Kodi Mulungu Ali Pamalo Oyamba m’Banja Lanu?
“Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse.”—MARKO 12:29, 30.
1. Kodi nchifukwa ninji kukonda kwathu Yehova kuli kofunika?
“LAMULO la mtsogolo la onse ndi liti?” mlembi anafunsa Yesu. M’malo mopereka malingaliro ake, Yesu anayankha funso lakelo mwa kugwira Mawu a Mulungu pa Deuteronomo 6:4, 5. Anayankha kuti: “La mtsogolo ndili, Mvera, Israyeli; [Yehova, NW] Mulungu wathu, [Yehova] ndiye mmodzi; ndipo uzikonda [Yehova] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.”—Marko 12:28-30.
2. (a) Kodi Yesu anayang’anizana ndi chitsutso chotani? (b) Kodi nchiyani nthaŵi zina chimene chingachititse kukondweretsa kwathu Yehova kukhala kovuta?
2 Kumvera lamulo limene Yesu anati ndi la mtsogolo—lofunika koposa—kumafuna kuti tizichita zokondweretsa Yehova nthaŵi zonse. Yesu anachita zimenezo, ngakhale kuti nthaŵi ina mtumwi Petro anatsutsa zochita za Yesu, ndipo nthaŵi inanso achibale ake enieni anamtsutsa. (Mateyu 16:21-23; Marko 3:21; Yohane 8:29) Nanga bwanji ngati mwapezeka mumkhalidwe wonga umenewo? Tinene kuti apabanja lanu akufuna kuti musiye kuphunzira Baibulo ndi kuyanjana ndi Mboni za Yehova. Kodi mudzaika Mulungu pamalo oyamba mwa kuchita zomkondweretsa? Kodi Mulungu ali pamalo oyamba, ngakhale pamene apabanja angatsutse kuyesayesa kwanu kumtumikira?
Msampha wa Chitsutso cha Apabanja
3. (a) Kodi ziphunzitso za Yesu zingakhale ndi ziyambukiro zotani pa banja? (b) Kodi apabanja angasonyeze motani amene amamkonda kwambiri?
3 Yesu sanachepse zovuta zimene zingakhalepo pamene ena m’banja atsutsa wapabanja amene walandira ziphunzitso zake. “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake,” Yesu anatero. Komabe, mosasamala kanthu za zotulukapo zachisoni zimenezo, Yesu anasonyeza amene ayenera kukhala pamalo oyamba mwa kunena kuti: “Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa ine, sayenera ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa ine, sayenera ine.” (Mateyu 10:34-37) Timaika Yehova Mulungu pamalo oyamba mwa kutsatira ziphunzitso za Mwana wake, Yesu Kristu, amene ali “chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe [cha Mulungu].”—Ahebri 1:3; Yohane 14:9.
4. (a) Kodi Yesu anati kukhala wotsatira wake kumatanthauzanji? (b) Kodi Akristu ayenera kuda apabanja pawo m’lingaliro lotani?
4 Nthaŵi ina pamene Yesu anali kufotokoza zimene kukhala wotsatira wake woona kumatanthauza kwenikweni, anati: “Munthu akadza kwa ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:26) Mwachionekere Yesu sanatanthauze kuti otsatira ake ayenera kudadi apabanja lawo, pakuti analamula anthu kukonda ndi adani awo omwe. (Mateyu 5:44) M’malo mwake, Yesu panopa anatanthauza kuti otsatira ake ayenera kukonda apabanja mocheperapo ndi mmene amakondera Mulungu. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:24.) Mogwirizana ndi chidziŵitso chimenecho, Baibulo limati Yakobo “anamuda” Leya nakonda Rakele, kutanthauza kuti sanakonde Leya monga momwe anakondera mphwake, Rakele. (Genesis 29:30-32) Yesu anati, ngakhale “moyo” wathu weniweni tiyenera kuuda kapena kuukonda mocheperapo kuposa Yehova!
5. Kodi Satana mwamachenjera amadyerera motani kakonzedwe ka banja?
5 Pokhala Mlengi ndi Mpatsi wa Moyo, Yehova amayenerera kulambira konse kwa atumiki ake. (Chivumbulutso 4:11) “Ndipinda maondo anga kwa Atate,” analemba motero mtumwi Paulo, “amene kuchokera kwa iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina.” (Aefeso 3:14, 15) Yehova analenga kakonzedwe ka banja mwa njira yabwino kwambiri kwakuti apabanja ali ndi chikondi chachibadwa kwa wina ndi mnzake. (1 Mafumu 3:25, 26; 1 Atesalonika 2:7) Komabe, Satana Mdyerekezi mwamachenjera amadyerera chikondi chachibadwa chimenechi cha pabanja, chimene chimaphatikizapo chikhumbo cha kukondweretsa okondedwa a munthu. Amasonkhezera chitsutso cha banja, ndipo ambiri kumawavuta kuchirimika pa choonadi cha Baibulo atayang’anizana nacho.—Chivumbulutso 12:9, 12.
Kulimbana ndi Vutolo
6, 7. (a) Kodi apabanja angathandizidwe motani kuzindikira kufunika kwake kwa phunziro la Baibulo ndi kuyanjana ndi Akristu? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti timakondadi apabanja pathu?
6 Kodi mungachitenji ngati mwakakamizika kusankhapo kukondweretsa Mulungu kapena kukondweretsa wapabanja? Kodi mungachepse nkhaniyo mwa kuganiza kuti Mulungu amamvetsetsa ngati tileka kuphunzira Mawu ake ndi kutsatira zitsogozo zake pamene kuphunzirako kugaŵanitsa banja? Koma tangoganizirani. Mukagonja ndi kusiya kuphunzira Baibulo kapena kuyanjana ndi Mboni za Yehova, kodi okondedwa anu adzadziŵa bwanji kuti chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo ndi nkhani ya moyo ndi imfa?—Yohane 17:3; 2 Atesalonika 1:6-8.
7 Tingafanizire nkhani imeneyi motere: Mwinamwake wina wapabanja amakonda moŵa mopambanitsa. Kodi kulinyalanyaza kapena kulilekerera vuto lake la kumwa moŵa kudzampindulitsadi iye? Kodi kungakhale bwino kumlekerera ndi kusachitapo kalikonse pa vutolo kotero kuti musasokoneze mtendere? Iyayi, mungavomereze kuti kungakhale bwino kuyesa kumthandiza kuthetsa vuto lake la kumwa, ngakhale ngati kungafune kulimbana ndi mkwiyo ndi ziwopsezo zake. (Miyambo 29:25) Momwemonso, ngati mumakondadi apabanja lanu, simudzagonja pa zoyesayesa zawo za kukuletsani kuphunzira Baibulo. (Machitidwe 5:29) Mungawathandize kuzindikira kuti kutsatira ziphunzitso za Kristu ndiko moyo wathu weniweni mwa kuchirimika basi.
8. Kodi kuchita kwa Yesu chifuniro cha Mulungu mokhulupirika kumatipindulitsa motani?
8 Kuika Mulungu pamalo oyamba kungakhale kovuta kwambiri nthaŵi zina. Koma kumbukirani, Satana anachititsa Yesu kuvutika pochita chifuniro cha Mulungu. Komabe Yesu sanasiye; anapirira ngakhale ululu wa pamtengo wozunzirapo kaamba ka ife. “Yesu Kristu [ndiye] Mpulumutsi wathu,” limatero Baibulo. “Anafa m’malo mwathu.” (Tito 3:6; 1 Atesalonika 5:10) Kodi sitikuyamikira kuti Yesu sanagonje potsutsidwa? Popeza anapirira imfa ya nsembe, tili ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano la mtendere lolungama mwa kukhulupirira m’mwazi wake wokhetsedwa.—Yohane 3:16, 36; Chivumbulutso 21:3, 4.
Mfupo Yaikulu Imene Ingakhalepo
9. (a) Kodi Akristu angathandizire motani kupulumutsa ena? (b) Kodi mkhalidwe pabanja la Timoteo unali wotani?
9 Kodi mukudziŵa kuti inunso mungakhale ndi mbali ya kupulumutsa ena, ndi achibale anu okondedwa omwe? Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Uzikhala mu izi [zimene waphunzira]; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Timoteo anali m’banja logaŵanika, atate wake Achigiriki anali osakhulupirira. (Machitidwe 16:1; 2 Timoteo 1:5; 3:14) Ngakhale kuti sitidziŵa ngati atate wake Timoteo anakhala wokhulupirira, koma ngati anatero chiyenera kuti chinali chifukwa cha khalidwe lokhulupirika la mkazi wawo, Yunike, ndi la Timoteo.
10. Kodi Akristu angachitenji kuthandiza anzawo osakhulupirira?
10 Malemba amasonyeza kuti amuna ndi akazi amene amachirikiza kwambiri choonadi cha Baibulo angathandizire kupulumutsa anzawo a mu ukwati amene saali Akristu mwa kuwathandiza kukhala okhulupirira. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Pakuti udziŵa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziŵa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?” (1 Akorinto 7:12, 13, 16) Mtumwi Petro anafotokoza mmene akazi kwenikweni angapulumutsire amuna awo, akumalimbikitsa kuti: “Mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi.”—1 Petro 3:1.
11, 12. (a) Kodi Akristu zikwi zambiri apata mfupo yotani, ndipo anachitanji kuti ailandire? (b) Simbani chokumana nacho cha wapabanja wina amene anafupidwa chifukwa cha kupirira mokhulupirika.
11 Zaka zaposachedwa anthu zikwi zambiri akhala Mboni za Yehova pambuyo potsutsa zochita Zachikristu za achibale awo omwe ali Mboni kwa miyezi yambiri ngakhale zaka zambiri. Imeneyi ndi mfupo yotani nanga kwa Akristu amene akhalabe ochirimika, ndipo ndi dalitso lotani nanga kwa aja amene kale anali otsutsa! Polankhula ndi mawu achisoni, mkulu wina Wachikristu wazaka 74 anasimba kuti: “Ndimathokoza mkazi wanga ndi ana anga nthaŵi zambiri chifukwa chogwiritsa choonadi pazaka zimene ndinawatsutsa.” Anati kwa zaka zitatu iye analetseratu ngakhale mkazi wake kulankhula naye za Baibulo. “Koma anandichenjerera,” anatero, “nayamba kundichitira umboni pondisisita kumapazi. Ndikuthokoza chotani nanga kuti sanagonje pa chitsutso changa!”
12 Mwamuna winanso amene anatsutsa banja lake analemba kuti: ‘Ndinali mdani woipitsitsa wa mkazi wanga chifukwa chakuti atalandira choonadi, ndinamuwopsa, ndipo tinali kulongolola masiku onse; ndiko kuti, ndinayambitsa kulongololako nthaŵi zonse. Koma zinali zosaphula kanthu; mkazi wanga sanalisiye Baibulo. Panapita zaka khumi ndi ziŵiri ndikumalimbana zowopsa ndi choonadi, ndi mkazi wanga ndi mwana. Kwa aŵiriŵa, ndinali ngati Mdyerekezi weniweni.’ M’kupita kwa nthaŵi mwamunayo anayamba kulingalira za zochita zake. ‘Ndinaona nkhanza yomwe ndinali nayo,’ anafotokoza motero. ‘Ndinaŵerenga Baibulo, ndipo chifukwa cha malangizo ake, ndine Mboni yobatizidwa tsopano.’ Tangolingalirani za mfupo yaikulu imene mkazi wake anapeza, inde, kuthandiza ‘kupulumutsa mwamuna wake’ mwa kupirira chitsutso chake mokhulupirika zaka 12!
Kuphunzira kwa Yesu
13. (a) Kodi ndi phunziro lalikulu lotani limene amuna ndi akazi ayenera kutengapo pa moyo wa Yesu? (b) Kodi anthu amene kumawavuta kugonjera Mulungu angapindule motani ndi chitsanzo cha Yesu?
13 Phunziro lalikulu limene amuna ndi akazi ayenera kuphunzira pa moyo wa Yesu ndilo kumvera Mulungu. “Ndichita ine zimene zimkondweretsa iye nthaŵi zonse,” anatero Yesu. “Sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.” (Yohane 5:30; 8:29) Ngakhale panthaŵi imene Yesu anapeza kuti mbali ina ya chifuniro cha Mulungu inali yoŵaŵa, anamvera. “Mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine,” anapemphera motero. Koma mwamsanga anawonjezera kuti: “Koma sikufuna kwanga ayi, koma kwanu kuchitike.” (Luka 22:42) Yesu sanapemphe Mulungu kusintha chifuniro Chake ayi; anasonyeza kuti anakondadi Mulungu mwa kugonjera momvera pa chilichonse chimene chinali chifuniro cha Mulungu kwa iye. (1 Yohane 5:3) Kuika chifuniro cha Mulungu pamalo oyamba nthaŵi zonse, monga anachita Yesu, nkofunika kwambiri kuti munthu apambane pa umbeta ndiponso mu ukwati ndi m’banja. Talingalirani chifukwa chake zili choncho.
14. Kodi Akristu ena amalingalira motani zosayenera?
14 Monga taonera kale, pamene okhulupirira aika Mulungu pamalo oyamba, amakonda kukhala ndi anzawo osakhulupirira ndipo nthaŵi zambiri akhoza kuwathandiza kuyenerera chipulumutso. Ngakhale pamene okwatirana ali okhulupirira, ukwati wawo ungakhalebe wovuta kwambiri. Chifukwa cha zikhoterero zauchimo, amuna ndi akazi samasonyezana chikondi nthaŵi zina. (Aroma 7:19, 20; 1 Akorinto 7:28) Ena amafika ngakhale pa kufuna kukwatira wina, ngakhale kuti alibe zifukwa za m’Malemba zolekerana. (Mateyu 19:9; Ahebri 13:4) Amayesa kuti zimenezi nzabwino kwa iwo, kuti chifuniro cha Mulungu kwa mwamuna ndi mkazi cha kukhalira pamodzi nchovuta kwambiri. (Malaki 2:16; Mateyu 19:5, 6) Imeneyi mosakayika ndi njira ina yotsatira zolingalira zaumunthu m’malo mwa zija za Mulungu.
15. Kodi nchifukwa ninji kuika Mulungu pamalo oyamba kuli chinjirizo?
15 Kuika Mulungu pamalo oyamba kuli chinjirizo lotani nanga! Okwatirana amene amatero amayesayesa kumamatirana ndi kuthetsa mavuto awo mwa kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu. Motero amapeŵa kuŵaŵa mtima kwa mtundu uliwonse kumene kumakhalapo chifukwa chonyalanyaza chifuniro chake. (Salmo 19:7-11) Zimenezi zikusonyezedwa ndi chomwe chinachitikira achichepere ena okwatirana amene anasankhapo kutsatira uphungu wa Baibulo atatsala pang’ono kulekana. Patapita zaka zambiri, pamene mkazi anasinkhasinkha za chimwemwe anali nacho mu ukwati wawo, anati: “Ndimakhala pansi ndi kulira ndikaganizira zakuti ndikanalekana ndi mwamuna wanga zaka zonsezi. Ndiyeno ndimapemphera kwa Yehova Mulungu kumyamikira kaamba ka uphungu wake ndi chitsogozo zimene zinatigwirizanitsa pa unansi wachimwemwe umenewo.”
Amuna, Akazi—Tsanzirani Kristu!
16. Kodi Yesu anaikira amuna ndi akazi omwe chitsanzo chotani?
16 Yesu, amene nthaŵi zonse anaika Mulungu pamalo oyamba, anaikira amuna ndi akazi omwe chitsanzo chabwino koposa, ndipo iwo ayenera kuchitsatira mosamalitsa. Amuna akulimbikitsidwa kutsanzira mmene Yesu amachitira umutu mwachikondi pa anthu a mumpingo Wachikristu. (Aefeso 5:23) Ndipo akazi Achikristu angaphunzirepo pa chitsanzo cha Yesu changwiro cha kugonjera Mulungu.—1 Akorinto 11:3.
17, 18. Kodi ndi m’njira zotani zimene Yesu anaikira amuna chitsanzo chabwino?
17 Baibulo limalamula kuti: “Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda [mpingo, NW], nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5:25) Njira yofunika imene Yesu anasonyezera chikondi chake pampingo wa otsatira ake inali mwa kukhala bwenzi lawo lapamtima. “Ndatcha inu abwenzi,” anatero Yesu, “chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.” (Yohane 15:15) Talingalirani za nthaŵi yonse imene Yesu anawononga akumalankhula ndi ophunzira ake—makambirano ambiri amene anachita nawo—ndi chidaliro chimene anaika mwa iwo! Kodi chimenecho si chitsanzo chabwino koposa kwa amuna?
18 Yesu anasamala kwambiri za ophunzira ake ndipo anali kuwakonda zedi. (Yohane 13:1) Pamene iwo sanamvetse ziphunzitso zake, iye moleza mtima anamveketsa nkhanizo mseri imodzi ndi imodzi. (Mateyu 13:36-43) Amuna inu, kodi mumaona ubwino wauzimu wa mkazi wanu kukhala nkhani yofunika mofananamo? Kodi mumacheza naye, mukumatsimikizira kuti aŵirinu muli ndi choonadi cha Baibulo chomveka m’maganizo ndi mumtima mwanu? Yesu anatsagana nawo atumwi ake mu utumiki, mwinamwake akumawaphunzitsa aliyense payekha. Kodi mumatsagana naye mkazi wanu mu utumiki, kupita naye kunyumba ndi nyumba ndi kukachititsa maphunziro a Baibulo?
19. Kodi nchifukwa ninji njira imene Yesu anachitira ndi zofooka zobwerezabwereza za atumwi ake inakhala chitsanzo kwa amuna?
19 Makamaka pochita ndi zofooka za atumwi ake, Yesu anapereka chitsanzo chopambana kwa amuna. Pachakudya chake chomaliza ndi atumwi ake, anaona kuti iwo anali kubwerezanso kusonyeza mzimu wa mkangano. Kodi anawadzudzula mwaukali? Iyayi, m’malo mwake anasambitsa mapazi awo onse modzichepetsa. (Marko 9:33-37; 10:35-45; Yohane 13:2-17) Kodi mumasonyeza kuleza mtima kotero kwa mkazi wanu? M’malo mwa kudandaula za chifooko chake chobwerezabwereza, kodi mumayesa kumthandiza moleza mtima ndi kumfika pamtima mwa chitsanzo chanu? Mwachionekere akazi amachiona chifundo ndi chikondi chotero, monga anachita atumwiwo pomalizira pake.
20. Kodi akazi Achikristu sayenera kuiŵala chiyani, ndipo ndani amene ali chitsanzo chawo?
20 Akazinso afunika kulingalira za Yesu, amene sanaiŵale konse kuti “mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” Nthaŵi zonse anagonjera kwa Atate wake wakumwamba. Momwemonso, akazi sayenera kuiŵala konse kuti “mutu wa mkazi ndiye mwamuna,” inde, kuti amuna awo ndiwo mutu wawo. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23) Mtumwi Petro analimbikitsa akazi Achikristu kulingalira chitsanzo cha “akazi oyera mtima” akale, makamaka chija cha Sara, amene “anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye.”—1 Petro 3:5, 6.
21. Kodi nchifukwa ninji ukwati wa Abrahamu ndi Sara unapambana pamene wa Loti ndi mkazi wake unalephera?
21 Mwachionekere Sara anasiya nyumba yabwino mumzinda wotukuka napita kukakhala m’mahema kudziko lachilendo. Chifukwa? Chifukwa chakuti anafuna moyowo? Ayi. Kodi chinali chifukwa chakuti mwamuna wake anampempha kupita naye? Mosakayikira chimenechi chinali chifukwa china, pakuti Sara anali kukonda Abrahamu ndipo anali kumlemekeza kaamba ka mikhalidwe yake yaumulungu. (Genesis 18:12) Koma chifukwa chachikulu chimene anapitira ndi mwamuna wake chinali chikondi chake pa Yehova ndi chikhumbo chake chachikulu cha kutsatira chitsogozo cha Mulungu. (Genesis 12:1) Kumvera Mulungu kunamkondweretsa iye. Komabe, mkazi wa Loti anazengereza kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo anayang’ana kumbuyo mokhumbira zinthu zotsala mumzinda wakwawo wa Sodomu. (Genesis 19:15, 25, 26; Luka 17:32) Ukwati umenewo unatha ndi tsoka lalikulu chotani nanga—chifukwa chabe cha kusamvera kwake Mulungu!
22. (a) Kodi ndi kudzipenda kotani kumene apabanja ayenera kuchita mwanzeru? (b) Kodi tidzalingalira za chiyani m’nkhani yathu yotsatira?
22 Chotero pokhala mwamuna kapena mkazi, mufunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu ali pamalo oyamba m’banja lathu? Kodi ndimayesayesa kukwaniritsa mbali ya m’banja imene Mulungu wandipatsa? Kodi ndimayesayesa mwakhama kukonda mnzanga ndi kumthandiza kupeza kapena kusunga unansi wabwino ndi Yehova?’ Mabanja ambiri alinso ndi ana. M’nkhani yotsatira tidzalingalira za mbali ya makolo ndi kufunika kwa aŵiriwo ndi ana awo kuika Mulungu pamalo oyamba.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ziyambukiro za ziphunzitso za Yesu zingakhale zotani pamabanja ambiri?
◻ Kodi zikwi za Akristu olimbika alandira mfupo yotani?
◻ Kodi chimene chingathandize okwatirana kupeŵa chisembwere ndi kulekana nchiyani?
◻ Kodi chitsanzo cha Yesu chingawaphunzitse chiyani amuna?
◻ Kodi akazi angathandizire motani kuti ukwati wawo ukhale wachimwemwe?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi Sara anathandizira motani ukwati wake kupambana?