“Mphindi Yakutonthola ndi Mphindi Yakulankhula”
KODI ndi kangati pamene mwadandaula kuti, “Bwenzi sindinanene zimenezo”? Komanso, mungakumbukire nthaŵi zina pamene munalephera kulankhula zimene zinali kukhosi. Pokumbukira zimenezo, mungakhale mutaganiza kuti, ‘Bwenzi ndikananenapo kanthu.’
Baibulo limati pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Apanso, mpamene pali vuto—kudziŵa mphindi yakulankhula ndi mphindi yakutonthola. Umunthu wathu wopanda ungwiro umatikakamiza kaŵirikaŵiri kuchita ndi kulankhula zinthu pamphindi yosayenera. (Aroma 7:19) Kodi tingalamulire motani lilime lathu losaweruzika?—Yakobo 3:2.
Njira Zolamulira Lilime
Kuti tithandizidwe kudziŵa mphindi yakulankhula ndi mphindi yakukhala chete, sitifunikira malamulo ochuluka olinganizidwa kukhudza mbali iliyonse imene ingakhaleko. M’malo mwake, tifunikira kutsogozedwa ndi mikhalidwe yofunika kwambiri pa umunthu wachikristu. Kodi mikhalidwe imeneyi njotani?
Yesu Kristu anafotokoza kuti chikondi ndicho mkhalidwe waukulu wosonkhezera ophunzira ake. “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake,” iye anatero. (Yohane 13:35) Pamene tisonyeza kwambiri chikondi cha pa abale chotero, mpamenenso tidzakhoza bwino kulamulira lilime lathu.
Mikhalidwe ina iŵiri yogwirizana nacho idzathandizanso kwambiri. Wina mwa imeneyi ndiwo kudzichepetsa. Kumatitheketsa ‘kuyesa anzathu kukhala otiposa ife eni.’ (Afilipi 2:3) Winawo ndiwo chifatso, chimene chimatichititsa kukhala “woleza.” (2 Timoteo 2:24, 25) Yesu Kristu ndiye chitsanzo changwiro cha mmene tiyenera kusonyezera mikhalidwe imeneyi.
Popeza nkovuta kwambiri kulamulira lilime lathu pamene tapanikizidwa, tiyeni tilingalire za usiku wotsatira imfa ya Yesu—nthaŵi pamene iye anali ‘wothedwa nzeru.’ (Mateyu 26:37, 38) Si zachilendo kuti Yesu anamva motero, popeza mtsogolo mosatha mwa anthu onse munadalira pa kukhala kwake wokhulupirika kwa Mulungu.—Aroma 5:19-21.
Iyitu inalidi nthaŵi yakuti Yesu alankhule kwa Atate wake wakumwamba. Chotero iye anachoka kupita kukapemphera, akumapempha atatu mwa ophunzira ake kudikira. Patapita nthaŵi pang’ono iye anadza nawapeza ali m’tulo. Ataona zimenezo anati kwa Petro: “Simukhoza kuchezera ndi ine mphindi imodzi?” Chidzudzulo chachikondi chimenechi chinatsagana ndi mawu omwe anasonyeza kumvetsetsa kwake kufooka kwawo. Iye anati: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.” Pambuyo pake, Yesu anabweranso napeza ophunzira ake ali m’tulo. Analankhula nawo mokoma mtima ndipo ‘anawasiya, napemphera kachitatu.’—Mateyu 26:36-44.
Pamene Yesu anapeza ophunzira ake ali m’tulo kachitatu, sanakalipe koma anati: “[Mukugona ndi kupumula panthaŵi ngati imeneyi! NW] Onani, nthaŵi yafika, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m’manja a ochimwa.” (Mateyu 26:45) Ndi munthu wa mtima wodzala chikondi, wofatsa ndi wodzichepetsadi, amene akanagwiritsira ntchito lilime lake mwanjira imeneyo panthaŵi yovuta chonchi.—Mateyu 11:29; Yohane 13:1.
Posapita nthaŵi, Yesu anagwidwa ndi kuzengedwa mlandu. Panopo tikuphunzira kuti nthaŵi zina ndi bwino kukhala chete, ngakhale pamene tili mu utumiki wathu wachikristu. Pofuna kumpezera chifukwa Yesu, ansembe aakulu sanafune konse kudziŵa choonadi. Chotero mumkhalidwe wovuta umenewo, Yesu anakhala chete.—Yerekezerani ndi Mateyu 7:6.
Komabe, Yesu sanakhale chete pamene mkulu wa ansembe ananena kuti: “Ndikulumbiritsa iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.” (Mateyu 26:63) Popeza anamlumbiritsa Yesu, inali nthaŵi yakuti iye alankhule. Chifukwa chake iye anayankha kuti: “Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pamitambo yakumwamba.”—Mateyu 26:64.
Patsiku lovutalo, Yesu analamulira mwangwiro lilime lake. Mwa iye, chikondi, chifatso, ndi kudzichepetsa zinali mbali zachibadwa za umunthu wake. Kodi tingagwiritsire ntchito motani mikhalidwe imeneyi kulamulira lilime lathu pamene tapanikizika?
Kulamulira Lilime Titakwiya
Titakwiya, nthaŵi zambiri timalephera kulamulira lilime lathu. Mwachitsanzo, Paulo ndi Barnaba anasemphana malingaliro tsiku lina. “Barnaba anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko. Koma sikunamkomera Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nawo kuntchito. Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake.”—Machitidwe 15:37-39
Michael,a amene wagwira ntchito zaka zingapo pantchito yomanga, akusimba kuti: “Panali munthu wina pamalo omangirapowo amene ndinali kumdziŵa ndi kumlemekeza. Koma ndinaona ngati kuti nthaŵi zambiri iye anali kupeza zifukwa ndi ntchito yanga. Zinandipweteka ndi kundikwiyitsa koma ndinabisa kukhumudwa kwangako. Tsiku lina zinthu zinafika poipa pamene anasuliza ntchito imene ndinali nditangoichita.
“Ndinasonyeza mkwiyo wanga wonse. Pokhala wokwiya, sindinaganize za chithunzi choipa chimene zimenezi zinasonyeza kwa otizinga. Tsiku lonselo, sindinafune kulankhula naye ngakhale kumuona. Ndikudziŵa tsopano kuti vutolo sindinalisamalire bwino. Zinthu zikanakhala bwino kwambiri ngati ndikanakhala chete ndi kulankhula pamene mtima wanga unakhala pansi.”
Mwaŵi wake ngwakuti chikondi chachikristu chinasonkhezera anthu aŵiriwa kuthetsa kusamvana kwawo. Michael akunena kuti: “Titalankhulana moona mtima, tinamvetsetsana bwino, ndipo tsopano tili paubwenzi wolimba.”
Malinga ndi zimene Michael anaphunzira, ngati takwiya, nthaŵi zina kumakhala kwanzeru kukhala chete. “Wofatsa mtima ali wanzeru,” imatero Miyambo 17:27. Nzeru ndi chikondi cha pa abale zidzatithandiza kulamulira chikhumbo chathu chofuna kubwetuka zoipa. Wina akatiputa, tiyeni tilankhule naye payekha mumzimu wachifatso ndi wodzichepetsa, ndi cholinga chokhazikitsanso mtendere. Bwanji ngati talongolola kale chifukwa cha mkwiyo? Pamenepo chikondi chidzatisonkhezera kupeŵa kunyada kwathu ndipo m’malo mwake kuyesa kuwongola zinthu modzichepetsa. Imeneyi ndiyo mphindi yakulankhula, kusonyeza chisoni pa zomwe munachita ndi kuchiritsa kuŵaŵa mtima mwa kulankhulana moona mtima.—Mateyu 5:23, 24.
Pamene Kukhala Chete Sikuthandiza
Mkwiyo kapena kuŵaŵidwa mtima kungatichititse kuleka kulankhula ndi munthu amene watiputa. Zimenezi zingakhale zovulaza kwambiri. “M’chaka choyamba cha ukwati wathu, panali nthaŵi pamene sindinali kulankhula kwa mwamuna wanga masiku angapo panthaŵi imodzi,” akutero María.b “Nthaŵi zambiri, sichinali chifukwa cha zovuta zazikulu koma, m’malo mwake, chifukwa cha kusunga zakukhosi pa tinthu tating’ono. Ndinali kuganizabe za zokwiyitsa zonsezo kufikira zitakhala chopinga chonga phiri. Ndiyeno nthaŵi inali kufika pamene ndinali kulephera kupirira, ndipo ndinali kungosiya kulankhula kwa mwamuna wanga kufikira mkwiyo utatha.”
María akuwonjezera kuti: “Lemba lina la Baibulo—‘dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire’—linandithandiza kusintha kalingaliridwe kanga. Ine ndi mwamuna wanga tinalimbikira kuwongolera kulankhulana kwathu kotero kuti zovuta sizinali kukula. Zakhala zovuta, koma pambuyo pokhala mu ukwati zaka khumi, ndili wokondwa kunena kuti nyengo zimenezi za kukhala du ngati omanga kukamwa nzakamodzikamodzi. Komabe, ndikuvomereza kuti ndikali kuyesayesa kulamulira khalidwe limeneli.”—Aefeso 4:26.
Malinga ndi zimene María anapeza, pamene anthu aŵiri sakumvana, kusiya kulankhulana sindiko kumathandiza. M’mikhalidwe imeneyo, zitheka kuti kuipidwa kungakule, ndipo unansiwo ungawonongeke. Yesu anati tiyenera ‘kufulumira kuyanjana.’ (Mateyu 5:25) “Mawu oyenera apanthaŵi yake” angatithandize ‘kulondola mtendere.’—Miyambo 25:11; 1 Petro 3:11.
Tifunikiranso kulankhula pamene tifuna thandizo. Ngati tikuvutika chifukwa cha vuto lina lauzimu, tingazengereze kuika mtolowo pa ena. Koma tikakhala chete, mwina vutolo lingakulireko. Akulu achikristu oikidwa amasamala za ife ndipo, tikawalola, amafunitsitsadi kutithandiza. Imeneyi ndiyo mphindi yakuti tilankhule.—Yakobo 5:13-16.
Koposa zonse, tiyenera kulankhula kwa Yehova nthaŵi zonse m’pemphero lochokera mumtima, monga momwe Yesu anachitira. Inde, tiyeni ‘titsanulire mitima yathu’ kwa Atate wathu wakumwamba.—Salmo 62:8; yerekezerani ndi Ahebri 5:7.
“Mphindi Yakulankhula” za Ufumu wa Mulungu
Utumiki wachikristu uli ntchito yaumulungu imene iyenera kuchitidwa mapeto asanafike. Chifukwa chake kuli kofunika kwambiri kuposa ndi kale lonse kuti atumiki a Yehova alengeze uthenga wabwino wa Ufumu. (Marko 13:10) Monga atumwi, Akristu oona ‘sangathe kuleka kulankhula zimene anaziona ndi kuzimva.’—Machitidwe 4:20.
Ndithudi, si aliyense amene afuna kumva uthenga wabwino. Kwenikweni, potumiza ophunzira ake kukalalikira, Yesu anawauza ‘kufunsitsa amene anali oyenera.’ Monga momwedi Yehova samakakamizira aliyense kumlambira, sitidzapitiriza kulankhula mouma mutu kwa munthu amene mwaliuma akukana uthenga wa Ufumu. (Mateyu 10:11-14) Koma timakonda kulankhula za ufumu wa Yehova kwa aja “ofuna moyo wosatha.”—Machitidwe 13:48, NW; Salmo 145:10-13.
Chikondi, chifatso, ndi kudzichepetsa ili mikhalidwe imene ingatithandize kulamulira chikhoterero chathu chopanda ungwiro cha kulankhula mwansontho kapena chokonda kukhaliratu chete. Pamene tikulitsa mikhalidwe imeneyi, tidzakhala okonzeka bwino kusiyanitsa mphindi yoyenera ndi mphindi yosayenera ya kulankhula.
[Mawu a M’munsi]
a Si dzina lake lenileni.
b Si dzina lake lenileni.
[Chithunzi patsamba 23]
Mavuto angathetsedwe mwa kulankhulana kwabwino