Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Chigumula chitatha, Nowa anatulutsa njiwa mu chingalawa imene inabwera ndi “tsamba la azitona.” Kodi njiwayo inakatenga kuti tsambalo?
Baibulo limatiuza kuti “madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse.” (Genesis 7:19) Madzi a Chigumula akuphwera, Nowa anatulutsa njiwa m’chingalawa maulendo atatu, ndipo anali kuchita zimenezi pakatha mlungu umodzi. Ulendo wachiŵiri, njiwa inabwera ‘m’kamwa mwake muli tsamba la azitona lothyoledwa kumene: ndipo anadziŵa Nowa kuti madzi anali kuphwa pa dziko lapansi.’—Genesis 8:8-11.
N’zoona kuti pakalipano palibe njira yodziŵira kuti malo enaake padziko lapansi anakhala ndi madzi kwa nthaŵi yaitali bwanji, chifukwa n’zodziŵikiratu kuti Chigumula chinasintha mmene dziko linkaonekera chigumulacho chisanachitike. Ngakhale zili choncho, n’zachidziŵikire kuti m’madera ambiri madzi anakhala kwa nthaŵi yaitali moti mitengo yambiri n’kufa. Komabe, mitengo ina mwachionekere inakhalabe ndi moyo, zimene zinapangitsa kuti iphukire pamene madzi anaphwera.
Ponena za mtengo wa azitona, buku lotanthauzira mawu la The New Bible Dictionary limati: “Ngati wadulidwa, muzu wake umatulutsa mphukira zatsopano, moti ukhoza kuphukira mitengo yatsopano isanu. Nthaŵi zambiri mitengo ya azitona imene yatsala pang’ono kufa imaphukiranso mwanjira imeneyi.” Zili “ngati kuti mtengowo suferapo,” imatero The New Schaff-Herzog Encyclopedia of Religious Knowledge. Palibe munthu masiku ano akudziŵa zinthu monga kuti madzi a Chigumula anali ndi mchere wochuluka bwanji ndiponso anali otentha kapena ozizira bwanji. Choncho, sitingadziŵe mmene anakhudzira mitengo ya azitona ndiponso zomera zina.
Komabe, mitengo ya azitona yam’thengo sikhala kumalo kozizira, monga kumakhalira kumene kuli mapiri ataliatali. Nthaŵi zambiri imamera m’madera okwera osaposa mamita 1,000, kumene kaŵirikaŵiri sikuzizira kuposa 10 digiri seshasi. Buku la The Flood Reconsidered, limati: “Chotero Nowa ataona tsamba lothyoledwa kumenelo anadziŵa kuti madzi anali kuphwera kumadera a kuchigwa.” Nowa atatulutsa njiwa ija patatha mlungu wina, sinabwerenso, kusonyeza kuti kunali zomera zambiri ndiponso malo oti njiwayo n’kukhala.—Genesis 8:12.