Uthenga Wabwino wa Paradaiso ku Tahiti
TAHITI! Dzinali likuoneka kuti limatanthauza kukongola kochititsa kaso. Linatchuka ndi amisiri ndi olemba monga Paul Gauguin, Robert Louis Stevenson, ndi Herman Melville, amene zithunzithunzi zawo zojambula pamanja ndi zolemba zawo zosonyeza kukongola kwa m’madera otentha ndi kudekha kwa zisumbu za ku South Sea kunakopa anthu ambiri.
Tahiti ndicho chisumbu chachikulu koposa mwa zisumbu zoposa 120 za ku French Polynesia, imene ili ku South Pacific. Ngakhale kuti anthu ambiri amaganiza kuti chisumbu cha ku South Sea chimenechi nchimodzimodzi ndi paradaiso, anthu a ku Tahiti afunikirabe kumva za paradaiso wina amene adzadza posachedwapa. (Luka 23:43) Mboni za Yehova zokwanira 1,918 lerolino ku Tahiti, nzotanganitsidwa ndi kuuza anthu 220,000 za uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posachedwapa udzadzetsa mikhalidwe yeniyeni ya paradaiso osati ku Tahiti kokha komanso padziko lonse lapansi.—Mateyu 24:14; Chivumbulutso 21:3, 4.
Kwa zaka zambiri ntchito yolalikira ku Tahiti inali kuyendetsedwa ndi ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ya ku Fiji, imene ili pamtunda wa makilomita 3,500. Chifukwa cha mtunda wautaliwu zinthu zinali zovuta, mwakuti ntchito siinali kuyenda bwino. Choncho, pa April 1, 1975, ofesi yanthambi inakhazikitsidwa ku Tahiti, ndipo zimenezi zinapangitsa ntchito ya Akristu oona a gawo limeneli kusintha kwambiri. Kodi chinapangitsa kusintha kumeneku nchiyani, nanga ntchito yolalikira inayamba bwanji ku Tahiti?
Kuyamba Pang’onopang’ono
Uthenga wabwino wa Ufumu unayamba kulalikidwa ku Tahiti cha m’ma 1930, ndipo anthu ambiri okhala pachisumbuchi, amene amalemekezadi Baibulo, anasonyeza chidwi chachikulu. Komabe, chifukwa cha chiletso cha boma ndi malamulo ena, pachisumbu chimenechi panalibe Mboni mpaka chakumapeto kwa ma 1950. Panthaŵiyo, Agnes Schenck, nzika ya ku Tahiti imene inali kukhala ku United States, anaganiza zobwerera ku Tahiti pamodzi ndi mwamuna wake ndi mwana wake wamwamuna. Iye akufotokoza mmene zinthu zinayendera.
“Pamsonkhano wachigawo wa mu 1957 ku Los Angeles, Mbale Knorr [pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo] anafotokoza kuti kunali kusoŵa kwakukulu kwa ofalitsa Ufumu ku Tahiti. Panthaŵiyo nkuti patatha chaka chimodzi nditabatizidwa, ndipo ndinanena kuti, ‘Tiyenitu tipite ku Tahiti!’ Mabanja aŵiri, banja la a Neill ndi banja la a Carano, mabwenzi athu apamtima, anamva zimene ndinanena. Anatiuza kuti iwo akanakonda kutsagana nafe, koma tinali ndi ndalama zochepa. Mwamuna wanga anali atadwala kwa nthaŵi yaitali, ndipo mwana wanga wamwamuna anali wakhanda. Choncho kunali kovuta kuti tipite. Abale a m’mipingo yoyandikana nayo anamva za cholinga chathu, ndipo anatitumizira ndalama ndi katundu wa m’nyumba. Kenaka m’May 1958 tinanyamuka pasitima ya m’madzi paulendo wopita ku Tahiti ndipo zina mwa zinthu zimene tinatenga zinali nsalu 36 zapabedi!
“Pamene tinafika ku Tahiti, malowa anandionekera achilendo kwambiri chifukwa panali patapita zaka 20 chichokere pachisumbuchi. Tinayamba kulalikira, koma tinali kusamala kwambiri chifukwa chakuti ntchito yathu yachikristu imeneyi inali yoletsedwa. Tinali kubisa magazini, ndipo tinali kugwiritsira ntchito Baibulo lokha. Poyamba tinachitira umboni kwa amene anali kale ndi masabusikripishoni a magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
“Clyde Neill ndi David Carano, pamodzi ndi mabanja awo, anadzatipeza utatha msonkhano wamitundu yonse wa ku New York City mu 1958. Tinayamba kulalikira pamodzi ndipo tinali kuitana anthu kuti adzamvetsere nkhani zoperekedwera m’nyumba za abale. Pang’ono ndi pang’ono zinthu zinalongosoka, ndipo tinayamba phunziro la Baibulo ndi gulu la anthu 15. Patatha miyezi itatu mabanja a a Neill ndi a Carano anayenera kubwerera chifukwa chakuti mavisa awo ochezera anatha ntchito. Choncho abale anaganiza kuti iwo asanachoke, abatiziretu okondwerera onse amene anayeneretsedwa. Ndinapatsidwa mwaŵi wotembenuza nkhani yoyamba yaubatizo. Panthaŵiyi anthu asanu ndi atatu a pachisumbuchi anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mwa ubatizo. Kenaka mabanja a a Neill ndi a Carano anabwerera ku United States.
“Ntchito yolalikira inapitirizabe. Tinagaŵana m’magulu ang’onoang’ono ndipo tinali kukalalikira madzulo. Nthaŵi zambiri tinali kukambitsirana ndi okondwerera mpaka pakati pausiku. Nthaŵi zina ngakhale atumiki achiprotesitanti anali kukhala nafe m’makambitsirano ameneŵa. Podzafika 1959 mpingo woyamba unapangidwa. Ndipo mu 1960 tinasangalala kwambiri pamene boma linaloleza gulu la Mboni za Yehova mwalamulo. Zaka zimenezo zoyambirira zinali zachimwemwe ndi kupita patsogolo kwauzimu. Yehova anadalitsadi lingaliro lathu la kupita kumene kunali kusoŵa kwakukulu.” Mlongo Schenck tsopano ali ndi zaka 87 zakubadwa, ndipo akutumikirabe Yehova mokhulupirika mumpingo wake.
Ntchito Inafutukuka
Mu 1969 Mboni ziŵiri za ku France, Jacques ndi Paulette Inaudi, anatumizidwa ku Tahiti monga apainiya apadera. Jacques akukumbukira kuti: “Pamene tinafika ku Tahiti, kunali ofalitsa 124 okha, mpingo umodzi ku Papeete, ndi apainiya apadera aŵiri ku Vairao, pakachisumbu.” Kamtunda kakang’ono kakatali kanalumikiza kachisumbu kameneka ndi Tahiti. Msonkhano Wamitundu Yonse wa “Mtendere Padziko Lapansi” unali pafupi kuchitika. “Imeneyi inali nthaŵi yanga yoyamba kulinganiza msonkhano waukulu,” akupitiriza motero Jacques. “Tinakonza programu yachingelezi kaamba ka alendo, tinakonza gulu loimba nyimbo za Ufumu, ndipo tinayeseza maseŵero aŵiri. Ntchito yonseyi inachitidwa ndi ofalitsa 126 okha. Ndikhulupirira kuti Yehova ndiye anachita mbali yaikulu.” Kupezekapo kwa anthu 488 kunawasangalatsa kwambiri abale a pachisumbucho. Ambiri a iwo, kunali kuyamba kuonanapo ndi Mboni zinzawo zochokera m’maiko ena.
Patapita nthaŵi yochepa, Jacques Inaudi anamsankha kukhala woyang’anira woyendayenda. Pamene iye anachezera zisumbu zosiyanasiyana, anapeza kuti kunali okondwerera ambiri koma kunali ofalitsa Ufumu ochepa kuti awathandize. “Nchifukwa chake ndinalimbikitsa mabanja ambiri kuti apite kuzisumbu zimenezi kukatumikira kumene kunali kusoŵa kwakukulu,” akufotokoza motero Jacques. “Choncho pang’ono ndi pang’ono, uthenga wabwino unafalitsidwa m’magulu amenewo a zisumbu.” Mbale Inaudi anatumikira monga woyang’anira woyendayenda kuyambira mu 1969 mpaka mu 1974, ndipo lerolino iye ndi mkulu mu umodzi wa mipingo ya ku Tahiti.
Mwa anthu amene anavomera pempho la Mbale Inaudi panali Auguste Temanaha, amene anali mmodzi wa anthu asanu ndi atatu amene anabatizidwa mu 1958. Iye akusimba zimene zinachitika. “Mu 1972 woyang’anira dera, Jacques Inaudi, anatilimbikitsa kuti tilingalire za kukatumikira ku Huahine, chimodzi mwa zisumbu za m’dera la Leeward Islands zimene zili m’gulu la zisumbu za Society Islands. Ndinali kukayikira chifukwa chakuti ndinali kungopereka nkhani yoŵerenga Baibulo mumpingo ndiye ndinaganiza kuti ndinali wosayenerera kupatsidwa ntchito imeneyo. Komabe, Mbale Inaudi anapitirizabe kundiuza kuti, ‘Usadandaule, ungakwanitse zimenezo!’ Patapita nthaŵi tinavomera. Choncho, mu 1973 tinagulitsa zonse tinali nazo ndipo tinapita ku Huahine ndi ana athu atatu.
“Titafika, ndinapeza kuti ndiyenera kuyambitsa zonse—Phunziro la Nsanja ya Olonda, Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ndi zina. Zinali zovuta, koma tinalandira chitetezo ndi thandizo la Yehova. Nthaŵi zambiri iye anatithandiza kupeza malo okhala. Kenaka, pamene gulu la otsutsa linayesa kupitikitsa Mboni pachisumbucho, mtsogoleri wina wandale anatitetezera. Zoonadi, Yehova anatiyang’anira nthaŵi yonseyo.” Tsopano, kuli mipingo iŵiri ku Huahine—mpingo wachifrenchi umene uli ndi ofalitsa 23 ndi wina wachitahiti umene uli ndi ofalitsa 55.
Mu 1969, Hélène Mapu anatumizidwa monga mpainiya wapadera kukagwira ntchito pakachisumbuka. “Panalidi okondwerera ambiri pakachisumbu kameneka, ndipo posapita nthaŵi, ndinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri,” akutero Hélène. Mwamsanga mpingo waung’ono unapangidwa ku Vairao, koma kunalibe akulu. M’kupita kwa nthaŵi, Colson Deane, amene ankakhala ku Papara pamtunda wa makilomita 35, anathandiza. “Tinafunikira kukonzekera bwino kuti tikatumikire ku Vairao,” akufotokoza motero Mbale Deane. “Ndinali kugwira ntchito ku Faaa, makilomita 70 kuchokera ku Vairao kumbali ina ya chisumbucho. Nditaŵeruka kuntchito, ndinali kuthamangira kunyumba, kukatenga banja langa, ndi kupita ku Vairao. Pambuyo pake tinasamukira ku Faaa kaamba ka ntchito yanga. Kodi tikanathabe kuthandiza Mpingo wa ku Vairao? Tinafunitsitsadi kuthandiza abale a kumeneko, choncho tinaganiza zopitirizabe kuwathandiza. Pamadzulo a misonkhano nthaŵi zambiri tinali kupita kunyumba pakati pausiku chifukwa chakuti tinali kuperekeza ena amene analibe galimoto. Tinachita zimenezi kwa zaka zisanu. Tsopano nzosangalatsa kuona mipingo inayi kumbali imeneyi ya chisumbu, ndipo timasangalala tikamakumbukira masiku amenewo.”
Ku Tahiti Kukhala Nthambi
Podzafika 1974 chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu ku Tahiti chinali chitafika 199. Chaka chotsatira, pamene N. H. Knorr ndi F. W. Franz, pulezidenti wapanthaŵiyo wa Watch Tower Society ndi wachiŵiri wake, anadzachezera French Polynesia, iwo anaona kuti kunali bwino kuti ntchito yolalikira iziyendetsedwera ku Tahiti, osati ku Fiji wokhala pamtunda wa makilomita oposa 3,500. Choncho, pa April 1, 1975, nthambi ya Tahiti inakhazikitsidwa, ndipo woyang’anira dera, Alain Jamet, anasankhidwa kukhala woyang’anira nthambi.
Zaka zingapo zapitazo, Mbale Jamet anafotokoza za madalitso aakulu ochokera kwa Yehova. “Chiyambire mu 1975 tayesetsa kufalitsa uthenga wabwino kuzisumbu zonse ndi magulu a zisumbu onse m’gawo lathu, amene ali mtunda wofanana ndi Western Europe kukula kwake. Zotsatirapo zake zakhala zosangalatsa kwambiri. Podzafika mu 1983 chiŵerengero cha ofalitsa chinali chitakwera kufika 538. M’chaka chimenecho ofesi yanthambi ndi Nyumba Yabeteli inamangidwa ku Paea. Tsopano, kuli ofalitsa pafupifupi 1,900 m’mipingo yosiyanasiyana 30 ya m’zisumbu za Society Islands, mpingo umodzi ndi gulu limodzi lokhala kwalokha kuzisumbu za Austral Islands, mpingo umodzi ndi magulu aŵiri okhala kwaokha ku Marquesas, ndiponso magulu ena ambiri okhala kwaokha ku Tuamotu ndi kuzisumbu za Gambier Islands. Nyumba zambiri Zaufumu zatsopano zikumangidwa—zitatu ku Marquesas ndiponso zisanu ndi ziŵiri ku Tahiti—kuti zizithandiza gulu lomawonjezereka la achatsopano amene akusonkhana nawo. Kuyambira zaka 20 zapitazo, Yehova wadalitsadi zoyesayesa zathu zolimirira munda wa Tahiti.”
Pakali Zochita Zambiri
Pali chiyembekezo chachikulu cha chiwonjezeko ku French Polynesia. Pa March 23, 1997, anthu okwana 5,376 anasonkhana pamodzi ndi Mboni za Yehova m’French Polynesia yense kaamba ka Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. Kuti tithandize zosoŵa zauzimu za anthu okondwerera ameneŵa, zofalitsa zathu za Baibulo zikupezeka m’zinenero zambiri zakuno. Kuwonjezera pa Chitahiti, mabuku afalitsidwa m’Chipaumotu, cholankhulidwa ku Tuamotu Archipelago, ndiponso m’Chimarques chakumpoto ndi chakummwera.
Chiwonjezeko chomakulirakulirabe pamodzi ndi zochitika zosangalatsa zathandiza ofalitsa Ufumu ku Tahiti kuzindikira mokwanira chikondi ndi chisamaliro cha Yehova, “amene chifuniro chake nchakuti anthu amtundu uliwonse apulumuke nafike pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi,” ngakhalenso m’zisumbu zakutali za ku South Sea. (1 Timoteo 2:4, NW) Mboni za Yehova ku Tahiti ndi m’zisumbu zina za ku French Polynesia zikukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.”—Yesaya 51:5.
[Mapu patsamba 26]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Nthambi ya Tahiti imasamalira zosoŵa za ku French Polynesia
AUSTRALIA
[Chithunzi patsamba 25]
Kuchokera Kulamanzere kupita Kulamanja: Alain Jamet, Mary-Ann Jamet, Agnes Schenck, Paulette Inaudi ndi Jacques Inaudi
[Chithunzi patsamba 27]
Ofesi Yanthambi ya Tahiti