Kuyamikira Mwayi wa Utumiki Wopatulika
NTCHITO za utumiki wopatulika siziyenera kuonedwa mopepuka. Pamene ansembe a mu Yuda wakale anayamba kupeputsa ntchito zawo za m’kachisi wa Yehova, iye anawadzudzula zolimba. (Malaki 1:6-14) Ndipo pamene ena mu Israyeli analimbikitsa Anaziri kuti aziona mopepuka ntchito zawo zimene anazilandira mogwirizana ndi utumiki wawo wopatulika, Yehova anadzudzula Aisrayeli ochimwawo. (Amosi 2:11-16) Akristu oona amachitanso utumiki wopatulika, ndipo sauona mopepuka. (Aroma 12:1) Utumiki wopatulika umenewu uli ndi mbali zambiri, ndipo zonsezo nzofunika.
Pamene Yesu anali padziko lapansi ndi otsatira ake, iye anawaphunzitsa kuti akhale alaliki a Ufumu wa Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi, uthenga wawo unali kudzafika kumalekezero a dziko lapansi. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Kulalikira kumeneku kwakhala kofunika kwambiri makamaka m’masiku ano otsiriza a dongosolo lazinthu lilipoli.
Mboni zonse za Yehova zimachita ntchito imeneyi. Mboni zikwizikwi zimapeza chisangalalo mwa kuchita zimenezo monga apainiya. Kuti asamalire zofunika zazikulu m’ntchito yapadziko lonse imeneyi, anthu zikwizikwi adzipereka kuchita utumiki wapadera wa nthaŵi zonse wa pa Beteli, m’ntchito yoyendayenda monga oyang’anira madera ndi oyang’anira zigawo, kapena mu utumiki waumishonale. Kodi zimenezi zingaloŵetseponji kwa anthu amene akufuna kupitiriza utumiki wapadera umenewu?
Pamene m’Banja Mubuka Mavuto Aakulu
Munthu asanayambe kuchita utumiki wapadera wa nthaŵi zonse, iye ayenera kusintha zochita zake. Si aliyense amene angachite zimenezi. Maudindo a m’Malemba amene munthu ali nawo kale angapangitse kuti iye asathe kutero. Komabe, kodi chimachitika nchiyani pamene m’banja mubuka mavuto, mwinamwake okhudza makolo okalamba, amene akufunikira kusamaliridwa mwamsanga ndi anthu amene ali kale mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse? Mapulinsipulo ndi uphungu wa m’Baibulo wotsatirawu zikupereka chitsogozo choyenerera.
Moyo wathu wonse uyenera kuzikidwa paunansi wathu ndi Yehova. (Mlaliki 12:13; Marko 12:28-30) Zinthu zopatulika zomwe tinaikiziridwa kuti tizisamalire tiyenera kuziona monga zamtengo wapatali. (Luka 1:74, 75; Ahebri 12:16) Nthaŵi inayake, munthu wina amene anafuna kusintha zochita zake anauzidwa ndi Yesu kuti anayenera kutanganitsidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira Ufumu wa Mulungu. Mwachionekere, munthuyo anafuna kudzachita ntchitoyo atate wake atamwalira. (Luka 9:59, 60) Komano, Yesu anatsutsa malingaliro oipa a munthu aliyense amene ananena kuti anapereka chilichonse kwa Mulungu komano amene ‘sanachitire kanthu atate wake kapena amayi wake.’ (Marko 7:9-13) Mtumwi Paulo anafotokozanso za udindo wofunika kwambiri wa kuthandiza ‘mbumba yako ya iwe wekha,’ kuphatikizapo makolo ndi agogo.—1 Timoteo 5:3-8.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti pamene pabuka mavuto ofunika kusamaliridwa mwamsanga ndiye kuti awo amene ali mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse ayenera kusiya utumiki wawo pofuna kukapereka thandizo? Yankho lake lili ndi mbali zambiri. Aliyense ayenera kudzisankhira payekha. (Agalatiya 6:5) Ambiri alingalira kuti ngakhale kuti ntchito yawoyo anali kuikonda kwambiri, kungakhale bwino kukakhala ndi makolo kuti azikawathandiza. Chifukwa ninji? Mwina chosoŵacho chinali chachikulu kwambiri, mwina pangakhale kuti panalibenso wina wa m’banjamo amene akanathandiza, mwinanso mpingo wakomweko unalephera kupereka thandizolo. Ena amachita upainiya kwinaku akumapereka thandizolo. Ena achitanso utumiki wapadera wa nthaŵi zonse atasamalira kaye zosoŵa za m’banja lawo. Komabe, nthaŵi zambiri, ena amapereka thandizolo m’njira zina.
Kukwaniritsa Udindo Wawo
Ngati pabuka mavuto aakulu, ena omwe ali mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse asamalira zosoŵazo kwinaku akupitirizabe utumiki wawo. Talingalirani zingapo mwa zitsanzo zambirimbiri.
Mwamuna wina ndi mkazi wake amene akutumikira palikulu ladziko lonse la Mboni za Yehova anayamba utumiki wa pa Beteli mu 1978, atatumikira kale m’ntchito ya m’dera ndi ya m’chigawo. Ntchito ya mbaleyo imaphatikizapo udindo wolemera m’makonzedwe ateokrase. Koma makolo ake anafunikiranso kuthandizidwa. Banja limeneli la pa Beteli lapita katatu kapena kanayi pachaka kukasamalira makolo omwe amakhala pamtunda wa makilomita pafupifupi 3,500 kupita ndi kubwera. Iwo anamanga nyumba kuti muzikhala makolowo. Akhala akumapitakonso kukapereka thandizo la mankhwala. Iwo kwenikweni agwiritsira ntchito nthaŵi yawo yonse yatchuti kwa zaka 20 kukasamalira udindo umenewu. Amakonda ndi kulemekeza makolowo, koma iwo amakondanso mwayi wawo wa utumiki wopatulika.
Mbale wina anali atagwira ntchito yoyendayenda kwa zaka 36 pamene anayang’anizana ndi chimene anachitcha nthaŵi yovuta koposa pamoyo wake. Mpongozi wake wazaka 85 zakubadwa, mtumiki wokhulupirika wa Yehova, anafunikira kumakhala ndi munthu wina kuti azimsamalira. Panthaŵiyo, ambiri a ana a mpongoziyo anaona kuti sakanatha kumakhala naye. Mmodzi mwa achibale ake anauza woyang’anira woyendayendayo kuti iye ndi mkazi wake anayenera kusiya utumikiwo ndi kuyamba kusamalira amayiwo m’malo mwa banja lonse. Koma mwamuna ndi mkaziyo sanasiye utumiki wawo wamtengo wapatali, ndiponso sananyalanyaze zosoŵa za amayiwo. Kwa zaka zisanu ndi zinayi zotsatira, iwo anali kukhala ndi amayiwo nthaŵi zambiri. Poyambirira iwo anali kukhala m’nyumba yoyenda nayo, ndipo kenaka anali kukhala m’nyumba zosiyanasiyana zimene madera anali kuwapatsa. Pamene anafunikira kukakhala kwina kwa nthaŵi yaitali, mbaleyo, amene panthaŵiyo anali woyang’anira chigawo, anali kupitirizabe kuyendayenda pofuna kukasamalira ntchito zake pamene mkazi wake anali kukhala ndi amayi wakewo kuti aziwasamalira mokwanira. Mlungu uliwonse pambuyo pa misonkhano ya Lamlungu, mwamunayo anali kuyenda maulendo aatali kukawathandiza. Ambiri amene anazindikira za chochitikachi anayamikira kwambiri chifukwa cha zimene mwamuna ndi mkazi wakeyu anali kuchita. M’kupita kwa nthaŵi, ena a m’banjamo anasonkhezeredwanso kuti athandizeponso. Anthu a Yehova zikwi zambiri amapitirizabe kupindula ndi zimene banja lodzimanali limachita pogwiritsitsabe mwayi wawo wa utumiki wapadera wa nthaŵi zonse.
Mwa Kuthandizana ndi a m’Banjamo
Pamene ambiri a m’banjamo azindikira kufunika kwa utumiki wapadera wa nthaŵi zonse, ena mwa iwo angathandizepo.
Mzimu umenewu wa kuthandizapo kwa a m’banjamo wathandiza kwambiri banja lina la ku Canada omwe amatumikira monga amishonale ku West Africa. Iwo sanangokhala manja lende, polingalira kuti sipadzachitika chilichonse. Asanapite ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, pokonzekera kukatumikira kudziko lina, mwamunayo anakambitsirana ndi mng’ono wake kuti azisamalira amayi wawo atadwala kapena atalephera kuchita zinthu zina. Chifukwa chakuti amakonda amayi wawo ndiponso chifukwa chakuti amazindikira kufunika kwa ntchito yaumishonale, mng’ono wakeyo anati: “Panopo ndili ndi banja ndiponso ana. Sindingapite kutali kukachita zinthu zimene inuyo mumachita. Choncho, ndidzathandiza Amayi pavuto lililonse.”
Mwamuna wina ndi mkazi wake omwe akutumikira ku South America anathandizidwa kwambiri pantchito yosamalira amayi ake a mkaziyo. Mkulu wake wa mkaziyo ndi mwamuna wake anasamalira amayiwo mpaka pamene mkulu wakeyo anadwala ndipo anamwalira. Nanga kenaka chinachitika nchiyani? Pofuna kuthetsa nkhaŵa zawo, mlamu wake analemba kuti: “Malinga ngati ineyo ndi ana anga tikhalabe ndi moyo, simudzasiya utumiki wanu waumishonale.” Thandizo lowonjezereka la a m’banjamo linafika pamene mng’ono wake wina ndi mwamuna wake anasiya nyumba yawo nakakhala ndi amayiwo kuti aziwasamalira, ndipo anatero mpaka pamene amayiwo anamwalira. Umenewo ndi mzimu wabwino chotani nanga wa kuthandizana! Onsewo anali kuthandizira kuchirikiza utumiki waumishonale.
Makolo Amene Amapatsa Yehova Modzifunira
Nthaŵi zambiri, makolo amasonyeza kuyamikira kwakukulu kwa utumiki wopatulika. Ana ali m’gulu la chuma chofunika koposa chimene makolowo angalemekezere Yehova. (Miyambo 3:9) Makolo ambiri achikristu amalimbikitsa ana awo kuti ayambe utumiki wa nthaŵi zonse. Ndipo ena a iwo amadzimva monga momwe anachitira Hana, yemwe anapereka mwana wake Samueli kwa Yehova kuti amtumikire “chikhalire,” ndiko kuti, “masiku onse a moyo wake.”—1 Samueli 1:22, 28.
Kholo lina lotero linalembera kalata mwana wake wamkazi ku Afirika kuti: “Timayamika Yehova chifukwa cha mwayi waukulu umene uli nawo. Sitinkadziŵa kuti iwe ungafike pamenepa.” Ndipo nthaŵi ina anati: “Nzoona kuti tiyenera kupirira chifukwa cholekana, koma timasangalala kwambiri kuona mmene Yehova amakusamalirira!”
Pokumbukira za mmene makolo ake okalamba anasamaliridwira nthaŵi zosiyanasiyana, mmishonale wina ku Ecuador analemba kuti: “Ndiganiza kuti thandizo lalikulu kwambiri limene ine ndi mkazi wanga tinalandira ndilo mapemphero a atate wanga. Iwo atamwalira, amayi anga anatiuza kuti: ‘Atate anu ankakupemphererani kwa Yehova tsiku lililonse kuti iye akuloleni kukhalabe mu utumiki wanu nonse aŵirinu.’”
Mwamuna ndi mkazi wake okalamba ku California, U.S.A., anasangalala pamene mmodzi mwa ana awo aamuna analoŵa mu utumiki wa nthaŵi zonse. Mwana ameneyo ndi mkazi wake anali ku Spain pamene amayi wake anamwalira. Ena a m’banjamo anaona kuti panafunikira makonzedwe oti azithandiza atatewo. Chifukwa chakuti anthuwo anali otanganika ndi ntchito zawo zakuthupi ndiponso kulera ana awo, iwo anaona kuti sangathe kugwira ntchitoyo. M’malo mwake, iwo anakakamiza mwamuna ndi mkazi uja amene anali mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse kuti abwerere kumudzi kukasamalira atatewo. Komabe, atatewo, ngakhale kuti anali ndi zaka 79 zakubadwa, anali ndi thanzi labwino ndithu, ndipo analinso ndi kaonedwe kabwino kauzimu. Pamsonkhano wa banjalo, ena onse atalankhulapo, atatewo anaimirira nanena motsimikiza kuti: “Ndikufuna kuti iwo abwerere ku Spain kukapitiriza ntchito yawo.” Iwo anaterodi, koma anathandizanso atatewo m’njira zina. Iwo tsopano akugwira ntchito yoyang’anira dera ku Spain. Kuchokera panthaŵi yomwe anasonkhanayo, ena a m’banjamo akuyamikira zimene akuchita mwamuna ndi mkazi otumikira kudziko linawo. Patapita zaka zingapo, mmodzi mwa ana ena anatenga atatewo kukakhala nawo kunyumba kwake ndipo anawasamalira mpaka pamene iwo anamwalira.
Ku Pennsylvania, U.S.A., mbale wina wodzozedwa amene anachita upainiya kwa zaka pafupifupi 40 anali ndi zaka zakubadwa zoposa 90 pamene mkazi wake anadwala matenda akayakaya namwalira. Iye anali ndi mwana wamwamuna mmodzi ndi ana aakazi atatu, kuwonjezera pa ana ambirimbiri auzimu. Mmodzi mwa ana ake aakazi anali mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zoposa 40, ndipo anali atatumikirapo pamodzi ndi mwamuna wake monga mmishonale, m’ntchito yoyendayenda, ndiponso pa Beteli. Iye anathandizira kupanga makonzedwe oti akapereke thandizo lokwanira kwa atate wake. Abale akomweko anathandizaponso mwa kumapita naye kumisonkhano yampingo ku Nyumba ya Ufumu. Pambuyo pake, mwamuna wake atamwalira, iye anafunsa atate wake ngati anafuna kuti iye achoke pa Beteli kuti akawasamalire. Atatewo amayamikira kwambiri zinthu zopatulika, ndipo analingalira kuti zosoŵa zawo zidzasamaliridwa m’njira zina. Choncho, anayankha kuti: “Kuchita zimenezo kungakhale kulakwa kwakukulu, ndipo kungakhale kulakwa kwakukulu zedi ngati nditakulolani kuti mutero.”
Mipingo Yothandiza
Mipingo ina yathandiza kwambiri kusamalira makolo okalamba a anthu amene ali mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse. Iyo imayamikira kwambiri awo amene achita utumiki umenewu kwa zaka zambiri. Ngakhale kuti singawamasule ku maudindo awo a m’Malemba, mipingo imeneyi imachita zambiri popeputsako ntchitoyo kotero kuti anawo asasiye utumiki wawo wapadera.
Mwamuna wina ndi mkazi wake ku Germany anagwira ntchito yawo ya kudziko lina kwa zaka pafupifupi 17, ndipo anagwira kwambiri ntchito yoyendayenda. Kenaka amayi wake wokalamba anafunikira thandizo lapafupipafupi. Chaka chilichonse iwo anali kukawathandiza patchuti. Anansi amene ndi Mboni anathandizaponso mwachikondi. Kenaka pamene okwatirana a mu utumiki wa nthaŵi zonse aja anali ndi amayiwo panthaŵi imene vutolo linakula zedi, akulu a mumpingo wakomweko anapanga makonzedwe oti akumane nawo. Iwo anadziŵa bwino lomwe zimene mwamuna ndi mkaziyo anali kuchitira amayiwo. Iwo anazindikiranso za kufunika kwa utumiki wapadera umene okwatirana ameneŵa anali kuchita. Choncho, akuluwo anafotokoza za programu imene anailinganiza kuti azithandiza amayiwo ndipo anati: “Simungathe kuwathandiza kuposa mmene mukuchitiramu; ife tikuthandizani pofuna kuti inuyo mupitirizebe ntchito yanu ku Spain.” Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri zapitazo, akulu ameneŵa akhala akuchita zimenezi.
Mofananamo, mbale wina amene wakhala akutumikira ku Senegal chiyambire mu 1967 analandira thandizo lachikondi kuchokera kumpingo wakwawo kwa atate wake. Pamene panabuka vuto lina, mwamunayo, mothandizidwa mwachikondi ndi mkazi wake, anayenda okha kupita ku United States kukathandiza makolo ake. Anaona kuti kunali kofunika kukhala kumeneko kwa miyezi ingapo. Vutolo linali lalikulu, koma pamene anayesetsa kuchita zimene angathe, mpingo unathandizaponso pofuna kuti iye apitirize utumiki wake waumishonale. Kwa zaka zoposa 18, mpingowo unapereka thandizo m’njira zosiyanasiyana, choyamba kwa atate wake (ngakhale kuti atatewo sanazindikirenso ambiri a iwo) ndipo kenaka kwa amayi wake. Kodi zimenezi zinamasula mwana wamwamunayo ku udindo wake? Ayi; iye ankachoka ku Senegal panthaŵi yatchuti kukapereka thandizo. Koma ambiri mumpingomo anasangalala kwambiri pamene anadziŵa kuti anali kuthandizira okwatirana akhama ameneŵa kuti apitirizebe utumiki wawo wapadera ku Senegal.
Yesu ananena kuti amene adzasiya zonse chifukwa cha uthenga wabwino adzakhala ndi abale, alongo, amayi, ndi ana makumi khumi. (Marko 10:29, 30) Zimenezi nzoonadi pakati pa atumiki a Yehova. Zimenezi zinachitikadi mwapadera kwa mwamuna wina ndi mkazi wake amene akutumikira ku Benin, West Africa, pamene Mboni ziŵiri za mumpingo wa makolo awo zinawauza kuti asadere nkhaŵa za makolowo. Izo zinawonjezera kuti: “Makolo anu ndi makolo athunso.”
Inde, pali njira zambiri zimene tingasonyezere kuti timayamikira mwayi wa utumiki wopatulika. Kodi pali njira zina zimene mungachitire zimenezi mokwanira?
[Zithunzi patsamba 26]
Adzipereka kaamba ka utumiki wapadera wa nthaŵi zonse