Chilamulo cha Pakamwa—Kodi N’chifukwa Chiyani Chinalembedwa?
KODI n’chifukwa chiyani Ayuda ambiri a m’zaka za zana loyamba sanalandire Yesu monga Mesiya? Mboni ina yoona ndi maso inati: “Mmene iye [Yesu] analoŵa m’Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?” (Mateyu 21:23) Kwa iwo, Wamphamvuyonse anapatsa mtundu wachiyuda Torah (Chilamulo), ndipo iyo inapatsa anthu ena ulamuliro wochokera kwa Mulungu. Kodi Yesu anali ndi ulamuliro umenewo?
Yesu anasonyeza ulemu waukulu pa Torah ndi kwa awo amene inawapatsadi ulamuliro. (Mateyu 5:17-20; Luka 5:14; 17:14) Koma nthaŵi zambiri anadzudzula anthu amene anadumpha malamulo a Mulungu. (Mateyu 15:3-9; 23:2-28) Anthu amenewa anali kutsatira miyambo imene inadzadziŵika kuti chilamulo cha pakamwa. Yesu anachikana. Chotero, ambiri anam’kana kuti si Mesiya. Iwo ankakhulupirira kuti munthu amene amachirikiza miyambo ya awo amene anali ndi ulamuliro pakati pawo ndi yekhayo amene angakhale ndi Mulungu.
Kodi chilamulo cha pakamwa chimenechi chinachokera kuti? Kodi Ayuda anayamba motani kuchiona kuti chili ndi ulamuliro wolingana ndi Chilamulo cholembedwa m’Malemba? Ndipo ngati chinali mwambo wofotokoza pakamwa, kodi n’chifukwa chiyani m’kupita kwa nthaŵi chinalembedwa?
Kodi Miyamboyo Inachokera Kuti?
Aisrayeli anakhala paunansi wa pangano ndi Yehova Mulungu mu 1513 B.C.E pa Phiri la Sinai. Kudzera mwa Mose, analandira malamulo a pangano limenelo. (Eksodo 24:3) Kutsatira malamulo amenewo kukanawapangitsa ‘kukhala oyera monga momwe Yehova Mulungu wawo analili woyera.’ (Levitiko 11:44) M’pangano la Chilamulo, kulambira Yehova kunaloŵetsapo nsembe zoperekedwa ndi ansembe oikidwa. Panali kudzakhala malo olambirirako—m’kupita kwa nthaŵi, malowo anakhala kachisi wa ku Yerusalemu.—Deuteronomo 12:5-7; 2 Mbiri 6:4-6.
Chilamulo cha Mose chinapereka maziko ofunika a kalambiridwe ka Israyeli monga mtundu polambira Yehova. Komabe, zinthu zina sizinafotokozedwe mwatsatanetsatane. Mwachitsanzo, Chilamulo chinaletsa kugwira ntchito pa Sabata, koma sichinafotokoze mwachindunji kusiyana kwa ntchito ndi zochita zina.—Eksodo 20:10.
Chikhala kuti Yehova anaona kuti kutero n’kofunika, akanapereka malamulo atsatanetsatane pachilichonse chimene munthu angafunsepo. Koma anthu anawalenga ndi chikumbumtima, ndipo anawapatsa nzeru kuti am’tumikire mwaufulu potsatira malamulo ake. Chilamulocho chinalola kuti milandu iweruzidwe ndi ansembe, Alevi, ndi oweruza. (Deuteronomo 17:8-11) Milanduyo itayamba kuchuluka, njira zina zoisamalirira zinakhazikitsidwa, ndipo mosakayikira zina mwa zimenezi anazipatsira kwa mibadwo yotsatira. Njira yosamalirira ntchito zaunsembe pakachisi wa Yehova zinaperekedwanso ndi atate kwa mwana. Pamene mtundu unali kukhala ndi chidziŵitso chochuluka, miyambo yawo inali kuchulukanso.
Koma chofunika kwambiri pa kulambira kwa Israyeli chinali Chilamulo cholembedwa choperekedwa kwa Mose. Eksodo 24:3, 4 imati: ‘Mose anadza nafotokozera anthu mawu onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mawu onse walankhula Yehova tidzachita. Ndipo Mose analembera mawu onse a Yehova.’ Mulungu anachita pangano ndi Aisrayeli monga mwa malamulo olembedwa amenewa. (Eksodo 34:27) Kwenikweni, palibe pamene Malemba amanena kuti kunali chilamulo cha pakamwa.
“Ndani Anakupatsani Ulamuliro Wotere?”
N’zosakayikitsa kuti Chilamulo cha Mose chinasiyira ansembe, mbadwa za Aroni, ulamuliro waukulu pa zachipembedzo ndi kulangiza. (Levitiko 10:8-11; Deuteronomo 24:8; 2 Mbiri 26:16-20; Malaki 2:7) Koma m’kupita kwa zaka mazana ambiri, ansembe ena anakhala osakhulupirika nakhalanso achinyengo. (1 Samueli 2:12-17, 22-29; Yeremiya 5:31; Malaki 2:8, 9) M’nthaŵi ya ulamuliro wa Girisi, ansembe ambiri anagonjera Agirikiwo pankhani zachipembedzo. M’zaka za zana lachiŵiri B.C.E., Afarisi—gulu latsopano m’Chiyuda limene silinali kukhulupirira ansembe—linayamba kukhazikitsa miyambo mwa imene munthu wamba anatha kudziona kukhala woyera mofanana ndi wansembe. Miyambo imeneyi inawakopa ambiri, koma inali yowonjeza ku Chilamulo komanso yosavomerezeka.—Deuteronomo 4:2; 12:32 (13:1 m’makope achiyuda).
Afarisi anakhala akatswiri atsopano a Chilamulo, akumachita ntchito imene anaona kuti ansembe sakuichita. Popeza kuti Chilamulo cha Mose sichinawapatsepo ulamuliro, iwo anapanga njira zatsopano zomasulirira Malemba mwa mafotokozedwe osokoneza ndi mwa njira zina zimene mwachionekere zinali kuchirikiza malingaliro awo.a Pokhala oyang’anira ndi ochirikiza aakulu a miyambo imeneyi, iwo anapanga gulu lina laulamuliro mu Israyeli. Podzafika m’zaka za zana loyamba C.E., Afarisi anali atakhala amphamvu koposa m’Chiyuda.
Pamene anali kusonkhanitsa miyambo ya pakamwa imene inalipo ndi kufufuza zifukwa za m’Malemba kuti akhazikitse miyambo yawo inanso, Afarisi anaona kuti zochita zawo ziyenera kukhala ndi ulamuliro wowonjezeka. Lingaliro latsopano la chiyambi cha miyambo imeneyi linabadwa. Arabi anayamba kuphunzitsa kuti: “Mose analandira Torah ku Sinai ndi kumpatsira Yoswa, Yoswa anaipereka kwa akulu, ndipo akulu kwa aneneri. Ndipo aneneri anaipereka kwa amuna a msonkhano waukulu.”—Avot 1:1, Mishnah.
Ponena kuti, “Mose analandira Torah,” arabi sanali kungonena malamulo olembedwa komanso miyambo yawo yonse ya pakamwa. Iwo ankanena kuti miyambo imeneyi—yopangidwa ndi anthu—ndi Mulungu amene anampatsa Mose ku Sinai. Ndipo anaphunzitsa kuti Mulungu sanasiyire anthu kuti aikemo zimene munalibe, koma anafotokoza pakamwa zimene Chilamulo cholembedwa sichinanene. Malinga ndi kunena kwawo, Mose anapatsira mibadwo yotsatira chilamulo cha pakamwa chimenechi, osati kwa ansembe, koma kwa atsogoleri ena. Afarisi iwo eni ankanena kuti ndiwo oloŵa mzere “wopitirizabe” umenewu wa ulamuliro.
Chilamulo Chikhala Pavuto—Kupeza Njira Ina
Yesu, amene ulamuliro wake wopatsidwa ndi Mulungu unakayikiridwa ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda, anali ataneneratu kuti kachisi adzawonongedwa. (Mateyu 23:37–24:2) Aroma atawononga kachisi mu 70 C.E., kupereka nsembe ndi utumiki wa ansembe zimene zinali zofunika m’Chilamulo cha Mose, zinasiya kuchitika. Mulungu anali atachita pangano latsopano lozikidwa pa nsembe ya dipo ya Yesu. (Luka 22:20) Pangano la Chilamulo cha Mose linathetsedwa.—Ahebri 8:7-13.
M’malo moona zochitika zimenezi monga umboni wakuti Yesu anali Mesiya, Afarisi anapeza njira ina. Iwo anali atalanda kale mphamvu zambiri za ansembe. Pokhala kachisi anali atawonongedwa, iwo anatenganso sitepe lina. Sukulu ya arabi ya ku Yavneh inakhala likulu la Sanhedrin yokonzedwanso—bwalo lamilandu lalikulu lachiyuda. Motsogozedwa ndi Yohanan ben Zakkai ndi Gamaliel II ku Yavneh, Chiyuda chinakonzedwanso kotheratu. Mautumiki a pasunagoge, otsogozedwa ndi arabi, analoŵa m’malo kulambira kwa pakachisi, koyang’aniridwa ndi ansembe. Mapemphero, makamaka a pa Tsiku la Chitetezo, analoŵa m’malo nsembe. Afarisi anafotokoza kuti chilamulo cha pakamwa choperekedwa kwa Mose ku Sinai chinaoneratu zimenezi ndipo chinapangiratu makonzedwe.
Masukulu a arabi anafalabe. Maphunziro ake aakulu anali makambirano akuya okhudza chilamulo cha pakamwa, kuchiloŵeza pamtima, ndi kuchigwiritsa ntchito. Kumbuyoko, chilamulo cha pakamwa chinali chozikidwa pa kumasulira Malemba—Midrash. Tsopano, miyambo imene inali kuwonjezeka nthaŵi zonse anayamba kuiphunzitsa ndi kuilinganiza payokha. Lamulo lililonse la m’chilamulo cha pakamwa anali kulifupikitsa kuti likhale losavuta kuloŵeza pamtima, ndipo nthaŵi zambiri linali kuimbidwa ngati nyimbo.
Anachilemberanji Chilamulo cha Pakamwa?
Kuchuluka kwa masukulu a arabi ndi kuwonjezeka kwa malamulo a arabi zinachititsa vuto lina. Adin Steinsaltz, katswiri wa maphunziro a arabi, anafotokoza kuti: “Mphunzitsi aliyense anali ndi njira yakeyake ndipo malamulo ake a pakamwa anali kuwalemba m’njira yakeyake. . . . Sikunalinso kokwanira kungophunzira maphunziro a mphunzitsi wako okha, ndipo wophunzira ankafunikira kuphunziranso malamulo a akatswiri ena . . . Motero ophunzira anakakamizika kuloŵeza pamtima zinthu zambirimbiri chifukwa cha ‘kuchulukitsitsa kwa chidziŵitso.’” Pokhala panali chidziŵitso chochuluka chosatsatirika bwino, zinali zovuta kotheratu kuti wophunzira akumbukire zonse.
M’zaka za zana lachiŵiri C.E., kupandukira Roma kwa Ayuda, motsogoleredwa ndi Bar Kokhba, kunapangitsa kuti akatswiri a maphunziro a arabi azunzidwe koopsa. Akiba—rabi wamkulu, amene anachirikiza Bar Kokhba—pamodzi ndi akatswiri ena otchuka anaphedwa. Arabi anaopa kuti chizunzo chitayambiranso chingawononge chilamulo chawo cha pakamwa. Iwo anali kukhulupirira kuti miyambo imaperekedwa bwino pakamwa kwa wophunzira kuchokera kwa mphunzitsi, koma kusintha kwa zinthu kumeneku kunapangitsa kuti ayeseyese mwamphamvu kukhala ndi makonzedwe olinganizidwa osungitsa ziphunzitso za amuna anzeru, kuti zisaiŵalidwe ku nthaŵi zonse.
Panthaŵi yotsatira atakhala pamtendere ndi Roma, Judah Ha-Nasi, rabi wamkulu kumapeto kwa zaka za zana lachiŵiri ndi kuchiyambi kwa zaka za zana lachitatu C.E., anasonkhanitsa akatswiri ambiri ndi kulinganiza miyambo ya pakamwa yambirimbiri mwa kuilemba m’Zigawo zisanu ndi chimodzi, chigawo chilichonse chogaŵidwanso m’zigawo zazing’ono—63 zonse pamodzi. Bukulo linadzatchedwa kuti Mishnah. Ephraim Urbach, wodziŵa za chilamulo cha pakamwa, anati: “Mishnah . . . inakhala yovomerezedwa ndipo inapatsidwa ulamuliro umene sunapatsidwepo kwa buku lina lililonse kusiyapo Torah.” Mesiya anakanidwa, kachisi anali wabwinja, koma popeza kuti chilamulo cha pakamwa chinalembedwa ndi kusungidwa monga Mishnah, nyengo yatsopano inayambika m’Chiyuda.
[Mawu a M’munsi]
a Njira imeneyi yomasulira Malemba imatchedwa kuti midrash.
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi n’chifukwa chiyani Ayuda ambiri anakana ulamuliro wa Yesu?