Tifunika Kudziŵa Kuti Mulungu Ndani
KODI simusangalala kuona nyenyezi zili mbuu kumwamba kopanda mtambo? Kodi kafungo ka maluŵa okongola sikasangalatsa? Kodi simukondwa kumva mbalame zikulira ndiponso kaphokoso ka masamba omwe akuuluzika ndi kamphepo kayeziyezi? Ndipo timachitanso chidwi kwambiri ndi anamgumi amphamvu ndiponso zolengedwa zina za m’nyanja zikuluzikulu. Ndiyeno, pali anthu amene amabadwa ndi mphamvu ya chikumbumtima ndi ubongo wocholoŵana kwambiri. Kodi mumati zinthu zonse zodabwitsa za m’dzikozi zinakhalapo motani?
Ena amakhulupirira kuti zinthu zonsezi zinangokhalapo zokha. Koma ngati ndi choncho, kodi n’chifukwa chiyani anthu amakhulupirira Mulungu? Kodi zingatheke bwanji kuti kusakanikirana kwa mankhwala osiyanasiyana kochitika mwangozi kupange zolengedwa zofuna kupembedza?
“Chipembedzo n’chibadwa cha munthu ndipo aliyense kaya ali ndi chuma chotani kapena wophunzira motani amafuna kupembedza.” Imeneyi ndiyo inali mfundo yaikulu pa kafukufuku yemwe Pulofesa Alister Hardy anafotokoza m’buku lake lakuti The Spiritual Nature of Man. Atayeza ubongo posachedwapa, asayansi ya ubongo ananena kuti mwina anthufe “timabadwa” ndi mtima wopembedza. Buku lakuti Is God the Only Reality? limati: “Anthu m’mafuko onse komanso amisinkhu yonse . . . amafunafuna tanthauzo la moyo m’chipembedzo kungochokera pamene munthu analengedwa.”
Taganizirani zimene munthu wina wophunzira kwambiri anafotokoza zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Analemba kuti: “Nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Ndipo vesi loyambirira la Baibulo limati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1.
Komabe, kodi Mulungu ndani? Anthu amatsutsana m’mayankho awo pafunso limeneli. Atafunsidwa kuti Mulungu ndani, mnyamata wina wachijapani, dzina lake Yoshi, anayankha kuti: “Sindikudziŵa bwinobwino. Ndine wachipembedzo cha Chibuda, ndipo ndinalibe nazo ntchito kuti ndidziŵe kuti Mulungu ndani.” Komabe, Yoshi anavomera kuti anthu ambiri amaona Buddha monga mulungu. Nick, wabizinesi amene ali m’zaka za m’ma 60, amakhulupirira Mulungu ndipo amaganiza kuti ndi wamphamvu yonse. Atapemphedwa kufotokoza zomwe amadziŵa ponena za Mulungu, Nick, atakhala chete kwa nthaŵi yaitali, anayankha kuti: “Bwanawe, limenelo ndi funso lovuta kwambiri. Zomwe ndinganene ndi zoti Mulungu alipo basi.”
Anthu ena “amalambira ndi kutumikira zinthu zimene Mulungu analenga m’malo mwa Mlengiyo.” (Aroma 1:25, Today’s English Version) Anthu ambiri amalambira makolo omwe anafa, poganiza kuti Mulungu ali kutali kwambiri moti sangafikirike. M’chipembedzo cha Chihindu, muli milungu yambiri yaimuna ndi yaikazi. M’masiku a atumwi a Yesu Kristu, anthu ankalambira milungu yosiyanasiyana, monga Zeu ndi Herme. (Machitidwe 14:11, 12) Matchalitchi ambiri Achikristu amaphunzitsa kuti Mulungu ndi Utatu, wopangidwa ndi Mulungu Tate, Mulungu Mwana, ndi Mulungu Mzimu Woyera.
Ndithudi, “iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri,” limatero Baibulo. Koma limanenanso kuti: “Koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye.” (1 Akorinto 8:5, 6) Inde, pali Mulungu mmodzi yekha woona. Komano kodi iye ndani? Ndi wotani? M’pofunika kwambiri kuti tidziŵe mayankho a mafunso ameneŵa. Yesu mwiniyo popemphera kwa Mulungu ameneyu ananena mawu aŵa: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) M’pomveka kukhulupirira kuti moyo wabwino wosatha umadalira kudziŵa zoona za Mulungu.
[Chithunzi patsamba 3]
Kodi zinakhalapo motani?
[Mawu a Chithunzi]
Namgumi: Mwachilolezo cha Tourism Queensland
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
COVER: Index Stock Photography © 2002