Senzani Yehova Nkhaŵa Yanu Nthaŵi Zonse
LEROLINO ambiri amalemetsedwa ndi nkhaŵa. Mavuto azachuma, mavuto osautsa a m’banja, matenda, zopweteka ndi kuvutika chifukwa cha kuponderezedwa ndi nkhanza, ndipo mavuto ena ambirimbiri amachita ngati mphero yoikidwa m’khosi mwawo. Kuwonjezera pa zitsenderezo zimenezi zakunja, enanso amalemetsedwa ndi kusadziŵerengera ndi kulephera kuchita zinthu chifukwa cha kusalungama kwawo. Ambiri amafuna kuleka kuchita zilizonse. Kodi mungachite motani pamene nkhaŵa zikhala zosapiririka?
Panthaŵi ina Mfumu Davide ya Israyeli inalingalira kuti chitsenderezo chake chinali chosapiririka. Malinga ndi kunena kwa Salmo 55, anasokonezeka maganizo ndi nkhaŵa chifukwa cha zitsenderezo ndi udani wa adani ake. Mtima wake unaŵaŵa ndipo anachita mantha. Ankangobuula chifukwa cha chisoni chake. (Salmo 55:2, 5, 17) Komabe, ngakhale kuti panali nsautso yonseyi, anapeza njira yoipiririra. Motani? Anayang’ana kwa Mulungu wake kaamba ka chichirikizo. Chilangizo chake kwa ena amene angamve monga momwe iyeyo anachitira nchakuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako.”—Salmo 55:22.
Kodi anatanthauzanji mwa kunena kuti “umsenze Yehova nkhaŵa zako”? Kodi ndi nkhani ya kungofikira Yehova mwapemphero ndi kufotokoza nkhaŵa yathu? Kapena kodi ife tingachite kanthu kena kuti tipeputse mkhalidwewo? Bwanji ngati tilingalira kuti tili osayenera konse kufikira Yehova? Tiyeni tione zimene Davide anatanthauza mwa kupenda zokumana nazo zina zimene mwina anakumbukira bwino pamene analemba mawu amenewo.
Chitani Zinthu ndi Nyonga ya Yehova
Kodi mukukumbukira mmene Goliati anawopsera amuna ankhondo a Israyeli? Chimphona chimenechi, choposa mamita 2.7 kutalika, chinawawopsa. (1 Samueli 17:4-11, 24) Koma Davide sanawope. Chifukwa ninji? Chifukwa sanayese kulimbana ndi Goliati ndi nyonga yake. Kuyambira pamene anadzozedwa kukhala mfumu ya Israyeli yamtsogolo, analola mzimu wa Mulungu kumtsogolera ndi kumlimbitsa m’zonse zimene anachita. (1 Samueli 16:13) Chotero iye anati kwa Goliati: “Ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza. Lerolino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa.” (1 Samueli 17:45, 46) Davide anali woponya mwala waluso, koma tikhulupirira kuti mzimu woyera wa Yehova unatsogolera mwala umene anauponya kwa Goliati ndi kuupatsa mphamvu ya kupha.—1 Samueli 17:48-51.
Davide anayang’anizana ndi chitokoso chachikuluchi ndi kulakika mwa kukhala ndi chidaliro chakuti Mulungu adzamchirikiza ndi kumlimbitsa. Anali atakulitsa unansi wabwino wodalirana ndi Mulungu. Mosakayikira zimenezi zinalimbitsidwa ndi njira imene Yehova anamlanditsira nayo poyamba. (1 Samueli 17:34-37) Monga Davide, inu mungasunge unansi wolimba wa inu mwini ndi Yehova ndi kukhala ndi chidaliro chotheratu m’kukhoza kwake ndi kufunitsitsa kwake kukulimbitsani ndi kukuchirikizani m’mikhalidwe yonse.—Salmo 34:7, 8.
Chitani Zonse Zomwe Mungathe Kuthetsa Vuto
Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti sipadzakhala nthaŵi za kuŵaŵidwa mtima, kuda nkhaŵa, ndipo ngakhale kuchita mantha, monga momwe Salmo 55 limasonyezera bwino lomwe. Mwachitsanzo, patapita zaka zina Davide atasonyeza kudalira Yehova kopanda mantha, anawopa kwambiri poyang’anizana ndi adani ake. Anadedwa ndi Mfumu Sauli ndipo anafunikira kuthaŵa kupulumutsa moyo wake. Yesani kuganizira nsautso imene zimenezi zinadzetsa kwa Davide, mafunso amene zinabutsa m’maganizo mwake ponena za kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Yehova. Ndiponso, iye anali atadzozedwa kudzakhala mfumu yamtsogolo ya Israyeli, komabe apa anafunikira kukhala ndi moyo monga wothaŵathaŵa m’chipululu, wosakidwa ngati nyama yakuthengo. Pamene anayesa kubisala mu mzinda wa Gati, kwawo kwa Goliati, anamzindikira. Nchiyani chimene chinachitika? Nkhaniyo imati “nawopa kwambiri.”—1 Samueli 21:10-12.
Koma sanalole mantha ndi nkhaŵa yake yaikulu kumletsa kufuna thandizo kwa Yehova. Malinga ndi Salmo 34 (lolembedwa chifukwa cha chokumana nacho chimenechi), Davide anati: “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse. Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m’masautso ake onse.”—Salmo 34:4, 6.
Zoonadi, Yehova anamchirikiza. Komabe onani kuti Davide sanangokhala ndi kuyembekezera Yehova kumpulumutsa. Anadziŵa kuti iye anafunikira kuchita zonse zomwe akanatha m’mikhalidweyo kuti awonjoke m’vuto lalikululo. Anadziŵa za dzanja la Yehova la chipulumutso chake, komanso iye mwiniyo anachitapo kanthu, akumachita ngati wamisala kuti mfumu ya Gati isamuphe. (1 Samueli 21:14–22:1) Nafenso tifunikira kuchita zonse zimene tingathe kulimbana ndi nkhaŵa, m’malo mwa kungoyembekezera Yehova kuti atipulumutse.—Yakobo 1:5, 6; 2:26.
Musawonjezere Zina pa Nkhaŵa Zanu
Davide anapeza phunziro lina pambuyo pake m’moyo wake, lopweteka kwambiri. Kodi linali lotani? Lakuti nthaŵi zina timawonjezera zina pa nkhaŵa zathu. Atagonjetsa Afilisti, zinthu zinayenda moipa kwa Davide pamene anasankha kusamutsa likasa la pangano kumka nalo ku Yerusalemu. Mbiriyo imatisimbira kuti: “Ndipo Davide ananyamuka, namuka nawo anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu. . . . Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, . . . ndipo Uza ndi Ahio ana a Abinadabu anayendetsa ng’ombe za pa galeta watsopanoyo.”—2 Samueli 6:2, 3.
Kunyamula Likasa pa galeta kunaswa malangizo onse amene Yehova anali atapereka ponena za ilo. Ananena mwachimvekere kuti onyamula ake okha ovomerezedwa, Alevi achikohati, ndiwo anayenera kunyamula Likasa pamapeŵa awo, akumagwiritsira ntchito mphiko zoloŵetsedwa mu mphete za pa Likasa. (Eksodo 25:13, 14; Numeri 4:15, 19; 7:7-9) Kunyalanyaza malangizo ameneŵa kunadzetsa tsoka. Pamene ng’ombe zokoka galeta zinatsala pang’ono kuligwetsa, Uza, amene mwachionekere anali Mlevi koma osati wansembe, anatambasula dzanja kuti achirikize Likasa ndipo anakanthidwa ndi Yehova chifukwa cha kupanda ulemu kwake.—2 Samueli 6:6, 7.
Davide monga mfumu analinso ndi mlandu wa kuchititsa zimenezi. Mchitidwe wake umasonyeza kuti ngakhale awo amene ali ndi unansi wabwino ndi Yehova nthaŵi zina angachite zinthu moipa pa mikhalidwe yoyesa. Choyamba Davide anakwiya. Ndiyeno anachita mantha. (2 Samueli 6:8, 9) Unansi wake wodalira Yehova unayesedwa kwambiri. Pachochitikachi iye mwachionekere analephera kusenza Yehova nkhaŵa yake, sanatsatire malamulo ake. Kodi mkhalidwewo ungakhale wotero kwa ife nthaŵi zina? Kodi timaimba mlandu Yehova wakuchititsa mavuto amene amakhalapo chifukwa chakuti tanyalanyaza malangizo ake?—Miyambo 19:3.
Kulimbana ndi Nkhaŵa ya Liwongo
Pambuyo pake, Davide anadzipangira nkhaŵa ya liwongo yaikulu mwa kuchimwira mowopsa miyezo ya Yehova yamakhalidwe. Pachochitika chimenechi Davide anali atatula udindo wake wa kutsogolera anyamata ake kunkhondo. Anatsalira ku Yerusalemu pamene iwo anapita kukamenya nkhondo. Zimenezi zinachititsa vuto lalikulu.—2 Samueli 11:1.
Mfumu Davide anaona Bateseba wokongola akusamba. Anachita naye chisembwere, ndipo anakhala ndi pakati. (2 Samueli 11:2-5) Poyesa kubisa khalidwe loipalo, analinganiza kuti mwamuna wa mkaziyo, Uriya, abwerere ku Yerusalemu kuchokera kunkhondo. Uriya anakana kugonana ndi mkazi wake pamene Israyeli anali kumenya nkhondo. (2 Samueli 11:6-11) Chotero tsopano Davide anagwiritsira ntchito njira ina yoipa ndi yonyenga kuti abise tchimo lake. Analinganiza kuti asilikali anzake a Uriya aike Uriya pamalo angozi m’nkhondoyo kuti aphedwe. Tchimo lalikulu kowopsa!—2 Samueli 11:12-17.
Zoonadi, potsirizira pake, tchimo la Davide linamtsatira, ndipo anavumbulidwa. (2 Samueli 12:7-12) Taganizirani za kulemetsa kwa chisoni ndi liwongo zomwe Davide ayenera kukhala anali nazo pamene anazindikira ukulu wa zimene anali atachita chifukwa cha chilakolako chake. Mwina analemetsedwa kwambiri chifukwa cha kulephera kwake, makamaka popeza kuti iye anali munthu wokhudzidwa mtima kwambiri. Mwina anadziona kukhala wachabechabe!
Komabe, mwamsanga Davide anavomera tchimo lake, akumanena kwa mneneri Natani kuti: “Ndinachimwira Yehova.” (2 Samueli 12:13) Salmo 51 limatiuza mmene anamvera ndi mmene anachondererera Yehova Mulungu kuti amuyeretse ndi kumkhululukira. Anapemphera kuti: “Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.” (Salmo 51:2, 3) Chifukwa chakuti analapadi, anali wokhoza kumanganso unansi wake wolimba ndi wapafupi ndi Yehova. Davide sanapitirize kulingalira moipidwa ndi kusadziŵerengera. Anasenza Yehova nkhaŵa zake mwa kuvomera tchimo lake modzichepetsa, akumasonyeza kulapa koona mtima, ndi kupempherera kwambiri chikhululukiro cha Yehova. Anapezanso chiyanjo cha Mulungu.—Salmo 51:7-12, 15-19.
Kulimbana ndi Kuperekedwa Kwake
Zimenezi zikutifikitsa pa chochitika china chimene chinasonkhezera Davide kulemba Salmo 55. Anali wopsinjika maganizo kwambiri. “Mtima wanga uŵaŵa mkati mwanga,” iye analemba motero, “ndipo zowopsa za imfa zandigwera.” (Salmo 55:4) Kodi nchiyani chinachititsa kuŵaŵa kwa mtima kumeneku? Abisalomu, mwana wa Davide, anapanga chiŵembu cha kulanda Davide ufumu. (2 Samueli 15:1-6) Chiŵembu chimenechi cha mwana wake chinali chovuta kwambiri kupirira, koma chimene chinachipangitsa kukhala choipa kwambiri chinali chakuti phungu wa Davide wodaliridwa kwambiri, munthu wotchedwa kuti Ahitofeli, anagwirizana ndi achiŵembu olimbana ndi Davide. Ndi Ahitofeli amene Davide akufotokoza pa Salmo 55:12-14. Monga chotulukapo cha chiŵembu ndi kuperekedwako, Davide anathaŵa mu Yerusalemu. (2 Samueli 15:13, 14) Zimenezi ziyenera kukhala zitamvutitsa maganizo chotani nanga!
Chikhalirechobe, sanalole kuvutika mtima kwake ndi chisoni kufooketsa chikhulupiriro ndi chidaliro chake pa Yehova. Anapemphera kwa Yehova kuti alepheretse zolinga za achiŵembuwo. (2 Samueli 15:30, 31) Kachiŵirinso tikuona kuti Davide sanangoyembekezera kuti Yehova achite zonse. Pamene mpata unapezeka, anachita zimene anakhoza kulimbana ndi chiŵembu chimene anampangira. Anatumiza phungu wake wina, Husai, kumka ku Yerusalemu kukachita ngati wagwirizana ndi achiŵembuwo, ngakhale kuti, kwenikweni, iyeyo anapita kumeneko kukachifooketsa. (2 Samueli 15:32-34) Limodzi ndi chichirikizo cha Yehova, njira imeneyi inagwira ntchito. Husai anapezetsa Davide nthaŵi yokwanira yakuti asonkhanitsenso anthu ake ndi kukonzekera kudzitetezera.—2 Samueli 17:14.
Ha, mmene Davide anayenera kukhalira woyamikira nanga chisamaliro chotetezera cha Yehova ndiponso kuleza mtima kwake ndi kufunitsitsa kukhululukira! (Salmo 34:18, 19; 51:17) Chili chifukwa cha zochitika zimenezi chimene Davide mwachidaliro amatilimbikitsa m’nthaŵi zathu zino zosautsa kutembenukira kwa Yehova kaamba ka thandizo, ‘kutaya nkhaŵa yathu yonse pa Yehova.’—Yerekezerani ndi 1 Petro 5:6, 7.
Kulitsani ndi Kusunga Unansi Wolimba ndi Wodalirana ndi Yehova
Kodi tingapeze motani mtundu wa unansi ndi Yehova umene Davide anali nawo, unansi umene unamlimbitsa m’nthaŵi za mayeso ndi chisautso chachikulu? Timakulitsa unansi wotero mwa kukhala ophunzira akhama a Mawu a Mulungu, Baibulo. Timamlola kutilangiza za malamulo ake, mapulinsipulo ake, ndi umunthu wake. (Salmo 19:7-11) Pamene tisinkhasinkha pa Mawu a Mulungu, timayandikira kwa iye ndi kuphunzira kumdalira kotheratu. (Salmo 143:1-5) Timazamitsa ndi kulimbitsa unansi umenewo pamene tiyanjana ndi olambira anzathu kuti tilangizidwe mowonjezereka ndi Yehova. (Salmo 122:1-4) Timakulitsa unansi wathu ndi Yehova mwa pemphero lochokera mumtima.—Salmo 55:1.
Zoonadi, Davide, mofanana nafe, anapsinjika mtima pamene unansi wake ndi Yehova unali wofooka mosiyana ndi mmene unafunikira. Nsautso ‘ingatiyalutse.’ (Mlaliki 7:7) Koma Yehova amaona zimene zikuchitika, ndipo amadziŵa zimene zili mumtima mwathu. (Mlaliki 4:1; 5:8) Tifunikira kugwira ntchito zolimba kuti unansi wathu ndi Yehova ukhale wamphamvu. Ndiyeno, pa nkhaŵa iliyonse imene tili nayo, tingadalire kuti Yehova adzaichotsa kapena adzatipatsa nyonga yolimbanira ndi mkhalidwe wathu. (Afilipi 4:6, 7, 13) Ndi nkhani ya kuyandikira kwathu kwa Yehova. Pamene Davide anachita zimenezi, anali wotetezerekadi.
Chotero, mulimonse mmene mikhalidwe yanu ingakhalire, akutero Davide, senzani Yehova nkhaŵa yanu nthaŵi zonse. Pamenepo tidzazindikiradi kuona kwa lonjezo lakuti: “Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”—Salmo 55:22.