Khalani Okonzekeratu Tsiku la Yehova
“Khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.”—MATEYU 24:44.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira za tsiku la Yehova?
LIDZAKHALA tsiku la nkhondo ndi mkwiyo, tsiku la zopsinja ndi masauko, komanso lamdima ndi chipasuko. “Tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa” libwera ndithu pa dongosolo loipali la zinthu, monga momwe Chigumula chinamizira dziko loipa la m’masiku a Nowa. Sililephera, libwera ndithu. Komatu, “yense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” (Yoweli 2:30-32; Amosi 5:18-20) Mulungu adzawononga adani ake ndi kupulumutsa anthu ake. Ndi mzimu wachangu, mneneri Zefaniya analengeza kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.” (Zefaniya 1:14) Komano, ndi liti pamene chiweruzo cha Mulungu chimenechi chidzaperekedwe?
2, 3. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti tikonzekere tsiku la Yehova?
2 Yesu anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Popeza kuti sitidziŵa nthaŵi yake yeniyeni, ndiyetu m’pofunika kulabadira mawu a lemba lathu la chaka cha 2004, akuti: ‘Dikirani . . . Khalani okonzekeratu.’—Mateyu 24:42, 44.
3 Pofuna kusonyeza mmene ntchito yosonkhanitsira anthu okonzeka kumalo otetezeka pamene anthu ena adzasiyidwe idzakhalire yodzidzimutsa, Yesu anati: “Adzakhala aŵiri m’munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: aŵiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.” (Mateyu 24:40, 41) Panthaŵi yofunika kwambiri imeneyo, kodi zinthu zidzatiyendera bwanji? Kodi tidzakhala okonzekera, kapena tsiku limenelo lidzatifikira modzidzimutsa? Zambiri zikudalira pa zimene ifeyo tikuchita tsopano lino. Kuti tikhale okonzekeratu tsiku la Yehova pakufunika kuti tipeŵe mtima winawake womwe wafala masiku ano, tipeŵe khalidwe linalake lauzimu, ndiponso tikane makhalidwe enaake.
Peŵani Kukhala Amphwayi
4. Kodi anthu a m’masiku a Nowa anali ndi mtima wotani?
4 Talingalirani masiku a Nowa. Baibulo limati: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” (Ahebri 11:7) Chingalawa chinali chinthu chachilendo kwambiri komanso choti wina aliyense akanatha kuchiona. Kuwonjezera apo, Nowa anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Anthu sanasinthe zochita zawo chifukwa cha ntchito yomanga ya Nowa ndiponso ulaliki wake. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa.” Anthu omwe Nowa ankawalalikira anali otanganidwa kwambiri ndi ntchito zawo ndiponso zinthu zosangalatsa moti ‘sanadziŵe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, nichipululutsa iwo onse.’—Mateyu 24:38, 39.
5. Kodi anthu a mu Sodomu m’masiku a Loti ankaziona motani zinthu?
5 Zinalinso chimodzimodzi m’masiku a Loti. Malemba amatiuza kuti: “Anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anatuluka m’Sodomu udavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba, ndipo zinawawononga onsewo.” (Luka 17:28, 29) Angelo atachenjeza Loti za chiwonongeko chomwe chinali kubwera, iye anauza akamwini ake zomwe zinali kudzachitika. Koma iwo, “anamuyesa wongoseka.”—Genesis 19:14.
6. Kodi tiyenera kupeŵa mtima wotani?
6 Monga momwe zinalili m’masiku a Nowa ndi Loti, “kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu,” anatero Yesu. (Mateyu 24:39; Luka 17:30) Inde, anthu ambiri masiku ano ngamphwayi. Tifunika kukhala odikira kuti tisatengere mtima umenewu. Palibe cholakwika chilichonse ndi kusangalala pamlingo woyenerera ndi zakudya ndiponso zakumwa zabwino. N’chimodzimodzi ndi ukwati womwe ndi makonzedwe a Mulungu. Koma ngati zimenezi ndiye nkhani yaikulu m’moyo wathu ndipo tikunyalanyaza zinthu zauzimu, kodi ndife okonzekera tsiku loopsa la Yehova?
7. Kodi ndi funso lofunika liti lomwe tiyenera kudzifunsa tisanachite chilichonse, ndipo n’chifukwa chiyani?
7 Mtumwi Paulo anati: “Yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe.” (1 Akorinto 7:29-31) Tangotsala ndi nthaŵi yochepa yogwirira ntchito yathu yolalikira za Ufumu yomwe Mulungu watipatsa. (Mateyu 24:14) Paulo anachenjeza ngakhale anthu okwatira kuti asaike mtima wawo wonse pa mkazi kapena mwamuna wawo moti n’kumaona zinthu za Ufumu ngati zosafunika kwambiri m’moyo wawo. N’zoonekeratu kuti Paulo sanali kutilimbikitsa kukhala amphwayi m’pang’ono pomwe. Yesu anati: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo cha [Mulungu].” (Mateyu 6:33) Pamene tikusankha chochita kapena tisanachite chinthu chilichonse, funso lofunika kwambiri kuti tizidzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi zimenezi zikhudza motani kuika kwanga zinthu za Ufumu poyamba m’moyo wanga?’
8. Ngati tatanganidwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku za m’moyo, kodi tiyenera kuchitanji?
8 Bwanji ngati tazindikira kuti ndife otanganidwa kale ndi zinthu zamasiku onse pamoyo moti tikulephera kuchita zinthu zauzimu? Kodi pali kusiyana kochepa pamoyo wathu ndi wa anthu omwe tayandikana nawo omwe sadziŵa zinthu zolondola za m’Malemba ndiponso salalikira za Ufumu? Ngati ndi choncho, ndiye kuti tifunika kuipempherera nkhani imeneyi. Yehova angatithandize kukhala ndi mtima woyenerera. (Aroma 15:5; Afilipi 3:15) Iye angatithandize kuti tiike zinthu za Ufumu pamalo oyamba, kuti tichite zinthu zabwino, ndiponso kuti tikwaniritse zomwe tiyenera kum’chitira.—Aroma 12:2; 2 Akorinto 13:7.
Peŵani Kugona Mwauzimu
9. Malinga ndi Chivumbulutso 16:14-16, n’chifukwa chiyani kupeŵa kugona mwauzimu kuli kofunika kwambiri?
9 Ulosi umene umanena za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” yomwe ikubwera pa Armagedo umatichenjeza kuti ena angathe kugona. Ambuye Yesu Kristu anati: “Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.” (Chivumbulutso 16:14-16) Zovala zotchulidwa pano ndi zinthu zimene zimatizindikiritsa kuti ndife Mkristu wa Mboni za Yehova. Zina mwa zinthu zimenezi ndizo ntchito yathu monga olengeza Ufumu ndiponso khalidwe lathu lachikristu. Ngati tikufooka, zimene zili ngati kugona tulo, tingavulidwe chizindikiro chathu chachikristu. Izi n’zochititsa manyazi komanso zoopsa kwambiri. Tiyenera kupeŵa kugona kapena kuchita ulesi mwauzimu. Kodi tingazipeŵe motani zimenezi?
10. N’chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kumatithandiza kukhala maso mwauzimu?
10 Baibulo limatsindika mobwerezabwereza kufunika kokhala maso ndiponso ogalamuka. Mwachitsanzo, Mauthenga Abwino amatikumbutsa kuti: “Dikirani.” (Mateyu 24:42; 25:13; Marko 13:35, 37); “khalani inunso okonzekeratu” (Mateyu 24:44); “yang’anirani, dikirani” (Marko 13:33); “khalani okonzeka” (Luka 12:40). Atafotokoza kuti tsiku la Yehova lidzafika modzidzimutsa padzikoli, mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:6) M’buku lomaliza la Baibulo, Kristu Yesu wokwezeka anatsindika kufulumira kwa kudza kwake, anati: “Ndidza msanga.” (Chivumbulutso 3:11; 22:7, 12, 20) Aneneri ambiri achihebri nawonso anafotokoza ndi kuchenjeza za tsiku lalikulu la chiweruzo cha Yehova. (Yesaya 2:12, 17; Yeremiya 30:7; Yoweli 2:11; Zefaniya 3:8) Kuŵerenga Mawu a Mulungu, Baibulo, tsiku ndi tsiku ndi kusinkhasinkha zomwe taŵerenga kudzatithandiza kwambiri kukhala maso mwauzimu.
11. N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo patokha kuli kofunika kuti tikhale maso mwauzimu?
11 Inde, kuphunzira kwathu mwakhama Malemba pogwiritsa ntchito mabuku ofotokoza Baibulo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kumatithandiza kwambiri kuti tikhale ogalamuka mwauzimu. (Mateyu 24:45-47) Koma kuti kuphunzira kwathuko kukhale kopindulitsa, kufunika kumapita patsogolo komanso kufunika kukhala kwanthaŵi zonse. (Ahebri 5:14–6:3) Tifunika kudya chakudya chotafuna nthaŵi zonse. Masiku ano kungakhale kovuta kupeza nthaŵi yochita phunziro latokha. (Aefeso 5:15, 16) Komabe, kuŵerenga Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Malemba panthaŵi yokhayo yomwe tafuna kutero sikokwanira. Kuphunzira nthaŵi zonse patokha n’kofunika kuti ‘tikhale olama m’chikhulupiriro’ ndi kukhala maso nthaŵi zonse.—Tito 1:13.
12. Kodi misonkhano yachikristu, yadera ndi yachigawo imatithandiza motani kulimbana ndi tulo tauzimu?
12 Misonkhano yachikristu, yadera ndiponso yachigawo imatithandizanso kulimbana ndi tulo tauzimu. Motani? Kudzera m’malangizo omwe timalandira. Pamisonkhano imeneyi, kodi sitikumbutsidwa nthaŵi zonse za kuyandikira kwa tsiku la Yehova? Komanso misonkhano yachikristu ya mlungu ndi mlungu imatipatsa mwayi ‘wofulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ Kufulumizana kumeneku kumathandiza munthu kukhala maso mwauzimu. M’posadabwitsa kuti tikulamulidwa kusonkhana nthaŵi zonse ‘monga momwe tiona tsiku lilikuyandika.’—Ahebri 10:24, 25.
13. Kodi utumiki wachikristu umatithandiza motani kukhala maso mwauzimu?
13 Timathandizidwanso kukhala maso pamene tichita nawo utumiki wachikristu ndi mtima wonse. Kodi pali njira ina yabwino yodziŵira bwino zizindikiro za nthaŵi ndi tanthauzo lake kuposa kufotokozera ena zizindikirozo? Ndipo tikamaona anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo akupita patsogolo, n’kuyamba kutsatira zomwe akuphunzirazo, changu chathu chimawonjezeka. Mtumwi Petro anati: “Dzimangireni m’chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga [“achangu,” NW].” (1 Petro 1:13) Kukhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse” ndi njira yabwino yothetsera ulesi wauzimu.—1 Akorinto 15:58.
Kanani Makhalidwe Owononga Mwauzimu
14. Malinga ndi kufotokoza kwa pa Luka 21:34-36, kodi Yesu anachenjeza za makhalidwe otani?
14 Mu ulosi wake waukulu wonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake, Yesu anaperekanso chenjezo lina. Anati: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) Yesu anafotokoza ndendende moyo umene anthu ambiri ali nawo: kudya kwambiri, kuledzera, ndiponso moyo womwe umadzetsa nkhaŵa.
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa kudya kwambiri ndiponso kumwa kwambiri?
15 Madyaidya ndiponso kuledzera n’kosemphana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo tifunika kuzikana. Baibulo limati: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka.” (Miyambo 23:20) Komabe, kuti kudya ndi kumwa kukhale koopsa sikuchita kulira kufika pamenepo. Kudya ndi kumwa kungagonetse munthu ndiponso kum’panga kukhala waulesi, munthuyo asanafike pokhala wamadyaidya kapena woledzera. Mwambi wa m’Baibulo umati: “Moyo wa wolesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.” (Miyambo 13:4) Munthu wotero angafune kuchita chifuno cha Mulungu, koma chifukwa chosasamala zofuna zakezo sizingakwaniritsidwe.
16. Kodi tingapeŵe motani kulefulidwa ndi nkhaŵa zosamalira banja lathu?
16 Kodi nkhaŵa za moyo zomwe Yesu anachenjeza ndi chiyani? Zikuphatikizapo nkhaŵa zomwe munthu amakhala nazo, kupezera banja zosoŵa, ndi zina zotero. Kulola kuti zimenezi zitilefule kungakhale kupanda nzeru kwambiri. Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu ndi kudera nkhaŵa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?” Anachenjeza anthu omwe ankam’vetsera kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo.” Kuika zinthu za Ufumu poyamba m’moyo wathu ndiponso kukhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzatipatsa zomwe tikuzisoŵa kudzatithandiza kuchepetsa nkhaŵa komanso kuti tikhale maso.—Mateyu 6:25-34.
17. Kodi kufunafuna chuma kungadzetse nkhaŵa motani?
17 Nkhaŵa zingadzenso chifukwa chofunafuna chuma. Mwachitsanzo, ena amadzivutitsa chifukwa chokhala moyo womwe sangaukwanitse. Ena akopeka ndi njira zolemeretsa munthu msanga ndiponso bizinesi zoika moyo pachiswe. Pamene ena, akodwa chifukwa choona maphunziro monga njira yoti zinthu zidzawayendere bwino pazachuma. Ndi zoona kuti maphunziro enaake angathandize munthu kuti apeze ntchito. Koma choonadi n’chakuti poyesayesa kuphunzira kwambiri komwe kumafunika nthaŵi yambiri, ena adzivulaza mwauzimu. N’zoopsa kwambiri ngati zimenezi zingatichitikire pamene tsiku la Yehova likuyandikira. Baibulo limachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.”—1 Timoteo 6:9.
18. Kuti tipeŵe kukodwa m’moyo wokonda chuma, kodi tiyenera kukhala ndi luso lotani?
18 Kuti tisakodwe m’moyo wokonda chuma tifunika kukhala ndi luso lozindikira chabwino ndi choipa pamene tikusankha zoti tichite. Munthu amapeza luso limeneli mwa kudya nthaŵi zonse ‘chakudya chotafuna cha anthu aakulu misinkhu’ ndiponso mwa ‘kuzoloŵeretsa [mphamvu] zathu za kuzindikira’ mwa kuzigwiritsa ntchito. (Ahebri 5:13, 14) ‘Kutsimikizira zinthu zofunika’ kudzatithandizanso kupeŵa kusankha zinthu zolakwika.—Afilipi 1:10, NW.
19. Tikazindikira kuti tili ndi nthaŵi yochepa kwambiri yochitira zinthu zauzimu, kodi tiyenera kuchitanji?
19 Moyo wokonda chuma ungathe kutipangitsa khungu, n’kutisiyira nthaŵi yochepa yochitira zinthu zauzimu, mwinanso osatisiyira n’komwe nthaŵiyo. Kodi tingadzipende motani ndi kupeŵa kukodwa ndi msampha wa moyo wotero? Tifunika kupemphera ndiyeno n’kulingalira mmene moyo wathu ungakhalire wosalira zambiri. Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inati: “Tulo ta munthu wogwira ntchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.” (Mlaliki 5:12) Kodi kusamalira katundu wosafunika kwenikweni kumakutayitsani nthaŵi ndiponso mphamvu? Pamene tili ndi katundu wambiri, pamakhalanso ntchito yambiri yokonzanso, kulipirira inshuwalansi, ndiponso kuteteza katunduyo. Kodi tingapindule mwa kusintha moyo wathu kuti ukhale wosalira zambiri mwa kupungula katundu wathu?
Yesetsani Kukhala Wokonzekeratu
20, 21. (a) Ponena za tsiku la Yehova kodi mtumwi Petro akutitsimikizira zotani? (b) Kodi ndi mayendedwe ndi ntchito zotani zomwe tiyenera kupitiriza kuchita pamene tikusonyeza kuti ndife okonzekera tsiku la Yehova?
20 Nthaŵi ya dziko la m’masiku a Nowa inafika pakutha, ndipo nthaŵi ya dongosolo lino la zinthu ithanso. Mtumwi Petro akutitsimikizira kuti: “Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.” Miyamba yophiphiritsa, yomwe ndi maboma oipa kapenanso dziko lapansi lophiphiritsa lomwe ndi anthu otalikirana ndi Mulungu, sizidzapulumuka kutentha kwa mkwiyo woyaka wa Mulungu. Posonyeza mmene tingakhalire okonzekera tsiku limenelo, Petro anati: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.”—2 Petro 3:10-12.
21 Kufika kwathu pamisonkhano yachikristu ndiponso kulalikira nawo uthenga wabwino nthaŵi zonse ndi mbali ya mayendedwe ndiponso ntchito zachipembedzo. Tiyeni tichite zimenezi titadzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu pamene tikudikira tsiku lalikulu la Yehova. Tiyeni ‘tichite changu kuti tidzapezedwe ndi [Mulungu] mumtendere, opanda banga ndi opanga chirema.’—2 Petro 3:14.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekeratu tsiku la Yehova?
• Ngati tikutanganidwa ndi zinthu zamasiku onse za pamoyo, kodi tiyenera kuchitanji?
• N’chiyani chingatithandize kupeŵa kugona mwauzimu?
• Kodi tiyenera kukana makhalidwe ati owononga mwauzimu, ndipo tingawakane motani?
[Zithunzi pamasamba 20, 21]
Anthu a m’masiku a Nowa sanadziŵe za chiweruzo chomwe chinali kubwera—kodi inu mukudziŵa?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi mungasinthe moyo wanu n’kukhala wosalira zambiri kuti mukhale ndi nthaŵi yambiri yochitira zinthu zauzimu?