Mboni za Yehova Zidzakhala ndi Misonkhano ya Mitundu Yonse
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likulinganiza kudzakhala ndi misonkhano ya mitundu yonse mu 1998. Chilengezo chimenechi chinawasangalatsa omwe anali pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe unachitikira mu Nyumba Yamsonkhano ku Jersey City pa Loŵeruka, October 5, 1996.
Limodzi ndi misonkhano yachigawo ya nthaŵi zonse, misonkhano ya mitundu yonse idzachitikira ku North America chapakati pa 1998. Tikuyembekezera kuti misonkhano imeneyi idzasonkhanitsa Mboni zikwi zochuluka zochokera kumadera ambiri padziko lapansi. Kuti atheketse maiko ambiri kukhala ndi owaimira, nthambi iliyonse ya maofesi a Watch Tower Society oposa 100 idzatumiza gulu la nthumwi ku msonkhano wa mitundu yonse ku mzinda womwe adzasankha ku North America.
Mwachionekere, si onse amene angapite ku North America ngakhale atafuna kupita. Komabe, nkotheka kuti anthu zikwi zambiri apezeke pamsonkhano wa mitundu yonse wapafupi ndi kwawo. Tikupanga makonzedwe oti misonkhano ya mitundu yonse ichitikire m’maiko aŵiri kapena atatu ku Ulaya ndi ina idzachitikira mu Afirika, Asia, Latin America, South Pacific, ndi ku Caribbean.
Panthaŵi yoyenera, maofesi a nthambi za Sosaite azadziŵitsa mipingo ya m’magawo ake za mzinda kapena mizinda ya msonkhanowo kumene awaitanira. Chidziŵitso chidzaperekedwa ponena za madeti a msonkhano ndi makonzedwe a kasankhidwe ka nthumwizo. Amene akuganiza zofunsira kusankhidwa monga nthumwi angayambe kumasunga ndalama zawo zina poyembekezera zochitika zapadera zimenezi.
Mboni za Yehova zonse padziko lonse lapansi zingayembekezere kuona zomwe zikutidikira pamisonkhano ya mitundu yonse imeneyi ya 1998. Misonkhano yachigawo m’maiko onse idzakhala ndi programu yofanana.