Kufikira Ochulukirapo ndi Uthenga Wabwino
PAMENE ndinali kuganizira za anthu a m’dziko limene ndimakhala, ndinaona kuti ambiri amadziŵa Mboni za Yehova kokha kuchokera m’nkhani zofalitsidwa. Ndinaganiza kuti, anthu amenewa ayenera kufikiridwa, kotero kuti angadziŵe amene Mboni za Yehova ali ndi zimene iwo kwenikweni amakhulupirira. Koma kodi ndikanawathandiza bwanji? Mwamuna wanga ndi mkulu wachikristu, ndipo anandipatsa chitsogozo ndi malingaliro anzeru.
Tinapeza lingaliro lothandiza m’nkhani yakuti “Magazini Amene Amapatsa Chitonthozo Chenicheni,” yomwe inatulutsidwa mu Galamukani! yachingelezi ya January 8, 1995. Ponena za ntchito ya Mboni ina, nkhaniyo inati: “Amayesetsa kusonkhanitsa magazini akale a Galamukani! amene Mboni zina zawunjika kunyumba. Kenako amafikira mabungwe amene akuona kuti angasonyeze chidwi chapadera m’nkhani zina.”
Ndi chithandizo cha mwamuna wanga, mosakhalitsa ndinasonkhanitsa magazini ochuluka. Ndinali wokhoza kusankha m’magaziniwa nkhani zosiyanasiyana zoyenerera anthu amene ndikayesa kuwafikira.
Pakugwiritsira ntchito mabuku a manambala atelefoni ndi mabuku olembamo anthu, ndinapanga mpambo wa maina a zipatala, nyumba zogonamo achinyamata, ndi nyumba zosamalira okalamba. Ndinandandalikanso maina a anthu oyang’anira za maliro, oyang’anira ndi alangizi a sukulu, ofufuza za mankhwala, ndi akuluakulu a ndende ndi mabwalo oweruza milandu. Mpambo wanga unaphatikizapo oyang’anira malo a anthu omwerekera ndi zakumwa zoledzeretsa ndi mankwala osokoneza bongo, mabungwe a zachilengedwe, a anthu olemala ndi ovutika ndi nkhondo, ndi ofufuza zakudya zopatsa thanzi. Sindinaiwalenso akuluakulu a maofesi oona za umoyo, za chikhalidwe cha anthu, ndi za m’banja.
Kodi Ndikanena Chiyani?
Chinthu choyamba chimene ndinachita pamene ndinali kuchezera anthu kunali kudzizindikiritsa bwino lomwe amene ndinali. Kenako ndinali kutchula kuti ulendo wanga ndi wamphindi zochepa chabe.
Pamene ndaonana ndi mkulu wa pamalopo, ndinkati: “Ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Komabe, sindinabwerere kuti tikambitsirane za chipembedzo, zimene zingakhale zosayenerera m’nthaŵi ya ntchito.” Kaŵirikaŵiri munthuyo anali kumasuka kwambiri. Kenaka, pogwirizanitsa ndemanga zanga ndi mkhalidwewo, ndinali kupitiriza kuti: “Kubwera kwanga kuli ndi zolinga ziŵiri. Choyamba, ndikufuna kuti ndikuyamikireni chifukwa cha ntchito imene ofesi yanu ikugwira. Sikuyeneradi kuonedwa mopepuka kuti munthu wina amawononga nthaŵi ndi nyonga zake kaamba ka anthu onse. Zimenezi zikuyeneradi kuyamikiridwa.” Nthaŵi zambiri munthu wofikiridwa mwa njirayi anali kudabwa.
Pofika tsopano ndiyesa munthuyo anali kudabwa kuti nanga chifukwa chachiŵiri cha ulendo wanga chinali chiyani. Ndinali kupitiriza kuti: “Chifukwa chachiŵiri chomwe ndabwerera ndi ichi: Ndasankha nkhani zina kuchokera m’magazini athu a Galamukani!, magazini amene amafalitsidwa padziko lonse, zimene zikulongosola za ntchito yomwe inu mumagwira ndi mavuto omwe amapezekapo. Ndili wotsimikiza kuti inu mungakonde kudziŵa mmene magazini ofalitsidwa padziko lonse amapendera mavuto amenewa. Ndidzakondwa kukusiyirani magaziniwa.” Kaŵirikaŵiri ndinali kuuzidwa kuti anali kuyamikira kuyesayesa kwanga.
Zotulukapo Zodabwitsa ndi Zofupa
Pamene ndinagwiritsira ntchito kafikidwe kameneka, anthu ambiri anandilandira mwaubwenzi; kokha munthu mmodzi mwa anthu 17 anakana. Ndinali ndi zokumana nazo zochuluka zimene zinali ponse paŵiri zodabwitsa ndi zofupa.
Mwachitsanzo, pambuyo pa maulendo anayi ndi kuyembekezera mopirira, ndinakhoza kukumana ndi woyendera sukulu za m’deralo. Anali munthu wotangwanidwa kwambiri. Komatu, anali waubwenzi kwambiri ndipo analankhula nane kwa kanthaŵi. Pamene ndinali kuchoka anati: “Ndikuyamikiradi zomwe mwachita, ndipo mosakayikira ndidzaŵerenga magazini anu mosamalitsa.”
Panthaŵi ina, ndinapita ku khoti la kuboma, ndipo ndinakumana ndi woweruza wamkulu, mwamuna wachikulirepo. Pamene ndinaloŵa mu ofesi yake, mokhumudwa anasiya kuŵerenga.
“Nthaŵi yantchito ndi Lachiŵiri mmaŵa basi, ndidzakhala womasuka kulankhula nanu panthaŵiyo,” anatero mozaza.
“Pepani kuti ndabwera panthaŵi yolakwika,” ndinayankha mofulumira nkuwonjezera kuti, “Inde, ndingasangalale kubweranso panthaŵi ina. Koma nkhani imene ndinabwera nayo kwenikweni ndi yaumwini.”
Tsopano woweruza uja anayamba kufunsitsa. Osati ndi mawu ozaza, anafunsa chimene ndinali kufuna. Ndinanenanso kuti ndidzabweranso Lachiŵiri.
“Chonde khalani pansi,” anandiumiriza, zinandidabwitsa. “Kodi mukufuna chiyani?”
Panali makambitsirano osangalatsa, ndipo anapepesa kuti sanali waubwenzi poyamba chifukwa analidi wotanganidwa kwambiri.
“Kodi mukudziŵa chimene chimandisangalatsa ndi Mboni za Yehova?” woweruzayo anafunsa patapita kanthaŵi. “Ali ndi mfundo zabwino zimene amazitsatira. Hitler anayesa kuchita chilichonse akanatha, koma Mboni sizinapitebe ku nkhondo.”
Pamene ine ndi mlongo wina tinaloŵa mu ofesi ina, alembi amene analimo anatizindikira. Mlembi wamkulu mosakhudzidwa analankhula kuti, “Mkulu wapano sacheza ndi anthu alionse.”
“Koma acheza nafe,” ndinayankha mofatsa, “chifukwa ndife Mboni za Yehova. Sindife odandaula, ndipo kucheza kwathu sikupitirira mphindi zitatu.” Mumtima mwanga ndinapemphera mofunitsitsa kuti, “O Yehova, chonde lolani kuti zitheke!”
Mlembiyo anayankha mopanda nsangala kwenikweni, “Chabwino, ndiye ndiyesa.” Anachoka. Patatha pafupifupi mphindi ziŵiri, zimene zinaoneka ngati zaka kwa ine, anabweranso ndi mkulu wa ofesiyo. Sananene kalikonse, anangotitsogolera kuofesi yake, tinadutsa zipinda zina ziŵiri.
Pamene tinayamba kucheza, anakhala waubwenzi kwambiri. Mofunitsitsa analandira magazini apadera a Galamukani! pamene tinamugaŵira. Tinathokoza Yehova kaamba ka mwaŵi umenewu wakupereka umboni wabwino wokhudza cholinga cha ntchito yathu.
Kuyang’ana pazokumana nazo zabwino zambirimbirizo, ndafika pakuzindikira bwino kwambiri zimene mtumwi Petro anali kunena pamene anati: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Chifuno cha Mulungu ndi chakuti anthu akakulidwe kosiyanasiyana, a zinenero zilizonse, ndi malo alionse apatsidwe mwaŵi wakudziŵa chifuno chake kaamba ka anthu ndi dziko lapansi.—Yoperekedwa.