Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Baibulo limasonyezanji ponena za chilango cha imfa kwa apandu?
Ndithudi, aliyense wa ife angakhale ndi maganizo akeake ozikidwa pa zimene wakumana nazo m’moyo kapena mkhalidwe wake. Komabe, pokhala Mboni za Yehova, tiyenera kutsatira maganizo a Mulungu pa chilango cha imfa, pamenenso tikukhala chete pankhani zandale zokhudza mfundoyi zimene ambiri amatengeka nazo.
Kunena molunjika, m’Mawu ake olembedwa, Mulungu samasonyeza kuti chilango cha imfa nchoipa.
Kuchiyambi kwa mbiri ya munthu, Yehova anasonyeza maganizo ake pankhaniyo, malinga ndi zimene timaŵerenga pa Genesis chaputala 9. Nkhaniyo imanena za Nowa ndi banja lake, amene anakhala makolo a banja lonse la anthu. Iwo atatuluka m’chingalaŵa, Mulungu anati iwo azidya nyama—ndiko kuti, kuzipha, kukhetsa mwazi wake, ndi kuzidya. Ndiyeno, pa Genesis 9:5, 6, Mulungu anati: “Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu iye anampanga munthu.” Chotero Yehova analamula kuti ambanda ayenera kupatsidwa chilango cha imfa.
Pamene Mulungu anali kuchita ndi Israyeli monga anthu ake, zolakwa zina zoopsa zamitundumitundu zakuswa lamulo laumulungu zinali ndi chilango cha imfa. Pa Numeri 15:30, timaŵerenga za mawu awa okhudza zambiri: “Munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m’dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.”
Bwanji nanga pambuyo poti mpingo wachikristu wakhazikitsidwa? Eya, tikudziŵa kuti Yehova analola maboma a anthu kukhalako, ndipo anawatcha maulamuliro aakulu. Ndipo, litalimbikitsa Akristu kumvera maulamuliro a boma otero, Baibulo limati iwo ndiwo “mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.”—Aroma 13:1-4.
Kodi zimenezo zikutanthauza kuti maboma amaloledwa ngakhale kunyonga apandu amene mlandu wawo uli waukulu koopsa? Inde. Tikunena zimenezo chifukwa cha mawu opezeka pa 1 Petro 4:15. M’vesi limenelo, mtumwiyo analangiza abale ake kuti: “Asamve zoŵaŵa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira.” Kodi mwamva kuti, “asamve zoŵaŵa wina wa inu ngati wambanda”? Petro sanali kunena kuti maboma alibe ufulu wa kulipitsa wambanda tchimo lake. M’malo mwake, anasonyeza kuti wambanda angalandire chilango chake chomuyenera. Kodi chimenecho chingaphatikizepo chilango cha imfa?
Chingatero. Zimenezi zikusonyezedwa bwino ndi mawu a Paulo opezeka m’Machitidwe chaputala 25. Ayuda anaimba Paulo mlandu wakuswa Chilamulo chawo. Potumiza wandende wake, Paulo, kwa bwanamkubwa wa Roma, kazembe wa nkhondo anati pa Machitidwe 23:29: ‘Ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chawo; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.’ Patapita zaka ziŵiri, Paulo anaonekera pamaso pa Bwanamkubwa Festo. Timaŵerenga pa Machitidwe 25:8 kuti: “Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwa kanthu kapena pachilamulo, kapena pa Kachisi, kapena pa Kaisara.” Tsopano tamvetserani mawu ake ponena za chilango, ngakhale chilango cha imfa. Timaŵerenga pa Machitidwe 25:10 ndi 11:
‘Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitira kanthu koipa, monga mudziŵanso nokha bwino. Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.’
Paulo, ataimirira pamaso pa wolamulira woikidwa mwalamulo, anavomereza kuti Kaisara anali ndi mphamvu ya kulanga ochita zoipa, ngakhale kuwapha. Iye sanakane kulangidwa ngati anali ndi mlandu. Ndipo sananene kuti Kaisara angangopereka chilango cha imfa pa ambanda okha.
Zoona, kaweruzidwe ka Aroma sikanali kangwiro; ngakhalenso makhoti a anthu lerolino saali. Anthu ena osachimwa kalelo ndi lerolino mlandu wawagwera ndipo alangidwa. Ngakhale Pilato anati ponena za Yesu: “Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.” Inde, ngakhale wolamulira wa boma anagamula kuti Yesu analibe mlandu, munthu wopanda mlanduyo anaphedwa.—Luka 23:22-25.
Koma chisalungamo chotero sichinasonkhezere Paulo kapena Petro kutsutsa kuti chilango cha imfa nchoipa kwenikweni. M’malo mwake, maganizo a Mulungu pankhaniyo ngakuti malinga ngati maulamuliro aakulu a Kaisara alipo, iwo ‘agwira lupanga kukwiyira wochita zoipa.’ Ndipo zimenezo zimaphatikizapo kugwiritsira ntchito lupanga mwa kupereka chilango cha imfa. Koma za mkangano woti kaya boma lililonse liyenera kugwiritsira ntchito kuyenera kwake kwa kunyonga ambanda, Akristu enieni amasungabe uchete mosamala. Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu, iwo amapeŵa mkangano uliwonse wokhudza nkhaniyi.