Chikristu Choona Chikukula
UTUMIKI wa Yesu Kristu unakhudza kwambiri anthu a m’zaka 100 zoyambirira. Uthenga wake unali wopatsa mphamvu, wotsegula anthu m’maso, ndiponso wolimbikitsa m’njira yodabwitsa. Anthu ambiri amene anamva iye akulankhula anakhudzidwa mtima kwambiri ndi mawu ake.—Mateyu 7:28, 29.
Mosaopa aliyense Yesu anakana kuloŵetsedwa m’magulu opondereza achipembedzo ndiponso andale a m’nthaŵi yake koma anthu wamba anali omasuka kulankhula naye. (Mateyu 11:25-30) Ananena poyera za kufalikira kwa mphamvu ya mizimu yoipa padziko lapansi ndipo anasonyeza mphamvu imene Mulungu anam’patsa yolamulira mizimuyo. (Mateyu 4:2-11, 24; Yohane 14:30) Yesu anafotokoza mwaluso kugwirizana kwakukulu pakati pa mavuto ndi uchimo, ndipo anatchula mwachikondi kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene ungabweretse mpumulo wosatha. (Marko 2:1-12; Luka 11:2, 17-23) Iye anachotseratu chophimba cha mdima chimene chinaphimba umunthu weniweni wa Atate ake kwanthaŵi yaitali, zimene zinachititsa kuti dzina la Mulungu lidziŵike kwa onse ofuna kukhala Naye paubwenzi.—Yohane 17:6, 26.
Choncho, sizodabwitsa kuti ngakhale ophunzira a Yesu anazunzidwa kwambiri ndi achipembedzo ndiponso andale, iwo analalikira mofulumira uthenga wake wamphamvu. M’zaka pafupifupi 30 zokha, mipingo yachikristu yachangu inakhazikitsidwa ku Africa, Asia, ndi Ulaya. (Akolose 1:23) Choonadi chosavuta chimene Yesu anaphunzitsa chinaŵalitsa mitima ya anthu odzichepetsa, anthu oongoka mtima mu ufumu wonse wa Roma.—Aefeso 1:17, 18.
Koma kodi zikanatheka bwanji kuti ophunzira atsopanoŵa amene anali opeza mosiyanasiyana, chikhalidwe chosiyanasiyana, zinenero zosiyanasiyana, ndiponso amene anali m’zipembedzo zosiyanasiyana akhale pamodzi mu “chikhulupiriro chimodzi” chogwirizanadi, monga momwe mtumwi Paulo ananenera? (Aefeso 4:5) Kodi n’chiyani chikanawathandiza kupitiriza ‘kunena chimodzimodzi’ kuti asagaŵikane? (1 Akorinto 1:10) Poona kusagwirizana kwakukulu kumene kulipo pakati pa amene amati ndi Akristu masiku ano, tingachite bwino kuona zimene Yesu mwiniyo anaphunzitsa.
Maziko a Umodzi Wachikristu
Pamene anali kuimbidwa mlandu ndi Pontiyo Pilato, Yesu ananena maziko a umodzi wachikristu. Iye anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mawu anga.” (Yohane 18:37) Choncho, kulandira zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso mbali ina yonse ya Mawu ouziridwa ndi Mulungu, Baibulo, kuli ndi mphamvu yogwirizanitsa ophunzira oona a Kristu.—1 Akorinto 4:6; 2 Timoteo 3:16, 17.
N’zoona kuti nthaŵi zina ophunzira a Yesu akanakhala ndi mafunso ochokadi pansi pa mtima kapena kusiyana maganizo pazifukwa zomveka. Kodi n’chiyani chikanawathandiza? Yesu anafotokoza kuti: “Atadza Iyeyo, mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m’choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.” (Yohane 16:12, 13) Chotero, mzimu woyera wa Mulungu ukanathandiza ophunzira oona a Yesu kumvetsa choonadi chimene Mulungu anali kuvumbula pang’onopang’ono. Ndiponso, mzimu umenewo ukanatulutsa chipatso monga, chikondi, chimwemwe, ndi mtendere, zimene kenako zikanapangitsa kuti akhale ogwirizana pakati pawo.—Machitidwe 15:28; Agalatiya 5:22, 23.
Yesu sanalole kuti pakhale magaŵano kapena timagulumagulu pakati pa ophunzira ake, komanso sanawalole kutanthauzira choonadi cha m’Baibulo kuti chigwirizane ndi miyambo yachikhalidwe kapena yachipembedzo ya anthu amene angakumane nawo. M’malomwake, pausiku womaliza kukhala nawo, anapemphera ndi mtima wonse kuti: “Sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mawu awo; kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti Inu munandituma Ine.” (Yohane 17:20, 21) Choncho, umodzi weniweni, mu mzimu ndi m’choonadi unali chizindikiro cha ophunzira a Kristu kuyambira pachiyambi chachikristu mpaka masiku athu ano. (Yohane 4:23, 24) Komabe, masiku ano matchalitchi, si ogwirizana, koma ogaŵanika. Chifukwa chiyani zili choncho?
Chifukwa Chake Matchalitchi Ndi Ogaŵanika
Chifukwa chenicheni chimene chapangitsa kuti zikhulupiriro ndi zochita za amene amati ndi Akristu masiku ano zikhale zosiyana kwambiri n’chakuti sanamvere zimene Yesu anaphunzitsa. Wolemba wina anati: “Monga m’mbuyomu, Akristu atsopano masiku ano amavomereza m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi zimene iwo akufuna—ndipo amanyalanyaza zimene sizikugwirizana ndi miyambo yawo ya chipembedzo cha makolo awo.” Zimenezi sizikusiyana m’pang’ono pomwe ndi zimene Yesu ndi atumwi ake ananena kuti zidzachitika.
Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauziridwa kulembera Timoteo yemwe anali wotsogolera mnzake kuti: “Idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.” Kodi Akristu onse akanasocheretsedwa? Ayi. Paulo anapitiriza kuti: “Koma iwe, khala maso m’zonse, imva zoŵaŵa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.” (2 Timoteo 4:3-5; Luka 21:8; Machitidwe 20:29, 30; 2 Petro 2:1-3) Timoteo ndi Akristu ena okhulupirika anatsatira uphungu wouziridwa umenewu.
Akristu Oona Ndi Ogwirizanabe
Monga Timoteo, Akristu oona masiku ano ali maso mwa kukana maganizo a anthu ndiponso mwa kulandira ziphunzitso za m’Malemba zokhazokha. (Akolose 2:8; 1 Yohane 4:1) Potsanzira Akristu a m’zaka 100 zoyambirira, Mboni za Yehova zikuchita utumiki wawo m’mayiko oposa 230, kuwapatsa anthu kulikonse uthenga woyambirira wa Yesu womwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Lingalirani njira zofunika zinayi zimene mogwirizana amatsanzirira Yesu ndi kuchita Chikristu choona mosasamala kanthu za kumene akukhala.
Zikhulupiriro zawo n’zochokera m’Mawu a Mulungu. (Yohane 17:17) Mbusa wa mpingo wina ku Belgium analemba za iwo kuti: “Chimodzi chimene tingaphunzire kwa iwo [Mboni za Yehova] ndi kufunitsitsa kwawo kumvera Mawu a Mulungu ndiponso kulimba mtima kwawo polalikira mawuwo.”
Amayembekezera kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo udzathetse mavuto padziko lonse. (Luka 8:1) Ku Barranquilla, m’dziko la Colombia, Mboni ina inalankhula ndi Antonio, wochirikiza kwambiri gulu linalake landale. Mboniyo sinachirikize nawo gulu la ndale limene iye anali kuchirikiza, kapena kuchirikiza mfundo zina zandale. M’malomwake, anapempha Antonio ndi azichemwali ake kuti aziphunzira nawo Baibulo kwaulere. Posakhalitsa Antonio anazindikira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzathandizedi anthu osauka a ku Colombia ndiponso apadziko lonse.
Amalemekeza dzina la Mulungu. (Mateyu 6:9) Mboni za Yehova zitakumana koyamba ndi Maria, Mkatolika wina wodzipereka wa ku Australia, iye analola kuti Mbonizo zimuonetse dzina la Mulungu m’Baibulo. Kodi anachitanji atamuonetsa? “Nditaona dzina la Mulungu m’Baibulo kwanthaŵi yoyamba, ndinalira. Ndinalimbikitsidwa kwambiri pozindikira kuti ndadziŵadi dzina lenileni la Mulungu ndipo nditha kuligwiritsa ntchito.” Maria anapitiriza kuphunzira Baibulo, ndipo kwanthaŵi yoyamba pamoyo wake, anam’dziŵa Yehova monga munthu ndipo anapanga naye ubwenzi wosatha.
Ndi ogwirizana chifukwa cha chikondi. (Yohane 13:34, 35) Nkhani ya mkonzi mu nyuzipepala ya The Ladysmith-Chemainus Chronicle, ku Canada, inanena kuti: “Kaya zikhulupiriro zanu zachipembedzo n’zotani, kaya mulibe, muyenera kuthokoza Mboni za Yehova 4,500 zimene zinagwira ntchito usiku ndi usana mlungu umodzi ndi theka wapitawo kumanga Nyumba ya Msonkhano ya masikweya mita 2,300 ku Cassidy . . . Kuchita zimenezi mosangalala popanda kukangana, magaŵano kapena kufuna ulemerero ndi chizindikiro cha Chikristu choona.”
Choncho, tapendani umboniwu. Ngakhale kuti anthu amaphunziro apamwamba azaumulungu ndi amishonale a m’Matchalitchi Achikristu, komanso amene amapita kutchalitchi akulimbana ndi mkangano umene ungabuke m’tsogolomu m’matchalitchi awo, Chikristu choona chikukula padziko lonse. Ndithudi, Akristu oona akuchita utumiki umene anapatsidwa wolalikira ndi kuphunzitsa Mawu a Mulungu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Ngati muli pagulu la anthu amene “akuusa moyo ndi kulira” chifukwa cha zinthu zonyansa zimene zikuchitika tsopano ndipo mukuvutika ndi kusagwirizana kumene kulipo pakati pa zipembedzo za Matchalitchi Achikristu, tikukupemphani kuti mugwirizane ndi Mboni za Yehova polambira mwachikristu ndiponso mogwirizana Mulungu woona yekha, Yehova.—Ezekieli 9:4; Yesaya 2:2-4.