Tsiku Lomaliza la Moyo Waumunthu wa Yesu
Ndi pafupifupi madzulo pa Lachisanu, Nisani 14, 33 C.E. Kagulu ka amuna ndi akazi kakufuna kuika m’manda bwenzi lawo lokondedwa. Mmodzi wa amunawo, Nikodemo, wabweretsa zonunkhira kuti akonzere thupilo. Mwamuna wina wotchedwa Yosefe wapereka nsalu zoyera kuti akulungire mtembo wozunzundidwa ndi wosupulidwawo.
KODI anthuŵa ndani, nanga akuika m’manda yani? Kodi zonsezi inu zikukukhudzani? Kuti tiyankhe mafunsoŵa, tiyeni tibwerere kuchiyambi kwa tsiku losaiwalika limenelo.
Lachinayi Madzulo, Nisani 14
Mwezi wathunthu wowala bwino ukukwera pang’onopang’ono ku Yerusalemu. Mumzinda wodzaza anthuwo mukuyamba kukhala bata pambuyo pa tsiku la zochita zambiri. Madzulo ano mpweya ukungonunkhira fungo la nyama yowotcha ya mwana wa nkhosa. Inde, anthu zikwizikwi akukonzekera chochitika chapadera—phwando la pachaka la Paskha.
M’chipinda chachikulu cha alendo, muli Yesu Kristu ndi atumwi ake 12 atakhala pathebulo lomwe lakonzedwa. Tamverani! Yesu akulankhula. Iye akuti: “Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa.” (Luka 22:15) Yesu akudziŵa kuti adani ake achipembedzo ali otsimikiza kumupha. Koma zimenezo zisanachitike, chinthu china chofunika kwambiri chichitika madzulo ano.
Atachita Paskhayo, Yesu akuti: “Mmodzi wa inu adzandipereka Ine.” (Mateyu 26:21) Zimenezi zikuvutitsa maganizo atumwiwo. Kodi angakhale ndani? Atakambiranakambirana, Yesu akuuza Yudase Isikariote kuti: “Chimene uchita, chita msanga.” (Yohane 13:27) Ngakhale kuti enawo sakuzindikira, Yudase ndi mdyerakuŵiri. Iye akuchoka kuti akachite mbali yake yomvetsa manyazi m’chiŵembu choukira Yesu.
Chochitika Chapadera
Tsopano Yesu akuyambitsa chochitika chatsopano kwenikweni—chimene chidzakhala kukumbukira imfa yake. Yesu akutenga mkate napereka pemphero lothokoza ndi kuugaŵa. “Tengani, idyani,” iye akuwalangiza motero. “Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu.” Pamene aliyense wa iwo wadyako mkatewo, iye akutenga chikho cha vinyo wofiira nam’dalitsa. “Mumwere ichi inu nonse,” Yesu akuwauza motero, nalongosola kuti: “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.” Iye akulangiza atumwi okhulupirika 11 otsalawo kuti: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.”—Mateyu 26:26-28; Luka 22:19, 20; 1 Akorinto 11:24, 25.
Madzulo amenewo mokoma mtima Yesu akukonzekeretsa atumwi ake okhulupirika pa zimene ziti zichitike ndipo akuwatsimikizira kuti amawakonda kwambiri. Iye akulongosola kuti: “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu.” (Yohane 15:13-15) Inde, atumwi 11 ameneŵa asonyeza kuti ndi mabwenzi oona a Yesu mwa kukhala naye m’mayesero ake.
Usiku wakewo—mwinamwake kupitirira pakati pausiku—Yesu akupereka pemphero losaiwalika, pambuyo pake iwo akuimba nyimbo zotamanda Yehova. Kenaka, ndi kuwala kwa mwezi wathunthu, akuchoka mumzindawo ndi kudutsa Chigwa cha Kidroni.—Yohane 17:1–18:1.
M’munda wa Getsemane
Patapita kanthaŵi kochepa, Yesu ndi atumwi ake akufika ku munda wa Getsemane. Atasiya asanu ndi atatu a atumwiwo pachipata cha mundawo, Yesu akutenga Petro, Yakobo, ndi Yohane napita nawo mkati mwa mitengo ya azitona. Iye akuuza atatuwo kuti: “Moyo wanga uli wa chisoni chambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimudikire.”—Marko 14:33, 34.
Atumwi atatuwo akudikira pamene Yesu akupita mkatikati mwa mundawo kukapemphera. Ndi mawu amphamvu komanso misozi, akuchonderera kuti: “Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine.” Yesu ali ndi udindo waukulu kwambiri. Zikumuvutitsa maganizo kwambiri kuganiza zimene adani a Yehova adzanena pamene Mwana Wake wobadwa yekha wapachikidwa monga mpandu! Chopweteka kwambiri kwa Yesu ndi kulingalira za chitonzo chimene chingadze pa Atate wake wakumwamba wokondedwa ngati iye atalephera kupirira chiyeso chopwetekachi. Yesu akupemphera moona mtima kwambiri ndipo akuvutika kwambiri kwakuti thukuta lake likukhala ngati kuti ndi madontho a magazi ogwera pansi.—Luka 22:42, 44.
Yesu wangotsiriza kumene kupemphera kachitatu. Tsopano kukufika anthu onyamula miuni ndi nyale. Amene ali patsogolo si winanso ayi koma Yudase Isikariote, amene akupita mwachindunji kwa Yesu. “Tikuoneni, Rabi,” iye akutero, nampsompsona Yesu mwachikondi. “Yudase,” akuyankha Yesu, “ulikupereka Mwana wa munthu ndi chimpsompsono kodi?”—Mateyu 26:49; Luka 22:47, 48; Yohane 18:3.
Dzidzidzi, atumwiwo akuzindikira chimene chikuchitika. Mbuyawo ndi bwenzi lawo lokondedwa ali pafupi kumangidwa! Motero Petro akutenga lupanga ndi kudula khutu la kapolo wa mkulu wa ansembe. Mwamsanga Yesu akuti: “Lekani zimenezi.” Akuyandikira nachiritsa kapoloyo ndipo akulamula Petro kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Luka 22:50, 51, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono; Mateyu 26:52) Akulu a asilikali ndi asilikali awo akugwira Yesu ndi kumumanga. Pogwidwa ndi mantha ndiponso chifukwa cha kusokonezeka, atumwiwo akumusiya Yesu ndi kuthaŵa usikuwo.—Mateyu 26:56; Yohane 18:12.
Lachisanu Mmaŵa, Nisani 14
Tsopano ndi m’mbandakucha wa Lachisanu. Choyamba Yesu akupita naye kunyumba kwa Mkulu wa Ansembe wakale Anasi, amene adakali ndi ulamuliro ndi mphamvu. Anasi akumufunsa mafunso ndiyeno akumutumiza ku nyumba kwa Mkulu wa Ansembe Kayafa kumene Sanihedirini yasonkhana.
Atsogoleri achipembedzowo tsopano akuyesa kupeza mboni zoti zipeke mlandu wokhudza Yesu. Komabe, umboni wa mboni zabodzazo sukugwirizananso. Yesu sakulankhula nthaŵi yonseyi. Pogwiritsa ntchito machenjera ena, Kayafa akulamula kuti: “Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.” Imeneyi ndi mfundo yosakanika, choncho Yesu molimba mtima akuyankha kuti: “Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.”—Mateyu 26:63; Marko 14:60-62.
Kayafa akufuula nati: “Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina?” Tsopano ena akupanda khofu Yesu ndi kumuthira malovu. Ena akumubwanyula ndi kumunyoza. (Mateyu 26:65-68; Marko 14:63-65) Mwamsanga dzuŵa litatuluka pa Lachisanu, Sanihedirini ikusonkhananso, mwina kuyesa kupangitsa kuzenga mlandu kopanda lamulo kochitidwa usikuko kuoneka ngati kwa lamulo. Yesu molimba mtima akusonyezanso kuti ali Kristu, Mwana wa Mulungu.—Luka 22:66-71.
Kenaka, ansembe aakulu ndi amuna akulu akumutenga Yesu kuti akazengedwe mlandu ndi Pontiyo Pilato, kazembe wa Roma mu Yudeya. Iwo akuimba Yesu mlandu wa kupatutsa mtundu, kuletsa anthu kupereka msonkho kwa Kaisara, ndi ‘kudzinenera kuti Iye yekha ndiye Kristu mfumu.’ (Luka 23:2; yerekezerani ndi Marko 12:17.) Atatha kufunsa Yesu, Pilato akulengeza kuti: “Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.” (Luka 23:4) Pamene Pilato akumva kuti Yesu kwawo ndi ku Galileya, akumutumiza kwa Herode Antipa, wolamulira wa Galileya, amene ali ku Yerusalemu chifukwa cha Paskha. Herode alibe malingaliro ochita zachilungamo. Akungofuna kuona Yesu atachita chozizwitsa. Popeza kuti Yesu sakukhutiritsa chikhumbo chake ndipo wangokhala chete osalankhula, Herode ndi asilikali ake akumuseŵeretsa ndi kumutumizanso kwa Pilato.
“Munthuyu anachita choipa chiyani?” akufunsanso motero Pilato. “Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamukwapula Iye ndi kumumasula.” (Luka 23:22) Motero iye akulamula kuti Yesu akwapulidwe ndi chikoti chokhala ndi zingwe zochuluka chimene chikudzetsa ululu kumsana kwa Yesu. Kenaka asilikaliwo akumumveka chisoti cha minga. Akumuseka ndi kumumenya ndi bango lolimba, kukhomerera chisoti cha mingacho m’mutu mwake. Mmene akumva ululu ndi kuzunzidwa konse kumeneku, Yesu akudzisungirabe ulemu wake ndipo ndi wamphamvu modabwitsa.
Pilato—mwinamwake poganiza kuti anthu amumvera chisoni Yesu chifukwa wazunzundidwa—akumusonyezanso kwa khamulo. Pilato akunena kuti: “Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziŵe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.” Koma ansembe aakulu akufuula kuti: “M’pachikeni, m’pachikeni.” (Yohane 19:4-6) Pamene khamulo likuumirirabe, Pilato akugonja ndi kumupereka Yesu kuti akapachikidwe.
Imfa Yaululu
Dzuŵa lakwera tsopano, mwina latsala pang’ono kufika pamutu. Yesu apita naye kunja kwa Yerusalemu kumalo otchedwa Gologota. Akukhomerera manja ndi mapazi a Yesu ku mtengo wozunzirapo ndi misomali ikuluikulu. Akumva ululu wosaneneka pamene kulemera kwa thupi lake kukukulitsa mabala a misomali pamene mtengo wozunzirapowo ukudzutsidwa. Khamu lasonkhana kuti lidzaonerere Yesu ndi apandu ena aŵiri akupachikidwa. Anthu ambiri akulankhula zonyoza Yesu. “Anapulumutsa ena,” ansembe aakulu ndi anthu ena akumuchitira chipongwe, “sangathe kudzipulumutsa yekha.” Nawonso asilikali ndi apandu aŵiri opachikidwawo akumunyoza Yesu.—Mateyu 27:41-44.
Mwadzidzidzi dzuŵa lili pamutu, Yesu atakhala pamtengo wozunzirapowo kwa kanthaŵi, mdima wochititsa mantha wochititsidwa ndi Mulungu ukugwa padzikolo kwa maola atatu.a Mwinamwake ndi mdimawu umene ukupangitsa mmodzi wa ochita zoipawo kuti adzudzule mnzake. Ndiyeno, potembenukira kwa Yesu, iye akupempha kuti: “Ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu.” Ndi chikhulupirirodi chodabwitsa poyang’anizana ndi imfa! Yesu akuyankha kuti: “Indetu, ndinena ndi iwe, lerolino udzakhala ndine m’Paradaiso.”—Luka 23:39-43.
Pafupifupi 3 koloko masana, Yesu akuona kuti watsala pang’ono kufa. “Ndimva ludzu,” iye akunena tero. Ndiyeno mofuula, akuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” Yesu akuzindikira kuti Atate wake, kunena kwake titero, aleka kumutetezera kuti kukhulupirika kwake kuyesedwe mpaka mapeto, ndipo iye akugwira mawu a Davide. Munthu wina akuika pakamwa pa Yesu chinkhupule choviikidwa mu vinyo wosasa. Atamwako vinyoyo, Yesu akuthatha nati: “Kwatha.” Ndiyeno akufuula kuti, “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga,” akuweramitsa mutu wake nafa.—Yohane 19:28-30; Mateyu 27:46; Luka 23:46; Salmo 22:1.
Popeza kuti tsopano ndi pafupifupi madzulo, pakupangidwa makonzedwe ofulumira oti Yesu aikidwe m’manda tsiku la Sabata (Nisani 15) lisanayambe pa kuloŵa kwa dzuŵa. Yosefe wa ku Arimateya, membala wa Sanihedirini wodziŵika bwino amene wakhala akuphunzira mwachinsinsi ndi Yesu, wapempha chilolezo choti amuike m’manda. Nikodemo, membalanso wa Sanihedirini amene mobisa anali kukhulupirira Yesu, akumuthandiza ndi makilogalamu 33 a mure ndi aloe. Mosamala, akuika thupi la Yesu m’manda achikumbukiro atsopano cha pafupi pompo.
Alinso Wamoyo!
Kudakali kachisisira Lamlungu mmaŵa pamene Mariya wa Magadala ndi akazi ena akufika pa manda a Yesu. Koma taonani! Mwala umene unali pakhomo pamandawo wachotsedwapo. Inde, m’manda mulibe kanthu! Mariya wa Magadala akuthamanga kuti akauze Petro ndi Yohane. (Yohane 20:1, 2) Iye atangochoka mngelo akuonekera kwa akazi enawo. Akunena kuti: “Musawope inu.” Akuwalangizanso kuti: “Pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, wauka kwa akufa.”—Mateyu 28:2-7.
Pamene akufulumira kubwerera kumudzi, akukumana ndi Yesu mwiniyo! Iye akuwauza kuti: “Pitani, kauzeni abale anga.” (Mateyu 28:8-10) Pambuyo pake, Yesu akuonekera kwa Mariya wa Magadala pamene iye akulira pamanda. Chimwemwe chake chasefukira ndipo akuthamangira kukauza ophunzira ena za nkhani yosangalatsayi. (Yohane 20:11-18) Kwenikweni, nthaŵi zisanu Lamlungu losaiwalika limenelo, Yesu woukitsidwayo akuonekera kwa ophunzira osiyanasiyana, sakusiya chikayikiro chilichonse chakuti iye alinso ndi moyo!
Mmene Zikukukhudzirani
Kodi zinthu zomwe zinachitika zaka 1,966 zapitazo zingakukhudzeni bwanji inuyo tsopano pamene tikuyamba zaka zana la 21? Mboni yoona ndi maso ya zochitika zimenezo inafotokoza kuti: “Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamutuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo [“nsembe yoombola,” NW] chifukwa cha machimo athu.”—1 Yohane 4:9, 10.
Kodi ndi motani mmene imfa ya Kristu ilili “nsembe yoombola”? Ndi yoombola chifukwa imatheketsa kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu. Munthu woyamba Adamu, anapandukira Mulungu ndipo motero anapatsa ana ake uchimo ndi imfa. Mosiyana ndi zimenezo, Yesu anapereka moyo wake monga dipo kulipira mtengo wa uchimo ndi imfa ya mtundu wa anthu, motero akumaika maziko oti Mulungu azisonyezera chifundo ndi chiyanjo. (1 Timoteo 2:5, 6) Mwa kusonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu yoombola ku machimo, mungamasulidwe ku mlandu umene munalandira kuchokera kwa Adamu wochimwayo. (Aroma 5:12; 6:23) Ndiyeno, zimenezi zimakupatsani mwayi wodabwitsa wokhala ndi unansi wabwino ndi Atate wanu wachikondi wakumwamba, Yehova Mulungu. Mwachidule, nsembe yamtengo wapatali ya Yesu ingakupatseni moyo wosatha.—Yohane 3:16; 17:3.
Nkhani zimenezi ndi zinanso zidzalongosoledwa Lachinayi madzulo, pa April 1, m’malo ambirimbiri padziko lonse lapansi pamene mamiliyoni a anthu adzasonkhana kuti akumbukire imfa ya Yesu Kristu. Tikukuitanani kuti mukapezekepo. Mboni za Yehova za m’dera lanu mosangalala zidzakufotokozerani malo ndi nthaŵi imene mungakapezekepo. Mosakayikira kupezekapo kwanu kudzakupangitsani kuyamikira kwambiri zimene Mulungu wathu wachikondi ndi Mwana wake wokondedwa anachita patsiku lomaliza la moyo waumunthu wa Yesu.
[Mawu a M’munsi]
a Mdimawo sunali chifukwa cha kadamsana chifukwa Yesu anafa panthaŵi imene mwezi unali wathunthu. Akadamsana amangochitika kwa mphindi zochepa ndipo amachitika pamene mwezi wakhala pakati pa dziko ndi dzuŵa panthaŵi imene ukukhala kumene.
[Tchati/Zithunzi patsamba 7]
IMFA NDI KUUKITSIDWA KWA YESU
NISANI 33 C.E. ZOCHITIKA MUNTHU WAMKULUb
14 Lachinayi Chikondwerero cha paskha; Yesu 113, ndime 2
madzulo asambitsa mapazi a atumwi; Yudase mpaka 117,
akuchoka kuti akapereke Yesu; ndime 1
Kristu akuyambitsa Chikumbutso cha
imfa yake (chaka chino chochitidwa
pa Lachinayi, April 1, dzuŵa
litaloŵa); chilimbikitso
chokonzekeretsa atumwi ake za
kuchoka kwake
Pakati Pambuyo pa pemphero ndi nyimbo 117 mpaka 120
pausiku mpaka zotamanda, Yesu ndi atumwi apita
dzuŵa lili kumunda wa Getsemane; Yesu apemphera
pafupi ndi mawu aakulu ndi misozi; Yudase
kutuluka Isikariote akufika ndi chikhamu ndipo
akupereka Yesu; atumwi akuthaŵa pamene
Yesu wamangidwa ndi kutengeredwa kwa
Anasi; Yesu atengeredwa kwa Mkulu wa
Ansembe Kayafa kuti akaonekere pamaso
pa Sanihedirini; akuweruzidwa kuti
aphedwe; akunyozedwa ndi kumenyedwa;
Petro akukana Yesu katatu
Lachisanu Pamene dzuŵa likutuluka, Yesu 121 mpaka 124
mmaŵa akuonekeranso kwa Sanihedirini;
akupita naye kwa Pilato;
akutumizidwa kwa Herode; kubwereranso
kwa Pilato; Yesu akubwanyulidwa,
kuchitidwa chipongwe, ndi kumenyedwa;
mokakamizidwa Pilato akumupereka kuti
akapachikidwe; dzuŵa litakwera akupita
naye ku Gologota kuti akaphedwe
Dzuŵa lili Akupachikidwa dzuŵa litangotsala 125, 126
pamutu mpaka pang’ono kufika pamutu; mdima kuyambira
masana dzuŵa dzuŵa lili pamutu mpaka pafupifupi
litapepa 3 koloko, pamene Yesu akufa; chivomezi
champhamvu;chinsalu cha m’kachisi
ching’ambika pakati
Pafupifupi Thupi la Yesu liikidwa m’manda a m’mund 127,
madzulo a la Sabata lisanayambe ndime 1-7
15 Lachisanu La Sabata liyamba
Madzulo
Loŵeruka Pilato akuloleza kuti alonda 127,
adikirire manda a Yesu ndime 8, 9
16 Lamlungu Mmamaŵa manda a Yesu akupezeka 127,
apululu; Yesu woukitsidwayo akuonekera ndime 10
(1) kwa kagulu ka ophunzira achikazi, mpaka 129,
kuphatikizapo Salome, Yohana, ndi ndime 10
Mariya amayi ake a Yakobo; (2) kwa Mariya
wa Magadala; (3) kwa Kleopa ndi mnzake;
(4) kwa Simoni Petro; (5) pamsonkhano wa
atumwi ndi ophunzira ena
[Mawu a M’munsi]
b Amene andandalikidwa pano ndi manambala osonyeza machaputala a m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Onani buku lakuti “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” tsamba 290 kuti mupeze tchati chomwe chili ndi tsatanetsatane yense wa malifalensi a Malemba a utumiki womalizira wa Yesu. Mabuku ameneŵa amafalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.