Kuchezera Munda Wakwathu Waumishonale
GULU la mipingo yachikristu yomwe ndimachezera limandiyendetsa kuchokera ku Portugal mpaka ku China—ndingoti zimaoneka choncho. Komabe, ineyo ndi mkazi wanga, Olive, sitimachoka mu Britain.
Timachezera mipingo ya Mboni za Yehova yolankhula zinenero zachilendo imene ikuwonjezeka ndipo ikupezeka kulikonse m’dziko lonse lino. Kuchokera pachisumbu cha Jersey, makilomita ngati 20 kuchoka kugombe la Normandy ku France, kumene kuli gulu lachipwitikizi, mpaka ku tauni ya Sunderland kumpoto kwa England, kumene timachezera anthu okondwerera olankhula Chitchaina, timagwira ntchito m’munda wachonde ndi wobala mwauzimu, wazinenero zambiri. Kodi tinalipeza bwanji gawo lachilendo limeneli? Nanga zikuchitika m’munda wakwathu waumishonale nzotani? Lekani ndifotokoze.
Ine ndi Olive tatumikira zaka 20 m’ntchito yoyendayenda, kuchezera mpingo wina mlungu uliwonse. Pamaulendo athu timafika kumpoto, kummwera, kummaŵa, kumadzulo, m’Britain monse, ndipo posachedwapa tinafika kwa abale athu achikristu pachisumbu cha Malta ku Mediterranean kumene anatichereza mwachikristu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 28:1, 2.) Titakhala zaka zitatu pa Malta, tinayamba kuganiza za kumene kudzakhala gawo lathu lina. Tinalingalira kuti mwina tikachezera dera lakumidzi la Azungu, ndiye tinayamba kumaganiza kuti nzimene zidzachitika. Koma ndiye zinangotidabwitsatu pamene tinalandira gawo lathu kuti tikatumikira m’dera latsopano la magulu ndi mipingo yolankhula zinenero 23 zosiyanasiyana!
Sitinadziŵe kuti tizikachita bwanji tsopano. Kusiyapo pamene tinali ku Malta, sitinakhalepo kwambiri ndi anthu achikhalidwe ndi miyambo yosiyana. Kodi tidzathadi kuwalimbikitsa amene samamvetsetsa Chingelezi? Nanga tizilankhulana bwanji osadziŵa zinenero zina? Bwanjinso za chakudya ndi miyambo yosiyanasiyana ya ena? Kodi tidzaziphunzira? Mafunso ngati ameneŵa anangoti mbwee m’maganizo mwathu pamene tinali kulingalira mwapemphero zoyankha chiitano cha ku Makedoniya chimenechi.—Machitidwe 16:9, 10; 1 Akorinto 9:19-22.
Kulaka Vuto la Chinenero
“Poyamba ndinangodziona ngati wosakhoza chifukwa sindinali kudziŵa zinenero zilizonse,” akutero Olive. “Sindinadziŵe mmene ndidzawathandizira alongo. Ndiye ndinakumbukira mbale wina ndi mkazi wake amene anatiphunzitsa Baibulo poyamba mmene anatilimbikitsira kuti tisadzakane gawo la ntchito. Anatiphunzitsa kuti Yehova samatipempha kuchita kanthu kena kamene sitingathe.” Choncho tonse tinalola kuilandira ntchitoyo.
Pambuyo poganizapo kwambiri, tikuona kuti kusadziŵa kwathu chinenero china kwatithandiza kuchita ndi munthu aliyense mosakondera. Mwachitsanzo, kupezeka pamisonkhano yachinenero china mlungu uliwonse kwatipangitsa kuzindikira mmene abale anamvera pamene anakhala pamisonkhano yachingelezi pomwe sanali kutolapo kanthu ngakhale kamodzi. Tifunikiradi kuikonzekera bwino misonkhanoyo kuti timvetsetse tanthauzo la zimene akunena. Nthaŵi zonse Olive amayankha limodzi la mafunso pamsonkhano. Amalikonza yankholo m’Chingelezi ndi kumpatsa mlongo wina kuti amtembenuzire ndipo iyeyo amalemba zimenezo mwanjira yoti zingatchulike. Akuvomera kuti amatukula mkono wake mozengereza pofuna kuyankha. Nthaŵi zina akayesa kuyankha anthu amaseka. Koma zimenezo iye sizimamletsa kuyankha. “Ndikudziŵa kuti abale amayamikira kuti ndikuyesayesa,” akutero. “Ndingoti, kuyankha kwanga kumawalimbikitsa amene amachidziŵa bwino chinenerocho kutengamo mbali pamsonkhanowo.”
Kwa ineyo, kukamba nkhani kwasiyananso, chifukwa ndiyenera kumpatsa nthaŵi womasulira wanga pamawu alionse. Nkwapafupi kwambiri kuiŵala zimene ndinali kufuna kunena. Ndimakakamizika kusumika maganizo kwambiri ndi kupungulako mfundo zina zambiri. Komabe zimandikondweretsa.
Utumiki Wathu Wosinthasintha
M’madera ambiri am’tauni muno m’Britain, anthu olankhula zinenero zina ngobalalika, mwina mupeza aŵiri pamsewu wina ndiyeno mudzafunikira kuyenda kamtunda ndithu kuti mupeze ena. Komabe, ukawapatsa moni m’chinenero chawo nkuona mmene amayankhira, umamva kuti sunawononge nyonga yako. Ngati mbale yemwe ndikuyenda naye amlongosolera mwini nyumbayo uthenga wa Ufumu m’chinenero chake, kaŵirikaŵiri amavomereza ndi chimwemwe chachikulu.
Ndithudi, utumiki wochitira m’munda wachinenero chachilendo ndiwo umodzi wa zokumana nazo zosangalatsa kwambiri zimene takhala nazo pazaka zathu 40 mu utumiki wa Ufumu. Nkotheka kuti mundawo udzakulanso kwambiri. Nkosakayikitsa kuti anthu ambiri amaphunzira msanga kwambiri ndipo amayamikira ndithu pamene akuphunzitsidwa m’chinenero chawo. (Machitidwe 2:8, 14, 41) Zimakhaladi zokhudza mtima kuona abale ndi alongo akutuluka misozi yachisangalalo pambuyo pa msonkhano, kwa ena kumakhala kuyamba kutha kumvetsera ndi kumvetsetsa programu yonse.
Polalikira kunyumba ndi nyumba, timayesa kunena mawu oyamba m’chinenero cha mwini nyumbayo, ngakhale kuti nthaŵi zina zimativuta. Mwachitsanzo, polonjera banja la Agujarati ndi malonje ozoloŵereka umati Kemcho, ndiko kuti “Moni.” Nthaŵi ina nditaphophonya ndinamveka ngati ndinali kusatsa malonda a mtundu wina wa kofi yotchuka. Komabe, panyumba ina mwamuna wina ndi mkazi wake anamwetulira pamene ndinawapatsa moni m’Chigujarati. Basi mwamsanga anatiloŵetsa m’nyumba natipatsa khofi—osatitu chifukwa ndinaphophonya kutchula iyayi. Tinadzadziŵa kuti anali pachibale ndi Mboni za Yehova zina m’gulu limene tinali kuchezera, ndipo anachita chidwi chenicheni ndi choonadi.
Kwa zaka zambiri mlongo wina wolankhula Chingelezi, kaŵirikaŵiri anali kusiyira magazini mayi wina wolankhula Chitchaina. Nthaŵi zina anali kumpempha mayiyo kuti azichita naye phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, koma anali kukana. Tsiku lina mlongo wina yemwe anali kuphunzira Chitchaina anatsagana naye ndipo anagaŵira buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi m’chinenero chomwecho, ndipo mwini nyumbayo anachita nalo chidwi nkulilandira.a Tsopano pokhala ndi bukulo m’chinenero chakechake, anavomereza phunziro la Baibulo. Mawu oŵerengeka amene anawalankhula m’chinenero cha mayiyo anamgwira mtima.
Makhalidwe Osiyanasiyana
Sitinadziŵe kuti mwa anthu ena amuna samafuna kuti akazi awo aziyenda okha usiku. Chifukwa cha zimenezo, alongo ochuluka zimawavuta kwambiri kuti apezeke pamisonkhano yamadzulo. Amwenye ena amaganiza kuti atsikana amene amasankha kusakwatiwa nkumakhalabe panyumba amachititsa banjalo manyazi. Bambo wa mlongo wina wachitsikana anafuna kudzipha ndi mankhwala chifukwa chakuti mlongoyo anakana kukhala mkazi wa mwamuna amene banja lake linamsankhira. Inde, zimene alongo oterowo ayenera kupirira nzazikulu kwabasi! Komabe, kungoona mmene choonadi chakhudzira moyo wa banjalo, mmenenso makolo amachitira chidwi ndi alongo pakukhulupirika kwawo kwa Yehova, nzodabwitsadi.
Kulandira kwathu ntchitoyi kwatisinthitsa zinthu zina. Tisanaiyambe ntchito yoyendayendayi, chakudya changa chinali chongophika chizungu, koma tsopano chakudya chokoleretsa chikundikhalira bwino. Tili achisoni kuti zaka zambiri zinapita tisanayambe kudya zakudya zosiyanasiyana—kungoyambira nsomba zaziŵisi ndi zakudya zothirako kale.
Tikuyembekeza Kuti Munda Wathu Udzakula
Kukuoneka ngati ino ndiyo nthaŵi yoti munda wachinenero chachilendo ufutukuke m’madera ambiri. Zofalitsa zambirimbiri tsopano zikupezeka m’zinenero zina. Pamene mipingo yatsopano ikupangidwa mukhoza kuona kuti dalitso la Yehova lilipodi. Abale odziŵa zinenero zina amachokera kutali kudzathandiza.
Chitsanzo chabwino kwambiri ndi chija cha amene avomera kukalalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’Chifrenchi. Anthu ambiri othaŵa kwawo olankhula Chifrenchi ochokera ku Zaire ndi maiko ena a mu Afirika abwera muno m’Britain m’zaka zaposachedwapa. Pamene mpingo woyamba wachifrenchi unakhazikitsidwa ku London, unali wa ofalitsa Ufumu 65. Patatha chaka chimodzi chiŵerengerocho chinakwera mpaka 117, ndipo pa onseŵa, 48 anali mu utumiki wanthaŵi zonse monga apainiya okhazikika. Posakhalitsa, anakhazikitsa mpingo wina kuti usamalire anthu okondwerera omachulukawo. Tsopano zitheka kuwasamala bwino okondwererawo, ena a ameneŵa okwanira 345 anapezeka paphwando la Chikumbutso cha 1995. Ena amene anamaliza maphunziro a Gileadi, omwe anatumikirapo ku Benin, Côte d’Ivoire, Morocco, ndi Zaire tsopano akugwiritsira ntchito maluso awo posamalira munda womakulawu, ndipo zotsatirapo zake zikudabwitsa.
Paulendo wina ndikuchezera mpingo wachifrenchi, ndinatsagana ndi mtsikana wina wachikuda ku phunziro la Baibulo. Pamene timatsazika, mtsikanayo anadandaula kuti: “Chonde musapite. Takhalanibe.” Anafunadi kudziŵa zambiri. Ndiye anangondikumbutsa Lidiya wa m’zaka za zana loyamba.—Machitidwe 16:14, 15.
Ntchito yathu yoyamba inali yothandiza timagulu tachinenero chachilendo kuti tikhale mipingo. Kumene abale anali kuchita Phunziro la Buku la Mpingo mlungu uliwonse, tinayambitsako Sukulu Yautumiki Wateokratiki yachidule kamodzi pamwezi. Imeneyi imawathandiza kulankhula bwino mu utumiki wakumunda. Ndiyeno mwapang’onopang’ono amalimbikira kuti mlungu uliwonse azichita misonkhano yampingo yonse isanu. Tili kale ndi mipingo yatsopano yolankhula Chitchaina, (Chikantonizi), Chifrenchi, Chigujarati, Chijapani, Chipwitikizi, Chipunjabi, Chithamili, ndi Chiwelshi.
Ndiponso tinauyamikira mwaŵi wokapezeka pamisonkhano ya abale ogontha. Kuona abale akuimba ndi manja awo kunali kodabwitsa kwambiri. Nditazindikira kuti mu utumiki wawo amalankhula mwa majesicha, ndinasirira khama lawo ladzaoneni potenga mbali pakulalikira za Ufumu. Palinso omwe amamasulira ndi manja kuti ogontha omwenso ngakhungu amve. Zikukhala ngati Yehova amatsimikiza kuti wina zisampite.
Titafuna kupempha kanthu kena, kangakhale kofanana ndi kamene Yesu anapempha, kuti: “Pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:38) Abale athu ambiri akuilandira ntchito yovuta yophunzira chinenero china m’gawo la mpingo wawo. Ngakhale tilibe mphatso yodabwitsa yolankhula zinenero zosiyanasiyana, ndithudi Yehova akuufutukula utumiki m’munda wakwathu umenewu waumishonale—munda umene wayera kale wongofuna kumweta. (Yohane 4:35, 36)—Yosimbidwa ndi Colin Seymour.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.