Choonadi Chimasanduliza Miyoyo
NZOMVETSA chisoni, komabe zoona, kuti miyoyo ya anthu ambiri lerolino njovuta, ndiponso yopanda chiyembekezo. Kodi nkotheka kuti anthu amenewo akhale achimwemwe? Ena ndi apandu ndipo amavulaza anansi awo. Kodi amenewo angadzakhale anthu abwino pakati pa anzawo? Yankho la mafunso aŵiri onseŵa nlakuti inde. Anthu angasinthe. Miyoyo ingasandulike. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti nzotheka pamene analemba kuti: “Mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:2.
Kungotchula za “chifuno cha Mulungu . . . changwiro” kumatikumbutsa zimene Yesu anauza ophunzira ake zaka zoposa 20 Paulo asanalembe mawu amenewo. Yesu anati: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Pamene anati “choonadi,” Yesu anatanthauza chidziŵitso chouziridwa ndi Mulungu—makamaka chidziŵitso chonena za chifuniro cha Mulungu—chimene chasungidwira ife m’Baibulo. (Yohane 17:17) Kodi choonadi cha m’Baibulo chimamasuladi anthu? Kodi kukhala motsatira chifuniro cha Mulungu kumasandulizadi miyoyo? Ndithudi kumaisanduliza. Tangoganizirani zitsanzo zoŵerengekazi.
Kukhala ndi Chifuno m’Moyo
Si kale kwambiri pamene Moisés, wa ku Gibraltar, anali munthu wopanda chimwemwe. Iye akuti: “Ndinali chidakwa ndipo ndinkagona pakhwalala. Ndinangosakazika. Usiku uliwonse ndinkapempha Mulungu kuti andichitire chifundo ndi kuti asandilole kuti ndione tsiku lina. Ndinkagwetsa misozi pofunsa Mulungu chifukwa chake ndinali moyo ngati ndinali wachabechabe, wosoŵa ntchito, wopanda banja, ndiponso wopanda aliyense wondithandiza. Ndizikhalabe moyo chifukwa chanji?” Ndiyeno, kanthu kena kanachitika.
Moisés akupitiriza kuti: “Ndinadziŵa kuti Mulungu anali atamva pemphero langa pamene ndinakumana ndi Roberto, mmodzi wa Mboni za Yehova. Roberto anandipatsa Baibulo ndi kope lina lothandiza kuphunzira Baibulo lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?a Tsiku ndi tsiku tinkaphunzira Baibulo pamodzi pabenchi pamene ndinkagona usiku. Patatha mwezi umodzi Roberto ananditenga nkupita nane ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yapafupi. Posakhalitsa, choonadi cha m’Baibulo chinali chitasinthiratu maganizo anga. Sindimagonanso pakhwalala, sindimamwanso kapena kusuta fodya. Moyo wanga wasintha, ndipo ndili wachimwemwe. Ndikuyembekezera kubatizidwa posachedwapa kuti ndizitumikira Yehova monga mmodzi wa Mboni zake.”
Kumenekotu nkusintha kwakukulu. Ngati anthu alibe chiyembekezo, nthaŵi zambiri chimakhala chifukwa cha kupanda chidziŵitso. Samadziŵa za Mulungu kapena za zifuno zake zodabwitsa. Ponena za Moisés, atangopeza chidziŵitso chimenecho, chinampatsa mphamvu ndipo chinamlimbikitsa kusintha njira yake ya moyo. Mulungu anayankha pemphero la wamasalmo ngati kuti anali Moisés yemwe anapemphera kuti: “Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere: zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.”—Salmo 43:3.
Ku Belize, Daniel anakumana ndi zofananazo. Daniel sankagona pakhwalala—anali pantchito yolemekezeka. Koma kwa zaka 20 ankayesetsa kusiya kumwa mankhwala osokoneza bongo ndi mkhalidwe wachiwerewere. Ngakhale kuti anakula ali Mkatolika, Daniel sankaona kuti moyo unali ndi tanthauzo ndipo anali kukayikira zoti Mulungu aliko. Anapita kumatchalitchi osiyanasiyana kukafuna thandizo koma anapeza kuti mabwenzi ake ochuluka omwe ankapitanso kutchalitchi, ngakhale mabwenzi ake omwe anali atsogoleri achipembedzo, nawonso ankamwa mankhwala osokoneza ubongo kapena moŵa. Kwinaku, mkazi wake anali atatsala pang’ono kulekana naye.
Atasoŵa chochita, Daniel anapita kuchipatala cha osokonezeka maganizo. Komabe, anadziŵa kuti atangotulukamo, pasanapite nthaŵi adzayambanso kumwa mankhwala osokoneza bongo akapanda kuthandizidwa. Koma kuthandizidwa motani? Mu May 1996, patapita masiku aŵiri Daniel atatuluka m’chipatalamo, iye anakafikira mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo anamdabwitsa ndi pempho lakuti: “Chonde ndiphunzitseni Baibulo.” Mboniyo inakonza kuti aziphunzira ndi Daniel kaŵiri pamlungu, ndipo mwamsanga Daniel anawongolera moyo wake kuti ugwirizane ndi chifuniro cha Mulungu, kenako anasiya mabwenzi ake akale nkupeza mabwenzi achikristu omwe samwa mankhwala osokoneza ubongo kapena moŵa ndiponso omwe amapeŵa uchiwerewere. Choncho, Daniel anaona kuti zimene Baibulo limanena nzoona, kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Pasanapite nthaŵi, iye anadzati: “Ino ndi nthaŵi yoyamba m’moyo wanga kudziŵa tanthauzo la kukhala ndi chikumbumtima choyera.” Moyo wa Daniel nawonso unasandulika.
Ku Puerto Rico, munthu winanso anasandulika modabwitsa. Anali m’ndende ndipo ankaonedwa monga woopsa kwambiri, chifukwa anali atapha anthu angapo. Kodi choonadi cha m’Baibulo chikanatha kumsintha? Inde. Mmodzi wa Mboni za Yehova anampatsa makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndipo iyeyo anapemphanso ena mwamsanga. Anayamba naye phunziro la Baibulo, ndipo pamene choonadi cha m’Baibulo chinayamba kukhudza mtima wake, anthu onse anamuona akusintha. Umboni woyamba wa kusintha kwake unali wakuti anameta tsitsi lake lalitali ndi ndevu zake zanyankhalala.
Baibulo limati Mulungu amakhululukira anthu amene amalapadi nkusintha njira yawo ya moyo. Paulo analemba kuti: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? . . . Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.” (1 Akorinto 6:9, 11) Mosakayikira, mawu ameneŵa anamtonthoza munthu ameneyo, monga momwe anamtonthozera mawu a Machitidwe 24:15, akuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Iye anati: “Ndikufuna kudzakhalapo pamene anthu akufa azidzaukitsidwa kuti ndidzapemphe amene ndinapha kuti adzandikhululukire.”
Banja Latsopano
Tsiku lina Luis, mlaliki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova ku Argentina, anadziŵa mnyamata wina yemwe anakula movutikira kwambiri. Popeza kuti makolo ake anamsiya atangobadwa kumene, iye anakulira m’nyumba zosiyanasiyana zosungiramo amphaŵi. Pamene anali ndi zaka ngati 20, anadziŵa kumene kunali mayi ake ndipo anaganiza zokakhala pafupi nawo. Anagwira ntchito zedi, nkusunga ndalama zambiri, ndipo anapita kumzinda kumene kunali amayi ake. Iwo anamlola kukhala mpaka ndalama zake zinatha ndiyeno anamuuza kuti achoke. Kukanidwa kumeneku kunampangitsa kufuna kudzipha.
Komabe, Luis anamphunzitsa mwamuna ameneyo choonadi cha m’Baibulo. Choonadi chimenecho chimaphatikizapo lonjezo lakuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Mnyamatayo anapeza kuti anali ndi Atate wakumwamba yemwe sakanamsiya konse. Tsopano mnyamatayo ngwokondwa pokhala m’banja latsopano, la Yehova.
Mwamuna winanso m’dziko lomwelo anauza mmodzi wa Mboni za Yehova kuti amakonda magazini ya Nsanja ya Olonda. Chifukwa? Chifukwa chakuti inapulumutsa ukwati wake. Zikuoneka ngati munthu ameneyo, poŵeruka kuntchito tsiku lina anaona m’chitini cha zinyalala magazini ya Nsanja ya Olonda yokhala ndi mutu wazilembo zazikulu wakuti “Chisudzulo.” Popeza kuti ukwati wake unali utatsala pang’ono kutha ndipo iye ndi mkazi wake anali atayamba kufunsira kuboma kuti liwamasule, anaitola magazini ija nkuyamba kuiŵerenga. Anapita nayo kunyumba kuti akaiŵerenge ndi mkazi wake. Mwamuna ndi mkazi wakeyo anayesa kugwiritsira ntchito uphungu wa m’Baibulo womwe unali m’magaziniyo. (Aefeso 5:21–6:4) Mwamsanga, unansi wawo unawongokera. Analeka zokafunsira kuti alekane ndipo tsopano akuphunzira Baibulo monga mwamuna ndi mkazi wake ogwirizana.
Ku Uruguay, mwamuna winanso wotchedwa Luis analibe chimwemwe ngakhale pang’ono. Kumwerekera ndi mankhwala osokoneza bongo, kukhulupirira mizimu, kulambira mafano, uchidakwa—zimenezi ndizo zina mwa zinthu zimene zinapangitsa moyo wake kusokonekera. Potsirizira, Luis, atanyansidwa kotheratu, anangokhala wokana Mulungu. Bwenzi lina linampatsa buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?b Limenelo linampangitsa kumaonana ndi Mboni za Yehova kwa kanthaŵi, koma Luis sanachedwe kubwereranso ku uchidakwa ndi mankhwala osokoneza ubongo. Tsiku lina, atakhala m’dzenje la zinyalala, ali wachisoni kwambiri, anapemphera kwa “atate wa Yesu Kristu,” popeza sanali kulidziŵa dzina la Mulungu.
Anapempha Mulungu kuti amsonyeze ngati panali chifukwa chilichonse chokhalira padziko. Luis anati: “Kucha kwa tsiku linalo, wina yemwe ndinkadziŵa, anandipatsa buku limene sanali kuligwiritsiranso ntchito. Mutu wake? Revelation—Its Grand Climax At Hand!c Bukulo linamyankha funso lake. Luis anapempheranso kuti athandizidwe kupeza chipembedzo chimene chikanamsonyeza njira yolambirira Mulungu. Zodabwitsa! Belu lapakhomo linalila, ndipo Mboni za Yehova ziŵiri zinali chilili panja. Nthaŵi yomweyo Luis anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Anaphunzira msanga ndipo tsopano akuganiza kuti ngwodala kukhala Mboni yobatizidwa. Pano ali ndi moyo wabwino ndipo akuthandiza enanso kudziŵa chifuno cha moyo wawo. Kwa iyeyo, mawu a Salmo 65:2 anakhala oona: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.”
Ku Philippines, Allan anali mwana wasukulu wachangu kwambiri pa ndale. Anali wa gulu lomwe cholinga chake chinali “cha kupasula boma kuti mibadwo yamtsogolo idzakhale yolingana.” Komabe, tsiku lina Mboni za Yehova zinamchezera ndipo anaphunzira m’Baibulo za chifuno cha Mulungu pa anthu. Chifuno chimenecho chimaphatikizapo lonjezo louziridwa lakuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) Allan anati: “Mwamsanga ndinapeza kuti zolinga zimene tinali kumenyera nkhondo, Baibulo linali litazilonjeza kalekale. Zinthu zimene tinali kukhumba kwambiri zidzakwaniritsidwa mu Ufumu wa Mulungu.” Tsopano Allan akuchirikiza Ufumu wa Mulungu ndipo akuthandiza enanso kukhulupirira choonadi cha m’Baibulo.
Inde, miyoyo imasandulikadi anthu akamamvera choonadi cha Mawu a Mulungu, Baibulo. Ndithudi, ikudza nthaŵi imene anthu onse amoyo adzatsatira chifuniro cha Mulungu m’moyo wawo Kumenekotu kudzakhala kusandulika kwakukulu! Pamenepo, ulosi uja udzakhala utakwaniritsidwa, wakuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.