Alephera Kuba ku West Africa
Yosimbidwa ndi Eunice Ebuh
“Tsiku limene timachita Phunziro la Buku la Mpingo mbala zamfuti zinakonzekera kuloŵa m’nyumba yathu. Timasiya geti lathu lotsegula kuti abale ndi alongo ndiponso anthu okondwerera aziloŵa. Mwachionekere mbalazo zinkadziŵa chizoloŵezi chathu ndiponso nthaŵi imene timasonkhana. Tikudziŵa kuti anali ataba kwina galimoto ndipo anabwera pafupi ndi geti lathu kudzadikira pa tsiku ndi nthaŵi ya phunziro la buku.
“Mwamwayi, mlungu umene anabwera unali mlungu umene tinali ndi woyang’anira dera. M’malo mosonkhana kunyumba kwathu, tinakasonkhana ku Nyumba ya Ufumu. Msonkhano utatha, kunali msonkhano wa akulu. Mwachizoloŵezi ana anga ndi ine tikanakhala titabwerera kunyumba koma mwamuna wanga, amene ndi mkulu, anati timudikire sachedwa. Choncho tinadikira.
“Kenako tinaona kuti galimoto likukana kulira. Woyang’anira dera ndi mwamuna wanga analephera kulikonza. Wokonza magalimoto yemwe tinamuitana analepheranso.
“Ana anga anayenda pansi kupita kunyumba. Patapita nthaŵi, ndinapitanso kunyumba. Ndinafika kunyumba cha m’mateni koloko ausiku. Ine ngakhale ana anga sitinaloŵe mu mpandamo pagalimoto, zimene zikanafuna kutsegula geti lalikululo.
“Pamene ndinaloŵa m’chipinda mwanga, ndinamva kulira kwa mfuti. Inalira kwambiri. Sindinadziŵe chomwe chinali kuchitika. Ndinayesa kuimba telefoni ku polisi, koma telefoni sinali kugwira ntchito. Mofulumira ndinatsika kuchoka ku chipinda chapamwamba kukakiya chitseko chachitsulo, mofulumiranso ndinakakiya chitseko chapakati. Ndinazimitsa magetsi. Ana anga anachita mantha, choncho ndinawauza kukhala odekha. Tonse pamodzi tinapempha chitetezo cha Yehova. Panthaŵi imeneyi, mwamuna wanga anali adakali ku Nyumba ya Ufumu kuyesa kukonza galimoto lija.
“Ndinasuzumira panja pazenera ndipo ndinaona mwamuna wina aligone pa msewu kunja kwa geti. Kunali kuoneka kuti mbalazo zinali zitapita, choncho ndinaika mwamuna wovulalayo m’galimoto langa ndi kuthamangira naye kuchipatala. Zinali zoopsa, komabe ndinayenera kuchitapo kanthu. Mwatsoka anamwalira tsiku lotsatira.
“Mosasamala kanthu za ngozi imeneyi, zinthu zikanaipa kwambiri. Kubwera kwa woyang’anira dera kunachititsa kuti phunziro la buku lisachitikire m’nyumba yathu. Kufa kwa galimoto kunapangitsa kuti tonse monga banja tisayende pa galimoto pobwerera ku nyumba. Mwamuna wanga, amene akanagwidwa ndi mbalazo, sanafike panyumba mpaka usiku kwambiri. Zimenezi ndi zinthu zina zinatipulumutsa usiku umenewo.
“Yehova ndiye linga ndi pobisala pathu. Nzofanana ndi mmene lemba limanenera kuti: ‘Akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe.’”—Salmo 127:1.