Kodi Tingachitenji Ngati Tikufooka?
KODI munthu angalimbane motani ndi zofooketsa? Limeneli linali funso lomwe linaperekedwa kwa oyang’anira oyendayenda ambiri, omwe kaŵirikaŵiri amachezera mipingo ya Mboni za Yehova. Mayankho awo angatithandize kupenda zomwe zimafooketsa ndi mmene tingathetsere mkhalidwe umenewu, womwe ungachitikire Mkristu aliyense.
Pakufunika zambiri kuposa kungopenda chabe kuti tithane ndi kufooka, koma zizindikiro zake zingaphatikizepo kupanda chidwi ndi pemphero komanso ndi phunziro laumwini, kusapezeka pa misonkhano mokhazikika, kusatenthedwa maganizo, ngakhalenso kuchita manyazi ndi mabwenzi achikristu. Komanso, chimodzi mwa zizindikiro zachionekere ndicho kuchepa kwa khama m’ntchito yolalikira. Tiyeni tipende zizindikirozi ndi kulingalira njira zina zothetsera vutolo.
Zofooketsa Pantchito Yathu Yolalikira
Yesu Kristu ankadziŵa bwino lomwe za mavuto omwe amadza mkati mwa ntchito yopanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Anatumiza otsatira ake monga “nkhosa pakati pa mimbulu,” akudziŵa kuti ntchito yawo yolalikirayo idzadzetsa chizunzo pa iwo. (Mateyu 10:16-23) Komabe, chimenechi sichinali chifukwa chakuti afookere. Kunena zoona, atumiki a Mulungu omwe mwapemphero adalira Yehova alimbitsidwa ndi chizunzo nthaŵi zambiri.—Machitidwe 4:29-31; 5:41, 42.
Ngakhale pamene ophunzira a Kristu sankazunzidwa kwambiri, sanali kulandiridwa bwino nthaŵi zonse. (Mateyu 10:11-15) Mofananamo, ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova lerolino, kaŵirikaŵiri simakhala yophweka kuchita.a Kwa anthu ambiri, kukhulupirira Mulungu ndi nkhani yaumwini yomwe safuna kukambirana ndi wina. Ena safuna chilichonse chokhudza gulu la chipembedzo lomwe iwo amalipeŵa. Mosakayika, kusoŵa chidwi kwa anthu, kusaona zotsatira, kapena mavuto ena osiyanasiyana angakhale magwero aakulu a kufooka. Kodi zopinga zimenezi zingathetsedwe bwanji?
Kupeza Zotsatira Zabwino
Chimwemwe chomwe timakhala nacho muutumiki wathu chimagwirizananso ndi zotsatira zomwe timapeza. Tsono, m’motani mmene tingakhalire ndi utumiki wopindulitsa kwambiri? Ndithudi, ndife “asodzi a anthu.” (Marko 1:16-18) Asodzi mu Israyeli wakale ankapita kukasodza usiku chifukwa chakuti imeneyo inali nthaŵi yomwe amapha nsomba zambiri. Ifenso lerolino tiyenera kupenda gawo lathu kuti “tizikasodza” pamene anthu ambiri ali panyumba ndiponso pamene angathe kulabadira uthenga wathuwo. Nthaŵi imeneyi ingakhale madzulo, kumapeto kwa mlungu, kapena panthaŵi ina yake. Malinga ndi mmene woyang’anira woyendayenda wina ananenera, kuchita zimenezi kumathandiza kwambiri m’madera omwe anthu amagwira ntchito tsiku lonse. Iye anati kuchitira umboni nthaŵi yamadzulo kaŵirikaŵiri kumadzetsa zotsatira zabwino zedi. Kuchitira umboni pa telefoni kapenanso umboni wamwamwayi umatithandizanso kuti tifikire anthu ambiri.
Kuchita khama muutumiki kumadzetsa zotsatira zabwino. Kumadzulo kwa Ulaya ndi m’mayiko ena a mu Afirika, ntchito yolalikira za Ufumu ikupita patsogolo zedi, ndipo zimenezi zachititsa kuti chiŵerengero chiwonjezeke. Mofananamo, mipingo yambiri yakhazikitsidwa m’madera omwe kwanthaŵi yaitali alingaliridwa kukhala osabala zipatso kapenanso m’magawo ofoledwa kaŵirikaŵiri. Komabe, bwanji ngati gawo lanu silikubala zipatso zoterozo?
Kukhalabe ndi Maganizo Abwino
Kuzindikira bwino lomwe zolinga zomwe Yesu anapereka kudzatithandiza kuti tisafooke pamene tiyang’anizana ndi kusoŵa chidwi muutumiki. Kristu anafuna kuti ophunzira ake afunefune oyenerera, osati kutembenuza anthu mwachisaŵaŵa. Nthaŵi zambiri ankanena kuti makamu a anthu sadzalandira uthenga wabwino, monga momwe Aisrayeli ambiri ankachitira, kusamvera zomwe aneneri akalewo ankawauza.—Ezekieli 9:4; Mateyu 10:11-15; Marko 4:14-20.
“Uthenga wabwino wa Ufumu” ukulandiridwa moyamikira ndi anthu “ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW; 24:14) Akufuna kutumikira Mulungu m’njira yomwe iye wasankha. Choncho, zotsatira za ntchito yathu n’zogwirizana kwambiri ndi mitima ya anthu kuposa kugwirizana kwake ndi luso lathu loperekera uthengawo. N’zoonadi kuti m’pofunika kuchita zomwe tingathe kuti uthenga wabwino ukhale wosangalatsa. Komabe, tingayang’ane kwa Mulungu kaamba ka zotsatira zake, pakuti Yesu anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.”—Yohane 6:44.
Ntchito yathu yolalikira imadziŵikitsa dzina la Yehova. Kaya anthu akumvetsera kapena ayi, ntchito yathu yolalikira imachitanso mbali yake yoyeretsa dzina lopatulika la Yehova. Komanso, kupyolera m’ntchito yathu yolalikirayi, timasonyeza kuti ndife ophunzira a Kristu, ndipo tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yofunika kwambiri yomwe ikuchitika m’masiku athu ano.—Mateyu 6:9; Yohane 15:8.
Zofooketsa ndi Maunansi
Maunansi ena pakati pa anthu, kaya mukhale m’banja kapena mu mpingo, angathe kutifooketsa. Mwachitsanzo, pali malingaliro akuti ena sakutimvetsetsa. Kupanda ungwiro kwa okhulupirira anzathu kungathenso kutifooketsa. Kachiŵirinso, Malemba angatithandize kwambiri.
“Gulu lonse la abale” padziko lonse likupanga banja lalikulu lauzimu. (1 Petro 2:17, NW) Koma kudzimva kuti tili m’gulu la anthu ogwirizana kungazilale pamene mavuto abuka chifukwa chosemphana malingaliro. N’zachionekere kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba nawonso anali ndi mavuto ngati amenewo, chifukwa chakuti mtumwi Paulo anali kuwakumbutsa mobwerezabwereza kuti azikhalira limodzi mogwirizana. Mwachitsanzo, anadandaulira akazi aŵiri achikristu, Euodiya ndi Suntuke, kuti athetse kusiyana maganizo kwawo.—1 Akorinto 1:10; Aefeso 4:1-3; Afilipi 4:2, 3.
Ngati tili ndi vuto limenelo, kodi tingadzutsenso motani chikondi chathu chochokera pansi pa mtima kwa abale ndi alongo athu? Mwa kudzikumbutsa ife eni kuti Kristu anaŵafera ndi kutinso iwo, monganso ife, akhulupirira nsembe yake ya dipo. Tiyeneranso kukumbukira kuti abale athu ambiri n’ngokonzeka kutsanzira Yesu Kristu mwakuika miyoyo yawo pangozi kaamba ka ife.
Zaka zambiri zapitazo, ku Paris, m’dziko la France, Mboni ina yachinyamata sinazengereze kunyamula sutukesi yomwe inali ndi bomba mkati yomwe inaikidwa kunja kwa Nyumba ya Ufumu. Anathamanga kutsika m’masitepe ambiri a nyumba yosanjikizana asanafike pakasupe pomwe anaponya sutikesiyo. Bombalo linaphulika atangotayira sutukesiyo pakasupepo. Atam’funsa chomwe chinam’sonkhezera kuika moyo wake pachiswe mwa njira imeneyi, iye anayankha kuti: “Ndinazindikira kuti miyoyo yathu inali pangozi. Choncho ndinaganiza kuti kunali bwino kuti ine ndekha ndife kusiyana ndikuti tonse tiphedwe nthaŵi imodzi.”b Ndi madalitso aakulu kwabasi kukhala ndi anzathu ngati ameneŵa omwe ali okonzeka kutsanzira chitsanzo cha Yesu!
Kuwonjezera pamenepo, tingasinkhesinkhe za mzimu wogwirizana womwe unali pakati pa Mboni za Yehova zomwe zinali mu ukaidi panthaŵi ya Nkhondo Yachiŵiri Yapadziko Lonse.c Posachedwapa, abale ndi alongo athu m’Malaŵi, mokhulupirika anasungabe umphumphu wawo monga Akristu oona. Kodi lingaliro lakuti abale athu m’mipingo mwathu angachitenso chimodzimodzi pamene tili m’mavuto silitisonkhezera kunyalanyaza kapenanso kusaona zododometsa ndi mavuto atsiku ndi tsiku ngati zazikulu kwambiri? Ngati tikulitsa maganizo a Kristu, unansi wathu watsiku ndi tsiku ndi alambiri anzathu udzakhala magwero a kutsitsimulidwa osati kufooketsedwa.
Malingaliro Aumwini Ofooketsa
“Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.” (Miyambo 13:12) Atumiki ena a Yehova amaona kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu akuchedwa. Akristu amaona kuti tikukhala m’nyengo ‘zoŵaŵitsa,’ monganso mmene ambiri osakhulupirira amaonera.—2 Timoteo 3:1-5.
Komabe, mosemphana ndi osakhulupirirawo, Akristu ayenera kukondwera poona “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Yesu m’mikhalidwe ino yodzetsa chiyeso. Chizindikiro chimenechi chikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uthetsa dongosolo loipali la zinthu posachedwapa. (Mateyu 24:3-14) Ngakhale mkhalidwewo utadzafika poipa kwambiri, monga momwedi zidzakhalira pa “chisautso chachikulu,” zochitika zimenezi ndizo magwero a chimwemwe kwa ife chifukwa chakuti zimalengeza za dziko latsopano la Mulungu lomwe likudzalo.—Mateyu 24:21; 2 Petro 3:13.
Kutaya chiyembekezo chakuti Ufumu udzaloŵerera m’zochitika zamakonozi kungachititse Mkristu kukhala wotanganidwa kwambiri ndi zinthu zakuthupi. Ngati atati alole kuti zinthu monga ntchito yakuthupi ndi kusangalala zimuthere nthaŵi ndi nyonga zake zonse, kudzakhala kovuta kwa iye kukwaniritsa bwino lomwe udindo wake wa m’Malemba. (Mateyu 6:24, 33, 34) Maganizo ngati ameneŵa amakhumudwitsa ndiponso kufooketsa. Woyang’anira woyendayenda wina anati: “M’dongosolo lino lazinthu n’zosatheka kuyesa kukhala ndi moyo wofanana ndi womwe udzakhale m’dongosolo latsopano.”
Ziŵiri mwa Njira Zothandiza Kwambiri
Pamene vutolo lapezeka, kodi munthu angapeze motani thandizo labwino? Phunziro laumwini ndi imodzi mwa njira zabwino zomwe zilipo. Chifukwa chiyani? “Limatikumbutsa chifukwa chake tiyenera kuchita zomwe timachitazo,” woyang’anira woyendayenda wina anatero pothirira ndemanga. Komanso wina analongosola kuti: “Kulalikira ndi lingaliro lokha lakuti ndi udindo wathu basi kumakhala kolemetsa m’kupita kwa nthaŵi.” Koma phunziro laumwini labwino limatithandiza kukhalanso ndi kaonedwe kabwino ka udindo wathu pamene tikuyandikira mapeto. M’lingaliro limodzimodzilo, Malemba amatikumbutsa mobwerezabwereza za kufunika kwa kudya bwino mwauzimu kuti tikhale ndi chimwemwe chenicheni pochita chifuno cha Mulungu.—Salmo 1:1-3; 19:7-10; 119:1, 2.
Akulu angathandize ena kuthana ndi zofooketsa mwa kupanga maulendo aubusa owalimbikitsa. M’maulendo apadera ameneŵa, akulu angaonetse kuti aliyense wa ife akuyamikiridwa kwambiri ndipo ali ndi malo ofunika kwambiri mkati mwa anthu a Yehova. (1 Akorinto 12:20-26) Ponena za Akristu anzake, mkulu wina anati: “Kuti ndisonyeze kufunika kwawo, ndimawakumbutsa zomwe akwaniritsa m’mbuyomu. Ndimaŵasonyeza kuti ali a mtengo wapatali zedi pamaso pa Yehova ndi kuti mwazi wa Mwana wake unaperekedwa m’malo mwa iwo. Malingaliro ameneŵa nthaŵi zonse amalandiridwa bwino. Pamene mawu ameneŵa achirikizidwa ndi maumboni amphamvu a m’Baibulo, onse amene amakhala ofooka amakhalanso okhoza kupanga zolinga zatsopano, monga pemphero ndi phunziro labanja komanso kuŵerenga Baibulo.”—Ahebri 6:10.
Mkati mwa maulendo aubusa, akulu ayenera kukhala osamala kuti asapereke malingaliro oti n’kovuta kukondweretsa Mulungu. M’malo mwake, akuluwo angathandize wolambira mnzawo wofookayo kuona kuti katundu wa otsatira a Yesu n’ngwopepuka. Choncho utumiki wathu wachikristu ndiwo magwero a chimwemwe.—Mateyu 11:28-30.
Kugonjetsa Kufooka
Mosasamala kanthu za chomwe chingachititse, kufooka ndi mliri umene tiyenera kuugonjetsa. Ngakhale zili choncho, kumbukirani kuti sitili tokha m’nkhondo imeneyi. Ngati tafooka, tiyeni tilandire thandizo la Akristu anzathu, makamaka akulu. Mwakuchita zimenezo, tingachepetse kufooka.
Choposa zonse, tiyenera kutembenukira kwa Mulungu kaamba ka chithandizo kuti tithe kulimbana ndi kufooka. Ngati tidalira Yehova mwapemphero, iye adzatithandiza kugonjetseratu kufooka. (Salmo 55:22; Afilipi 4:6, 7) Mwa njira ina iliyonse, monga anthu ake tidzakhalanso ndi malingaliro a wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Odala anthu odziŵa liwu la lipenga; ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova. Akondwera m’dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m’chilungamo chanu. Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yawo; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.”—Salmo 89:15-17.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Ntchito Yovuta ya Kunyumba ndi Nyumba” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 15, 1981.
b Onani patsamba 12 ndi 13 mu Galamukani! yachingelezi ya February 22, 1985, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c Onani nkhani yakuti “I Survived the ‘Death March’” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya August 15, 1980, komanso nkhani yakuti “Kusunga Umphumphu M’Jeremani Wachinazi” mu Galamukani! ya March 8, 1986.
[Chithunzi patsamba 31]
Maulendo aubusa olimbikitsa ochitidwa ndi akulu achikondi angathandize Akristu kuthetsa kufooka