Kodi Mulungu Amachita Zinthu ‘Mokhotakhota’?
“DEUS ESCREVE CERTO POR LINHAS TORTAS” (“Mulungu amalemba zabwino koma m’mizere yokhotakhota”), umatero mwambi wina ku Brazil. Umatanthauza kuti nthaŵi zonse Mulungu amachita zinthu ‘zolondola’ koma nthaŵi zina amazichita mwanjira imene imaoneka kukhala yokhotakhota kwa anthu. Mwachitsanzo, pamene munthu amene wafika pachimake m’moyo wamwalira, ambiri amati, ‘Mulungu wamuitana kumwamba.’ Ngati munthu ali wopunduka kapena wagweredwa tsoka, ena amati, ‘Ndi chifuno cha Mulungu.’ Popeza Mulungu ndi amene amaimbidwa mlandu wa imfa, matenda, ndi zinthu zina zimene zimadzetsa chisoni, mawu ngati ameneŵa amasonyeza kuti Mulungu ‘amalemba mokhotakhota,’ kuti amachita zinthu mwanjira imene munthu sangamvetse.
N’chifukwa chiyani anthu ambiri achipembedzo amakhulupirira kuti Mulungu ndiye amachititsa imfa ndi mavuto? Iwo ali ndi zikhulupiriro zimenezi chifukwa cha kusamvetsetsa ena mwa malemba a m’Baibulo ongotengedwa apa ndi apo. Tiyeni tione mwachidule ena mwa iwo.
● “Analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Sindine Yehova kodi?”—Eksodo 4:11.
Kodi izi zikutanthauza kuti Mulungu ndi amene ayenera kuimbidwa mlandu chifukwa cha onse amene akuvutika ndi kulumala kwa mtundu uliwonse? Ayi. Izi zingakhale zosemphana ndi umunthu wa Mulungu. Baibulo limatiuza kuti: “Cholengedwa chonse cha Mulungu n’chabwino.” (1 Timoteo 4:4) Sayenera kuimbidwa mlandu ngati wina wabadwa wakhungu, wosalankhula, kapena wogontha. Iye amafunira chilengedwe chake zabwino zokhazokha, popeza kwa iye ndiye Gwero la “mphatso iliyonse yabwino ndi chininkho chilichonse changwiro.”—Yakobo 1:17.
Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, ndi amene modzifunira anasankha kupandukira Mulungu ndipo anataya ungwiro wawo ndiponso mphamvu yobereka ana angwiro. (Genesis 3:1-6, 16, 19; Yobu 14:4) Pamene ana awo anayamba kukwatira ndi kukhala ndi ana, ndi pamenenso zophophonya, komanso zilema zinayamba kuwonjezereka kwambiri ndi kuonekera pakati pa anthu. Ngakhale kuli kwakuti si Yehova Mulungu amene anachititsa zimenezi, iye walola kuti zichitike. Choncho, anadzinenera yekha kukhala monga amene “analenga” wosalankhula, wogontha, ndi wakhungu.
● “Chokhotakhota sichingawongokenso.”—Mlaliki 1:15.
Kodi ndi Mulungu amene anapanga zinthu kuti zikhale zokhotakhota? Ndithudi ayi. Mlaliki 7:29 akuti: “Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.” Baibulo la Contemporary English Version linatembenuzira vesili kuti: “Pamene Mulungu ankatilenga tinali oona mtima kwambiri, koma tsopano tili ndi maganizo okhotakhota.” M’malo mochita mogwirizana ndi malamulo olungama a Mulungu, nthaŵi zambiri amuna ndi akazi mwadala amasankha kuchita zolingalira zawo mwanjira yawo—zimene zabweretsa mavuto.—1 Timoteo 2:14.
Komanso, monga mmene mtumwi Paulo ananenera, chifukwa cha uchimo wa anthu, “cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru.” (Aroma 8:20) Ndipo mkhalidwe umenewu ‘sungawongoke’ mwa mphamvu za anthu. Kokha mwa Mulungu kukhotakhota konse ndi kupanda pake kwa zinthu za padziko lapansi kudzachoka.
● “Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa?”—Mlaliki 7:13.
Mwa mawu ena, Mfumu Solomo anali kufunsa kuti: ‘Ndani pakati pa anthu angawongole zilema ndi zophophonya zimene Mulungu wazilola?’ Palibe, chifukwa chakuti Yehova Mulungu ali ndi cholinga polola zinthu zimenezi kuti zizichitika.
Choncho, Solomo akulangiza kuti: “Tsiku la mwayi kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m’tsogolo mwawo.” (Mlaliki 7:14) Munthu ayenera kuyamikira tsiku limene zinthu zamuyendera bwino ndi kusonyeza chiyamikiro mwa kukhala wokoma mtima. Ayenera kuona tsiku labwino monga mphatso yochokera kwa Mulungu. Koma bwanji ngati tsikulo lili latsoka? Munthu angachite bwino ‘kupenya,’ kutanthauza kuti ayenera kuzindikira kuti Mulungu walola kuti tsokalo lichitike. Chifukwa chiyani watero? Kuti “anthu asapeze kanthu ka m’tsogolo mwawo,” akuyankha motero Solomo. Kodi izi zikutanthauzanji?
Popeza kuti Mulungu amalola zinthu zosangalatsa komanso mavuto kutichitikira, zimatikumbutsa kuti sitingadziŵe zimene zingachitike m’tsogolo. Matsoka amafikira anthu abwino ndi oipa omwe. Sasankha. Izi ziyenera kutithandiza kuzindikira kufunika kodalira Mulungu, osati kudzidalira, tikumakumbukira kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Ngakhale kuti panopo sitingamvetse zinthu zina, tingakhale otsimikiza kuti pamene zonse zachitika, zimene Mulungu walola zidzakhala zitagwira ntchito yothandiza kwa onse amene zikuwakhudza.
Zilizonse zimene wazilola kuchitika sizidzavulaza kotheratu anthu oona mtima. Mtumwi Petro anamveketsa izi pamene anali kuthirira ndemanga pamavuto amene okhulupirira anzake a m’nthaŵi yake anali kukumana nawo: “Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthaŵi, adzafikitsa inu opanda chilema mwiniwake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.”—1 Petro 5:10.
Nthaŵi Yowongola Zinthu
Yehova amatipatsa mphamvu kuti tipirire ziyeso zimene timakumana nazo pakalipano. Akulonjezanso kuti adzapanga “zonse zikhale zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Inde, n’cholinga chake kuti posachedwapa Ufumu wake wakumwamba udzabwezeretsa thanzi kwa awo amene ali opunduka ndi kuukitsa anthu akufa. Boma limeneli lidzachotsanso munthu amene njira zake zili zokhotakhota zedi—Satana Mdyerekezi. (Yohane 5:28, 29; Aroma 16:20; 1 Akorinto 15:26; 2 Petro 3:13) Ndithudi, lidzakhala dalitso kwa anthu oopa Mulungu padziko lonse lapansi, pamene nthaŵi ya Mulungu yoti awongole zinthu yafika!
[Mawu a Chithunzi patsamba 28]
Yobu Akuuzidwa za Kuwonongeka kwa Zinthu Zake/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications