Kodi Oipa Adzakhalabe kwa Utali Wotani?
‘Mukhaliranji chete [Yehova] pamene woipa am’meza munthu wolungama woposa iye mwini?’—HABAKUKU 1:13.
1. Kodi ndi liti pamene chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova chidzadzaza dziko lonse lapansi?
KODI Mulungu adzawonongadi oipa? Ngati adzatero, kodi tiyembekezere kwa utali wotani? Mafunso otereŵa amafunsidwa ndi anthu padziko lonse. Kodi mayankho ake tingawapeze kuti? Tingawapeze m’mawu aulosi ouziridwa ndi Mulungu onena za nthaŵi yake yoikika. Amatitsimikizira kuti Yehova posachedwapa adzapereka chiweruzo kwa onse ochita zoipa. Ndi kokha panthaŵiyo kuti dziko lapansi “lidzadzazidwa ndi chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja.” Limeneli ndi lonjezo laulosi lopezeka m’Mawu Opatulika a Mulungu pa Habakuku 2:14.
2. Ndi ziweruzo za Mulungu zitatu ziti zomwe zikupezeka m’buku la Habakuku?
2 Buku la Habakuku, lomwe linalembedwa cha m’chaka cha 628 B.C.E., lili ndi ziweruzo za Yehova Mulungu zitatu zotsatizana. Ziweruzo ziŵiri mwa zitatuzo zaperekedwa kale. Choyamba chinali chiweruzo cha Yehova pa mtundu wopulupudza wa Yuda wakale. Nanga chachiŵiri? Icho chinali chiweruzo cha Mulungu pa Babulo woponderezayo. Motero tili ndi chidaliro chonse kuti chiweruzo chachitatu cha ziweruzo zaumulungu zimenezi chidzaperekedwanso. Ndipotu tingachiyembekezere posachedwapa. Mulungu adzawononga oipa onse kaamba ka ubwino wa anthu olungama m’masiku otsiriza ano. Womaliza wa ameneŵa adzathera pa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” yomwe ikuyandikira mofulumira kwambiri.—Chivumbulutso 16:14, 16.
3. Kodi n’chiyani chomwe chili chotsimikizirika kugwera ochita zoipa m’nthaŵi yathu?
3 Nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu ikuyandikiradi nthaŵi zonse. Ndipo kuperekedwa kwa chiweruzo chaumulungu pa oipa m’nthaŵi yathu n’kotsimikizirika ngati mmene kukwaniritsidwa kwa ziweruzo za Yehova pa Yuda ndi Babulo kunalili. Komabe, bwanji titayerekezera kuti tili mu Yuda m’nthaŵi ya Habakuku? Kodi mukuchitika chiyani m’dziko limenelo?
Chipwirikiti M’dziko
4. Kodi ndi nkhani yochititsa mantha yotani imene Habakuku akumva?
4 Ingoyerekezerani kuti mukuona mneneri wa Yehova Habakuku atakhala patsindwi lathyathyathya la nyumba yake, akupitidwa kamphepo kayeziyezi kamadzulo. Chapambali pake pali chipangizo choimbira nyimbo. (Habakuku 1:1; 3:19, NW, timawu tating’ono tomalizira) Koma Habakuku akumva nkhani yochititsa mantha. Yehoyakimu, Mfumu ya Yuda wapha Uriya ndipo mtembo wa mneneri ameneyo wauponya m’manda a anthu achabe. (Yeremiya 26:23) Inde, Uriya anataya chikhulupiriro chake mwa Yehova, anachita mantha nathaŵira ku Aigupto. Komabe Habakuku akudziŵa kuti Yehoyakimu wachita upanduwo osati chifukwa chosonkhezeredwa ndi kufunitsitsa kulemekeza Yehova ayi. Zimenezi zikuchitiridwa umboni pamene mfumuyo ikunyalanyaziratu malamulo a Mulungu komanso chidani chomwe ilinacho pa mneneri Yeremiya ndi ena omwe akutumikira Yehova.
5. Kodi mkhalidwe wauzimu n’ngwotani mu Yuda, ndipo kodi Habakuku akuchita chiyani?
5 Habakuku akuona utsi wa zofukiza ukutuluka m’nyumba zoyandikana nazo. Anthuŵatu sakufukiza zimenezi ngati olambira a Yehova. Iwo aloŵa m’kachitidwe ka kulambira konyenga komwe kakuchirikizidwa ndi Mfumu yoipa ya Yuda Yehoyakimu. N’zochititsatu manyazi zedi! M’maso mwa Habakuku mwadzala misozi, ndipo iye akudandaula kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa. Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndewu, nauka makani. Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.”—Habakuku 1:2-4.
6. Kodi n’chiyani chomwe chachitikira chilamulo ndi chiweruzo mu Yuda?
6 Inde, kufunkha ndi chiwawa zachulukadi. Kulikonse kumene Habakuku akuyang’ana, akuona mavuto, ndewu, mikangano. “Chilamulo chalekeka,” chatha mphamvu. Nanga bwanji chiweruzo? Indedi, icho ‘sichikutulukira konse’ ndi chilakiko! Sichikupambana. M’malo mwake, ‘woipa akuzinga wolungama,’ akupotoza malamulo omwe cholinga chake n’kuteteza anthu osalakwa. Ndithudi, ‘chiweruzo chikutuluka chopindika.’ Chikupotozedwa. N’zomvetsatu chisoni kwambiri!
7. Kodi Habakuku watsimikiza mtima kuchitanji?
7 Habakuku wakhala kaye duu ndi kulingaliranso mkhalidwewo. Kodi adzaleka ntchito yakeyi? Ndithudi ayi! Atalingaliranso za kuzunzidwa konse kwa atumiki okhulupirika a Mulungu, munthu wokhulupirikayu akutsimikizanso mtima kukhalabe mneneri wa Yehova wolimba ndi wosasunthika. Habakuku adzapitirizabe kulengeza uthenga wa Mulungu, ngakhale kuti izi zingamuphetse.
Yehova Akuchita “Ntchito” Yovuta Kuikhulupirira
8, 9. Kodi ndi “ntchito” yovuta kuikhulupirira yotani imene Yehova akuchita?
8 M’masomphenya, Habakuku akuona opembedza onyenga, omwe sakulemekeza Mulungu. Tamvani zomwe Yehova akuwauza. Iye akuti: “Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu.” Mwachionekere, Habakuku sakumvetsa chifukwa chake Mulungu akuuza zimenezi anthu oipawo. Kenaka iye akumva Yehova akuwauza kuti: “Pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozereni.” (Habakuku 1:5) Alitu Yehova mwiniyo amene akuchita ntchito imeneyi imene sangavomereze. Koma kodi ntchitoyo n’njotani?
9 Habakuku akumvetsera mwachidwi mawu a Mulungu otsatira, omwe alembedwa pa Habakuku 1:6-11. Uwu ndi uthenga wa Yehova, ndipo palibe mulungu wonyenga kapena fano lililonse lopanda moyo lomwe lingalepheretse kukwaniritsidwa kwake. Uthengawo n’ngwakuti: “Pakuti taonani, ndiukitsa Akasidi, mtundu uja woŵaŵa ndi waliŵiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kuloŵa m’malo mosati mwawo, mukhale mwawomwawo. Ali oopsa, achititsa mantha, chiweruzo chawo ndi ukulu wawo zituluka kwa iwo eni. Akavalo awo aposa anyalugwe liŵiro lawo, aposa mimbulu ya madzulo ukali wawo, ndipo apakavalo awo atanda [“agugudaguguda pansi,” NW], inde apakavalo awo afumira kutali; auluka ngati chiwombankhanga chofulumira kudya. Adzera chiwawa onsewo; nkhope zawo zikhazikika zolunjika m’tsogolo [“zili ngati mphepo yakummaŵa,” NW]; asonkhanitsa andende ngati mchenga. Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga lililonse; popeza aunjika dothi, nalilanda. Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.”
10. Ndani omwe akuutsidwa ndi Yehova?
10 Ndi ulosi wochenjezatu kwabasi wochokera kwa Wam’mwambamwambayo! Yehova akuutsa Akasidi, mtundu woopsa zedi wa Babulo. Popita mu “chitando cha dziko lapansi,” adzagonjetsa malo ambirimbiri. N’zoopsa bwanji! Gulu la Akasidi ‘n’loopsa ndi lochititsa mantha,’ lamphamvu koposa. Limaika malamulo akeake okhwima. ‘Chiweruzo chawo chimatuluka kwa iwo eni.’
11. Kodi kubwera kwa gulu lankhondo la Babulo kudzaukira Yuda mungakulongosole motani?
11 Akavalo a Babulo ndi aliŵiro kuposa anyalugwe othamanga kwambiri. Apakavalo awo n’ngaukali kuposa mimbulu yanjala yosaka usiku. Pofunitsitsa kupita, ‘akavalo ake akugugudaguguda pansi,’ sakuugwira mtima. Kuchokera ku Babulo kutalitaliko, iwo akuloŵera ku Yuda. Pothamanga ndi liŵiro ngati la chiwombankhanga chothamangira chakudya chokoma, Akasidiŵa posachedwapa adzambwandira adani awo. Koma kodi izi zikachitika kwa kanthaŵi kochepa chabe, kungokhala kuukira kwa asilikali ochepa? Ndithudi ayi! “Adzera chiwawa onsewo,” monga chigulu cha ankhondo okhamukira kukawononga. Nkhope zawo zikusonyeza kuti akufunitsitsa kukamenya nkhondo, akuloŵera chakumadzulo, kulunjika Yuda ndi Yerusalemu, akuthamanga ndi liŵiro ngati la mphepo ya kummaŵa. Asilikali a Babulo akugwira anthu ambiri kwakuti ‘akusonkhanitsa andende ngati mchenga.’
12. Kodi Ababulo akuchitanji, ndipo kodi mdani woopsayu ‘akulakwa ndi kupalamula’ motani?
12 Ankhondo a Akasidi akunyoza mafumu ndi kulalatira akalonga. Onseŵatu alibe mphamvu zowaletsera kufika. ‘Akuseka linga lililonse,’ pakuti mzinda uliwonse walinga ukulandidwa pamene Ababulo ‘akuunjika dothi’ mwa kukonza chimtumbira pamene akuukirirapo mzindawo. Panthaŵi yoikika ya Yehova, mdani woopsayu “adzapitirira ngati mphepo.” Poukira Yuda ndi Yerusalemu, ‘adzalakwa ndi kupalamula’ chifukwa chopweteka anthu a Mulungu. Atapambana mofulumira, kazembe wa Akasidi adzadzitama kuti: ‘Mphamvu imeneyi ndi ya mulungu wathu.’ Komatu iye sakudziŵa zenizeni!
Maziko Enieni a Chiyembekezo
13. N’chifukwa chiyani Habakuku akukhala ndi chiyembekezo komanso chidaliro?
13 Chiyembekezo chikukula mumtima mwa Habakuku chifukwa cha kumvetsetsa chifuno cha Yehova. Pokhala ndi chidaliro chonse, iye akulankhula molemekeza Yehova. Monga mmene zalembedwera pa Habakuku 1:12, NW, mneneriyu akuti: “Kodi si ndinu wakale lomwe, Yehova? Mulungu wanga, Woyera wanga, Inu simufa.” Indedi, Yehova wakhala Mulungu “kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha,” kapena kuti kwamuyaya.—Salmo 90:1, 2.
14. Kodi n’njira yotani imene ampatuko a mu Yuda akutsata?
14 Polingalira za masomphenya ake opatsidwa ndi Mulungu ndiponso posangalala ndi zimene masomphenyawo amudziŵitsa, mneneriyu akupitiriza kuti: “Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamukhazika kuti alangidwe.” Mulungu waweruza motsutsana nawo Ayuda ampatuko, ndipo ali pamzere wolandira chiweruzo, chilango chachikulu, cha Yehova. Anafunika kumuona ngati Thanthwe lawo, ngaka yokha yeniyeni, pothaŵirapo, ndi Gwero la chipulumutso. (Salmo 62:7; 94:22; 95:1) Komatu, atsogoleri ampatukoŵa a mu Yuda sakuyandikira kwa Mulungu, ndipo akuponderezabe olambira a Yehova odzichepetsawo.
15. Kodi Yehova ali “wa maso osalakwa, osapenya choipa” m’lingaliro lotani?
15 Mkhalidwewu ukumuvutitsa kwambiri mneneri wa Yehova. Chotero iye akuti: “Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta.” (Habakuku 1:13) Zoonadi, Yehova ndi “wa maso osalakwa, osapenya choipa,” kapena kuti kulola zoipa.
16. Kodi zomwe zalembedwa pa Habakuku 1:13-17 mungazilongosole motani mwachidule?
16 Choncho Habakuku ali ndi mafunso ochititsa chidwi m’maganizo mwake. Iye akufunsa kuti: “Mupenyereranji iwo akuchita mochenjera, ndi kukhala chete pamene woipa amumeza munthu wolungama woposa iye mwini; ndi kuyesa anthu ngati nsomba za m’nyanja, ngati zokwawa zopanda wakuzilamulira. Aziŵedza zonse ndi mbedza, azigwira m’ukonde wake, nazisonkhanitsa m’khoka mwake; chifukwa chake asekera nakondwerera. Chifukwa chake aphera nsembe ukonde wake, nafukizira khoka lake, pakuti mwa izi gawo lake lilemera, ndi chakudya chake chichuluka. Kodi m’mwemo adzakhuthula m’ukonde mwake osaleka kuphabe amitundu?”—Habakuku 1:13-17.
17. (a) Poukira Yuda ndi Yerusalemu, kodi Ababulo akutumikira motani chifuno cha Mulungu? (b) Kodi Yehova adzavumbulanji kwa Habakuku?
17 Poukira Yuda ndi likulu lake, Yerusalemu, Ababulo adzachita mogwirizana ndi zolinga zawo. Sadzadziŵa kuti ali chida chimene Mulungu wagwiritsa ntchito kupereka chiweruzo cholungama pa anthu osakhulupirika. Tingamvetsetse chifukwa chake Habakuku sakumvetsa kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ababulo oipawo kupereka chiweruzo Chake. Akasidi okakala moyowo salambira Yehova. Amaona anthu ngati ‘nsomba ndi zokwawa’ basi, zongoyenera kugwidwa ndi kuponderezedwa. Koma Habakuku sadabwa kwa nthaŵi yaitali. Posachedwa Yehova amuvumbulira mneneri wakeyu kuti nawonso Ababulo adzalangidwa chifukwa cha kufunkha kwawo kwadyera ndiponso kupha anthu mopanda chifundo.—Habakuku 2:8.
Wokonzeka Kumva Mawu Enanso a Yehova
18. Kodi tingaphunzirenji pa malingaliro a Habakuku osonyezedwa pa Habakuku 2:1?
18 Komabe, padakali pano Habakuku akuyembekezera kumva Yehova akumuuza mawu enanso. Mneneriyu akunenetsa kuti: “Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang’anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamuyankha chiyani pa choneneza changa.” (Habakuku 2:1) Habakuku akufunitsitsa kudziŵa zimene Mulungu ati anene kupyolera mwa iyeyu ngati mneneri. Chikhulupiriro chake mwa Yehova monga Mulungu amene salola zoipa chikumupangitsa kusamvetsetsa chifukwa chake pali kuipa, koma ndi wokonzeka kusintha kaganizidwe kake. Chabwino, nanga bwanji ifeyo? Pamene sitikumvetsetsa chifukwa chimene zinthu zina zoipa zimachitikira, chidaliro chathu m’chilungamo cha Yehova Mulungu chiyenera kutithandiza kukhalabe olimba ndi kuyembekezera pa iye.—Salmo 42:5, 11.
19. Mogwirizanadi ndi mawu a Mulungu kwa Habakuku, kodi n’chiyani chomwe chinachitikira Ayuda opulupudzawo?
19 Malinga ndi mawu ake kwa Habakuku, Mulungu anapereka chiweruzo pa mtundu wopulupudzawo wa Ayuda mwa kulola Ababulo kugonjetsa Yuda. Mu 607 B.C.E. anawononga Yerusalemu ndi kachisi, anapha anthu akuluakulu ndi ana omwe, ndi kutenga andende ochuluka. (2 Mbiri 36:17-20) Atakhala akaidi m’Babulo kwanthaŵi yaitali, otsalira a Ayuda okhulupirika anabwerera kwawo ndipo anamanganso kachisi. Komabe, Ayudaŵa pambuyo pake anasonyezanso kusakhulupirika kwa Yehova makamaka pamene anakana Yesu monga Mesiya.
20. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito motani Habakuku 1:5 ponena za kukana Yesu?
20 Mogwirizana ndi Machitidwe 13:38-41, mtumwi Paulo anauza Ayuda a ku Antiokeya zimene kukana Yesu, moteronso kukana nsembe yake ya dipo, kukatanthauza. Pogwira mawu Habakuku 1:5 mu Septuagint yachigiriki, Paulo anachenjeza kuti: “Penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo: Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupira wina akakuuzani.” Mogwirizana ndi kunena kwa Paulo, kukwaniritsidwa kwachiŵiri kwa Habakuku 1:5 kunachitika pamene magulu ankhondo a Roma anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake mu 70 C.E.
21. Kodi Ayuda a m’tsiku la Habakuku anaiona motani “ntchito” ya Mulungu yochititsa Ababulo kuwononga Yerusalemu?
21 Kwa Ayuda a m’tsiku la Habakuku, “ntchito” ya Mulungu ya kuchititsa Ababulo kuwononga Yerusalemu inali yosaganizirika chifukwa mzinda umenewo unali kuchimake kolambirirako Yehova ndiponso malo amene mfumu yake yodzozedwa inakhazikitsidwa pampando. (Salmo 132:11-18) Pachifukwachi, Yerusalemu anali asanawonongedwepo. Kachisi wake sanatenthedwepo. Banja lachifumu la Davide silinachotsedwepo pampando. Palibe anakhulupirira kuti Yehova angalole zoterozo kuchitika. Koma kupyolera mwa Habakuku, Mulungu anapereka chenjezo lokwanira kuti zinthu zochititsa manthazi zidzachitikadi. Ndipo mbiri imatsimikizira kuti zinachitikadi monga momwe zinalosedwera.
“Ntchito” ya Mulungu Yovuta Kuikhulupirira M’tsiku Lathu
22. Kodi “ntchito” yovuta kuikhulupirira ya Yehova iphatikiza chiyani m’tsiku lathu?
22 Kodi Yehova adzachitanso “ntchito” yovuta kuikhulupirira m’tsiku lathu? Khalani otsimikiza kuti adzatero, ngakhale kuti kwa anthu okayikira zingaoneke zovuta kuzikhulupirira. Tsopano lino ntchito yovuta kuikhulupirira ya Yehova idzakhala kuwonongedwa kwa Matchalitchi a Chikristu. Mofanana ndi Yuda wakale, amanena kuti amalambira Mulungu komatu aipa kotheratu. Yehova adzaonetsetsa kuti mbali iliyonse ya zipembedzo za m’Gawo la Matchalitchi Achikristu yafafanizidwa posachedwapa, monga mmene “Babulo Wamkulu” yense, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, adzachitira.—Chivumbulutso 18:1-24.
23. Kodi mzimu wa Mulungu ukusonkhezera Habakuku kuchitanso chiyani?
23 Yehova analinso ndi ntchito ina yoti Habakuku agwire Yerusalemu asanawonongedwe mu 607 B.C.E. Kodi Mulungu amuuzanji mneneri wake? Eya, Habakuku amva zinthu zoti zimupangitsa kutenga chipangizo chake choimbira ndi kuimba nyimbo zachisoni popemphera kwa Yehova. Komabe, choyamba mzimu wa Mulungu umusonkhezera mneneriyu kulengeza masoka ochititsa mantha. Ndithudi tiyamikira kudziŵa tanthauzo lakuya la mawu aulosi oterowo a panthaŵi yoikika ya Mulungu. Tiyeni tsono tikhalebe tcheru pa ulosi wa Habakuku.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi mu Yuda munkachitika zotani m’tsiku la Habakuku?
• Kodi Yehova anachita “ntchito” yovuta kuikhulupirira yotani m’nthaŵi ya Habakuku?
• Kodi Habakuku anali ndi maziko achiyembekezo otani?
• Kodi Mulungu achita “ntchito” yovuta kuikhulupirira yotani m’tsiku lathu?
[Chithunzi patsamba 9]
Habakuku sankamvetsa chifukwa chomwe Mulungu ankalolera kuipa kupitirizabe. Kodi inuyo mukumvetsa?
[Chithunzi patsamba 10]
Habakuku analosera kuti Ababulo adzawononga dziko la Yuda
[Chithunzi patsamba 10]
Mabwinja ofukulidwa a Yerusalemu, yemwe anawonongedwa mu 607 B.C.E.