Anthu Aŵiri a Pachibale Amene Anali ndi Mitima Yosiyana
ZIMENE makolo asankha kuchita, zivute zitani, zimakhudza ana awo. Zimenezi n’zimene zimachitika lerolino monganso mmene zinalili kalelo m’munda wa Edene. Kupanduka kwa Adamu ndi Hava kunakhudza kwambiri anthu onse. (Genesis 2:15, 16; 3:1-6; Aroma 5:12) Komabe tonsefe, aliyense payekha, tili ndi mwayi wokhala ndi ubale wabwino ndi Mlengi wathu ngati tingafune kutero. Zimenezi tikuziona m’nkhani ya Kaini ndi Abele, anthu aŵiri a pachibale oyamba m’mbiri ya anthu.
Palibe Lemba limene limanena kuti Mulungu analankhulapo ndi Adamu ndi Hava atawathamangitsa m’munda wa Edene. Komabe, Yehova analankhula ndi ana awo. Mosakayika, Kaini ndi Abele anadziŵa kuchokera kwa makolo awo zimene zinachitika. Ankatha kuona “Makerubi . . . ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.” (Genesis 3:24) Amuna ameneŵa anaonanso kuti zimene Mulungu ananena kuti adzavutika zinalidi zoona.—Genesis 3:16, 19.
Kaini ndi Abele ayenera kuti anali kudziŵa zimene Yehova anauza njoka kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Zimene Kaini ndi Abele anadziŵa zokhudza Yehova zikanawathandiza kukhala pa ubale woyanjidwa ndi iye.
Kusinkhasinkha ulosi wa Yehova ndi makhalidwe ake monga Wopatsa wachikondi kunayenera kuchititsa Kaini ndi Abele kufuna kuti Mulungu awayanje. Koma kodi akanafuna kuchita zimenezo mpaka pati? Kodi akanatsatira chibadwa chawo chofuna kulambira Mulungu ndi kupita patsogolo mwauzimu kufika mpaka pom’khulupirira?—Mateyu 5:3.
Anthu a Pachibalewo Apereka Nsembe
Patapita nthaŵi, Kaini ndi Abele anapereka nsembe kwa Mulungu. Kaini anapereka nsembe ya zipatso za nthaka, ndipo Abele anapereka nsembe ya mwana woyamba wa nkhosa. (Genesis 4:3, 4) Panthaŵi imeneyi, amunaŵa ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 100, chifukwa Adamu anali ndi zaka 130 pamene anabereka mwana wake, Seti.—Genesis 4:25; 5:3.
Kupereka nsembe kwa Kaini ndi Abele kunasonyeza kuti ankazindikira kuti anali ochimwa ndipo anafuna kuti Mulungu awayanje. Ayenera kuti anaganizira lonjezo la Yehova lokhudza njoka ndi Mbewu ya mkazi. Baibulo silinena za nthaŵi imene anatenga ndi zimene anachita kuti akhale pa ubale woyanjidwa ndi Yehova. Komabe zimene Mulungu anachita pamene amunaŵa anapereka nsembe, zikutithandiza kuona mitima yawo.
Akatswiri ena amati Hava ankaona ngati Kaini anali “mbewu” imene inali yoti idzawononge njoka, chifukwa chakuti atabadwa Kaini, Hava anati: “Ndalandira munthu kwa Yehova.” (Genesis 4:1) Ngati nayenso Kaini ankaganiza zimenezo, analemba m’madzi. Mosiyana ndi Kaini, Abele anapereka nsembe yake ndi chikhulupiriro. Motero, “ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini.”—Ahebri 11:4.
Anthu aŵiri a pachibaleŵa sanangosiyana chabe pankhani yoti Abele anali wozindikira mwauzimu pamene Kaini sanali wotero ayi. Analinso osiyana mitima. Motero, “Yehova . . . anayang’anira Abele ndi nsembe yake: koma sanayang’anira Kaini ndi nsembe yake.” Kaini ayenera kuti sanapereke nsembe yake ndi mtima wonse ndipo anangoipereka mwamwambo chabe. Koma Mulungu sanavomereze kulambira kwa mwambo chabe. Kaini anali ndi mtima woipa, ndipo Yehova anazindikira kuti anali ndi zolinga zolakwika. Zimene Kaini anachita pamene Mulungu anakana nsembe yake zikuonetsa mtima wake weniweni. M’malo moti akonze mtima wake ndi zolinga zake, “Kaini . . . anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake.” (Genesis 4:5) Zimene anachitazi zinavumbula maganizo ndi zolinga zake zoipa.
Kum’chenjeza ndi Zimene Anayankha
Mulungu atadziŵa maganizo a Kaini, anam’chenjeza kuti: “Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzam’lamulira iye.”—Genesis 4:6, 7.
Tingaphunzirepo kanthu pamenepa. Kunena zoona, pali mipata yambiri yoti tingachimwe. Komabe, Mulungu watipatsa ufulu wosankha ndipo tingasankhe kuchita zabwino. Yehova anam’pempha Kaini “kuchita zabwino,” koma sanamuumirize kuti asinthe. Kaini sanasankhe kuchita zabwino.
Nkhani youziridwayo ikupitiriza kuti: “Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake, [Tiye tipite kumunda, NW]. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.” (Genesis 4:8) Motero, Kaini anakhala wosamvera ndiponso wambanda wopanda chifundo. Pamene Yehova anamufunsa kuti: “Ali kuti Abele mphwako?,” iye sanasonyeze n’pang’ono pomwe kuti analakwa. M’malo mwake, Kaini anayankha mopanda chifundo komanso mwamwano kuti: “Sindidziŵayi: kodi ndine woyang’anira mphwanga?” (Genesis 4:9) Bodza la mkunkhuniza limenelo ndi kukana kuti analibe udindo pa mphwake zinavumbula kupanda chifundo kwa Kaini.
Yehova anatemberera Kaini ndipo anam’thamangitsa kum’chotsa ku dera lozungulira munda wa Edene. Mwachionekere, kutemberera nthaka kumene Yehova anachita poyamba, kukanagwira ntchito kwambiri pa Kaini ndipo nthaka sikanabala kanthu iye akailima. Anali woti adzakhala woyendayenda ndi wothaŵathaŵa padziko. Kudandaula kwa Kaini chifukwa cha kukula kwa chilango chimene anam’patsa, kunasonyeza kuti anali ndi nkhaŵa yoti amubwezera chifukwa cha kupha mng’ono wake, koma sanasonyeze kulapa kwenikweni. Yehova anaika “chizindikiro” pa Kaini, lomwe liyenera kuti linali lamulo lamphamvu limene anthu ena ankalidziŵa ndi kulitsatira ndiponso limene analiika n’cholinga choti liteteze Kaini kuti anthu asamuphe pom’bwezera zimene anachita.—Genesis 4:10-15.
Ndiyeno Kaini “anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m’dziko la Nodi, kummaŵa kwake kwa Edene.” (Genesis 4:16) Atatenga m’modzi mwa alongo ake kapena mwana wamkazi wa azibale ake kukhala mkazi wake, iye anamanga mudzi womwe anautcha dzina la mwana wake woyamba, Enoke. Lameke yemwe anali mbadwa ya Kaini anali wachiwawa monga mmene linalili kholo lake losaopa Mulungulo. Ndipo mbadwa zonse za Kaini zinawonongedwa pa Chigumula cha nthaŵi ya Nowa.—Genesis 4:17-24.
Zimene Tikuphunzira Pankhaniyi
Tingaphunzirepo kanthu pankhani ya Kaini ndi Abele. Mtumwi Yohane analimbikitsa Akristu kuti azikondana wina ndi nzake, “osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. . . . Ntchito [za Kaini] zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.” Yohane ananenanso kuti: “Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziŵa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.” Inde, mmene timachitira ndi Akristu anzathu zimakhudza ubale wathu ndi Mulungu ndiponso chiyembekezo chathu cha m’tsogolo. Mulungu sangatiyanje pomwe tikudana ndi wokhulupirira mnzathu wina.—1 Yohane 3:11-15; 4:20.
Kaini ndi Abele ayenera kuti analeredwa mofanana, koma Kaini sanakhulupirire Mulungu. Kunena zoona, iye anasonyeza mzimu wa Mdyerekezi, yemwe ali ‘wambanda ndi atate wake wa bodza’ kuyambira pachiyambi. (Yohane 8:44) Zimene Kaini anachita zikusonyeza kuti tonsefe tingathe kusankha, ndi kuti amene amasankha kuchimwa amadzisiyanitsa yekha ndi Mulungu ndi kutinso Mulungu amalanga anthu osalapa.
Koma Abele anakhulupirira Yehova. Inde, “ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, amene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake.” Ngakhale kuti m’Malemba mulibe liwu lililonse limene Abele ananena, mwa chitsanzo chake cha chikhulupiriro, iye “alankhulabe.”—Ahebri 11:4.
Abele anali woyamba mwa anthu ambiri okhulupirira. Mwazi wake, umene ‘unafuulira kwa Yehova kuchokera ku nthaka,’ sunaiwalike. (Genesis 4:10; Luka 11:48-51) Ngati tikhala ndi chikhulupiriro monga mmene Abele anachitira, ifenso tingakhale pa ubale wamtengo wapatali ndiponso wokhalitsa ndi Yehova.
[Bokosi patsamba 22]
MLIMI NDI MBUSA
Zina mwa ntchito zimene Mulungu anam’patsa Adamu zinali kulima nthaka ndi kusamalira nyama. (Genesis 1:28; 2:15; 3:23) Mwana wake, Kaini, anakhala mlimi ndipo Abele anakhala mbusa. (Genesis 4:2) Komano, n’chifukwa chiyani ankaŵeta nkhosa pamene anthu panthaŵiyo ankangodya zipatso ndi ndiwo zamasamba mpaka nthaŵi ya Chigumula?—Genesis 1:29; 9:3, 4.
Nkhosa zimafuna kuti munthu azisamalire kuti zikhale moyo. Ntchito ya Abele ikupereka umboni woti anthu anayamba kuweta nyama kuyambira pachiyambi penipeni pa mbiri ya anthu. Baibulo silimanena ngati anthu oyambawo ankamwa mkaka wa nyama kapena ayi, koma ngakhale anthu amene amangodya zamasamba zokha angagwiritse ntchito ubweya wa nkhosa. Ndipo nkhosa zikafa, zikopa zawo zimagwira ntchito zopindulitsa kwambiri. Mwachitsanzo, Yehova poveka Adamu ndi Hava, anawapangira “malaya [aatali] a zikopa.”—Genesis 3:21.
Mulimonse mmene zinalili, zikuoneka kuti sikulakwa kuganiza kuti Kaini ndi Abele anali ogwirizana poyamba. Aliyense ankapanga zinthu zimene zinkathandiza kuti ena m’banjamo apeze zovala ndi chakudya chabwino.
[Chithunzi patsamba 23]
“Ntchito [za Kaini] zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.”