“Tadzilimbikani mwa Ambuye”
“Tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.”—AEFESO 6:10.
1. (a) Kodi ndi nkhondo yachilendo yotani imene inachitika zaka pafupifupi 3,000 zapitazo? (b) N’chifukwa chiyani Davide anapambana?
ZAKA pafupifupi 3,000 zapitazo, adani aŵiri ochokera m’magulu ankhondo aŵiri amene anali kumenyana anakumana. Wamng’ono mwa amunawo anali Davide yemwe anali mnyamata wobusa ziŵeto. Anali ataimitsana ndi Goliati, amene anali wamphamvu kwambiri komanso wamtali mochititsa mantha. Malaya ake ausilikali omwe anali achitsulo ankalemera makilogalamu pafupifupi 57, ndipo anali ndi mkondo waukulu komanso wolemera ndiponso lupanga lalikulu kwambiri. Davide sanavale chovala chilichonse chankhondo, ndipo chida chomwe anali nacho chinali choponyera miyala basi. Goliati, chimphona cha Afilisti, anaona kuti wanyozeka kwambiri chifukwa chakuti Mwisrayeli amene anabwera kudzamenyana nayeyu anali mnyamata wamng’ono. (1 Samueli 17:42-44) Kwa Aisrayeli ndi Afilisti amene anali kuonerera zimene zinkachitikazo zinali zosachita kufunsa kuti apambane ndani. Koma sinthaŵi zonse pamene anthu amphamvu amapambana nkhondo. (Mlaliki 9:11) Davide anapambana chifukwa chakuti anamenya nkhondoyo mwa mphamvu za Yehova. Iye anati: “Yehova ndiye mwini nkhondo.” M’Baibulo, nkhaniyi imati “Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake.”—1 Samueli 17:47, 50.
2. Kodi Akristu amamenya nkhondo yotani?
2 Akristu samenya nkhondo yeniyeni. Ngakhale kuti amakhala mwamtendere ndi anthu onse, iwo amamenya nkhondo yauzimu ndi adani amphamvu kwambiri. (Aroma 12:18) Paulo m’chaputala chomaliza cha kalata yomwe analembera Aefeso anafotokoza za nkhondo imene Mkristu aliyense akumenya nawo. Iye analemba kuti: ‘Kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi mizimu yoipa yakumwamba.’—Aefeso 6:12.
3. Mogwirizana ndi Aefeso 6:10, kodi tikufunika chiyani kuti tipambanedi?
3 ‘Mizimu yoipa’ imeneyi ndi Satana ndi ziwanda, amene akufunitsitsa kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Popeza kuti adaniŵa n’ngamphamvu kwambiri kuposa ifeyo, zinthu zilinso ngati mmene zinalili kwa Davide, ndipo sitingapambane ngati sitidalira mphamvu za Mulungu. Ndipotu, Paulo akutilimbikitsa kuti ‘tikhale olimba mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.’ (Aefeso 6:10) Mtumwiyu atatha kupereka malangizo ameneŵa, anafotokoza zinthu zauzimu ndiponso makhalidwe achikristu amene angatithandize kupambana pankhondoyi.—Aefeso 6:11-17.
4. Kodi ndi mfundo zazikulu ziŵiri ziti zimene tione m’nkhaniyi?
4 Tsopano tiyeni tione zimene Malemba amanena zokhudza mphamvu ndi njira za mdani wathuyu. Kenako tiona zimene tiyenera kuchita kuti tidziteteze. Ngati titsatira malangizo a Yehova, sitingakayikire n’komwe kuti adani athuŵa sangatigonjetse.
Kulimbana ndi Mizimu Yoipa
5. Kodi kugwiritsa ntchito mawu akuti “kulimbana” pa Aefeso 6:12 kukutithandiza motani kuzindikira cholinga cha Satana polimbana nafe?
5 Paulo anafotokoza kuti ‘tikulimbana . . . ndi mizimu yoipa yakumwamba.’ Ndipotu mzimu umene umachititsa kwambiri kuipa ndi Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “mkulu wa ziwanda.” (Mateyu 12:24-26) Baibulo limafotokoza za nkhondo yathu kuti ndi “kulimbana,” kapena kuti ndewu yeniyeni. Kalekale ku Girisi anthu ankachita mipikisano imene munthu ankalimbana ndi mnzake kuti am’gwetse pansi. Mofanana ndi zimenezi, Mdyerekezi akufuna kuti atigwetse mwauzimu. Kodi iye angatani kuti ife tigwe?
6. Sonyezani pogwiritsa ntchito Malemba mmene Mdyerekezi angagwiritsire ntchito njira zosiyanasiyana n’cholinga choti afooketse chikhulupiriro chathu.
6 Nthaŵi zina Mdyerekezi angakhale ngati njoka, mkango wobuma, kapenanso mngelo wa kuunika. (2 Akorinto 11:3, 14; 1 Petro 5:8) Iye angathe kugwiritsira ntchito anthu kuti atizunze kapena kutifooketsa. (Chivumbulutso 2:10) Popeza kuti dziko lonseli lili m’manja mwa Satana, iye angagwiritse ntchito zinthu zimene dzikoli limakonda kapena zinthu zokopa n’cholinga choti atikole. (2 Timoteo 2:26; 1 Yohane 2:16; 5:19) Angagwiritsire ntchito maganizo a anthu a m’dzikoli kapena a anthu ampatuko kuti atisokeretse, monga mmene ananyengera Hava.—1 Timoteo 2:14.
7. Kodi ziwanda zilibe mphamvu zotani ndipo kodi ifeyo tili ndi mwayi wotani?
7 Ngakhale kuti zida ndiponso mphamvu za Satana ndi ziwanda zake zingaoneke kuti ndi zochuluka kwambiri, palinso zinthu zina zimene sangathe kuchita. Mizimu yoipa imeneyi singatikakamize kuchita zinthu zoipa zimene Atate wathu wakumwamba sakondwera nazo. Anthufe tinalengedwa ndi nzeru zotha kusankha chabwino ndi choipa, ndipo tingathe kulamulira maganizo ndi zochita zathu. Kuwonjezera apo, sitili tokha pankhondoyi. Mmene zinthu zinalili m’nthaŵi ya Elisa ndi mmene zililinso masiku ano. “Okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” (2 Mafumu 6:16) Baibulo limatitsimikizira kuti ngati timvera Mulungu ndi kutsutsa Mdyerekezi, iye adzatithaŵa.—Yakobo 4:7.
Timadziŵa Machenjera a Satana
8, 9. Kodi Satana anam’bweretsera mayesero otani Yobu pofuna kuti asakhalenso wokhulupirika kwa Mulungu, ndipo kodi masiku ano timakumana ndi zinthu zotani zimene zingatigwetse mwauzimu?
8 Malemba amatiuza njira zimene Satana amakonda kugwiritsira ntchito, choncho timawadziŵa machenjera ake. (2 Akorinto 2:11) Mdyerekezi polimbana ndi Yobu amene anali wolungama, anagwiritsira ntchito mavuto aakulu a zachuma, imfa za anthu amene ankawakonda, kutsutsidwa ndi a m’banja lake, matenda, ndiponso kudzudzulidwa popanda chifukwa chomveka ndi anthu omwe ankanamizira kuti ndi anzake. Yobu anafooledwa kwambiri n’kuyamba kuganiza kuti Mulungu wamutaya. (Yobu 10:1, 2) Ngakhale kuti Satana masiku ano sangachititse mwachindunji mavuto ameneŵa, Akristu ambiri timakumana ndi mavuto ngati ameneŵa, ndipo Mdyerekezi angapezerepo mwayi pamenepo.
9 M’nthaŵi zamapeto zino zinthu zimene zingatisokoneze mwauzimu zachuluka kwambiri. Tikukhala m’dziko limene anthu amaona kuti chuma ndiye chofunika kwambiri kuposa zolinga zauzimu. Nthaŵi ndi nthaŵi zinthu monga mawailesi ndi manyuzipepala zimasonyeza kuti chiwerewere chimabweretsa chimwemwe osati mavuto. Ndipo anthu ambiri tsopano ‘n’ngokonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.’ (2 Timoteo 3:1-5) Ngati ‘sitilimba chifukwa cha chikhulupiriro’ maganizo ngati ameneŵa angathe kutigwetsa mwauzimu.—Yuda 3.
10-12. (a) Kodi ndi chenjezo lina liti limene Yesu anapereka m’fanizo lake la wofesa mbewu? (b) Fotokozani mmene zinthu zauzimu zingakanyangidwire.
10 Imodzi mwa njira zamphamvu kwambiri zimene Satana amazigwiritsira ntchito ndi yotichititsa kuti titengeke ndi dzikoli ndiponso mtima wadzikoli wolakalaka chuma. Yesu m’fanizo lake la wofesa mbewu anachenjeza kuti nthaŵi zina ‘kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma zimatsamwitsa mawu [a Ufumu].’ (Mateyu 13:18, 22) Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kutsamwitsa’ pa vesili amatanthauza “kukanyanga mpaka kupheratu.”
11 M’nkhalango zachilengedwe za m’madera otentha mumatha kupezeka mitengo ya kachere yomera mokulungiza mitengo inzake. Mtengo wa kacherewu umakula pang’onopang’ono n’kumakulungiza mtengo womwe wamerapowo. Pang’ono ndi pang’ono mizu ya kachereyo imakuta mtengowo ndipo mizuyo imamka nikula. M’kupita kwa nthaŵi, mizu ya kachereyo yomwe imakhalapo yambirimbiri imatenga chakudya chambiri chopezeka patsinde pa mtengo winawo, ndipo nthambi za kachereyo zimatsekereza mtengo winawo kuti usawombedwe ndi dzuŵa. Mapeto ake, mtengowo umafa.
12 Mofanana ndi zimenezi, kulabadira zinthu za dongosolo lino ndiponso kufunafuna chuma ndi moyo wa mwanaalirenji, pang’ono ndi pang’ono kungayambe kutidyera nthaŵi ndi mphamvu zathu. Ngati maganizo athu onse ali pa zinthu za m’dzikoli, kungakhale kosavuta kuyamba kunyalanyaza phunziro laumwini la Baibulo ndiponso kuyamba kukhala ndi chizoloŵezi chophonya misonkhano yachikristu, zimene zingachititse kuti tisiye kulandira chakudya chauzimu. Zikafika pamenepa, kufunafuna chuma kumaloŵa m’malo mwa ntchito zauzimu, ndipo mapeto ake sizivuta kuti Satana atigwire.
Tikufunika Kuchirimika
13, 14. Kodi tiyenera kutani Satana akamatitsutsa?
13 Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti ‘achirimike pokana machenjerero a Mdyerekezi.’ (Aefeso 6:11) Ndi zoona kuti sitingathe kugonjetseratu Mdyerekezi ndi ziwanda zake. Mulungu anapereka ntchito imeneyo kwa Yesu Kristu. (Chivumbulutso 20:1, 2) Koma, panopo tikufunika ‘kuchirimika’ kuti asatigonjetse akamalimbana nafe, mpaka pamene Satana adzachotsedwe.
14 Nayenso mtumwi Petro anatsindika kufunika kochirimika polimbana ndi Satana. Petro analemba kuti “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire; ameneyo mum’kanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zowawa zomwezo zirimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” (1 Petro 5:8, 9) Ndipotu, thandizo la abale athu auzimu ndi lofunika kwambiri kuti tichirimike Mdyerekezi akamalimbana nafe ngati mkango wobuma.
15, 16. Perekani chitsanzo cha m’Malemba posonyeza mmene thandizo la okhulupirira anzathu lingatithandizire kuchirimika.
15 Mkango ukabangula m’nkhalango zina za mu Africa muno, mbaŵala zimayatsa liŵiro la mtondo wadooka mpaka zitakafika kumalo otetezeka. Koma njovu zimathandizana. Buku lina lofotokoza za njovu, lakuti Elephants—Gentle Giants of Africa and Asia, limati: “Nthaŵi zambiri gulu la njovu limadziteteza popanga bwalo ndipo njovu zikuluzikulu zimaima moyang’ana kumene kuli chinthu chomwe chikuwopsezacho pamene ana amakhala otetezedwa m’kati mwa bwalolo.” Chifukwa cha mphamvu ndiponso kuthandizana kotereku, ngakhale ana a njovu sagwidwa kaŵirikaŵiri ndi mikango.
16 Tikawopsedwa ndi Satana ndi ziwanda zake, nafenso timafunika kukhala pamodzi, kukhala pafupi ndi abale athu olimba m’chikhulupiriro. Paulo anavomereza kuti anzake ena achikristu anali ‘chomutonthoza mtima’ pamene anali m’ndende ku Roma. (Akolose 4:10, 11) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘chotonthoza mtima’ amapezeka kamodzi kokha m’Malemba Achigiriki Achikristu. Malinga ndi buku la Vine lakuti Expository Dictionary of New Testament Words, “liwuli limanena za mankhwala amene amachepetsa ululu.” Monga mankhwala opha ululu, thandizo la anthu okhwima mwauzimu olambira Yehova lingathandize kuchepetsa ululu wa kuvutika maganizo kapena kupweteka m’thupi.
17. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala okhulupirika kwa Mulungu?
17 Kulimbikitsidwa ndi Akristu anzathu masiku ano kungatithandize kutsimikiza mtima kutumikira Mulungu mokhulupirika. Makamaka akulu achikristu ndiwo ali okonzeka kupereka thandizo lauzimu. (Yakobo 5:13-15) Zina mwa zinthu zimene zingatithandize kukhala okhulupirika ndizo kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse ndiponso kufika nthaŵi zonse pamisonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo. Kukhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu kumatithandiza kupitiriza kukhala okhulupirika kwa iye. Zoonadi, kaya tidya, timwa, kapena kuchita chinthu china chilichonse, tiyenera kukhala ndi cholinga chochita zinthu zonse mopatsa Mulungu ulemerero. (1 Akorinto 10:31) Nthaŵi zonse, kudalira Yehova ndiponso kupemphera ndi zofunika kwambiri kuti tipitirize kuchita zinthu zomukondweretsa.—Salmo 37:5.
18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulema ngakhale pamene mavuto atithera mphamvu zathu?
18 Nthaŵi zina Satana amalimbana nafe panthaŵi yomwe tafooka mwauzimu. Mkango umambwandira nyama yofooka. Mavuto a m’banja, a zachuma, kapena matenda angatithere mphamvu zonse zauzimu. Koma tisaleme pakuchita zinthu zokondweretsa Mulungu, chifukwa Paulo anati: “Pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:10; Agalatiya 6:9; 2 Atesalonika 3:13) Kodi anali kutanthauzanji? Ankatanthauza kuti m’malo mofooka Yehova angatipatse mphamvu malinga ngati timudalira. Zimene Davide anachita pogonjetsa Goliati zimasonyeza kuti Mulungu angathe kuwapatsa mphamvu anthu ake ndipo amaterodi. Mboni za Yehova zamakono zingaikire umboni kuti zinthu zitathina kwambiri pamoyo wawo, izo zinaona kuti Mulungu anali kuzipatsa mphamvu.—Danieli 10:19.
19. Perekani chitsanzo posonyeza mmene Yehova amalimbitsira atumiki ake.
19 Pankhani ya thandizo limene analandira kuchokera kwa Mulungu, mwamuna wina ndi mkazi wake analemba kuti: “Kwa zaka zonsezi, takhala tikutumikira Yehova pabanja lathuli ndipo talandira madalitso ambiri ndiponso tadziŵana ndi anthu abwino ambiri. Yehova wakhalanso akutiphunzitsa ndi kutilimbitsa kuti tizitha kupirira mavuto. Mofanana ndi Yobu, sikuti nthaŵi zonse tinkamvetsa chifukwa chake zinthu zinkachitika mwanjira inayake, koma tinkadziŵa kuti nthaŵi iliyonse Yehova anali wokonzeka kutithandiza.”
20. Kodi ndi umboni uti wa m’Malemba wosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu ake nthaŵi zonse?
20 Mkono wa Yehova sufupika moti n’kulephera kuthandiza ndi kulimbitsa atumiki ake okhulupirika. (Yesaya 59:1) Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Yehova agwiriziza onse akugwa, nawongoletsa onse owerama.” (Salmo 145:14) Inde, Atate wathu wakumwamba ‘amatisenzera tsiku ndi tsiku katundu’ wathu ndipo amatipatsa zinthu zimene tikufunikadi.—Salmo 68:19.
Tikufunika “Zida Zonse za Mulungu”
21. Kodi Paulo anatsindika motani kufunika kwa zida zauzimu?
21 Taona zina mwa njira zimene Satana amagwiritsira ntchito ndipo taona kufunika kochirimika iye akamalimbana nafe. Tsopano tiyeni tione thandizo lina lofunika kwambiri kuti titeteze chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo m’kalata imene analembera Aefeso, anatchulamo kaŵiri konse zinthu zofunika kuti tithe kuchirimika polimbana ndi machenjera a Satana ndiponso kuti tithe kupambana pa kulimbana kwathu ndi mizimu yoipa. Paulo analemba kuti: “Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi. . . . Mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachirimika.”—Aefeso 6:11, 13.
22, 23. (a) Kodi zida zathu zauzimu n’chiyani? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tiphunzira chiyani?
22 Zoonadi, tikufunika kuvala ‘zida zonse za Mulungu.’ Pamene Paulo ankalemba kalata yake kwa Aefeso, n’kuti msilikali wachiroma akumulondera, ndipo n’kutheka kuti nthaŵi zina msilikaliyo ankavala zovala zonse zankhondo. Komabe, ndi Mulungu amene anauzira mtumwiyu kuti afotokoze za zida zankhondo zauzimu zomwe ndi zofunika kwambiri kwa mtumiki aliyense wa Yehova.
23 Zida za Mulungu zimenezi zikuphatikizapo makhalidwe amene Mkristu ayenera kukhala nawo komanso zinthu zauzimu zimene Yehova watikonzera. M’nkhani yotsatirayi, tiona chida chauzimu chilichonse pachokha. Izi zitithandiza kuona kuti taikonzekera motani nkhondo yathu yauzimu. Komanso, tidzaona mmene chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu Kristu chingatithandizire kulimbana ndi Satana Mdyerekezi.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Akristu onse ali pankhondo yotani?
• Fotokozani njira zina zimene Satana amagwiritsira ntchito.
• Kodi thandizo la okhulupirira anzathu lingatilimbitse motani?
• Kodi tiyenera kudalira mphamvu za ndani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kutero?
[Zithunzi patsamba 11]
Akristu ‘akulimbana ndi mizimu yoipa’
[Chithunzi patsamba 12]
Kuganizira kwambiri zinthu za dongosolo lino kungatsamwitse mawu a Ufumu
[Chithunzi patsamba 13]
Akristu anzathu angathe kukhala ‘chotonthoza mtima’
[Chithunzi patsamba 14]
Kodi mumapemphera kwa Mulungu kuti akupatseni mphamvu?