwa 558
OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 249,271
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 8,487
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 100,927
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 5,183
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 751
OFESI YA NTHAMBI: FACATATIVÁ
[Chithunzi patsamba 9]
Ogwira ntchito pa ofesi ya nthambi ndi amishonale mu 1956
[Chithunzi patsamba 9]
Chinthunzi chojambulidwira m’mlengalenga cha ofesi yanthambi