N’chifukwa Chiyani? ‘Mulungu, N’chifukwa Chiyani Mwalola Zimenezi Kuchitika?’
RICARDO amakumbukirabe atakhala ndi mkazi wake, Maria, m’chipinda chimene odwala amayembekeza dokotala.a Onse aŵiri zinawavuta kulimba mtima kuti aŵerenge zimene dokotala wapeza kumene atamuyeza Maria. Ndiyeno, Ricardo anatsegula enivulupu, ndipo onse anayang’ana mwamsanga zimene dokotalayo analemba. Iwo anaona liwu loti “kansa” ndipo anayamba kulira chifukwa anadziŵa tanthauzo la liwulo.
Ricardo anati: “Dokotalayo anali wokoma mtima kwambiri koma anazindikira kuti vutolo linali lalikulu chifukwa ankangotiuza kuti tidalire Mulungu.”
Asanayambe kulandira thandizo la mankhwala a matendawa, dokotala wa Maria anaona kuti phazi lake lakumanja linkangonjenjemera. Atamuyezanso anapeza kuti kansa inafalikira ku ubongo wake. Mlungu umodzi utangotha anaimikira kaye kupereka mankhwalawa. Maria anakomoka ndipo miyezi iŵiri itatha anamwalira. Ricardo anati: “Ndinasangalala kuti kuvutika kwake kunatha koma ndinam’soŵa kwambiri moti ndinkalakalaka n’tamwalira inenso. Nthaŵi zambiri ndinkalilira Mulungu kuti: ‘N’chifukwa chiyani mwalola zimenezi kuchitika?’”
Mavuto Akagwa, Mafunso Pwirikiti
Mofanana ndi Ricardo, anthu ambiri padziko lapansi akukumanadi ndi mavuto. Ndipo nthaŵi zambiri anthu osalakwa ndi amene amavutika. Taganizani chisoni chachikulu chimene anthu ali nacho chifukwa cha nkhondo zosaletseka. Kapenanso ganizirani mmene anthu ambiri avutikira chifukwa cha kugwiriridwa, kuzunzidwa kwa ana, kumenyedwa m’mabanja, ndiponso zoipa zina zimene anthu achita. Zikuoneka kuti m’mbiri yonse kupanda chilungamo ndi mavuto zimene anthu achitira anzawo zilibe malire. (Mlaliki 4:1-3) Ndiyeno palinso anthu amene akuvutika kwambiri chifukwa cha masoka achilengedwe kapena kuvutika maganizo ndiponso matenda. N’zosadabwitsa kuti ambiri amafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola mavuto ameneŵa?”
Ngakhale anthu amene amakhulupirira zachipembedzo, amavutika kuthana ndi mavuto. Inunso mungafunse chifukwa chimene Mulungu wachikondi ndiponso Wamphamvuyonse walolera anthu kuti azivutika. Kupeza yankho lokwanira ndi loona la funso lovutitsa maganizo limeneli n’kofunika kwambiri kuti tikhale ndi mtendere wa maganizo ndi ubwenzi ndi Mulungu. Baibulo lili ndi yankho lotere. Taonani zimene likunena m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina asinthidwa.
[Zithunzi patsamba 3]
Dokotala ankangotiuza kuti tidalire Mulungu