Kodi Ndipemphe Ngongole kwa Mbale?
MWANA wamng’ono kwambiri wa Simon akudwala ndipo akufunikira mankhwala mofulumira. Koma Simon ndi wosauka kwambiri ndipo sangakwanitse. Kodi atani? Koma Mkristu mnzake wotchedwa Michael ngwandalamako kusiyana ndi iye. Mwinamwake Michael adzamkongoza ndalama. Koma Simon akudziŵa mumtima mwake kuti sangathe kubweza.a
Pamene Simon apita kwa iye, Michael akuthedwa nzeru. Akuzindikira kuti Simon akufunadi thandizo koma akuganiza kuti Simon sadzatha kubweza ndalamazo chifukwa amavutika ngakhale kupezera banja lake chakudya. Kodi Michael achitenji?
M’maiko ochuluka, anthu angachotsedwe ntchito mwadzidzidzi ndi kukhala opanda ndalama ngakhale inshuwalansi yolipirira mankhwala. Zokakongola ku banki kungakhale kulibe kapena zingakhale ndi chiwongola dzanja chochuluka. Pamene vuto libuka, njira imene ingakhalepo ndiyo kukakongola ndalama kwa mnzanu. Koma musanakapemphe ngongoleyo, pali mfundo zina zaphindu zoti mulingalire.
Ŵerengerani Mtengo
Malemba amapereka malangizo kwa onse, wokongoza ndi wokongola. Mwa kutsatira uphungu umenewu, tingapewe kusamvana ndi kukhumudwitsana.
Mwachitsanzo, Baibulo limatikumbutsa kuti tisaone mopepuka nkhani yobwereka ndalama. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu a ku Roma kuti: “Musakhale ndi mangaŵa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.” (Aroma 13:8) Choncho, ngongole yokha imene Mkristu ayenera kukhala nayo kwa ena ndi chikondi. Nchifukwa chake, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ngongole imeneyi ikufunikiradi?’
Ngati yankho ndilo inde, ndiye nkwanzeru kulingalira zotsatirapo za kuloŵa mu ngongole. Yesu Kristu anasonyeza kuti kusankha kwa nzeru kumafuna kulingalira ndi kukonzekera mosamalitsa. Anafunsa ophunzira ake kuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?” (Luka 14:28) Pulinsipulo limeneli limagwira ntchito pamene tilingalira ngakhale zokapempha ngongole kwa mbale. Kuŵerengera mtengo wa ngongole kumatanthauza kuŵerengera mmene tidzabwezere ndiponso pamene tidzabweze.
Wokongoza ali ndi ufulu wodziŵa mmene tidzabwezere ngongoleyo ndiponso pamene tidzabweze. Mwa kupenda zinthu mosamala, tidzatha kupereka mayankho enieni. Kodi mwaŵerengera mtengo wodzabweza ngongoleyo panthaŵi yake? Zoonadi, nkwapafupi kumuuza mbale kuti: “Ndidzakubwezera posachedwapa. Ndikhulupirire.” Koma kodi nkhani zimenezi sitiyenera kuzitenga mosamala? Tiyenera kutsimikiza poyambirira kudzabweza ngongoleyo, popeza zimenezo ndi zimene Yehova amafuna kwa ife. “Woipa akongola, wosabweza,” limatero Salmo 37:21.
Mwa kuŵerengera mmene tidzabwezere ndiponso pamene tidzabweze ngongoleyo, timazikumbutsa kuopsa kwa mapangano amene tikupanga. Zimenezi zimachepetsa kudziloŵetsa mu ngongole kosafunikira. Ngati tipeŵa ngongole, tidzapindula. Miyambo 22:7 imachenjeza kuti: “Wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.” Ngakhale pamene wokongola ndi womkongoza onse ali abale auzimu, ngongole ingasokoneze ubwenzi wawo, kumlingo winawake. Kusamvana pankhani za ngongole kwasokoneza mtendere wa mipingo ina.
Fotokozani Chifukwa Chake Ndalama Zikufunika
Wokongoza ali ndi ufulu wodziŵa bwino mmene ndalama zokongolazo zikagwirire ntchito. Kuwonjezera pa ngongole imeneyi, kodi tikukongolanso ndalama kwa ena? Ngati ndi choncho, tiyenera kumveketsa bwino zimenezi, chifukwa zingalepheretse kubweza ngongoleyo.
Nkofunika kwambiri kusiyanitsa ngongole yochitira bizinesi ndi yolipirira zochitika za mwadzidzidzi. Malemba sakakamiza mbale kukongoza ndalama zochitira bizinesi, koma angafune kuthandiza ngati mbale wina, popanda kuchitira dala, asoŵa ndalama zopezera chakudya, zovala kapena zolipirira zofunika za chipatala. Kunena mosabisa ndiponso zoona pankhani zimenezi kudzathandiza kupewa kusamvana.—Aefeso 4:25.
Lembani Mapanganowo
Pangano lolembedwa, ndilo sitepe lofunika kwambiri ngati tikufuna kupeŵa kusamvana m’tsogolo. Nkwapafupi kuiŵala mfundo zenizeni zimene mwapangana pokhapokha ngati zalembedwa. Tiyenera kulemba kuchuluka kwa ndalama takongolazo ndiponso pamene tidzabweze. Kukakhala kwanzeru kwa onse, wokongola ndi womkongoza, kusaina pangano lolembedwalo ndipo aliyense kusunga kope lake. Baibulo limasonyeza kuti mapangano a zandalama ayenera kulembedwa. Patatsala nthaŵi yochepa kuti Ababulo awononge Yerusalemu, Yehova anauza Yeremiya kugula munda kwa mmodzi mwa abale ake. Tingapindule mwa kupenda njira zake.
“Ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga,” anatero Yeremiya. “Ndimyesera ndalama, masekele khumi ndi asanu ndi aŵiri a siliva. Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m’miyeso. Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wobvundukuka; ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamaso pa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m’bwalo la kaidi.” (Yeremiya 32:9-12) Ngakhale kuti chitsanzochi chikukhudza malonda osati ngongole, chikusonyeza kufunika kwa kusamalira bwino ndiponso motsimikiza nkhani zokhudza ndalama.—Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 1, 1973, masamba 287-8.
Ngati mikangano ibuka, Akristu ayenera kuyesa kuithetsa mogwirizana ndi uphungu wa Yesu wolembedwa pa Mateyu 18:15-17. Koma mkulu wina amene wayesa kuthandiza m’nkhani zoterezi anati: “Pafupifupi pankhani iliyonse, panalibe pangano lolembedwa. Zotsatirapo zake, onse aŵiriwo sanagwirizane kuti ngongoleyo inayenera kubwezedwa motani. Ndatsimikiza kuti kulemba nkhani zimenezi ndi chizindikiro cha chikondi, osati kusakhulupirirana.”
Pamene talemberana pangano, tiyenera kuyesetsa kulisunga. Yesu analangiza kuti: ‘Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi; ndipo chowonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.’ (Mateyu 5:37) Ngati mavuto osayembekezeka atilepheretsa kubweza ngongole panthaŵi imene tinapangana, mwamsanga tiyenera kukafotokoza kwa wotikongozayo mmene zinthu zilili. Mwina adzatilola kuti tidzipereka ngongoleyo pang’onopang’ono kwa nthaŵi yaitali.
Komabe, mikhalidwe yovuta sitichotsera mangaŵa athu. Munthu woopa Yehova sasintha mawu ake. (Salmo 15:4) Ngakhale ngati zinthu sizikhala mmene timafunira, tiyenera kukhala okonzeka kudzimana kuti tithetse ngongoleyo, popeza monga Akristu tiyenera kuchita zimenezo.
Muzisamala Pokongoza Ndalama
Zoonadi, wokongola yekha sindiye afunikira kupenda zinthu mosamalitsa. Mbale amene akupemphedwa ngongoleyo ayeneranso kuŵerengera mtengo. Tisanakongoze ndalama, tingachite bwino kukhala ndi nthaŵi yolingalira nkhaniyo mosamalitsa ndi mosatengeka maganizo. Baibulo limatilimbikitsa kusamala kuti: “Usakhale wodulirana mpherere, ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake.”—Miyambo 22:26.
Musanavomereze, lingalirani chimene chingachitike ngati mbaleyo alephera kubweza. Kodi mudzakhala ndi mavuto a zandalama aakulu? Ngakhaletu ngati mbaleyo ali ndi zolinga zabwino, mikhalidwe ingasinthe kapena zoŵerengera zake zingasokonekere. Yakobo 4:14 amatikumbutsa tonsefe kuti: “Inu amene simudziŵa chimene chidzagwa maŵa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka.”—Yerekezerani ndi Mlaliki 9:11.
Makamaka pa ngongole yochitira bizinesi, kukakhala kwanzeru kulingalira mbiri ya wokongolayo. Kodi amadziŵika kukhala wokhulupirika ndi wodalirika, kapena kodi amalephera kusunga bwino ndalama? Kodi ali ndi chizoloŵezi chomapempha anthu ndalama mumpingo? Ndi kwanzeru kukumbukira mawu awa: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.
Nthaŵi zina, ngongole simapindulitsa ngakhale wokongola. Ingangokhala chimtolo kwa iye, ndi kumlanda chimwemwe chake. Kodi tikufuna mbaleyo kuti akhale “kapolo” wathu? Kodi ngongole idzasokoneza ubale wathu, ikumadzetsa kumangika ngakhalenso manyazi ngati alephera kubweza?
Ngati pali kufunikira kwenikweni, kodi tingalingalire zongopereka mphatso m’malo mwa kukongoza, ngakhale ngati ndalamazo zili zochepa? Malemba amatilimbikitsa kukhala achifundo pamene tiona mbale wathu ali wosoŵa. “Wolungama achitira chifundo, napereka,” anaimba motero wamasalmo (Salmo 37:21) Chikondi chiyenera kutisonkhezera kuchita zimene tingathe popereka thandizo kwa abale athu osoŵa.—Yakobo 2:15, 16.
Lingalirani Zosankha Zanu Mosamalitsa
Popeza ngongole ingadzetse kusamvana, sitiyenera kuiona ngati njira yachidule yothetsera mavuto koma monga chinthu chimene tingapemphe kokha ngati palibe mwina mochitira. Monga mmene taonera poyamba, wokongola ayenera kufotokoza zinthu mosabisa kwa womkongoza, ndi kulemba mmene adzabwezere ngongoleyo ndiponso pamene adzabweze. Ndipo panthaŵi ya mavuto, kupereka mphatso kungakhale njira yabwino kwambiri.
Michael sanakongoze Simon ndalama zimene anapempha. Mmalo mwake, Michael anampatsa ndalama pang’ono monga mphatso. Simon anayamikira kwambiri thandizolo ndipo analipirira mankhwala a mwana wake. Ndipo Michael anasangalala kuti anakhoza kuonetsa chikondi chake pa abale mwa njira imeneyi. (Miyambo 14:21; Machitidwe 20:35) Onse Michael ndi Simon akuyembekezera nthaŵi ya ulamuliro wa Ufumu pamene Kristu ‘adzapulumutsa waumphaŵi wofuulira thandizo’ ndipo palibe adzati, “Ine ndidwala.” (Salmo 72:12; Yesaya 33:24) Mpaka panthaŵiyo, tiyeni tilingalire zosankha zathu mosamalitsa ngati tikufunitsitsadi kupempha ngongole kwa mbale.
[Mawu a M’munsi]
a Maina asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 25]
Kulemba mapangano a nkhani za ngongole ndi chizindikiro cha chikondi, osati kusakhulupirirana