Kanizani Mzimu wa Dziko Lomwe Likusinthali
“Sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu.”—1 Akorinto 2:12.
1. Kodi Hava ananyengedwa m’njira ziti?
“NJOKA inandinyenga ine.” (Genesis 3:13) Mkazi woyamba, Hava, ananena mawu ochepa ameneŵa poyesetsa kufotokoza chifukwa chake anapandukira Yehova Mulungu. Zimene ananenazo zinali zoona, ngakhale kuti chimenecho sichinali chifukwa choti sakanachitira mwina koma kulakwa. Patapita nthaŵi, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: ‘[Hava] ananyengedwa.’ (1 Timoteo 2:14) Iye ananyengedwa n’kukhulupirira kuti kusamvera, mwa kudya chipatso chimene analetsedwa, kudzamuthandiza chifukwa kudzam’chititsa kufanana ndi Mulungu. Ananyengedwanso osadziŵa kuti amene anamusocheretsayo anali ndani kwenikweni. Sanadziŵe kuti njokayo inali cholankhulira chabe cha Satana Mdyerekezi.—Genesis 3:1-6.
2. (a) Kodi Satana amanyenga bwanji anthu masiku ano? (b) Kodi “mzimu wa dziko lapansi” n’chiyani, ndipo tsopano tikambirana mafunso ati?
2 Kuyambira m’nthaŵi ya Adamu ndi Hava, Satana wapitiriza kunyenga anthu. Ndipotu, iye ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9) Njira zake zonyengera anthu sizinasinthe. Ngakhale kuti masiku ano sagwiritsa ntchito njoka yeniyeni, amapitirizabe kudzibisa. Kudzera m’zinthu zosangulutsa, ma TV, mawailesi, manyuzipepala ndi njira zina, Satana akunyenga anthu powachititsa kukhulupirira kuti safunikira ndiponso sangapindule ndi malangizo amene Mulungu amatipatsa chifukwa choti amatikonda. Ntchito ya Mdyerekezi yonyenga anthu yachititsa anthu kulikonse kukhala ndi mtima wopandukira malamulo ndi mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Baibulo limatcha zimenezi kuti ndi “mzimu wa dziko lapansi.” (1 Akorinto 2:12) Mzimu umenewu umakhudza mwamphamvu zikhulupiriro, maganizo, ndi makhalidwe a anthu amene sadziŵa Mulungu. Kodi mzimu umenewu umaonekera motani, ndipo tingatani kuti tisalole kuti utiloŵerere? Tiyeni tione.
Makhalidwe Abwino Akuloŵa Pansi
3. N’chifukwa chiyani “mzimu wa dziko lapansi” ukuonekera kwambiri masiku ano?
3 Masiku ano, “mzimu wa dziko lapansi” ukuonekera kwambiri. (2 Timoteo 3:1-5) Mosakayika, mwaonapo kuti makhalidwe abwino akuloŵa pansi. Malemba amafotokoza chifukwa chake zinthu zili choncho. Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa m’chaka cha 1914, kumwamba kunaulika nkhondo. Satana ndi ziŵanda zake anagonjetsedwa ndipo anaponyedwa ku dziko lapansi. Satana wagundika kwambiri pa ntchito yake yonyenga anthu padziko lonse popeza wakwiya kwambiri. (Chivumbulutso 12:1-9, 12, 17) Iye akuyesetsa m’njira iliyonse imene angathe kuti ‘anyenge, ngati n’kotheka, osankhidwa omwe.’ (Mateyu 24:24) Monga anthu a Mulungu, ife ndi amene watifiirira maso kwambiri. Amayesetsa kuwononga moyo wathu wauzimu kuti Yehova asatiyanjenso ndiponso kuti tisadzapeze moyo wosatha.
4. Kodi atumiki a Yehova amaona bwanji Baibulo, ndipo dziko lapansi limaliona bwanji?
4 Satana amayesetsa kuchititsa anthu kuti asamakhulupirire Baibulo, buku lamtengo wapatali limene limatiphunzitsa za Mlengi wathu wachikondi. Atumiki a Yehova amakonda Baibulo ndipo amaliona kukhala lamtengo wapatali. Timadziŵa kuti ndi Mawu a Mulungu ouziridwa osati mawu a anthu. (1 Atesalonika 2:13; 2 Timoteo 3:16) Koma dziko la Satana limafuna kuti tisamalione motero Baibulo. Mwachitsanzo, mawu oyamba m’buku lina limene limatsutsa Baibulo, amati: “Baibulo si ‘lopatulika,’ ndiponso si ‘mawu a Mulungu.’ Silinalembedwe ndi anthu oyera mtima ouziridwa ndi Mulungu, m’malo mwake linalembedwa ndi ansembe amene ankafuna kulamulira.” Amene angakhulupirire mawu ameneŵa sizingakhale zovuta kuti akhale ndi maganizo olakwika akuti ali ndi ufulu wolambira Mulungu mmene iwowo angafunire, kapenanso osamulambira n’komwe.—Miyambo 14:12.
5. (a) Kodi wolemba mabuku wina anati chiyani pankhani ya zipembedzo zimene zimagwiritsa ntchito Baibulo? (b) Kodi maganizo amene anthu ambiri ali nawo m’dzikoli akusiyana bwanji ndi zimene Baibulo limanena? (Phatikizani mfundo za m’bokosi la patsamba lotsatira.)
5 Kutsutsa Baibulo mwachindunji kapena kudzera m’njira zina, pamodzinso ndi chinyengo chimene a zipembedzo akuchita omwe amati amakhalira kumbuyo Baibulo, zachititsa kuti anthu ambiri azidana ndi zipembedzo, kuphatikizapo zipembedzo zimene zimagwiritsa ntchito Baibulo. Nkhani za pa TV, m’manyuzipepala kapena pawailesi pamodzinso ndi anthu ophunzira kwambiri zikutsutsa zipembedzo. Wolemba mabuku wina anati: “Anthu ambiri sakusangalala ndi Chiyuda ndiponso Chikristu. Akati aziganizire bwinopo zipembedzozi, amaziona ngati ndi zinthu zabwino zakale; koma ku mbali yaikulu amaziona monga zinthu zakale zotha ntchito zimene zimabwezera m’mbuyo nzeru za anthu ndi ntchito za sayansi. M’zaka zaposachedwapa kuipidwa ndi zipembedzozi kwawonjezeka n’kufika pozinyoza kapena kusonyeza kudana nazo poyera.” Kudana nazoku nthaŵi zambiri amayambitsa ndi anthu amene amakana zoti kuli Mulungu ndiponso amene amakhala “opanda pake m’maganizo awo.”—Aroma 1:20-22.
6. Kodi dziko limaona bwanji kugonana kumene Mulungu amaletsa?
6 Motero, n’zosadabwitsa kuti anthu akupatuka kwambiri pa mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo limafotokoza kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi chinthu “chamanyazi.” (Aroma 1:26, 27) Limafotokozanso kuti amene amachita dama ndi chigololo sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9) Komabe, m’mayiko ambiri kugonana kotereku amakuvomereza ndiponso amakutchukitsa m’mabuku, m’magazini, m’nyimbo, m’mafilimu, ndi m’mapulogalamu a pa TV. Anthu amene amatsutsa makhalidwe oterowo amawaona ngati anthu osalolera maganizo a ena, okonda kudzudzula anzawo, ndiponso otsalira. M’malo moona kuti mfundo za Mulungu zinaperekedwa chifukwa chotikonda, dziko limaona zimenezo kukhala zopinga ufulu wa munthu ndiponso ufulu wochita zimene zingamusangalatse.—Miyambo 17:15; Yuda 4.
7. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
7 Popeza tili m’dziko limene likupitirizabe kutsutsana kwambiri ndi Mulungu, ndi nzeru kuonanso maganizo ndi makhalidwe athu. Nthaŵi ndi nthaŵi tiyenera kudzipenda moona mtima ndiponso mwapemphero kuti titsimikizire kuti sitikupatuka pang’onopang’ono pa maganizo a Yehova ndi mfundo zake. Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakonda kuganizira zinthu zomwe sindikanaziganizira zaka zingapo zapitazo? Kodi ndikulolera makhalidwe amene Mulungu amaletsa? Kodi ndimakonda kuona zinthu zauzimu mopepuka kusiyana ndi mmene ndinkachitira kale? Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndimaika zinthu za Ufumu pa malo oyamba m’moyo wanga?’ (Mateyu 6:33) Kusinkhasinkha koteroko kudzatithandiza kukaniza mzimu wa dziko.
‘Musatengedwe ndi Kusiyana Nazo’
8. Kodi munthu angatengeke bwanji ndi kusiyana ndi Yehova?
8 Mtumwi Paulo analembera Akristu anzake kuti: “Tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.” (Ahebri 2:1) Sitima ya m’madzi ikatengeka n’kusiya njira imene inayenera kuyenda, sifika pa malo amene inafunika kukocheza. Ngati woyendetsa sitimayo sasamala za mphepo ndi mphamvu ya kayendedwe ka madzi, sitima yakeyo ingatengeke mosavuta n’kupitirira pa doko lotetezeka n’kukagunda gombe la miyala. Mofanana ndi zimenezi, ngati sitisamalira choonadi chamtengo wapatali cha m’Mawu a Mulungu, tingatengeke mosavuta n’kusiyana ndi Yehova ndipo tingasweke mwauzimu ngati chombo. Sikuti kukumana ndi vuto limeneli kumalira kukaniratu choonadi ayi. Ndipotu, si anthu ambiri amene amakana Yehova mwadzidzidzi ndiponso mwadala. Nthaŵi zambiri, amayamba pang’onopang’ono kuchita zinthu zimene zimawapangitsa kusiya kuganizira kwambiri Mawu a Mulungu. Asanazindikire zimenezo bwinobwino, amapezeka kuti achita tchimo. Mofanana ndi woyendetsa sitima amene akugona, anthu oterowo sadzuka mpaka zitafika poti ndi m’mbuyo mwa alendo.
9. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Solomo?
9 Taganizirani moyo wa Solomo. Yehova anam’patsa ufumu wa Israyeli. Mulungu analola kuti Solomo amange kachisi ndipo anamuuza kuti alembe mbali zina za Baibulo. Yehova analankhula naye kaŵiri ndipo anam’patsa chuma, ulemu, ndi mtendere panthaŵi ya ulamuliro wake. Koposa zonsezi, Yehova anapatsa Solomo nzeru zambiri. Baibulo limati: “Mulungu anampatsa Solomo nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziŵa zamitundumitundu, zonga mchenga uli m’mbali mwa nyanja. Ndipo nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a kum’maŵa, ndi nzeru zonse za ku Aigupto.” (1 Mafumu 4:21, 29, 30; 11:9) Kunena zoona, munthu akhoza kuganiza kuti ngati panali munthu amene akanakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, anali Solomo. Komatu, Solomo anatengeka n’kukhala wampatuko. Kodi zinatheka bwanji zimenezo?
10. Kodi Solomo analephera kumvera langizo lotani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
10 Solomo ankadziŵa ndiponso kumvetsa bwinobwino Chilamulo cha Mulungu. Mosakayikira, ayenera kuti ankaona mwapadera malangizo amene anaperekedwa kwa amene anakhala mafumu ku Israyeli. Limodzi mwa malangizo amenewo linali lakuti: ‘[Mfumu] isadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake.’ (Deuteronomo 17:14, 17) Ngakhale kuti panali langizo losapita m’mbali limeneli, Solomo anakhala ndi akazi 700 ndi akazi achabe kapena kuti zibwenzi 300. Ambiri mwa akazi ameneŵa ankalambira milungu yachikunja. Sitikudziŵa chifukwa chake Solomo anali ndi akazi ambiri choncho, ndipo sitikudziŵa kuti anaona kuti kunali koyenera kuchita zimenezo pa chifukwa chiti. Chimene tikudziŵa n’choti iye analephera kumvera langizo la Mulungu lomveka bwino. Zotsatira zake zinagwirizana ndendende ndi zimene Yehova anali atachenjezeratu. Timaŵerenga kuti: “Akazi ake [a Solomo] anapambutsa mtima wake atsate milungu ina.” (1 Mafumu 11:3, 4) Pang’ono ndi pang’ono nzeru zake zomwe Mulungu anam’patsa zinayamba kuzimiririka. Anatengeka. Patapita nthaŵi, kufuna kusangalatsa akazi ake achikunjawo kunachititsa Solomo kusiya kumvera ndi kusangalatsa Mulungu. Zinalitu zomvetsa chisoni, poganizira kuti ndi Solomo yemweyo amene zisanachitike zimenezi analemba kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”—Miyambo 27:11.
Mzimu wa Dzikoli Ndi Wamphamvu
11. Kodi zinthu zimene timaika m’maganizo mwathu zimakhudza bwanji mmene timaganizira?
11 Chitsanzo cha Solomo chikutiphunzitsa kuti ndi ngozi kuganiza kuti popeza timadziŵa choonadi, zochitika za m’dzikoli sizingatisokoneze maganizo. Monga mmene chakudya chenicheni chimakhudzira thupi lathu, zimene timaika m’maganizo mwathu zimakhudzanso mmene timaganizira. Zimene timaloŵetsa m’maganizo mwathu zimakhudza mmene timaonera zinthu. Pozindikira zimenezi, makampani amagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola mabiliyoni ambiri chaka chilichonse potsatsa malonda awo. Akamatsatsa malonda kuti ziwayendere bwino amagwiritsa ntchito mawu ndi zithunzi zokopa zimene zingakwaniritse zimene mtima wa anthu ogula umafuna. Otsatsa malonda amadziŵanso kuti kuona malondawo kamodzi kapena kaŵiri kokha, nthaŵi zambiri sikungachititse anthu kuthamangira kukagula. Koma kuona mobwerezabwereza m’kupita kwa nthaŵi kumachititsa wogulayo kuyamba kuchikonda chinthucho. Kutsatsa malonda kumawapindulitsa, chifukwa zikanakhala kuti sapindula sibwenzi akuchita zimenezo. Kumakhudza kwambiri maganizo a anthu ndi mmene akuchionera chinthucho.
12. (a) Kodi Satana amasintha bwanji maganizo a anthu? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Akristu angakhudzidwe?
12 Mofanana ndi munthu wotsatsa malonda, Satana amalimbikitsa maganizo ake powakonza kukhala okopa kwambiri, akudziŵa kuti m’kupita kwa nthaŵi adzakopa anthu kuti aziganiza mmene iye amaganizira. Pogwiritsa ntchito zosangulutsa ndi njira zina, Satana amanyenga anthu n’kumakhulupirira kuti chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino. (Yesaya 5:20) Ngakhalenso Akristu oona agwera mumsampha wokhulupirira mabodza amene Satana amafalitsa. Baibulo limachenjeza kuti: “Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda, m’maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m’chikumbumtima mwawo monga ndi chitsulo chamoto.”—1 Timoteo 4:1, 2; Yeremiya 6:15.
13. Kodi mayanjano oipa n’chiyani, ndipo kodi anthu amene timacheza nawo angatikhudze bwanji?
13 Tonsefe tikhoza kukhudzidwa ndi mzimu wa dziko. Zinthu zokopa za dongosolo la Satanali ndi zamphamvu. Baibulo limalangiza mwanzeru kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Mayanjano oipa ndiwo china chilichonse kapena munthu wina aliyense, ngakhale mumpingo wachikristu, chimene chimasonyeza kapena amene amasonyeza mzimu wa dziko. Ngati tingaganize kuti mayanjano oipa sangativulaze, kodi sitingaganizenso kuti mayanjano abwino sangatithandize? Kungakhaletu kulakwitsa kwakukulu kumeneko. Baibulo limafotokoza nkhani imeneyi momveka bwino kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”—Miyambo 13:20.
14. Kodi tingakanize bwanji mzimu wa dziko?
14 Kuti tikanize mzimu wa dziko, tiyenera kumacheza ndi anthu anzeru, anthu amene amatumikira Yehova. Tiyenera kuganizira zinthu zimene zingalimbitse chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” (Afilipi 4:8) Monga anthu oti tili ndi ufulu wosankha zochita, tingasankhe zinthu zimene tingaziganizire. Tiyeni nthaŵi zonse tiziganizira zinthu zimene zingatichititse kuyandikira kwambiri kwa Yehova.
Mzimu wa Mulungu Ndi Wamphamvu Kwambiri
15. Kodi Akristu a mumzinda wakale wa Korinto anasiyana bwanji ndi anthu ena a mumzindawo?
15 Akristu oona akutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu mosiyana ndi anthu amene mzimu wa dziko ukuwasocheretsa. Paulo analembera mpingo wa ku Korinto kuti: “Sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziŵe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.” (1 Akorinto 2:12) Mzinda wakale wa Korinto unadzala ndi mzimu wa dziko. Anthu ambiri a mumzindawo anali okonda chiwerewere moti patapita nthaŵi, mawu oti “kuchita chikorinto” ankatanthauza “kuchita chiwerewere.” Satana anachititsa khungu maganizo a anthu. Chifukwa cha zimenezi, iwo ankangodziŵa zochepa chabe zokhudza Mulungu woona kapenanso sankadziŵa n’komwe. (2 Akorinto 4:4) Komabe, pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova anatsegula maso a Akorinto ena, zimene zinawathandiza kudziŵa choonadi. Mzimu wake unawalimbikitsa ndiponso kuwatsogolera kusintha kwambiri pa moyo wawo kuti Mulungu awayanje ndi kuwadalitsa. (1 Akorinto 6:9-11) Ngakhale kuti mzimu wa dziko unali wamphamvu, mzimu wa Yehova unali wamphamvu kwambiri kuposa wa dziko.
16. Kodi tingatani kuti tilandire mzimu wa Mulungu ndi kukhala nawobe?
16 Zimenezi zikuchitikanso masiku ano. Mzimu woyera wa Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa china chilichonse m’chilengedwe chonse, ndipo amaupereka kwaulere ndiponso mooloŵa manja kwa anthu amene amaupempha ndi chikhulupiriro. (Luka 11:13) Komabe, kuti tikhale ndi mzimu wa Mulungu, tiyenera kuchita zambiri osati kungokaniza chabe mzimu wa dziko. Tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse ndi kutsatira zimene tikuphunzirazo kuti mzimu wathu, kapena kuti maganizo athu, agwirizane ndi maganizo a Mulungu. Ngati tichita zimenezo, Yehova adzatilimbitsa kuti tithe kulimbana ndi machenjera alionse amene Satana angagwiritse ntchito kuti awononge moyo wathu wauzimu.
17. Kodi zimene Loti anakumana nazo zingatilimbikitse motani?
17 Ngakhale kuti Akristu sali mbali ya dziko, iwo akukhala m’dzikoli. (Yohane 17:11, 16) Palibe amene angapeŵeretu mzimu wa dziko, chifukwa mwina tingakhale tikugwira ntchito kapena kukhala pamodzi ndi anthu amene sakonda Mulungu kapena njira zake. Kodi timamva mumtima mwathu monga mmene anamvera Loti amene ‘analema mtima,’ ngakhale kuipidwa kumene, ndi makhalidwe oipa a anthu a ku Sodomu, amene anali kukhala nawo? (2 Petro 2:7, 8) Ngati ndi choncho, tingakhazike mtima pansi. Yehova anateteza ndi kupulumutsa Loti, ndipo angachitenso chimodzimodzi kwa ife. Atate wathu wachikondi amaona ndiponso amadziŵa mmene zinthu zilili pa moyo wathu, ndipo angatithandize ndi kutilimbitsa monga mmene tikufunikira kuti tikhalebe ndi moyo wabwino wauzimu. (Salmo 33:18, 19) Ngati timudalira, kumukhulupirira, ndi kum’pempha, adzatithandiza kukaniza mzimu wa dziko, ngakhale zinthu zitakhala zovuta motani pa moyo wathu.—Yesaya 41:10.
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamalira ubwenzi wathu ndi Yehova?
18 M’dziko lino limene lapatuka kwa Mulungu ndiponso lanyengedwa ndi Satana, ife monga anthu a Yehova tadalitsidwa podziŵa choonadi. Motero, timakhala ndi chimwemwe ndi mtendere zimene dzikoli lilibe. (Yesaya 57:20, 21; Agalatiya 5:22) Timakhala ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chodzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso, m’mene mzimu wa dziko limene latsala pang’ono kuthali sudzakhalamo. Ndiyetu tiyeni tisamalire ubwenzi wathu wamtengo wapatali ndi Mulungu ndi kuchita changu kukonza maganizo alionse ofuna kutengeka mwauzimu. Tiyeni tiyandikire kwambiri kwa Yehova, ndipo iye adzatithandiza kukaniza mzimu wa dzikoli.—Yakobo 4:7, 8.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi Satana wanyenga ndi kusocheretsa anthu m’njira ziti?
• Kodi tingapeŵe bwanji kutengeka n’kusiyana ndi Yehova?
• N’chiyani chikusonyeza kuti mzimu wa dzikoli ndi wamphamvu?
• Kodi tingatani kuti tilandire mzimu wa Mulungu ndi kukhala nawobe?
[Tchati patsamba 11]
NZERU ZA DZIKO ZIMASIYANA NDI NZERU ZA MULUNGU
Palibe choonadi chenicheni—anthu amapanga choonadi chawochawo.
“Mawu [a Mulungu] ndi choonadi.”—Yohane 17:17.
Kuti musiyanitse chabwino ndi choipa, ingotsatirani zimene mtima wanu ukunena.
“Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.”—Yeremiya 17:9.
Chitani zimene mukufuna.
“Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
Kulemera ndiye chinsinsi cha chimwemwe.
“Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama.”—1 Timoteo 6:10.
[Chithunzi patsamba 10]
Solomo anatengeka ndi kusiyana nako kulambira koona ndipo anayamba kulambira milungu yonyenga
[Chithunzi patsamba 12]
Mofanana ndi wotsatsa malonda, Satana amalimbikitsa mzimu wa dziko. Kodi inu mumaukaniza?