Ukwati wa Zaka 403 Uli m’Vuto
KU Sweden, Tchalitchi ndi Boma zakhala paunansi wolimba zaka zoposa 400. Tsopano ukwati wa chipembedzo ndi boma ukufooka.
Chipembedzo cha Lutheran chinakhazikitsidwa monga chipembedzo cha Boma mu 1593, ndipo Aswedi onse anayenera kukhala mamembala obatizidwa. Patapita zaka zambiri, cha m’ma 1850, anasintha. Aswedi sanafunikirenso kubatizidwa; koma anayesedwa mamembala a Tchalitchi cha Lutheran. Monga mamembala, anafunikira kulipira 1 peresenti ya ndalama zawo zochotsedwapo msonkho kuti achirikize tchalitchi ndi kulipirira mautumiki ena a boma ochitidwa ndi tchalitchi. Posachedwapa anasinthanso. Kuyambira mu 1952, Aswedi anakhala ndi ufulu wa kuchoka m’tchalitchi mwalamulo namasuka pakulipira mbali yaikulu ya msonkho.
Pazaka za posachedwapa Tchalitchi cha Lutheran chatha mphamvu ku Sweden. Zimenezi zinali zosapeŵeka, popeza 10 peresenti ya nzika za Sweden ndi alendo osakhala a tchalitchi cha Lutheran, kuphatikizapo Ayuda, Akatolika, ndi Asilamu. Choncho, kuchiyambi kwa 1996, Aswedi okwanira 86 peresenti okha ndiwo anali a Tchalitchi cha Lutheran, ndipo chiŵerengerocho chikutsikabe.
Mphwayi yomawonjezeka ikukulitsa mpata pakati pa Tchalitchi ndi Boma. Boma lalengeza kale kuti mfumu siiyenera kukhala ya tchalitchi cha Lutheran, ndipo ana obadwa kwa makolo a m’tchalitchi cha Lutheran sangangokhala mamembala a Tchalitchi cha Lutheran cha Boma. Ndiponso, malinga ndi The Dallas Morning News, pamene chaka cha 2000 chifika, “matchalitchi a kumaloko ndi boma adzayenera kuŵerengera mtengo wa katundu ndi kugaŵana. Tchalitchi chiyenera kuchepetsa bajeti yake ya [$1,680,000,000] pachaka, imene yochuluka yake imachokera pa msonkho.” Pambuyo pa chaka cha 2000, tchalitchi chidzadziikira mabishopu akeake.
Pamene kuli kwakuti mphwayi ndi kutsika kwa mamembala zikusakaza Dziko Lachikristu, Mboni za Yehova ku Sweden zikuwonjezekabe. Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1997 ikufotokoza kuti m’dzikomo muli ofalitsa Ufumu wa Mulungu okwanira 24,487, ndipo pafupifupi 10 peresenti akulalikira monga atumiki anthaŵi zonse aupainiya. Ambiri akukalimira mwaŵi wokulirapo wa utumiki. Mwachitsanzo, mkati mwa misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova mu 1995, abale 20 ndi akazi awo anafunsira maphunziro a umishonale ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Panthaŵiyo nkuti pali Aswedi okwanira 75 otsiriza maphunziro m’makalasi apapitapo omwe anali mu utumiki wa umishonale kumadera osiyanasiyana a dziko lapansi. Mosakayika, chitsanzo chawo chabwino ndi makalata awo olimbikitsa ndi maulendo zili ndi mphamvu yowasonkhezera awo omwe akulakalaka mwaŵi waukulu umenewu.
Chotero, pamene mamiliyoni ambiri a Dziko Lachikristu akusweka mtima, Mboni za Yehova ‘zikuimba ndi mtima wosangalala.’—Yesaya 65:13, 14.
[Mapu patsamba 30]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Sweden