Kuphunzira Njira Yoposa ya Chikondi
Kosovo, Lebanon, ndi Ireland. Awa ndi mayina omwe akhala akuoneka m’nyuzi m’zaka zaposachedwapa. Anthu akamva za mayina amenewa, amangoganiza za mikhalidwe ya kukhetsa mwazi, kuphulitsa mabomba, ndi kuphana. N’zoona kuti, ziwawa zoyambitsidwa ndi zipembedzo, mafuko, mitundu ya anthu, kapenanso mikangano yosiyanasiyana, sizachilendo. Kunena zoona m’mabuku a zochitika zam’mbiri n’ngodzaza ndi zomwezo, ndiponso zachititsa mavuto osaneneka ku mtundu wa anthu.
POONA kuti nkhondo zakhala zikuchitika kuyambira kalekale, ambiri afika pogamula kuti nkhondo n’zosapeŵeka ndi kuti n’chachibadwa kuti athu azidana. Komabe, malingaliro amenewo, n’ngosiyana kotheratu ndi ziphunzitso za Mawu a Mulungu, Baibulo. Malemba amanena motsimikiza kuti: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) N’chachionekere kuti Mlengi amafuna kuti anthu azikondana.
Baibulo limasonyezanso kuti munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. (Genesis 1:26, 27) Zimenezi zikutanthauza kuti mtundu wa anthu unapatsidwa ufulu wonse wosonyeza mikhalidwe ya Mulungu, yomwe wotchuka mwa imeneyi ndiwo chikondi. Popeza kuti zili choncho, n’chifukwa chiyani anthu alephereratu kusonyezana chikondi m’mbiri yonse? Panonso Baibulo likupereka yankho. Chili chifukwa chakuti mwamuna ndi mkazi oyambawo, Adamu ndi Hava, anapandukira Mulungu ndi kulowa mu tchimo. Zotsatira zake zinali zakuti, mbadwa zawo zonse zinabadwa ndi uchimo ndi kupanda ungwiro kwa makolo awowo. Aroma 3:23 amalongosola kuti: “Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” Mkhalidwe wa kukonda, umene tinapatsidwa ndi Mulungu, unasokonezedwa ndi uchimo ndi kupanda ungwiro. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu onse sangathenso kukondana? Kodi pali chiyembekezo chilichonse chakuti mwina n’kudzasangalala ndi mtendere ndi ubwenzi ndi anthu anzathu?
Tiyenera Kuphunzira Kukonda Mulungu
Yehova Mulungu akudziwa kuti mtundu wa anthu ungathe kusonyezana chikondi, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro. N’chifukwa chake iye amafuna kuti onse amene amafuna kumukondweretsa azisonyeza chikondi mmene angathere. Chifuno chake chimenechi, chinafotokozedwa bwino lomwe ndi Mwana wa Mulunguyo, Yesu Kristu, pamene anamufunsa kuti atchule lamulo lalikulu pa Chilamulo choperekedwa kwa Aisrayeli. Iye anati: “ Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.” Ndipo anapitiriza kunena kuti: “Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini. Pa malamulo awa aŵiri m’pokoloŵekapo chilamulo chonse ndi aneneri.”—Mateyu. 22:37-40.
Komabe, anthu ambiri amaona ngati n’kovuta zedi kukonda munthu yemwe sungathe kumuona, ndipo anthufe sitingathe kuona Yehova Mulungu chifukwa chakuti iye ndi Mzimu. (Yohane 4:24) Komabe, zomwe Mulungu amachita zimatikhudza tsiku ndi tsiku, chifukwatu tonse timadalira zabwino zonse zimene iye analenga kuti tipindule nazo. Mtumwi Paulo ananena mfundo imeneyi pamene anati: “[Mulungu] sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.”—Machitidwe. 14:17.
Ngakhale kuti aliyense amapindula ndi zomwe Mlengi wathu amatipatsa m’njira zosiyanasiyana, n’ngochepa amene amam’yamikira kapena kum’thokoza. Choncho tiyenera kupenda zinthu zabwino zonse zimene Mulungu watichitira ndi kulingalira za mikhalidwe yake yabwino kwambiri imene imaonekera m’zomwe amachita. Kuchita zimenezo kudzatithandiza kuzindikira nzeru zozizwitsa ndi mphamvu za Mlengi Wamkulu. (Yesaya 45:18) Choposa zonse, kuyenera kutithandiza kuona kuti Mulungu n’ngwa chikondi, chifukwa sanatipatse moyo wokha, komanso anatipanga kuti tisangalale ndi zokondweretsa zochuluka m’moyo.
Mwachitsanzo, ganizirani za maluwa okongola amitundu yosiyanasiyana amene Mulungu analenga padziko lapansi. N’chochititsadi chidwi zedi kwa ife kuti iye anatipatsanso mphamvu kuti tizikhoza kuona ndi kusangalala kwambiri ndi zokongola zimenezi! Mofananamo, Mulungu anatipatsanso zakudya zamitundumitundu kuti tisangalale nazo. Poonetsanso kuti amatiganizira kwambiri, anathanso kutilenga ndi mphamvu ya kumva kukoma kuti tizitha kusangalala ndi chakudya! Kodi umenewu si umboni wamphamvu wakuti Mulungu amatikondadi ndipo amatifunira zabwino zokhazokha?—Salmo 145:16, 17; Yesaya 42:5, 8.
Pambali podzivumbula yekha kwa ife kudzera mu “buku la chilengedwe,” Mlengiyo, kudzera m’Mawu ake, Baibulo, amatisonyezanso mtundu wa Mulungu umene iye ali. Chifukwa chakuti m’Baibulo mwalembedwa zochuluka zimene Yehova Mulungu wachita mwa chikondi m’zaka zam’mbuyomu, ndi madalitso ochuluka amene akulonjeza kudzakhuthulira mtundu wa anthu posachedwapa. (Genesis 22:17, 18; Eksodo 3:17; Salmo 72:6-16; Chivumbulutso 21:4, 5) Choposa zonse, Baibulo limativumbulira chikondi chachikulu koposa chimene Mulungu anasonyezera ku mtundu wa anthu—kupereka Mwana wake wobadwa yekha kuti atiwombole ndi kutimasula ku nsinga za uchimo ndi imfa. (Aroma 5:8) Ndithudi, tikamaphunzira zochuluka za Mlengi wathu wachikondiyo, chikondi chathu chochokera pansi pa mtima chimakulanso.
Kuphunzira Kukonda Anthu Anzathu
Monga mmene Yesu ananenera kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi nzeru zathu zonse, anapitiriza kunenanso kuti tiyenera kukonda mabwenzi anthu monga mmene timadzikondera ife eni. Inde, chikondi cha Mulungu chimatisonkhezera kukondanso anthu anzathu. Mtumwi Yohane ananena kuti: “Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.” Iye anapitiriza kunena motsimikiza kuti: “Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona. Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.”—1 Yohane. 4:11, 20, 21.
Lerolino tikukhala m’dziko limene anthu ambiri ali ndi maganizo akuti nditchuke ndine, “odzikonda okha,” monga momwe Baibulo linaloserera. (2 Timoteo 3:2) Choncho, ngati tikufuna kuphunzira njira yoposa yachikondi, tiyenera kuyesetsa mwakhama kukonzanso mitima yathu ndi kutsanzira Mlengi wathu wachikondiyo m’malo molondola njira zodzikonda za anthu ochuluka. (Aroma 12:2; Aefeso 5:1) ‘Mulungu amachitira zokoma ngakhale anthu osayamika ndi oipa,’ ndipo iye “amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” Popeza kuti Atate wathu wakumwamba watisonyeza chitsanzo chabwino, tiyesetse kuchitira onse chokoma ndi kukhala othandiza kwa onse. Mwa kuchita zimenezo, tidzasonyeza kuti ndife ‘ana a Atate wathu wakumwamba.’—Luka 6:35; Mateyu. 5:45.
Nthaŵi zina ntchito za chikondi ngati zimenezo, zingathandize anthu ena kukhala olambira a Mulungu woona. Zaka zingapo zapitazo, mayi wina yemwe ndi Mboni ya Yehova, anayesa kugaŵana uthenga wabwino wa m’Baibulo ndi mnansi wake, koma mnansiyo anakanitsitsa kumvetsera. Komabe, iye sanafooketsedwe ndi kukanako. M’malo mwake anapitiriza kusonyeza chikondi ndi kuthandiza mnansiyo. Panthaŵi ina anathandiza mnansiyo posamukira ku nyumba ina. Panthawi inanso anapempha munthu woti aperekeze mnansi wakeyo ku bwalo la ndege kuti akachingamire mbale wake wa mnansiyo. Pambuyo pake, mnansiyo anavomera phunziro la Baibulo ndipo pang’ono ndi pang’ono anakhala Mkristu wakhama mosasamala kanthu kuti mwamuna wake anam’zunza kwambiri. Inde, chikondi chimene anachisonyezacho, chinayala maziko a madalitso osatha.
Kunena zoona, tingavomereze kuti Mulungu amatikonda osati chifukwa chakuti timachita zolungama nthaŵi zambiri. M’malo mwake, amatikonda ngakhale kuti ndife ochimwa komanso tili ndi zophophonya zambiri. Pa chifukwa chimenecho, tiyeneranso kuphunzira kukonda anthu anzathu mosasamala kanthu za zophophonya zawo zambiri. Ngati tiphunzira kuzindikira ndi kuyamikira mikhalidwe yabwino mwa ena m’malo moyang’ana zophophonya zawo, kudzakhala kosavuta kwenikweni kuti tiwakonde. Tingawasonyeze chikondi chakuya kuposa chimene tingasonyeze chifukwa cha chikhulupiriro. Monga chikondi chachikulu ndi ubwenzi zomwe anthu okondana zedi amasonyezana.
Kukulitsa Chikondi Chanu
Chikondi ndi ubwenzi tiyenera kuzilimbikitsa ndi kuzikulitsa, ndipo zina mwa zimene zingathandize kutero ndizo kuona mtima ndi kukhulupirika. Ena amayesa kubisa zophophonya zawo ndi cholinga choti anthu amene akufuna kupalana nawo ubwenziwo aziŵasirira. Komabe, nthaŵi zonse mchitidwe umenewo umadzakubwerera, makamaka m’kupita kwa nthawi pamene ena ayamba kudziwa zoona zenizeni, ndipo amanyansidwa ndi chinyengo chotero. Choncho, sitiyenera kuopa kuti ena atidziŵe monga mmene tilili—ngakhale tili ndi zophophonya zomwe tikuyesetsa kuzithetsa. Zimenezi zidzathandiza kuti tipange nawo ubwenzi.
Mwachitsanzo, mlongo wina wachikulire m’mpingo wa ku Far East anali wosaphunzira. Koma, sanayesepo kubisira ena kuti iye n’ngwosaphunzira. Mwachitsanzo, iye amanena moona mtima kuti satha kusonyeza ena mmene angaŵerengere zaka m’maulosi a Baibulo ndi m’mbiri yakale pofuna kusonyeza kuti Nthaŵi za Akunja zinatha mu 1914.a Komabe, amasonyeza chitsanzo chabwino zedi kwa abale pokhala wakhama mu utumiki, ngakhalenso m’chikondi ndi kupatsa mooloŵa manja, mwakuti mwachikondi anamutcha mwala wamtengo wapatali wa mu mpingo.
M’zikhalidwe zina, kusonyeza chikondi poyera amanyansidwa nako; anthu amaphunzitsidwa kusonyeza khalidwe la ulemu m’zochita zawo ndi ena. Pamene kuli kwakuti n’kwabwino nthaŵi zonse kukhala waulemu ndi woganizira ena, tisalole chikhalidwe chathu kutilepheretsa kusonyeza ena chikondi chathu. Yehova sankachita manyazi pamene ankasonyeza chikondi chake kwa anthu ake osankhika, Israyeli wakale, ankawauza kuti: “Ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha.” (Yeremiya 31:3) Mofananamo, mtumwi Paulo anauza okhulupirira anzake a ku Tesalonika kuti: “Kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:8) Choncho, pamene tikuyesa kukulitsa chikondi kwa anthu anzathu, tidzachita zogwirizana kotheratu ndi ziphunzitso za Baibulo ngati tisonyeza malingaliro amenewo kaŵirikaŵiri, m’malo mowabisa.
Khama Likufunikabe
Kuphunzira kusonyeza chikondi kwa ena uyenera kukhala mchitidwe wosalekeza. Kuchita zimenezo kumafuna khama kumbali yathu chifukwa chakuti tifunikanso kulimbikira kuti tilake kupanda ungwiro kwathuku, limodzinso ndi kupewa zisonkhezero zamphamvu za dziko lopanda chikondi lino. Komabe, mphotho zimene zimadza chifukwa chochita zimenezi zimapangitsa zochitikazo kukhala zoyenerera.—Mateyu 24:12.
Ngakhale m’dziko lopanda ungwiro lino, tingasangalale ndi ubwenzi wabwino ndi anthu anzathu, zomwe zingadzetse chimwemwe, mtendere, ndi kukhutira kwa enife ndi kwa enanso. Mwa kuyesetsa kutero, tingasonyeze kuti tili ndi chiyembekezo chabwino koposa chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Choposa zonse, mwa kuphunzira njira ya chikondi, tingavomerezedwe ndi kudalitsidwa ndi Mlengi wathu wa chikondi, lero ndi kunthaŵi zosatha!
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, masamba 132-5.
[Zithunzi patsamba 10]
Chikondi chachikristu chimaoneka pamene musonyeza kukoma mtima
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
UN PHOTO 186226/M. Grafman