N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Zimapitirizabe Kukuyenderani?
PADZIKO lonse, Mboni za Yehova n’zodziŵika kuti sizileka kuyendera anthu mu utumiki wawo wa kunyumba ndi nyumba. Anthu ena amadabwa chifukwa chake Mboni zimapitirizabe kuwayendera, makamaka ngati paulendo woyamba analibe chidwi kwenikweni ndi uthenga wa Mbonizo. Makalata aŵiri ochokera ku Russia akuthandiza kufotokoza chifukwa chake zimapitiriza kukuyenderani.
Masha, mtsikana wa zaka 19 wa ku Khabarovsk, anati: “Kunena zoona, kale ndinkayesetsadi kwambiri kupeŵa Mboni za Yehova.” Koma ataŵerenga magazini angapo osindikizidwa ndi Mboni, anasintha maganizo. “Zonse zimene ndinaŵerenga m’magaziniwo zinali zosangalatsa ndi zotsegula m’maso,” analemba choncho Masha, “koma chofunika kwambiri n’chakuti, zimene zili m’magaziniŵa zimathandiza munthu kuliona dziko mosiyana ndi mmene anali kulionera poyamba. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kumvetsa cholinga cha moyo.”
Svetlana, wa mu mzinda wa Ussuriysk, pafupifupi makilomita 80 kumpoto kwa Vladivostok, analemba kuti: “Ndangoyamba kumene kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Magazini ameneŵa ndi ofunika kwambiri masiku athu ano. Nkhani zonse za m’magaziniŵa zimandisangalatsa. Zimakhala zosangalatsa, zophunzitsa, ndiponso zotsegula m’maso kwambiri. Zikomo anthu inu! Zikomo kwambiri chifukwa chopezeka m’dzikoli ndiponso chifukwa chogwira ntchito yothandiza ndi yofunika imeneyi.”
Mboni za Yehova padziko lonse zimaona funso lochititsa chidwi la mtumwi Paulo kukhala lofunika kwambiri. Iye anafunsa kuti: “Ndipo [anthu] adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:14) Bwanji nthaŵi ina osadzapatula mphindi zingapo kuti mumvetsere Mboni zikadzakuyenderani? Inunso mungasangalale ndi uthenga wolimbikitsa wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo.