Olengeza Ufumu Akusimba
Kuchitira Umboni Kubala Zipatso Panyumba ndi Kusukulu
UMOYO wa Mkristu umaphatikizapo kuchitira ena zabwino, makamaka mwa kugaŵana nawo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Miyambo 3:27 imati: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.” Ku Argentina Mboni yachichepere m’chaka chake chachitatu cha sukulu ya sekondale inafuna kugaŵana uthenga wabwino wa Ufumu ndi mnzake wa pasukulu. Kuchita kwake motero kunali ndi zotulukapo zabwino kwambiri.
Tsiku lina Mboni yachichepereyo inanena kwa mnzake kuti si zipembedzo zonse zimene zili zabwino. Pamene wachichepereyo anayankha kuti sanachite chilichonse choipa, Mboniyo inati: “Ndipo sumachitiranso Mulungu kalikonse.” Zimenezi zinapangitsa wachichepereyo kulingalirapo. Pambuyo pake Mboniyo inafotokoza kuti ano ndiwo masiku otsiriza ndi kunena kuti, kuti munthu akhale ndi chiyanjo cha Mulungu, ayenera kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka ndi kuchigwiritsira ntchito. Mnzakeyo wa pasukulu anavomereza. Koma kodi banja lake linamvomereza kukhala ndi phunziro la Baibulo? Kuti apatse bwenzi lake chinachake cholingalirapo, Mboniyo inampempha kuti aŵerenge buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi Kosatha.
Nthaŵi inapitapo, ndipo mnzakeyo anasiya sukulu. Sikunamveke kalikonse za iye kwa nthaŵi yoposa chaka chimodzi. Ndiyeno tsiku lina Mboni yachichepereyo inadabwa kulandira foni kuchokera kwa mnzake amene ananena kuti anaona kuti maulosi a Baibulo anali kukwaniritsidwadi. Panthaŵi yomweyo Mboniyo inalinganiza kuphunzira naye Baibulo.
Pamene anapita kunyumba ya mnzake wa pasukulu wakale, anaona kuti makolo a mnzakeyo anali odera nkhaŵa ndi zimene mwana wawo anali kudziloŵetsamo. Ngakhale mng’ono wa mnzakeyo analingalira kuti anali kusokonekera maganizo. Motero makolo anauza mng’ono wake kutsutsa pa phunziro lotsatira. Pambuyo pake, ndi misozi m’maso mwake, wachichepereyu anauza makolo ake kuti mkulu wake sanali wosokonekera maganizo, zimene zinachititsa amayi ake kudandaula kuti, “M’malo mwa vuto limodzi, tsopano ndakhala ndi aŵiri!”
Motero, pa phunziro lotsatirapo amakewo anakhalapo ndipo anavomereza kuti anyamatawo sanali osokonekera maganizo. Pambuyo pake phunziro la Baibulo la amakewo ndi amuna awo linalinganizidwa. Posapita nthaŵi banja lonse linayamba kupezeka pamisonkhano ya mpingo pa Nyumba ya Ufumu. M’kupita kwa nthaŵi, agogo ake nawonso anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kupita ku misonkhano. Kuyambira pamenepo, wachichepere woyambayo anabatizidwa. Anakwatira, ndipo iye ndi mkazi wake ali ofalitsa achangu.
Ndiponso, mwa ulaliki wamwamwaŵi kusukulu, Mboni yachichepereyo yathandiza anzake ena aŵiri a pasukulu pamodzinso ndi amayi ndi mlongo wa mmodzi wa iwo kuyamba kuphunzira Baibulo. Onse pamodzi, anthu 11 aphunzira choonadi cha Baibulo chifukwa chakuti Mboni yachichepereyo siinaleke kuchitira anzake a kusukulu chabwino. Ha! nchotulukapo chosangalatsa chotani nanga? Moonadi, “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15.