Ufumu wa Mulungu—Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
“Ufumu . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”—DANIELI 2:44.
1. Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani pa Baibulo?
BAIBULO ndi vumbulutso la Mulungu kwa anthu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakulandira mawu a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Baibulo limalongosola zimene tifunikira kudziŵa ponena za Mulungu: limatiuza za umunthu wake, zifuno zake, ndi zimene amafuna kwa ife. Baibulo lili ndi uphungu wabwino koposa wokhudza moyo wabanja ndi khalidwe la tsiku ndi tsiku. Limalongosola mwatsatanetsatane maulosi amene anakwaniritsidwa kalelo, amene akukwaniritsidwa tsopano, ndi amene adzakwaniritsidwa m’tsogolo. Zoonadi, “lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
2. Kodi Yesu anatsindika motani nkhani yaikulu ya m’Baibulo?
2 Chinthu chofunika koposa m’Baibulo ndicho nkhani yake yaikulu: kukwezedwa kwa ufumu wa Mulungu (ufulu wake wolamulira) kudzera mu Ufumu wake wakumwamba. Ndiyo inali mfundo yaikulu ya utumiki wa Yesu. “Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Iye anasonyeza pamene tiyenera kuuika m’moyo wathu pamene anatilimbikitsa kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:33) Anasonyezanso kufunika kwake pophunzitsa otsatira ake kupemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10.
Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
3. N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu uli wofunika koposa kwa ife?
3 N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu uli wofunika kwambiri chotere kwa anthu? Chifukwa chakuti posachedwapa udzachita kanthu kena komwe kadzasinthiratu ulamuliro wa dziko lapansi kosatha. Ulosi wa pa Danieli 2:44 umati: “Masiku a mafumu aja [amene akulamulira tsopano] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [boma la kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [maboma a padziko lapansi]. Nudzakhala chikhalire.” Ufumu wakumwamba wa Mulungu ukadzayamba kulamulira ponseponse, anthu sadzalamuliranso dziko lapansi. Maulamuliro a anthu ogaŵanitsa anthu ndiponso osakhutiritsa adzakhala mbiri yakale kunthaŵi zosatha.
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ndiye woyenerera kwambiri kukhala Mfumu ya Ufumu? (b) Kodi Yesu adzakhala ndi ntchito yotani posachedwapa?
4 Kristu Yesu, Wolamulira Wamkulu mu Ufumu wa kumwamba, wotsogoleredwa ndi Yehova iye mwini, ndiye woyenera kwambiri. Asanadze padziko lapansi, iye analiko kumwamba monga “mmisiri” wa Mulungu, pokhala woyamba kubadwa wa zolengedwa zonse za Mulungu. (Miyambo 8:22-31) Iye “ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko.” (Akolose 1:15, 16) Ndipo pamene Yesu anatumizidwa padziko lapansi ndi Mulungu, anachita chifuniro cha Mulungu nthaŵi zonse. Anapirira ziyeso zoŵaŵa kwabasi ndipo anafa ali wokhulupirika kwa Atate wake.—Yohane 4:34; 15:10.
5 Chifukwa chakuti anali wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa, Yesu anafupidwa. Mulungu anamuukitsira kumwamba ndipo anam’patsa mphamvu yokhala Mfumu ya Ufumu wa kumwamba. (Machitidwe 2:32-36) Monga Mfumu ya Ufumuwo, Kristu Yesu adzakhala ndi ntchito yochititsa nthumanzi yopatsidwa ndi Mulungu yotsogolera miyandamiyanda ya zolengedwa zamphamvu zauzimu pochotsa maulamuliro a anthu padziko lapansi ndi kuthetsa zoipa zonse padzikoli. (Miyambo 2:21, 22; 2 Atesalonika 1:6-9; Chivumbulutso 19:11-21; 20:1-3) Pamenepo Ufumu wakumwamba wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu udzakhala ulamuliro watsopano, boma lokhalo lolamulira dziko lonse lapansi.—Chivumbulutso 11:15.
6. Kodi ulamuliro wa Mfumu ya Ufumu tingauyembekeze kukhala wotani?
6 Ponena za Wolamulira watsopano wa dziko lapansi, Mawu a Mulungu amati: “Anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” (Danieli 7:14) Chifukwa chakuti Yesu adzatsanzira chikondi cha Mulungu, kudzakhala mtendere wochuluka ndi chimwemwe chachikulu mu ulamuliro wake. (Mateyu 5:5; Yohane 3:16; 1 Yohane 4:7-10) “Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha, . . . kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo.” (Yesaya 9:7) Lidzakhaladi dalitso lalikulu kwambiri kukhala ndi Wolamulira amene akulamulira ndi chikondi ndi chilungamo! Ndiye chifukwa chake 2 Petro 3:13 akuneneratu kuti: “Tiyembekezera miyamba yatsopano [Ufumu wakumwamba wa Mulungu], ndi dziko latsopano [anthu okhala padziko lapansi olinganizidwa mwatsopano] mmenemo mukhalitsa chilungamo.”
7. Kodi Mateyu 24:14 akukwaniritsidwa motani lerolino?
7 M’posakayikitsa kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo uthenga wabwino koposa kwa onse okonda zabwino. Ndiye chifukwa chake, monga mbali ya chizindikiro chakuti panopa tili mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu loipali, Yesu analosera kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:14) Ulosi umenewu uli m’kati mokwaniritsidwa tsopano lino, pamene Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi m’mayiko 234 zimathera maola oposa biliyoni imodzi chaka chilichonse pouza ena za Ufumu wa Mulungu. M’pakedi kuti nyumba yawo iliyonse yolambiriramo ya mipingo 90,000 padziko lonse lapansi imatchedwa kuti Nyumba ya Ufumu. Anthu amadza kunyumbazo kudzaphunzira za boma latsopano likudzalo.
Anzake Olamulira Nawo
8, 9. (a) Kodi olamulira anzake a Kristu adzachokera kuti? (b) Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani mu ulamuliro wa Mfumu ndi anzake olamulira nawo?
8 Kristu Yesu adzakhala ndi anzake olamulira nawo mu Ufumu wa kumwamba wa Mulungu. Chivumbulutso 14:1-4 chinalosera kuti anthu 144,000 ‘adzagulidwa mwa anthu’ ndipo adzaukitsidwira kumwamba. Ameneŵa ndi amuna ndi akazi amene, m’malo motumikiridwa, anatumikira Mulungu ndi anthu anzawo modzichepetsa. “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.” (Chivumbulutso 20:6) Chiŵerengero chawo n’chochepa kwambiri kusiyana ndi “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” amene adzapulumuka mapeto a dongosolo lino. Ameneŵanso ‘atumikira Mulungu usana ndi usiku,’ koma sadzapita kumwamba. (Chivumbulutso 7:9, 15) Adzakhala oyambirira kukhala padziko lapansi latsopano, nzika zolamulidwa ndi Ufumu wakumwamba wa Mulungu.—Salmo 37:29; Yohane 10:16.
9 Posankha amene adzalamulira pamodzi ndi Kristu kumwamba, Yehova anasankha anthu okhulupirika amene anaona moyo ndi mavuto ake onse. Palibe chimene anthu akumanapo nacho chimene mafumu ansembe ameneŵa sanakumanepo nacho. Chotero moyo wawo padziko lapansi udzawonjezera luso lawo polamulira anthu. Ngakhale Yesu iye mwini “anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuŵaŵa nazo.” (Ahebri 5:8) Ponena za iye mtumwi Paulo anati: “Sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.” (Ahebri 4:15) N’zotonthoza kwambiri kudziŵa kuti m’dziko latsopano lolungama la Mulungu, anthu adzalamulidwa ndi mafumu ndi ansembe achikondi ndi achifundo!
Kodi Ufumu Unali Chifuniro cha Mulungu?
10. N’chifukwa chiyani Ufumu wakumwamba sunali mbali ya chifuniro choyambirira cha Mulungu?
10 Kodi Ufumu wa kumwamba unalinso chifuniro choyambirira cha Mulungu pamene analenga Adamu ndi Hava? Nkhani ya m’Genesis yosimba za kulengedwa kwa zinthu, sitchulapo za Ufumu wodzalamulira anthu. Yehova iye mwini anali Wolamulira wawo, ndipo malinga ngati akanapitiriza kum’mvera, ulamuliro winanso wamtundu wina sunali wofunikira. Genesis chaputala 1 chimasonyeza kuti Yehova ndiye anali kuchita zonse zofunikira kwa Adamu ndi Hava, mwachionekere kudzera mwa Mwana wake wa kumwamba woyamba kubadwa. Nkhaniyo imatchula mawu monga akuti ‘Mulungu anati kwa iwo’ ndi akuti “anati Mulungu” kwa iwo.—Genesis 1:28, 29; Yohane 1:1.
11. Kodi anthu anali ndi chiyambi chotani changwiro?
11 Baibulo limati: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Zonse za m’munda wa Edene zinali zabwino zokhazokha. Adamu ndi Hava ankakhala m’paradaiso. Anali ndi maganizo ndi matupi angwiro. Ankatha kuyankhulana ndi Wowapanga ndipo iyenso ankayankhula nawo. Ndipo mwa kukhalabe okhulupirika, iwo akanabereka ana angwiro. Boma latsopano lakumwamba silikanafunikira.
12, 13. Powonjezeka anthu angwiro, n’chifukwa chiyani Mulungu akanathabe kulankhulana nawo?
12 Powonjezeka banja la anthu, kodi Mulungu akanatha bwanji kulankhulana nawo onse? Talingalirani za nyenyezi kumwamba. Izo zili m’magulumagulu onga mlalang’amba. Magulu ena ali ndi nyenyezi biliyoni imodzi. Enanso ali ndi nyenyezi pafupifupi thililiyoni imodzi. Ndipo asayansi akunena kuti payenera kukhala magulu a nyenyezi ameneŵa pafupifupi mabiliyoni 100 amene angathe kuwaona! Komabe, Mlengiyo akuti: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.”—Yesaya 40:26.
13 Popeza kuti Mulungu akudziŵa bwino zinthu zakuthambo zonsezi, ndithudi silikanakhala vuto kudziŵa bwino anthu omwe chiŵerengero chawo n’chochepa kwambiri. Ngakhale panopo, atumiki ake mamiliyoni angapo amapemphera kwa iye tsiku ndi tsiku. Mapemphero amenewo amam’fika Mulungu nthaŵi yomweyo. Chotero kulankhulana ndi anthu angwiro okhaokha sikukanakhala kovuta kwa iye. Sakanafunikira Ufumu winawake wakumwamba woti uziwayang’anira. Ndi makonzedwe osangalatsadi kwambiri—Yehova kukhala Wolamulira, kulankhulana naye mwachindunji, ndi kukhala ndi moyo popanda kuganizira za imfa, moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso!
“Sikuli kwa Munthu”
14. N’chifukwa chiyani anthu adzafunikirabe ulamuliro wa Yehova kwamuyaya?
14 Komabe, anthu—ngakhale angwirowo—akanafunikirabe ulamuliro wa Mulungu kwamuyaya. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yehova sanawalenge m’njira yoti angadziimire paokha popanda ulamuliro wake. Chimenecho n’chibadwa cha anthu, monga momwe mneneri Yeremiya anavomerezera kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.” (Yeremiya 10:23, 24) Kukanakhala kupusa anthu akanaganiza kuti angayendetse zinthu zonse popanda Yehova kuwalamulira. Zikanasemphana ndi mmene anapangidwira. Kudziimira paokha popanda ulamuliro wa Yehova kungabale dyera, chidani, nkhanza, chiwawa, nkhondo, ndi imfa, ndipo zimenezi sizingalephere. ‘Wina angapweteke mnzake pom’lamulira.’—Mlaliki 8:9.
15. Makolo athu oyambirira atasankha choipa kodi chotsatira chake chinali chiyani?
15 Chomvetsa chisoni n’chakuti makolo athu oyambirira anasankha kudziimira paokha, sanafune Mulungu kukhala Wolamulira wawo. Chotsatira chake chinali chakuti Mulungu sanawasungebe kukhala angwiro. Iwo tsopano anali ngati chipangizo chogwiritsa ntchito magetsi chimene sichikulandiranso mphamvu ya magetsiwo. Chotero m’kupita kwa nthaŵi, anali kudzatha mphamvu pang’onopang’ono kenako kuimiratu—pa imfa. Anakhala ngati chikombole chopindika, ndipo ndi mkhalidwe umene anapatsira ana awo onse. (Aroma 5:12) “Thanthwe [Yehova], ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo. . . . Anam’chitira zovunda sindiwo ana ake, chilema n’chawo.” (Deuteronomo 32:4, 5) Zoonadi, Adamu ndi Hava anasonkhezeredwa ndi cholengedwa chauzimu chopanduka chomwe chinakhala Satana, komatu iwo anali ndi maganizo angwiro moti akanatha kukana malingaliro ake opotokawo.—Genesis 3:1-19; Yakobo 4:7.
16. Kodi mbiri ikuchitira motani umboni wa zotsatira za kusafuna kulamulidwa ndi Mulungu?
16 Mbiri ili ndi umboni wonse wosonyeza zotsatira za kusafuna kulamulidwa ndi Mulungu. Kwa zaka mazana ambiri, anthu ayesa mitundu yonse ya maboma a anthu, maluso onse oyendetsera zachuma ndi zachikhalidwe cha anthu. Koma m’pamene zoipa ‘zikuipa chiipire.’ (2 Timoteo 3:13) Zaka za ma 1900 zasonyeza zimenezo. Zinali zaka za chidani choopsa, chiwawa chochititsa mantha, nkhondo zazikulu, njala yadzaoneni, umphaŵi wothetsa nzeru, ndi kuvutika kosaneneka kusiyana ndi kale lonse. Komanso mosasamala kanthu za mankhwala atsopano amene apangidwa, nthaŵi imafikabe imene aliyense amafa. (Mlaliki 9:5, 10) Mwa kuyesa kuwongolera mapazi awo, anthu adzipereka okha kuti asokonezedwe ndi Satana ndi ziwanda zake, moti Baibulo limatcha Satana kuti “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.”—2 Akorinto 4:4.
Mphatso ya Ufulu wa Kudzisankhira
17. Kodi mphatso ya Mulungu ya ufulu wa kudzisankhira inayenera kugwiritsidwa ntchito motani?
17 N’chifukwa chiyani Yehova analola anthu kuchita zofuna zawo? Chifukwa chakuti anawalenga ndi mphatso yodabwitsa ya ufulu wa kudzisankhira. “Pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu,” anatero mtumwi Paulo. (2 Akorinto 3:17) Palibe munthu amene akufuna kukhala ngati makina, kuti wina azimuuza china chilichonse chimene ayenera kunena ndi kuchita. Koma Yehova anafuna kuti anthu azigwiritsa ntchito mosamala mphatso imeneyo ya ufulu wa kudzisankhira, kuti aziona kufunika kochita chifuniro chake ndi kukhalabe ogonjera kwa iye. (Agalatiya 5:13) Chotero ufuluwo sunali ufulu pa china chilichonse, chifukwa zimenezo zikanayambitsa chisokonezo. Unayenera kulamulidwa ndi malamulo othandiza a Mulungu.
18. Kodi Mulungu wasonyeza chiyani polola munthu kudzisankhira zochita?
18 Polola banja la anthu kuchita zofuna zawo, Mulungu, kamodzi kokha, wasonyeza kwamuyaya kuti tifunikira ulamuliro wake. Kulamulira kwake, ufumu wake, ndiko kokha kuli kolondola. Kumadzetsa chimwemwe chachikulu, chikhutiro, ndi chitukuko. Zili motero chifukwa chakuti Yehova anapanga maganizo athu ndi matupi athu kuti azigwira bwino kwambiri ntchito ngati titsatira malamulo ake. “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (Yesaya 48:17) Ufulu wodzisankhira potsatira malamulo a Mulungu sukanakhala wotopetsa koma ukanapangitsa kuti kukhale mitundu yosangalatsa yosiyanasiyana ya zakudya, nyumba, maluso, ndi nyimbo. Pogwiritsidwa ntchito bwino, ufulu wodzisankhira ukanadzetsa moyo wosangalatsa ndi wochititsa chidwi nthaŵi zonse padziko lapansi la paradaiso.
19. Kodi Mulungu akugwiritsa ntchito njira iti pobwezeretsa anthu kwa iye?
19 Koma chifukwa cha kusasankha bwino kwawo, anthu anadzilekanitsa ndi Yehova, ndipo anakhala opanda ungwiro, n’kuyamba kufooka, kenako kufa. Chotero anayenera kuwomboledwa ku mavuto omvetsa chisoni amenewo kuti akhalenso paunansi wabwino ndi Mulungu monga ana ake aamuna ndi aakazi. Njira yochitira zimenezi imene Mulungu anasankha ndiyo Ufumu, ndipo Wolanditsayo ndi Yesu Kristu. (Yohane 3:16) Kudzera m’dongosolo limeneli, anthu olapadi mumtima—ofanana ndi mwana woloŵerera wa m’fanizo la Yesu—adzabwezeretsedwa kwa Mulungu ndipo iye adzawalandiranso monga ana ake.—Luka 15:11-24; Aroma 8:21; 2 Akorinto 6:18.
20. Kodi Ufumu udzakwaniritsa motani chifuniro cha Mulungu?
20 Chifuniro cha Mulungu chidzachitika padziko lapansi mosalephera. (Yesaya 14:24, 27; 55:11) Kudzera mu Ufumu wake wolamulidwa ndi Kristu, Mulungu adzakweza (kutsimikizira kapena kusonyeza umboni wa) mphamvu yake yokhala Wolamulira wathu Wamkulu. Ufumuwo udzathetsa maulamuliro a anthu ndi a ziwanda padziko lapansili, ndipo uwo wokha ndi umene udzalamulira uli kumwamba kwa zaka 1,000. (Aroma 16:20; Chivumbulutso 20:1-6) Koma panthaŵi imeneyo, kodi njira ya Yehova yolamulira idzasonyezedwa motani kuti ndiyo yabwino? Ndipo zaka 1,000 zimenezo zikadzatha, kodi Ufumuwo udzakhala wantchito yanji? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
Mfundo Zobwereramo
• Kodi nkhani yaikulu m’Baibulo ndi yotani?
• Kodi ndani akupanga ulamuliro watsopano wa dziko lapansi?
• N’chifukwa chiyani ulamuliro wa anthu popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu sungapambane?
• Kodi ufulu wa kudzisankhira uyenera kugwiritsidwa ntchito motani?
[Chithunzi patsamba 10]
Pophunzitsa, Yesu anatsindika za ulamuliro wa Mulungu kudzera mu Ufumu
[Zithunzi patsamba 12]
M’dziko lililonse Mboni za Yehova zimapanga Ufumu kukhala chiphunzitso chawo chachikulu
[Zithunzi patsamba 14]
Mbiri ikusonyeza zotsatira zoipa za kusafuna kulamulidwa ndi Mulungu
[Mawu a Chithunzi]
Asilikali m’nkhondo yoyamba ya padziko lonse: Chithunzi cha U.S. National Archives; msasa wa chibalo: Oświęcim Museum; mwana: CHITHUNZI CHA UN 186156/J. Isaac