Magwero a Kulimba Mtima Kosalephera
“PHOKOSO laukali linatichititsa kuima mwadzidzidzi. Kenako, mbalame ziŵiri zitatambasula mapiko zinathamanga kulinga kwa ife kuchokera pachitsamba chakumanzere. Patsogolo pathu, tinaona mazira aŵiri ali pamalo okumbika pang’ono. Mbalamezo zinali zitatiletsa kuponda chisa chawo mwangozi. Nthaŵi iliyonse pamene tinayesa kufika pafupi kuti tijambule chithunzi cha mazira okongolawo a madontho ofiirira, mbalamezo zinabwerezanso kuwopseza kwawo. ‘Nkulimba mtima kotani nanga,’ tinalingalira motero.”
Chimenecho chinali chokumana nacho cha achikulire anayi pofika pafupi ndi chisa cha mbalame ya maŵanga yotchedwa dikkop. Mbalame yocheperapo ndiyo blacksmith plover. M’buku lakuti Everyone’s Guide to South African Birds, akatswiri a mbalame Sinclair ndi Mendelsohn akufotokoza kuti: “Mbalame ziŵiri zoswa ana yaimuna ndi yaikazi zimatetezera chisa chawo ndi ana mwamphamvu ndipo zimakhala zaukali kwambiri ngati pafika mdani aliyense. Izo sizimaopa ukulu wa woloŵererayo ndipo zimauluka m’mwamba zikumalira mwaukali, ndi kudziponya pansi mwamphamvu ndi mopanda mantha ngakhale pa anthu zikumayesa kuwathamangitsa.”
Ena aona njovu zazikulu zikumayenda mosadziŵa kulinga ku chisa cha mbalame ya blacksmith plover, ndi kuputa machitidwe akuwopseza a mbalameyo. Kaŵirikaŵiri njovu zimagonja mwa kukhotera kwina.
Kodi mbalame zimapeza kuti kulimba mtima koteroko? Kumachokera kwa Uyo amene anazilenga. Yehova Mulungu analenga zolengedwa zazing’ono zimenezi ndi machitidwe achibadwa kuti ziletse nyama zazikulu kuwononga zisa zawo kapena anapiye awo.
Phunziro kwa Akristu
Akristu angatengepo phunziro pa zimenezi, ngakhale kuti amafuna kuchita zoposa pa kulimba mtima kwachibadwa. Iwo amafunikira kutsanzira Mbuye wawo, Yesu Kristu, yemwe anamvera malamulo a Mulungu mopanda mantha. (Ahebri 12:1-3) Baibulo limatsutsa amantha omwe amawopa kutumikira Mulungu. (Ahebri 10:39; Chivumbulutso 21:8) Panthaŵi imodzimodziyo, Yehova amazindikira chipangidwe chathu chopanda ungwiro ndipo amadziŵa kuti nthaŵi zina tikhoza kuchimwa kapena kusoŵa kulimba mtima kofunikira kuti tichite chifuniro chake mokwanira. (Salmo 103:12-14) Kodi munthu angachitenji ngati mantha amlepheretsa kuchita choyenera?
Mkristu ayenera kutembenukira kwa Mulungu ndi kupempherera nyonga yakuti ayang’anizane ndi mayesero ndi kupitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu. Baibulo lili ndi lonjezo lolimbikitsa limeneli la chithandizo cha Yehova lakuti: “Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziwombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yesaya 40:29-31) Anthu ambiri opanda ungwiro aona choonadi cha mawu ameneŵa ndipo kuchokera pa ‘kukhala ofooka akhalitsidwa amphamvu.’ (Ahebri 11:34) Chitsanzo chabwino chinali mtumwi Paulo Wachikristu, yemwe analemba kuti: “Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konse konse, ndi amitundu onse amve.”—2 Timoteo 4:17.
Ngakhale okondwerera atsopano omwe afuna kukhala otsatira a Yesu Kristu akhoza kulandira chithandizo chopatsa nyonga choterocho. Talingalirani za mwamuna wina wa ku South Africa wotchedwa Henry, yemwe anali msungi chuma wa tchalitchi chake ndipo ankakhala moyandikana khomo ndi pasitala wake. Henry ankafunafuna choonadi. Mosasamala kanthu za kugwirizana kwake ndi tchalitchicho, tsiku lina anavomera kuchititsidwa phunziro la Baibulo lapanyumba laulere ndi Mboni za Yehova. M’kupita kwa nthaŵi, anasonyeza chikhumbo cha kukhala Mboni ndipo anafunsa zimene anafunikira kuchita kuti afikire chonulirapo chimenecho. Anamlongosolera kuti choyamba iye anafunikira kuchoka ku tchalitchi chake. (Chivumbulutso 18:4) Popeza kuti pasitalayo anali woyandikana naye khomo ndi bwenzi, Henry anaona kuti sakanakhoza kulemba kalata ya kuchoka ku tchalitchicho koma kuti anafunikira kufotokoza nkhaniyo maso ndi maso. Iye anachitadi zimenezo molimba mtima.
Pasitalayo anadabwa kwambiri ndipo pambuyo pake anatenga tcheyamani wa chigawo chake ndi ziŵalo zina za tchalitchi kukaonana ndi Henry. Iwo anafuna kudziŵa chifukwa chake iye anasiya tchalitchi chake ndi kukhala chiŵalo cha chipembedzo chimene, malinga ndi kunena kwawo, chilibe mzimu woyera wa Mulungu. “Poyamba, ndinachita mantha kuwayankha,” anafotokoza motero Henry, “chifukwa chakuti nthaŵi zonse iwo anali ndi chisonkhezero chachikulu kwambiri pa ine. Koma ndinapempherera thandizo kwa Yehova, ndipo anandikhozetsa kupereka chodzikanira ichi: ‘Pa zipembedzo zonse kuzungulira dziko lonse, kodi ndi chiti chokha chimene chimagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova? Kodi sindicho cha Mboni za Yehova? Kodi mukulingalira kuti Mulungu akanalola iwo kutchedwa ndi dzina lake ndi kusawapatsanso mzimu wake woyera?’” Akuluakulu a tchalitchiwo analephera kutsutsa kalingaliridwe kameneko. Moyamikira chidziŵitso ndi nyonga zimene Mulungu amapereka, Henry tsopano amakhala ndi phande molimba mtima mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba pamodzi ndi Mboni za Yehova.
Inde, kukhala Mkristu woona kumafuna kulimba mtima. Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, ziyeso za chikhulupiriro zidzawonjezereka. Satana akufuna kulanda atumiki a Mulungu chiyembekezo chawo chabwino koposa cha moyo wosatha mwa kuyesa kuswa umphumphu wawo kwa Yehova. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 2:10.) Koma sitiyenera kuleka. Ngakhale ngati tibwevuka kwakanthaŵi chifukwa cha mantha, Yehova akhoza kutithandiza kulimbanso. Pitirizani kuyang’ana kwa iye kaamba ka nyonga ya kupitiriza kuchita chifuniro chake. Kumbukirani, iye amene analenga mbalame zopanda mantha alinso Magwero a kulimba mtima kosalephera. Ndithudi, Akristu oona ayenera “kukhala olimba mtima ndi kunena: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzawopa. Adzandichitanji munthu?’”—Ahebri 13:6, NW.