Kulepa Zochuluka Chifukwa cha Kanthu Kena Kokulirapo
YOSIMBIDWA NDI JULIUS OWO BELLO
Kwa zaka 32 ndinali Mwaladura.a Ndinakhulupirira kuti kuchiritsa mwachikhulupiriro ndi mapemphero zikanathetsa mavuto anga onse ndi kuchiritsa matenda onse. Sindinagule konse mankhwala alionse, osati ngakhale ongopha ululu. M’zaka zimenezozo, palibe wina m’banja langa yemwe anagonekedwapo m’chipatala. Nthaŵi zonse pamene aliyense wa ana anga anadwala, ndinawapempherera usana ndi usiku mpaka atachira. Ndinakhulupirira kuti Mulungu anali kuyankha mapemphero anga ndi kundidalitsa.
NDINALI wa Egbe Jolly, kalabu yotchuka kwambiri m’Akure, tauni ina chakumadzulo kwa Nigeria. Mabwenzi anga anali anthu olemera kopambana ndi amphamvu m’tauni yathu. Deji, mfumu ya Akure, kaŵirikaŵiri ankandichezera kunyumba kwanga.
Ndinalinso wamitala, ndi akazi asanu ndi mmodzi ndi akazi apambali ambiri. Bizinesi yanga inali kukula. Chilichonse chinali kundiyendera bwino. Komabe, ngati wamalonda wam’fanizo la Yesu la ngale, ndinapeza kanthu kena kamtengo wapatali kwambiri kwakuti ndinalepa akazi anga asanu ndi akazi apambali omwe, tchalitchi, kalabu, ndi kutchuka kwakudziko kuti ndikapeze kanthu kameneko.—Mateyu 13:45, 46.
Mmene Ndinadzakhalira Mwaladura
Ndinayamba kumva za Aaladura kwa nthaŵi yoyamba mu 1936, pamene ndinali wazaka 13 zakubadwa. Bwenzi lina lotchedwa Gabriel linandiuza kuti: “Ukapita ku Tchalitchi cha Atumwi a Kristu, udzamva Mulungu akulankhula.”
“Kodi Mulungu amalankhula bwanji?” ndinamfunsa.
Anati: “Tangobwera, ndipo uona.”
Ndinali wofunitsitsa kumvetsera Mulungu. Chotero usiku womwewo ndinatsagana ndi Gabriel kutchalitchiko. Nyumba yaing’onoyo inali thothotho ndi alambiri. Mpingowo unayamba kuimba: “Idzani, anthu inu! Yesu ali kuno!”
Mkati mwa kuimbako, wina anafuula: “Tsikani, mzimu woyera!” Winawakenso nkuliza belu, ndipo mpingowo unakhala chete. Kenako, mkazi wina anayamba kubwebweta monyanyuka m’chinenero chachilendo. Mwadzidzidzi anakuwa: “Mvetserani uthenga wa Mulungu, anthu inu! Mulungu akutero kuti: ‘Pemphererani osaka nyama kuti asaphe anthu!’” Onse mmenemomo anakhala amantha.
Ndinakhulupiriradi kuti Mulungu anali atalankhula kupyolera mwa iye. Choncho chaka chotsatira ndinabatizidwa monga membala wa Tchalitchi cha Atumwi a Kristu.
Kukumana Koyamba ndi Mboni za Yehova
Mu 1951 ndinalandira kope la magazini a Nsanja ya Olonda kwa Mboni ina yotchedwa Adedeji Boboye. Magaziniwo anali osangalatsa, choncho ndinalembetsa kuti ndiziwaŵerenga kaŵirikaŵiri. Mu 1952 ndinaloŵa nawo msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova wa masiku anayi ku Ado Ekiti.
Zimene ndinaona kumsonkhanoko zinandichititsa chidwi. Ndinalingalira mwamphamvu za kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova koma ndinalitayanso lingalirolo. Vuto langa linali lakuti panthaŵiyo ndinali ndi akazi atatu ndi mkazi wapambali mmodzi. Ndinaganiza kuti sindikanakhoza konse kukhala ndi mkazi mmodzi yekha.
Pamene ndinabwerera ku Akure, ndinamuuza Adedeji kuleka kumadzandichezera, ndipo sindinadzalembetsenso sabusikripishoni yanga ya Nsanja ya Olonda. Ndinakhala wokangalika kwambiri m’tchalitchi changa. Ndiiko komwe, ndinalingalira kuti, Mulungu anandidalitsa chiyambire kugwirizana kwanga ndi Tchalitchi cha Atumwi a Kristu. Ndinali nditakwatira akazi atatu ndi kubala ana ambiri. Ndinali nditamanga nyumba yangayanga. Sindinagonekedwepo m’chipatala. Popeza kuti Mulungu anaoneka kukhala akuyankha mapemphero anga, ndisinthirenjinso chipembedzo changa?
Kutchuka Kowonjezeka Limodzi ndi Kugwiritsidwa Mwala
Ndinayamba kumapereka ndalama zochuluka kutchalitchi. Posakhalitsa anandisankha kukhala mkulu watchalitchi, malo amene ananditheketsa kuona zochitika zamseri za tchalitchi. Zimene ndinaona zinandisokoneza maganizo. Apasitala ndi “aneneri” anakonda ndalama; dyera lawo linandiopsa.
Mwachitsanzo, m’March 1967 akazi anga anandibalira ana atatu. Unali mwambo watchalitchi kukhala ndi dzoma lakubatiza ndi kumtcha dzina mwana. Choncho ndinapereka mphatso—nsomba, lemonedi, ndi zakumwa zosaledzeretsa za m’botolo—kwa pasitalayo pokonzekera dzomalo.
Patsiku lautumiki watchalitchi, pasitalayo pamaso pa mpingo wonse anati: “Anthu olemera m’tchalitchi muno andidabwitsa. Amafuna kuchita dzoma lakubatiza ndi kutchula mwana dzina, koma angobwera ndi zakumwa ndi nsomba basi. Popanda nyama iyayi! Popanda mbuzi! Tangolingalirani! Kaini anapereka kwa Mulungu nsembe yamaungu akuluakulu, koma Mulungu sanalandire nsembe imeneyo chifukwa inalibe mwazi. Mulungu amafunatu zinthu zokhala ndi mwazi. Abele anapereka nyama, ndipo nsembe yake inalandiridwa.”
Nditamva zimenezo ndinangonyamuka nkubulikamo. Komabe, kutchalitchiko ndinali kumapitakobe. Ndinali kumathera nthaŵi yochuluka kumacheza ndi kukhala nawo pamisonkhano yakalabu yanga. Nthaŵi zina ndinkaloŵa misonkhano pa Nyumba ya Ufumu, ndipo ndinalembetsanso sabusikripishoni yanga ya Nsanja ya Olonda. Komabe, ndinali ndidakali wosakonzekera kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova.
Chosankha cha Kutumikira Yehova
Zinthu zinadzandisinthira mu 1968. Tsiku lina ndinayamba kuŵerenga nkhani ina mu Nsanja ya Olonda imene inali kufotokoza za kuzunzidwa kwankhanza kwa Mboni za Yehova ku Malaŵi. Inanena za mtsikana wazaka 15 yemwe anamangiliridwa pamtengo ndi kugonedwa kasanu ndi kamodzi chifukwa chakuti sanafune kukana chikhulupiriro chake. Monyansidwa, ndinaleka kuŵerenga magaziniwo, koma ndinaganizabe zimenezo. Ndinazindikira kuti palibe mtsikana m’tchalitchi changa yemwe akanasonyeza mtundu umenewo wachikhulupiriro. Pambuyo pake madzulo omwewo, ndinatenganso magazini aja nkuŵerenganso tsambalo.
Ndinayamba kulimbikira kuphunzira Baibulo. Pamene ndinakula m’chidziŵitso, ndinayamba kuona mmene tchalitchi chinasochezera kwambiri. Monga momwedi zinachitikira m’nthaŵi zakale, ansembe athu anali ‘kuchita choipitsitsa.’ (Hoseya 6:9) Anthu otere anali pakati pa aneneri onyenga omwe Yesu anachenjeza za iwo! (Mateyu 24:24) Sindinakhulupirirenso masomphenya awo ndi ntchito zawo zamphamvu. Ndinasankha kuwonjokamo m’chipembedzo chonyenga ndi kuthandiza ena kuteronso.
Zoyesayesa za Kundikanikizira M’tchalitchi
Pamene akuluakulu atchalitchi anaona kuti ndinali nditatsimikiza kuchoka m’tchalitchi, anatumiza kagulu ka anthu kudzandichonderera. Sanafune kutaikidwa thumba lofunika landalama. Anati andiike ndikhale Baba Egbe, woyang’anira wa chimodzi cha matchalitchi Aatumwi a Kristu ku Akure.
Ndinawakanira chopereka chawocho ndipo ndinawauza chifukwa chake. “Tchalitchi chakhala chikutinamiza,” ndinatero. “Amati anthu onse abwino adzapita kumwamba. Koma ine ndaliŵerenga Baibulo, ndipo ndikutsimikizira kuti ndi anthu 144,000 okha omwe adzapita kumwamba. Anthu ena olungama adzakhala padziko lapansi la paradaiso.”—Mateyu 5: 5; Chivumbulutso 14:1, 3.
Pasitala watchalitchicho anayesa kuchititsa akazi anga kundiukira. Anawauza kuti aziletsa Mboni za Yehova zisamafike panyumba pathu. Mmodzi wa akazi anga anandiikira mankhwala m’chakudya. Aŵiri anandichenjeza za masomphenya omwe anaona kutchalitchi. Masomphenyawo anasonyeza kuti ndidzafa ngati ndichoka m’tchalitchi. Komabe, ndinapitiriza kuwachitira umboni akazi anga, ndikumawapempha kupita limodzi nane kumisonkhano. “Mukapeza amuna ena kumeneko,” ndinatero. Komabe, palibe ndi mmodzi wa iwo anasonyeza chikondwerero, ndipo anapitiriza kuyesa kundilefula.
Potsirizira pake, pa February 2, 1970, pamene ndinangofika panyumba kuchokera kuulendo wa kutauni ina yapafupi, ndinapeza nyumba ili pululu. Akazi anga onse anali atathaŵa ndi ana.
Kuphatikana ndi Mkazi Mmodzi
‘Tsopano ndingathe kuwongolera ukwati wanga,’ ndinaganiza choncho. Ndinapempha mkazi wanga wamkulu, Janet, kuti abwerere kunyumba. Analola. Komabe, banja lake linatsutsa mwamphamvu lingaliro limenelo. Pamene akazi anga enawo anamva kuti ndinali nditampempha Janet kubwerera, anapita kwawo kwa atate wake ndi kuyesa kummenya. Am’banja lake pomwepo anandiitanira kuupo.
Panali anthu pafupifupi 80 amene anapezekapo pa upo umenewo. Bambo wamng’ono wa Janet, yemwe anali mutu wabanjalo, anati: “Ngati mukufuna kukwatiranso mwana wathuyu, ndiye kuti muyenera kutenganso akazi ena aja. Koma ngati mufuna kuchita chipembedzo chanu chatsopanochi ndi kukhala ndi mkazi mmodzi, ndiye kangopezani mkazi wina. Ngati mumtenganso Janet, akazi anzake aja adzamupha, ndipo sitikufuna kuti mwanathu afe.”
Titakambitsirana zambiri, banjalo linazindikira kuti ndinatsimikiza kukhala ndi mkazi mmodzi yekha. Potsirizira pake analolera. Bambo wamng’onoyo anati: “Sitikulandani mkazanuyo. Tiyeni zimkani naye.”
Pa May 21, 1970, Janet ndi ine tinakwatirana mwa lamulo. Masiku asanu ndi anayi pambuyo pake ndinabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Mu December wa chaka chimodzimodzicho, Janet nayenso anabatizidwa.
Kusangalala ndi Dalitso la Yehova
Mamembala atchalitchi chathu chakale analosera kuti ngati tinakhala Mboni tidzafa. Papita zaka pafupifupi 30 tsopano. Ngakhale nditafa tsopano lino, kodi chingakhale chifukwa chakuti ndinakhala mmodzi wa Mboni za Yehova? Ngati mkazi wanga ati afe tsopano lino, kodi aliyense anganene kuti chinali chifukwa chakuti anali atakhala mmodzi wa Mboni za Yehova?
Ndamenyera nkhondo kusonyeza ana anga 17 njira ya choonadi. Ngakhale kuti ambiri a iwo anali achikulire pamene ndinakhala Mboni, ndinawalimbikitsa kumaphunzira Baibulo ndipo ndinali kuwatengera kumisonkhano ndi yaikulu yomwe. Ndili wosangalala kuti asanu a iwo akutumikira Yehova limodzi nane. Mmodzi amatumikira monga mkulu m’nzanga mumpingo. Wina ndi mtumiki wotumikira mumpingo wapafupi. Aŵiri a ana anga akutumikira monga apainiya okhazikika.
Ndikayang’ana kumbuyo, ndimadabwa chisomo cha Yehova pakundithandiza kukhala mtumiki wake. Ngoona chotani nanga mawu a Yesu akuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye.”—Yohane 6:44.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu la Chiyoruba lotanthauza “wopemphera.” Limasonya kwa munthu yemwe ndi membala wa tchalitchi cha Afirikani yemwe amachiritsa mwauzimu.