Pamene Mbala Zamfuti Zikuloŵerani
KU Ikoyi, dera la anthu apamwamba ku West Africa, nyumba zazikulu zakhala ngati midzi ya malinga. Zambiri zili ndi makoma aatali mamita atatu, okhala ndi zinsonga zachitsulo, magalasi osongoka, kapena mawaya aminga pamwamba pake. Alonda amakhala pa mageti aakulu omanga ndi mabouti, zitsulo zopingasapingasa, tcheni ndi maloko. Mazenera ali ndi zitsulo zopingasapingasa. Makomo oloŵera ku zipinda zogona kuchokera ku zipinda zina m’nyumbazo ali ndi zitseko zachitsulo. Nthaŵi ya usiku, agalu akuluakulu amtundu wa—Alsatians ndi Rottweilers—amawamasula ku zingwe zawo. Magetsi owala kwambiri amachotsa mdima, ndipo makina a kompyuta oteteza nyumba amalira pang’onopang’ono pamene zinthu zonse zili bwino.
Palibe amatsutsa kufunika kwa kuteteza nyumba. Mitu ya nkhani m’nyuzipepala inati: “Mbala Zamfuti Zisesa Katundu m’Mudzi”; “Mbala Zachinyamata Zalusa”; ndiponso “Mantha, Pamene Zigawenga Zilanda [Mzinda].” Ndimo mmene zinthu ziliri m’maiko ambiri. Monga mmene Baibulo linanenera, tikukhaladi m’nthaŵi zoŵaŵitsa.—2 Timoteo 3:1.
Chiŵerengero cha apandu, komanso cha mbala zamfuti, chikuchuluka kwambiri padziko lonse. Maboma akulephereralephererabe kapena samafuna kuteteza nzika zawo. M’maiko ena apolisi ndi ochepa ndiponso ali ndi mfuti zochepa poyerekezera ndi zimene mbala zili nazo, choncho satha kuthandiza anthu ofunikira thandizo chifukwa chosoŵa zida. Anthu ambiri amene amaona pamene wina akuukiridwa amaopa kuthandiza.
Oukiridwawo, pokhala sadaliranso thandizo la apolisi kapena la anthu, amayesa kudziteteza okha. Mkulu wina wachikristu wa m’dziko lomatukuka anati: “Ukaimba belu, mbala zidzakuvulaza kapena kukupha. Osadalira thandizo la ena. Ngati angathandize, chabwino, koma musayembekezere kapena kufuulira thandizo chifukwa kungakhale kuitana mavuto ochuluka.”
Chitetezo ndi Mawu a Mulungu
Pamene kuli kwakuti Akristu sali a dziko lapansi, iwo ali m’dziko lapansi. (Yohane 17:11, 16) Chotero monga wina aliyense, iwo amapanga makonzedwe oyenera a chitetezo. Komabe, mosiyana ndi amene satumikira Yehova, anthu a Mulungu amapeza chitetezo pogwiritsa ntchito mapulinsipulo achikristu.
Mosiyana ndi zimenezi, anthu m’maiko ena a mu Afirika amagwiritsa ntchito matsenga pofuna kudziteteza kwa akuba. Sing’anga angateme mphini padzanja, pachifuwa kapena kumsana kwa munthu wofuna thandizoyo. Ndiyeno amatikitirapo mankhwala kwinaku akumalankhula yekha. Akatere, munthuyo amakhala wotetezeka woti mbala sizingamvutitse. Ena amaika njirisi kapena mankhwala nyumba zawo, akukhulupirira kuti kutsirikako kudzapangitsa mbala kusawavutitsa.
Akristu oona sachita matsenga amtundu uliwonse. Baibulo limaletsa kukhulupirira mizimu kwa mtundu uliwonse, ndipo liyenera kutero, chifukwa machitachita amenewa amayanjanitsa anthu ndi ziŵanda, zimene zikusonkhezera chiwawa padziko lapansi. (Genesis 6:2, 4, 11) Baibulo momveka bwino limati: “Musamachita . . . kuombeza ula.”—Levitiko 19:26.
Anthu ena pothedwa nzeru amapeza chitetezo mwa kukhala ndi mfuti. Komabe, Akristu amatsatira mawu a Yesu onena kuti: “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Anthu a Mulungu ‘asula malupanga awo kukhala zolimira’ ndipo sagula mfuti zodzitchinjirizira kwa akuba kapena pamene avutitsidwa.—Mika 4:3.
Bwanji nanga za kukhala ndi alonda amfuti? Ngakhale kuti zimenezi ndi chosankha chamwini, dziŵani kuti mwa kuchita zimenezo mumapatsa mfuti munthu wina. Kodi mwinintchito adzayembekezera alondawo kuchitanji ngati kwabwera mbala? Kodi adzayembekezera alondawo kuombera mbalayo kuti ngati nkotheka ateteze zinthu zimene akulondera?
Kukana kwa Akristu matsenga ndi zida zodzitetezera kungaoneke kopusa kwa amene sadziŵa Mulungu. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” (Miyambo 29:25) Pamene kuli kwakuti Yehova amateteza anthu ake onse, iye saloŵerera m’nkhani iliyonse kuti atchinjirize atumiki ake kwa akuba. Yobu anali wokhulupirika kwambiri, komabe Mulungu analola olanda kufunkha ziweto za Yobu, ndi kusakaza miyoyo ya anyamata ake. (Yobu 1:14, 15, 17) Mulungu analolanso mtumwi Paulo kupezeka “mowopsa mwake mwa olanda.” (2 Akorinto 11:26) Ngakhale zili choncho, Mulungu amaphunzitsa atumiki ake kugwiritsa ntchito mapulinsipulo amene amachepetsa kuvutitsidwa ndi mbala. Ndipo amaperekanso chidziŵitso chimene chimawathandiza kudziŵa zomwe angachite pamene mbala zifuna kuwabera kotero kuti zisawavulaze.
Kuchepetsa Kuvutitsidwa ndi Mbala
Kalekale munthu wanzeru anati: “Kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.” (Mlaliki 5:12) M’mawu ena tinganene kuti, amene ali ndi zinthu zambiri amaopa kuti mwina adzaberedwa zinthuzo chotero sagona tulo podera nkhawa za zimenezi.
Choncho njira imodzi yochepetsera nkhawa komanso kuvutitsidwa ndi mbala ndiyo kupewa kukhala ndi katundu wochuluka wamtengo wapatali. Mtumwi mouziridwa analemba kuti: “Zilizonse m’dziko—chikhumbo cha thupi ndi chikhumbo cha maso ndi kudzionetsera kwa moyo wa munthu—sizichokera kwa Atate, koma zichokera ku dziko.” (1 Yohane 2:16, NW) Chikhumbo chimene chimasonkhezera anthu kugula zinthu zamtengo wapatali ndicho chimasonkhezeranso ena kuba. Ndipo ‘kuonetsera moyo wa munthu’ kungakhale kuitana mbala.
Kuphatikiza pa kusadzionetsera, china chimene chingatiteteze kwa akuba ndi kudzidziŵikitsa kuti ndinu Mkristu woona. Ngati musonyeza chikondi kwa ena, kuona mtima pa zochita zanu, ndiponso changu muutumiki wachikristu, mungapange mbiri yabwino m’dera lanu chifukwa chokhala munthu wabwino, wofunika ulemu. (Agalatiya 5:19-23) Mbiri yachikristu imeneyi ingakhale chitetezo champhamvu koposa chida.
Pamene Mbala Zamfuti Zikuloŵerani
Kodi muyenera kuchitanji ngati mbala zaloŵa m’nyumba mwanu ndipo zakupezani? Kumbukirani kuti moyo wanu ndiwo wofunika kwambiri kuposa katundu. Kristu Yesu anati: “Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso. Ndipo kwa iye wofuna . . . kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.”—Mateyu 5:39, 40.
Umenewu ndi uphungu wanzeru. Ngakhale kuti si lamulo kwa Akristu kupatsa akuba katundu, akubawo amachita chiwawa kwambiri ngati aona kuti mukuletsa, simukuwamvera komanso mukunena bodza. Ambiri a iwo, “sazindikiranso kanthu konse,” chotero sachedwa kuyamba chiwawa.—Aefeso 4:19.
Samuel amakhala m’nyumba ina pamdadada. Akuba anazungulira mdadadawo nayamba kufunkha khomo ndi khomo. Samuel anamva kulira kwa mfuti, kumenyetsedwa kwa zitseko, komanso kufuula, kulira, ndi kuchema kwa anthu. Kuthaŵa kunali kosatheka. Samuel anauza mkazi wake ndi ana ake aamuna atatu kugwada pansi, kukweza manja awo m’mwamba, kutseka maso, ndi kudikira. Pamene okubawo analoŵa, Samuel analankhula nawo ataŵeramitsa nkhope yake pansi, podziŵa kuti akawayang’ana kumaso, iwo angaganize kuti adzawazindikira pambuyo pake. “Loŵani,” iye anatero. “Chilichonse chimene mukufuna, tengani. Muli aufulu kutenga chilichonse. Sitikuletsani, ndife Mboni za Yehova.” Mbalazo zinadabwa ndi zimenezi. Kwa ola lotsatirapo kapena kuposapo, amuna okwanira 12 amfuti anali kuloŵa m’magulumagulu. Ngakhale kuti anaba majuwelo, ndalama, ndi zipangizo za magetsi, banjalo silinamenyedwe kapena kutemedwa ndi zikwanje monga ena pa mdadadawo. Banja la Samuel linathokoza Yehova kamba kowasunga ndi moyo.
Zimenezi zikusonyeza kuti pamene akuba afika, ngati oberedwawo aloleza ndalama ndi zinthu zina, sangavulazidwe.a
Nthaŵi zina pamene Mkristu apereka umboni zimamtchinjiriza kuti asavulazidwe. Pamene mbala zinaloŵa m’nyumba ya Ade, anaziuza kuti: “Ndikudziŵa zinthu zili zokuvutani, ndicho chifukwa chake mukuchita zimenezi. Monga Mboni za Yehova, timakhulupirira kuti tsiku lina aliyense adzakhala ndi chakudya chochuluka cha iye ndi banja lake. Aliyense adzakhala mu mtendere ndiponso wosangalala mu Ufumu wa Mulungu.” Zimenezi zinachepetsa mkhalidwe wa chiwawa wa mbalazo. Mmodzi wa iwo anati: “Pepa kuti tabwera m’nyumba yako, koma uyenera kumvetsa kuti tili ndi njala.” Ngakhale anaba katundu wa Ade, iye ndi banja lake sanakhudzidwe nkomwe.
Khalani Wodekha
Si kwapafupi munthu kukhala wodekha mu mkhalidwe woopsa, makamaka ngati cholinga chachikulu cha mbalazo chili kuopseza anthuwo kuti awagonjere. Pemphero lidzatithandiza. Kulirira kwathu thandizo, ngakhale kwakachetechete ndi kwachidule, Yehova akhoza kumva. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake achereza kulira kwawo.” (Salmo 34:15) Yehova amamva ndipo angatipatse nzeru kuti tichite modekha pa mkhalidwe uliwonse.—Yakobo 1:5.
Kuphatikiza pa pemphero, thandizo lina pa kukhala wodekha ndilo kulingalira pasadakhale zimene mudzachita ndi zimene simudzachita pamene mbala zakuloŵerani. Nzoona, sikotheka kudziŵa pasadakhale mkhalidwe umene mudzapezekemo. Komabe, nkwanzeru kukhala ndi mapulinsipulo m’maganizo, monga mmene kulili kwa nzeru kukhala ndi njira zodzitetezera m’maganizo mutapezeka muli nyumba imene ikupsa ndi moto. Kulingalira pasadakhale kumathandiza kukhala wodekha, kusachita mantha ndi kupeŵa kuvulala.
Lingaliro la Mulungu pa kuba nlofotokozedwa bwino kuti: “Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa.” (Yesaya 61:8) Yehova anauzira mneneri wake Ezekieli kulemba kuba monga tchimo loopsa kwambiri.(Ezekieli 18:18) Komanso, buku lomwelo la Baibulo limasonyeza kuti Mulungu mwachifundo adzakhululukira munthu amene alapa ndi kubweza chimene analanda mwachifwamba.—Ezekieli 33:14-16.
Mosasamala kanthu kuti akukhala m’dziko lodzala ndi upandu, Akristu amasangalala ndi chiyembekezo cha moyo mu Ufumu wa Mulungu, pamene sikudzakhalanso kuba. Kunena za nthaŵiyo, Baibulo limalonjeza kuti: “[Anthu a Mulungu] adzakhala yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”—Mika 4:4.
[Mawu a M’munsi]
a Zoonadi, pali malire akulolera. Atumiki a Yehova salolera m’njira iliyonse imene imaswa malamulo a Mulungu. Mwachitsanzo, Mkristu sadzalola kumgwirira mwadala.