Mmene Baibulo Limafotokozera Moyenera Umutu
NKHANI ya umutu inayamba pamene anthu oyamba analengedwa. Munthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo anali ndi ufulu wosankha kuchita zimene akufuna. Anali ndi ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. Mwa kumvera kwake Mlengi chifukwa cha chikondi komanso mofuna yekha, iye anali ndi mpata wolemekeza Mulungu. Akanatamanda Mulungu mwanzeru chifukwa cha makhalidwe Ake abwino kwambiri ndipo akanakhala ku mbali ya ufumu Wake.
Koma ufulu wa Adamu unali ndi polekezera; sunali wopanda malire. Iye akanapitiriza kukhala mwachimwemwe kokha ngati akanalemekeza ulamuliro wa Yehova. Zimenezi zinasonyezedwa ndi mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa, umene Adamu analetsedwa kudya zipatso zake. Kudya zipatso za mtengowo kukanakhala kusamvera, kupandukira ulamuliro wa Mulungu.—Genesis 2:9, 16, 17.
N’kofunikanso kwambiri kuti olambira Mulungu masiku ano azizindikira mmene iye amaonera umutu. Lemba la 1 Akorinto 11:3 limafotokoza mmene umutu ulili. Ilo limati: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.”
Malo a Yesu Kristu
Yesu Kristu monga mutu wa mpingo ali ndi ufulu wosankha zochita zokhudza mpingowo ndiponso kuulamulira. (Aefeso 5:23) Koma umutu wakewo umam’chititsanso kuvomereza ntchito yosamalira mpingowo ndiponso kukhala ndi udindo woyankha pa zimene wasankha kuchita.
Yesu Kristu nthaŵi zonse wachita zinthu mogwirizana ndi mfundo ya umutu, kusonyeza kugonjera kwambiri umutu wa Atate wake mwa zolankhula ndi zochita zake. Ngakhale akadzamaliza kulamulira dziko lapansi kwa zaka 1,000, iye adzalemekezanso umutu wa m’chilengedwe chonse wa Yehova mwa kupereka Ufumu kwa Iye, kugonjera “kwa Iye amene anam’gonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”—1 Akorinto 15:24-28; Afilipi 2:5-8.
Malo a Mwamuna
Ngakhale kuti mwamuna amachita umutu m’banja, iye si wodziimira payekha ndipo sikuti safunika kugonjera “mutu.” M’malo mwake, iye ayenera kutsatira malangizo ndi chitsanzo cha mutu wake, Kristu. (1 Yohane 2:6) Ayenera kuchita zimenezi pa nkhani zokhudza ntchito zake zachipembedzo ndiponso pankhani zokhudza iye payekha.
Mwachitsanzo, ngati ali pa banja, pofuna kulemekeza mutu wake, Kristu, mwamunayo ayenera kutsatira langizo lokhala ndi mkazi wake mwachidziŵitso, ‘kum’chitira ulemu monga chotengera chochepa mphamvu.’ Ayeneranso kuchita khama kwambiri kuphunzitsa ana ake moyenera.—1 Petro 3:7; Aefeso 6:4.
Popeza mwamuna anali woyamba kulengedwa, anapatsidwa udindo woyang’anira mkazi. (1 Timoteo 2:12, 13.) Mkazi anapangidwa kuchokera ku nthiti ya mwamuna. (Genesis 2:22, 23) Mkazi analengedwa chifukwa cha mwamuna, osati mwamuna chifukwa cha mkazi. (1 Akorinto 11:9) Motero, m’makonzedwe a Mulungu a banja, mkazi anayenera nthaŵi zonse kugonjera mwamuna wake ndipo sanayenera kulanda udindo wa mwamunayo. (Aefeso 5:22, 23) Ndiponso, mu mpingo wachikristu mkazi sayenera kuphunzitsa amuna ena odzipatulira kapena kuwalamulira.—1 Timoteo 2:12.
Ahebri akale ankalemekeza udindo waukulu wa mwamuna m’banja ndiponso m’fuko. Sara anali wogonjera, ankamutcha Abrahamu kuti “mbuye,” ndipo anamuyamikira kwambiri chifukwa cha kulemekeza kwake umutu wa mwamuna wake.—Genesis 18:12; 1 Petro 3:5, 6.
Malo a Mkazi
M’nthaŵi zakale, panali zochitika zina pamene mkazi ankavala chophimba kumutu posonyeza kugonjera. (Genesis 24:65) Pofotokoza za umutu mumpingo wachikristu, mtumwi Paulo anafotokoza kuti ngati mkazi apemphera kapena anenera mumpingo, kutenga udindo umene Mulungu wapereka kwa mwamuna, ayenera kuvala chophimba kumutu.
Pochita zinthu zimenezi kwa kanthaŵi chifukwa chakuti palibe mwamuna wachikristu wodzipatulira amene akanachita zimenezo, mkaziyo ngakhale atakhala ndi tsitsi lalitali, sayenera kunena kuti tsitsi lake lalitalilo n’lokwanira kusonyeza kugonjera. M’malo mwake, zochita zake ziyenera kusonyeza kugonjera kwake ndi kulemekeza kwake umutu wa mwamuna. Mkazi wachikristu amachita zimenezi mwa kuvala chophimba kumutu monga “[chizindikiro, NW] cha ulamuliro.”—1 Akorinto 11:5-16.
Zimenezi ziyenera kuchitika “chifukwa cha angelo,” amene amaona zimene Akristu amachita ndiponso amene amakhudzidwa nazo, monga otumikira mpingo wachikristu. Mwa kuvala chophimba kumutu kukakhala kofunika kutero pa zifukwa zauzimu, mkazi wachikristu amalemekeza dongosolo la umutu la Mulungu.—Ahebri 1:14.
Dongosolo loyenera la Mulungu limeneli la mumpingo ndiponso m’banja sililepheretsa mkazi kutumikira Mulungu, ndiponso silidodometsa khama lake pogwira ntchito zake komanso kusamalira udindo wake wa m’banja. Limam’patsa ufulu wonse ndiponso wa m’Malemba wotumikira pa malo ake, pamene akusangalatsabe Mulungu mogwirizana ndi mfundo yakuti: “Mulungu anaika ziŵalo zonsezo m’thupi, monga anafuna.”—1 Akorinto 12:18.
Akazi ambiri a makedzana anali ndi mwayi wabwino wotumikira koma akulemekeza umutu wa mwamuna ndipo anasangalala pa moyo wawo. Ena mwa iwo anali Sara, Rebeka, Abigayeli, ndi akazi achikristu monga Priskila ndi Febe.
Phindu la Umutu
Kusonyeza umutu umene munthu wapatsidwa kumapangitsa munthu kukhala ndi ufulu wochita zinthu zina, koma kumam’patsanso ntchito. Mwachitsanzo, mwamuna posonyeza umutu wake, ali ndi ufulu wogamula zochita m’banja ndiponso kukhala woyang’anira. Koma kuwonjezera pamenepo, iye ayenera kuvomereza udindo wosamalira banja lake. Ali ndi udindo waukulu wopezera banja lake zinthu zofunika pa moyo ndiponso kulidyetsa mwauzimu.—1 Timoteo 5:8.
Mwamuna wachikristu ayenera kusonyeza umutu wake mwanzeru, kukonda mkazi wake monga mmene amadzikondera yekha. (Aefeso 5:33) Yesu Kristu amasonyeza umutu wake pa mpingo wachikristu mwa njira imeneyi. (Aefeso 5:28, 29) Tate monga mutu wa ana ake, sayenera kuwakwiyitsa koma ayenera kuwalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.
“Akulu,” monga abusa a nkhosa za Mulungu mumpingo wachikristu sayenera kuchita ufumu pa “nkhosa” za Mulungu koma ayenera kukumbukira kugonjera kwawo Yesu Kristu ndi Yehova Mulungu. (1 Petro 5:1-4) Akristu, omwe ndi otsatira a Yesu Kristu, ayeneranso kulemekeza umutu waukulu wa Yehova, kupemphera kwa iye ndi kumugonjera monga Atate ndi Mulungu Wamphamvuyonse.—Mateyu 6:9; Chivumbulutso 1:8.
Inde, kusonyeza moyenera umutu wa m’Malemba kumapindulitsa anthu. Mtendere ndi mgwirizano umene umakhalapo umalemekezetsa Mlengi wa anthuwo.