Ukwati Wapadera Kwambiri
CHA kumpoto kwa Mozambique kuli chigwa chokongola pakati pa mapiri—ena a miyala yokhayokha, ena okhala ndi mitengo yambiri. Kumeneku nkumene kuli mudzi wa Fíngoè. Usiku m’nyengo yachisanu, thambo limangoti mbuu ndi nyenyezi, ndipo mwezinso umawala kwambiri moti nyumba za udzu za pamudzipo zimaoneka. Kumalo okongola ameneŵa nkumene kunachitikira ukwati wapadera kwambiri.
Anthu mazana ambiri anayenda kwa maola ambiri, ngakhale kutha masiku, kuti akapezeke pachochitika chapadera chimenechi. Ena anadutsa mitunda yachipululu ndiponso yoopsa yodzala ndi afisi, mikango, ndi njovu. Kuwonjezera pazola zawo, apaulendo ambiri anatenganso nkhuku, mbuzi, ndi ndiwo zamasamba. Atafika pamudzipo, anapita pamalo ena apamtetete pamene nthaŵi zambiri amachitira misonkhano yaikulu yachikristu. Ngakhale kuti anali atatopa ndi ulendowo, iwo anali achimwemwe, ndipo nkhope zawo zomwetulira zinasonyeza kuti akuyembekezera mwachidwi kuona zimene zidzachitika.
Kodi ndani anali kukwatirana? Anali ambiri! Inde, amuna ambiri ndi akazi awo. Iwo sanali kuchita ukwati wa anthu ambiri wotchuka ndi m’manyuzipepala momwe ayi. M’malo mwake, iwo anali anthu oona mtima ndiponso okhala ndi zolinga zabwino amene poyamba sanathe kulembetsa maukwati awo chifukwa chokhala kutali kwambiri ndi maofesi olembetsera ukwati. Okwatirana onsewa anadziŵa malamulo a Mulungu a ukwati ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Anaphunzira kuti ayenera kukwatirana mogwirizana ndi malamulo a dzikolo kuti akondweretse mlengi wawo, Woyambitsa ukwati, monga momwe Yosefe ndi Mariya anatsatirira malamulo olembetsa panthaŵi imene Yesu anabadwa.—Luka 2:1-5.
Kukonzekera Chochitikacho
Ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Mozambique inalingalira zothandizapo. Choyamba anafunsa Unduna wa Zachilungamo ndi Unduna wa za m’Dziko kulikulu la dzikolo, Maputo, kuti awafotokozere za njira zololedwa mwalamulo. Kenako, amishonale a kulikulu la chigawo cha Tete analankhula ndi akuluakulu aboma a kumeneko kuti awathandize kupanga makonzedwe owonjezereka. Tsiku linaikidwa loti amishonale ndi mabwana a ku Notary (Ofesi Yosaina Zikalata) ndi a ku Civil Identification Department (Dipatimenti Yopereka Zikalata Zodziŵikitsa Munthu) akapite kumudzi wa Fíngoè. Ndiponso, ofesi yanthambi inali itatumiza kale kalata yofotokoza malangizo kumipingo yonse yokhudzidwa. Mboni pamodzi ndi mabwanawo anachiyembekezera mwachidwi chochitika chapaderacho.
Tsiku Lamlungu, May 18, 1997, amishonale atatu pamodzi ndi akuluakulu aboma anafika ku Fíngoè. Akuluakulu a kumeneko anali atakonza malo abwino oti mabwanawo adzagonemo pafupi ndi ofesi yaikulu. Komabe, mabwana obwerawo anachita chidwi kwambiri ndi kuchereza kwa Mboni za Yehova moti anasankha zogona m’misasa pamodzi ndi amishonale. Iwo anadabwa kumva kuti mmodzi mwa ophika anali mkulu wa mumpingo wina wakomweko ndi kuti woyang’anira woyendayenda anali pakati pa antchito odzifunira ochita ntchito wamba pokonzekera ukwatiwo. Anaonanso chimwemwe cha amishonalewo, amene, mosadandaula, ankagona m’kamsasa ndi kusambira m’kachitini. Mabwanawo anali asanaonepo mgwirizano wathithithi ngati umenewu pakati pa anthu ochokera kumalo osiyanasiyana. Komabe, chimene chinawachititsa chidwi kwambiri ndicho kukhulupirika kumene anasonyeza popanga kudzimana kwakukulu kumeneko kuti atsatire malamulo a dzikolo ndi makonzedwe a Mulungu.
Chochitika Chosangalatsa
Pamene okwatiranawo anali kufika, nthaŵi yomweyo anali kukonzekera mbali yoyamba ya ukwatiwo: kupeza chikalata chonena za kubadwa kwa munthu. Onse anali kuyembekezera moleza mtima pamzere kutsogolo kwa antchito a ku Ofesi Yakalembera kuwafotokozera zoti alembe. Kenako anali kupita pamzere wina kukajambulitsa chithunzi, napita kwa antchito a ku Dipatimenti Yoyang’anira Zikalata Zodziŵikitsa Munthu kuti akatenge makhadi awo owadziŵikitsa. Kenako, anali kubwereranso kwa antchito a ku Ofesi Yakalembera kuti akawakonzere mtchato wofunikawo. Pambuyo pake, anaimirira moleza mtima kuyembekezera kuti awaitane maina awo pachokuzira mawu. Panali kukhudzika mtima polandira mitchato imeneyo. Panali chisangalalo chadzaoneni pamene mwamuna aliyense ndi mkazi wake anatukula mtchato wawo monga mphotho yamtengo wapatali kwambiri.
Zonsezi zinachitika dzuŵa lili ng’a. Koma dzuŵalo ndi fumbi sizinasokoneze chisangalalo cha anthuwo.
Amuna anavala bwino, ambiri anavala majekete ndi matayi. Akazi anavala zovala zakwawo, zophatikizapo nsalu yaitali, yamitundu yosiyanasiyana yotchedwa capulana yovala m’chiuno. Ena anabereka ana ndi nsalu yoteroyo.
Zinthu zinayenda bwino, koma ofuna mitchato anali ambiri moti sakanatha kuwapatsa onse patsiku limodzi. Kutada, akuluakulu aboma mokoma mtima analingalira zopitiriza kupereka mitchatoyo. Iwo anati sangalole “abale athu” kuyembekezera chifukwa chakuti abalewo anapanga kudzimana kwakukulu kuti afike kumeneko. Mzimu wamgwirizano ndiponso wodzimana umenewu sitidzauiŵala konse.
Kutada choncho kunazizira kwambiri. Pamene kuli kwakuti angapo anagona m’misasa, amuna ambiri ndi akazi awo anagona panja, atazungulira moto. Zimenezi sizinawalande chimwemwe chawo. Moto ukuthetheka, panali kumvekanso kuseka ndi nyimbo, zoimbidwa m’matchuni anayi. Ambiri anali kusimbirana za ulendo wawo, atagwira zikalata zawo zatsopanozo.
Mmamaŵa, ena analaŵira naloŵa m’mudzi kukagulitsa nkhuku zawo, mbuzi, ndi ndiwo zamasamba kuti athandizire kulipirira mitchato yawoyo. Ambiri anaperekadi nyamazo monga “nsembe,” kuzigulitsa pamtengo wotsika kwambiri kuposa mtengo wake weniweni. Kwa anthu osauka, mbuzi nchinthu chofunika kwambiri ndiponso chodula; komabe iwo anali ofunitsitsa kupereka nsembe imeneyi kuti akwatirane ndi kukondweretsa Mlengi wawo.
Zovuta za Ulendowo
Amuna ena ndi akazi awo anayenda ulendo wautali kuti akafike kumeneko. Nzimene Chamboko ndi mkazi wake, Nhakulira, anachita. Iwo anasimba nkhani yawo akuwamba mapazi pamoto usiku wachiŵiri wachochitikacho. Ngakhale kuti Chamboko ali ndi zaka 77 zakubadwa, diso lake limodzi nlakhungu ndipo linalo siliona bwino, iye anayenda pansi wopanda nsapato kwa masiku atatu motsagana ndi mpingo wake wonse, chifukwa chakuti anali wotsimikiza mtima kukalembetsa mwalamulo ukwati wake wazaka 52.
Anselmo Kembo, wazaka 72 zakubadwa, anali atakhala kale ndi Neri kwa zaka pafupifupi 50. Kutatsala masiku ochepa kuti apite paulendowo, minga yaikulu inamlasa kumwendo polima m’munda mwake. Anapita naye kuchipatala kuti akalandire mankhwala. Komabe, iye anasankha zoyenda ulendowo, akumatsimphina ndi mwendo wopweteka mpaka ku Fíngoè. Anayenda kwa masiku atatu. Anselmo anali ndi chimwemwe choonekeratu pamene ananyamula mtchato wake.
Winanso wokwatira mwatsopano wochititsa chidwi anali Evans Sinóia, wamitala wakale. Ataphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu, anasankha zolembetsa mwalamulo ukwati wake ndi mkazi wake woyamba, koma mkaziyo anakana, nathaŵira kwa mwamuna wina. Mkazi wake wachiŵiri, amenenso anali kuphunzira Baibulo, analola kulembetsa ukwati wawo. Aŵiriwo anayenda m’dera loopsa la mikango ndi nyama zina zakuthengo. Atayenda ulendowo kwa masiku atatu, iwonso anakhaladi okwatirana mwalamulo.
Ntchitoyo inamalizidwa Lachisanu, masiku asanu kuchokera pamene amishonale ndi mabwanawo anafika kumeneko. Chotsatirapo chake chinali chakuti makhadi 468 odziŵikitsa munthu ndiponso zikalata 374 zonena za kubadwa kwa munthu zinaperekedwa. Chiŵerengero cha mitchato imene inaperekedwa chinali 233! Kunali chimwemwe chokhachokha. Ngakhale kuti anali otopa, onse anati mpakedi. Mosakayikira, onse okhudzidwa ndi chochitikacho sadzachiiŵala konse. Unalidi ukwati wapadera kwambiri!