Kudikirabe Yehova Moleza Mtima Kuyambira Ubwana Wanga
YOSIMBIDWA NDI RUDOLF GRAICHEN
Tsoka linagwa mwadzidzidzi ngati mphezi m’banja lathu pamene ndinali ndi zaka 12 zokha. Choyamba, atate wanga anaponyedwa m’ndende. Kenako, ine ndi mlongo wanga anatichotsa panyumba motikakamiza ndi kutipereka kukakhala ndi anthu osawadziŵa. Pambuyo pake, Agestapo anandimanga ine ndi amayi anga. Ine ndinapita kundende, ndipo iwo anakafika mpaka kumsasa wachibalo.
ZOCHITIKA zotsatizana zimenezo zinali chiyambi chabe cha zizunzo zoŵaŵa zimene ndinakumana nazo paubwana wanga monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Agestapo Anazi oipawo ndiponso a Stasi a ku East German anayesayesa kuti aswe chikhulupiriro changa kwa Mulungu. Tsopano, pambuyo pa zaka 50 za utumiki wodzipatulira kwa iye, ndinganene monga ananenera wamasalmoyo kuti: “Anandisautsa kaŵirikaŵiri kuyambira ubwana wanga; koma sanandilaka.” (Salmo 129:2) Ndikuyamikira Yehova chotani nanga!
Ndinabadwa pa June 2, 1925, mu tauni yaing’ono ya Lucka pafupi ndi Leipzig, Germany. Ngakhale ndisanabadwe, makolo anga, Alfred ndi Teresa, anazindikira kuti munali choonadi cha Baibulo m’zofalitsa za Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Ndikukumbukira kuti tsiku lililonse ndinali kuyang’ana pa zithunzi za malo otchulidwa m’Baibulo zopachika pamakoma m’nyumba mwathu. Chithunzi china chinali cha mmbulu ndi mwana wankhosa, mwana wambuzi ndi nyalugwe, mwana wang’ombe ndi mkango—zonse zili pamtendere, mnyamata wamng’ono akuzitsogolera. (Yesaya 11:6-9) Ndinazikumbukirabe zithunzizo kwa nthaŵi yaitali.
Pamene kunali kotheka, makolo anga anali kundilola kuchita nawo ntchito zampingo. Mwachitsanzo, mu February 1933, masiku oŵerengeka chabe Hitler atatenga ulamuliro, “Photo-Drama of Creation”—ndi kanema yake, ndi nkhani yake yojambula—inasonyezedwa m’katauni kathu. Ndinakondwa chotani nanga, pokhala mnyamata chabe wazaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa, nditakwera nawo kumbuyo kwa galimoto la vani pomapanga kampeniyo yolengeza “Photo-Drama”! Pachochitika chimenechi ndi zochitika zinanso, abale anandipangitsa kumva kukhala wofunika mumpingowo mosasamala kanthu za kuchepa kwanga. Choncho kungoyambira ndili wamng’ono, Yehova anandiphunzitsa ndipo Mawu ake anaumba khalidwe langa.
Ndinaphunzitsidwa Kudalira Yehova
Chifukwa cha uchete wachikristu, Mboni za Yehova sizinaloŵe m’ndale za Anazi. Nchifukwa chake mu 1933 Anazi anaika lamulo lotiletsa kulalikira, kusonkhana, ngakhale kuŵerenga mabuku athu ofotokoza Baibulo. Mu September 1937 abale onse mumpingo wathu, kuphatikizapo atate wanga, anamangidwa ndi Agestapo. Zimenezo zinandikhalitsa wachisoni kwambiri. Atate wanga anaweruzidwa kukhala zaka zisanu m’ndende.
Zinthu zinayamba kutivuta kwambiri kunyumba. Koma mwamsanga tinaphunzira kudalira Yehova. Tsiku lina nditangofika kuchokera kusukulu, amayi anga anali kuŵerenga Nsanja ya Olonda. Ndiye anafuna kundikonzera chakudya chopepuka, choncho anaika magazini ija pakhabati. Titatha kudya, pamene tinali kulongedza mbale, wina anagogoda chitseko mwamphamvu. Anali wapolisi amene anafuna kufufuza m’nyumba mwathu ngati munali mabuku ofotokoza Baibulo. Ndinachita mantha kwambiri.
Tsiku limenelo linali lotentha kwabasi. Chotero chinthu choyamba chimene wapolisiyo anachita chinali kuvula chisoti chake nkuchikhazika pathebulo. Kenako anayamba kufufuza kwakeko. Pamene anali kuyang’ana kunsi kwa thebulo, chisoti chija chinayamba kutsetsereka. Ndiye amayi anga anafulumira kuchigwira chisoticho nkuchikhazika pakhabati pamwamba penipeni pa Nsanja ya Olonda! Wapolisiyo anafufuzafufuza m’nyumba mwathu koma sanapezemo mabuku alionse. Sanaganizenso zoti ayang’ane pansi pa chisoti chakecho. Atakonzeka kuti azipita, anapepesa amayi anga kwinaku akutenga chisoti kumbuyo kwake. Basi mtima wanga unakhala pansi!
Zokumana nazo ngati zimenezo zinandikonzekeretsa kuyang’anizana ndi mayeso ena ovuta kwambiri. Mwachitsanzo, kusukulu anandiumiriza kuloŵa gulu la Anyamata a Hitler, momwe ana anali kuphunzitsidwa nkhondo ndi kuwalangiza nzeru ya Anazi. Aphunzitsi ena anali ndi cholinga choti ana awo onse atengemo mbali. Mphunzitsi wanga, Herr Schneider, ayenera kukhala atadziona ngati wolephera kwambiri chifukwa chakuti, pamene ophunzira a aphunzitsi onse pasukulu yathu anali kutengamo mbali, iyeyo ake anali kupereŵera ndi mmodzi. Wophunzira ameneyo ndinali ine.
Tsiku lina Herr Schneider anauza kalasi yonse kuti: “Anyamata, maŵa tidzapita kokayenda monga kalasi.” Aliyense analikonda lingaliro limenelo. Ndiyeno anawonjezera kuti: “Nonsenu muyenera kudzavala mayunifomu anu aja a Anyamata a Hitler kuti pamene tikuguba pamsewu, onse aone kuti ndinu anyamata abwino a Hitler.” Mmaŵa mwake anyamata onse anabwera atavala mayunifomu awo kusiyapo ineyo. Mphunzitsi anandiitana nkundiimika kumaso kwa kalasi ndi kundiuza kuti: “Tayang’ana anyamata enawa ndiyeno udziyang’ane wekha.” Anawonjezera kuti: “Ndikudziŵa kuti makolo ako ngosauka ndipo sangathe kukugulira yunifomu, koma taleka ndikusonyeze kanthu kena.” Anandikokera ku desiki yake, nkutsegula dulowa, ndiyeno nkudzati: “Ndikufuna kukupatsa yunifomu yatsopanoyi. Njokongola eti?”
Ndi bwino ndikanangofa m’malo movala yunifomu ya Nazi. Pamene mphunzitsi wanga anaona kuti sindinafune kuivala, anapsa mtima, ndipo kalasi yonse inandijeda. Ndiye anapita nafe koyenda kuja koma anayesa kundibisa mwa kundiyendetsa pakati pa anyamata onse omwe anali atavala mayunifomu awo. Komabe, anthu ambiri m’taunimo anandiona kuti ndinali wosiyana ndi am’kalasi anzanga. Aliyense anadziŵa kuti ine ndi makolo anga tinali Mboni za Yehova. Ndikuyamika Yehova kuti anandipatsa nyonga yauzimu yomwe ndinafunikira ndili wamng’ono.
Chizunzo Chikulakulabe
Tsiku lina kuchiyambi kwa 1938, ine ndi mlongo wanga anatitenga kusukulu nkutikweza galimoto yapolisi ndikumka nafe kusukulu yandende ku Stadtroda, yokhala pamtunda ngati makilomita 80. Kodi mwadziŵa chifukwa chake? Makhoti anaganiza zotilekanitsa ndi makolo athu kuti akatitembenuze tikhale ana a Anazi. Posapita nthaŵi woyang’anira sukulu yandendeyo anaona kuti ine ndi mlongo wanga tinali aulemu ndi omvera, komanso okaniratu kwa mtu wa galu kutenga mbali m’ndale pokhala Akristu. Woyang’anira wachikaziyo anachita chidwi kwambiri koti anafuna kuonana ndi amayi anga. Ngakhale ena onse amawaletsa kuloŵa, koma amayi anga analoledwa kudzatichezera. Ine, amayi anga ndi mlongo wangayo tinakondwa kwabasi ndipo tinathokoza Yehova potipatsa mpata woti tikhale pamodzi kuti tilimbikitsane tsiku lonse. Tinachifunadi chilimbikitso.
Tinakhalakobe kusukulu yandendeyo miyezi ngati inayi. Ndiyeno anatipereka kukakhala ndi banja lina ku Pahna. Anawauza kuti asatipereke kwa achibale athu iyayi. Amayi anga sanaloledwe ngakhale kudzacheza. Komabe, nthaŵi zina anali kupeza njira yotionera. Pamipata yosapezekapezeka imeneyi, amayi anga anachita zotheka kutilimbikitsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova, pamayeso ndi mikhalidwe iliyonse imene iye angalole.—1 Akorinto 10:13.
Ndipo mayesowo anadzadi. Pa December 15, 1942, pamene ndinali ndi zaka 17 zokha, Agestapo ananditenga nkukandiponya m’ndende ku Gera. Patapita ngati mlungu umodzi, amayi anga anamangidwanso ndi kudzakhala nane m’ndende imodzi. Popeza ndinali wamng’ono, khoti silinandizenge mlandu. Chotero ine ndi amayi anga tinakhala miyezi isanu ndi umodzi titangotsekeredwa pamene khoti limadikira tsiku limene ndidzakwanitsa zaka 18. Tsiku limene ndinangokwanitsa zaka 18, ine ndi amayi anga tinazengedwa mlandu.
Ndisanazindikire zimene zinali kuchitika, mlanduwo anali ataumaliza kale. Sindinadziŵe kuti mmene zatere basi sindiwaonanso amayi anga. Zimene ndikukumbukira za iwo nkuwaona atakhala pambali panga pabenchi lamatabwa tili m’khoti. Tonse anatipeza ndi mlandu. Ine ndinaweruzidwa kukhala m’ndende zaka zinayi, amayi anga chaka chimodzi ndi theka.
Masiku amenewo m’ndende ndi m’makampu munali Mboni za Yehova zambirimbiri. Komabe, ine ananditumiza kundende ya ku Stollberg, kumeneko Mboni ndinali ndekhandekha. Ndinakhala m’chipinda chandekha koposa chaka chimodzi, komabe Yehova anali nane. Chikondi chimene ndinamkonda nacho paubwana wanga nchimene chinandithandiza kukhalabe wamoyo mwauzimu.
Pa May 9, 1945, nditakhala zaka ziŵiri ndi theka m’ndende, tinalandira uthenga wabwino—nkhondo inali itatha! Tsiku lomwelo ndinamasulidwa. Nditayenda makilomita 110, ndinafika kunyumba nditadwaladi chifukwa chotopa ndiponso njala. Panapita miyezi ingapo kuti thanzi langa libwerenso.
Pamene ndinangofika, ndinakhwethemuka ndi uthenga wosautsa maganizo. Woyamba unali wonena za amayi anga. Atakhala m’ndende chaka chimodzi ndi theka, Anazi anawauza kusaina chikalata chokana chikhulupiriro mwa Yehova. Anakana. Ndiyeno Agestapo anapita nawo kumsasa wachibalo wa akazi, ku Ravensbrück. Kumeneko nkumene anadzafa ndi malungo nkhondo isanathe. Anali Mkristu wolimba mtima—wankhondo wamphamvu yemwe anakana kugonja. Yehova awakumbukiretu mwachifundo.
Ndiye panalinso uthenga wonena za mkulu wanga, Werner, yemwe sanafune kudzipatulira kwa Yehova. Analoŵa m’gulu lankhondo la Germany ndipo anaphedwa ku Russia. Nanga atate wanga? Anabwera kunyumba, inde, koma zachisoni zinali zoti anali mmodzi wa Mboni zoŵerengeka zimene zinasaina chikalata chamwano chija chokanira chikhulupiriro chawo. Pamene ndinawaona, anagwetsa nkhope ndipo anali ovutika maganizo.—2 Petro 2:20.
Nthaŵi Yaifupi ya Kukangalika m’Ntchito Yauzimu
Pa March 10, 1946, ndinapezeka pamsonkhano waukulu ku Leipzig, woyamba nkhondo itatha. Zinali zosangalatsa kwambiri chotani nanga kumva akulengeza kuti patsiku lomwelo padzakhalanso ubatizo! Ngakhale kuti zaka zambiri zinali zitapita nditapatulira kale moyo wanga kwa Yehova, uno unali mpata woyamba woti ndibatizidwe. Tsiku limenelo sindidzaliiŵala konse.
Pa March 1, 1947, nditachita upainiya mwezi umodzi, ndinaitanidwa ku Beteli ku Magdeburg. Maofesi a Sosaite anali atawonongeka kwambiri ndi mabomba. Unali mwaŵi wotani nanga kuthandiza nawo pantchito yokonzanso! Chilimwe chimenecho, ndinagaŵiridwa mzinda wa Wittenberge kuti ndikachiteko upainiya wapadera. Miyezi ina ndinatha maola oposa 200 ndikulalikira kwa ena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndinakondwatu kwabasi kuti ndinali womasukanso—popandanso nkhondo, popandanso chizunzo, popandanso ndende!
Koma chimene chinaipapo nchakuti ufuluwo sunakhalitse. Nkhondo ija itatha, Germany anagaŵidwa, ndipo dera limene ndimakhalalo linalamulidwa ndi a komyunizimu. Mu September 1950 apolisi osavala yunifomu a ku East Germany, otchedwa Stasi anayamba kumanga abale m’magulumagulu. Mlandu umene anandineneza nawo ine unali woseketsa. Anandineneza kuti ndinali kazitape wa boma la America. Ananditumiza kundende ya a Stasi yankhanza kwambiri m’dzikomo, ku Brandenburg.
Abale Anga Auzimu Anandichirikiza
Kumeneko a Stasi sanandilole kugona masana. Ndiyeno usiku wonse kunali kundifunsa kokhakokha. Nditatopa nayo nkhanza imeneyo yamasiku angapo, zinthu zinaipanso kwambiri. Mmaŵa wina, m’malo mondibwezera kuchipinda changa, anakandiika m’ndende yawo ina imene amati U-Boot Zellen (zotchedwa ndende zapansi pa madzi chifukwa anazimanga pansi penipeni pa nthaka). Anatsegula chitseko chachitsulo chokutidwa dzimbiri, ndi kundiuza kuloŵa mmenemo. Ndinatansa mwendo pansi pakuyapo. Pamene ndinakhazika mwendo wanga pansi, ndinazindikira kuti pansi ponsepo anali madzi okhaokha. Chitsekocho anachitseka mongochimenyetsa nichichita phokoso lochititsa mantha lija. Munalibe nyali ngakhale zenera. Mdima wake unali wandiweyani.
Popeza madziwo anali ofikabe cha m’mawondomu, sindinathe kukhala, kutambalala pansi, kapena kugona tulo. Nditadikira kwa nthaŵi imene inaoneka ngati yamuyaya, ananditenga kukandifunsanso panyali zoŵala kwabasi. Sindidziŵa kuti chopweteka kwambiri chinali chiti—kuiimirira m’madzi tsiku lonse mumdima wabii kapena kupirira nyali zoŵala mochititsa khungu atazilozetsa kumaso kwanga usiku wonse.
Nthaŵi zingapo anandiloza ndi mfuti. Masiku angapo a kufunsidwako atapita, ofesala wankhondo wa Russia anadzandichezera mmaŵa wina. Ndinapeza mpata womuuza kuti a Stasi achijeremani anali kuchita nane mwankhanza yoposa imene Agestapo a Nazi anali kundichita. Ndinamuuza kuti Mboni za Yehova sizinatenge mbali m’boma lachinazi ndipo sizinatengenso mbali m’boma lachikomyunizimu ndi kuti sitimaloŵerera m’ndale kulikonse padziko lapansi. Koma ndinati, ambiri amene tsopano ali maofesala a Stasi kale anali mamembala a gulu la Anyamata a Hitler, limene mwina linawaphunzitsa kuzunza mwankhanza anthu osalakwa. Mmene ndinali kulankhula choncho, thupi langali linali njenjenje ndi chisanu, njala, ndi kulefuka.
Zinandidabwitsa kuti ofesala wa Russiayo sanandipsere mtima. M’malo mwake, anandifundika bulangete ndipo anandichitira chifundo. Mwamsanga atatha kucheza nane, anandibwezera ku chipinda chabwinopo. Pambuyo pamasiku angapo, anandipereka kukhoti la Germany. Pamene ndimadikirabe kumva mlandu wanga, ndinakondwa kuti ndinakhala m’chipinda chimodzi ndi Mboni zina zisanu. Nditapirira nkhanza yadzaoneniyo, ha, kunali kotsitsimulatu nanga kukhala pamodzi ndi abale anga auzimu!—Masalmo 133:1.
Kukhoti anandiimba mlandu waukazitape ndipo ndinaweruzidwa kukhala m’ndende zaka zinayi. Chimenecho chinaoneka ngati chilango chaching’ono. Abale ena anaweruzidwa kukhalamo zaka zoposa khumi. Ananditumiza kundende yachitetezo champhamvu. Ndiganiza kuti ngakhale mbeŵa siikanatha kuloŵa kapena kutuluka m’ndendemo—anaichingadi ndende imeneyo. Komabe, mwa chithandizo cha Yehova abale ena olimba mtima anatha kuzembetseramo Baibulo lathunthu. Tinaligaŵa nkukhala buku limodzilimodzi ndipo tinawagaŵira abale omwe anali akaidiwo.
Kodi tinazipanga bwanji? Zinali zovutadi. Nthaŵi yokha imene tinali kuonana wina ndi mnzake inali pamene anamka nafe kosamba. Panthaŵi ina, ndikusamba, mbale wina anandinong’oneza m’kutu kuti anali atabisa masamba a Baibulo m’thaulo lake. Nditatha kusamba ndinayenera kutenga thaulo lakelo m’malo mwa langa.
Mmodzi wa alonda anamuona mbaleyo akundinong’oneza ndipo anammenya kwambiri ndi ndodo yake. Ndinangolitenga thaulolo mwamsangamsanga ndi kuloŵerera mwa akaidi enawo. Mwamwaŵi sanandigwire nawo masamba a Baibulowo. Akanandigwira, programu yathu ya chakudya chauzimu ikanalephereka. Tinakumana ndi zambiri zotero. Nthaŵi zonse tinali kuŵerenga Baibulo titabisala ndipo moika moyo pachiswe. Mawu a mtumwi Petro akuti, “Khalani odzisungira, dikirani,” ndithudi anali oyenera.—1 Petro 5:8.
Pazifukwa zina, oyang’anira ndende anaganiza kumatisamutsasamutsa kuchoka pandende ina kumka ku ndende ina. Pazaka zoposa zinayi, anandisamutsira kundende ngati khumi zosiyanasiyana. Komabe, nthaŵi zonse ndinali kutha kupeza abale. Ndinafikira pakuwakonda kwambiri abale onsewo, ndipo ndinali kungomva chisoni kwambiri mumtima mwanga chifukwa ndinali kulekana nawo nthaŵi zonse posamutsidwa.
Potsirizira pake ananditumiza ku Leipzig, ndipo kumeneko nkumene ndinadzamasulidwa m’ndende. Mlonda wandende yemwe anandimasulayo sananene kuti kafikeni bwino iyayi, koma anati, “Tikuonanso posachedwapa.” Maganizo ake oipa anafuna kuti ndiikidwenso m’ndende. Kaŵirikaŵiri ndimaganiza za Salmo 124:2-3, limene limati: “Akadapanda kukhala nafe Yehova, pakutiukira anthu: akadatimeza amoyo, potipsera mtima wawo.”
Yehova Amalanditsa Atumiki Ake Okhulupirika
Tsopano ndinalinso mfulu. Mlongo wanga mphasa, Ruth, ndi Mlongo Herta Schlensog anali kundidikira kugeti. Zaka zonsezi zimene ndinali m’ndende, Herta anali kunditumizira kaphukusi kachakudya mwezi uliwonse. Ndithudi ndikukhulupirira kuti pakanapanda timaphukusi timeneto, bwenzi nditafera m’ndende. Yehova amkumbukiretu mwachifundo.
Kungoyambira pamene ndinamasulidwa, Yehova wandidalitsa ndi maudindo ambiri autumiki. Ndinakhalanso mpainiya wapadera, ku Gronau, Germany, ndiponso woyang’anira dera kumapiri a Alps a muno mu Germany. Pambuyo pake ndinapemphedwa kuloŵa kalasi ya 31 ya Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower yophunzitsa umishonale. Programu yathu yotsiriza maphunziro inachitikira ku Yankee Stadium pamsonkhano wadera wamitundu yonse wa Mboni za Yehova mu 1958. Anandipatsa mwaŵi woti ndilankhule ndi khamu lalikulu la abale ndi alongo ndi kusimba zokumana nazo zanga zina.
Nditatsiriza maphunziro ndinapita ku Chile kukatumikira monga mmishonale. Kumeneko ndinakhalanso woyang’anira dera, cha kummaŵa kwenikweni kwa Chile—ndinatumizidwadi kumalekezero a dziko lapansi. Mu 1962, ndinakwatira Patsy Beutnagel, mmishonale wokongola wa ku San Antonio, Texas, U.S.A. Ndinasangalala zaka zambiri potumikira Yehova ndili naye pambali pangapa.
Pazaka zoposa 70 za moyo wanga, ndaona zabwino zambiri ndi masautsonso ambiri. Wamasalmo anati: “Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.” (Salmo 34:19) Mu 1963, tidakali ku Chile konko, ine ndi Patsy tinasweka mtima ndi imfa yatsoka ya mwana wathu wakhanda wamkazi. Kenako, Patsy naye anadwala kwambiri, ndipo tinasamukira ku Texas. Pamene anali wazaka 43 zokha, anamwalira, mwatsoka nayenso. Kaŵirikaŵiri ndimapemphera kuti Yehova adzamkumbukire mwachifundo mkazi wanga wokongolayo.
Tsopano, ngakhale ndili wodwaladwala ndi wokalamba, ndine mpainiya wokhazikika ndiponso mkulu muno mu Brady, Texas. Zoonadi, moyo sunali wosangalatsa nthaŵi zonse, ndipo pangakhalebe mayeso ena amene ndidzakumana nawo. Komabe, monga wamasalmoyo ndinganene kuti: “Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu.”—Salmo 71:17.
[Zithunzi patsamba 23]
(1) Lerolino ndikutumikira monga mkulu komanso mpainiya, (2) ndili ndi Patsy, ukwati wathu utayandikira,(3) m’kalasi lake Herr Schneider, (4) amayi, a Teresa, omwe anafera ku Ravensbrück