Pewani Kudandaula
“Chitani zonse kopanda madandaulo.”—AFILIPI 2:14.
1, 2. Kodi ndi uphungu wotani womwe mtumwi Paulo anapatsa Akristu a ku Filipi ndi Korinto, ndipo n’chifukwa chiyani?
M’KALATA yake youziridwa ndi Mulungu imene mtumwi Paulo analembera mpingo wachikristu wa m’nthawi ya atumwi ku Filipi, iye anawayamikira kwambiri. Anayamikira Akristu anzake omwe ankakhala mu mzinda umenewu chifukwa chokhala owolowa manja ndi achangu, ndipo anakondwera chifukwa cha ntchito zawo zabwino. Komabe, Paulo anawakumbutsa kuti ‘azichita zonse kopanda madandaulo.’ (Afilipi 2:14) N’chifukwa chiyani mtumwiyu anawachenjeza motero?
2 Paulo ankadziwa chomwe chingachitike munthu akamang’ung’udza. Zaka zingapo asanawauze zimenezi, anali atakumbutsa mpingo wa ku Korinto kuti kung’ung’udza n’koopsa. Paulo ananena kuti nthawi imene Aisrayeli anali m’chipululu, anakwiyitsa Yehova mobwerezabwereza. Kodi anachita motani zimenezi? Mwa kukhumba zoipa, kupembedza mafano, kuchita dama, kuyesa Yehova ndiponso kudandaula. Paulo analimbikitsa Akorinto kuti atengerepo phunziro pa zimenezi. Iye analemba kuti: ‘Musadandaule, monga ena a iwo anadandaula, nawonongeka ndi wowonongayo.’—1 Akorinto 10:6-11.
3. N’chifukwa chiyani nkhani yodandaula ndi yofunika kuiganizira masiku ano?
3 Monga atumiki a Yehova masiku ano, tili ndi mzimu wofanana ndi womwe mpingo wa ku Filipi unali nawo. Ndife achangu pantchito zabwino, ndipo timakondana wina ndi mnzake. (Yohane 13:34, 35) Koma tikaona mmene kalekale kudandaula kunalowetsera m’mavuto anthu a Mulungu, tili ndi zifukwa zomveka zolabadirira uphungu wakuti: “Chitani zonse kopanda madandaulo.” Choyamba tiyeni tione zitsanzo za anthu omwe anadandaula zotchulidwa m’Malemba. Ndiyeno tikambirana zinthu zomwe tingachite masiku ano kuti kudandaula kusatilowetse m’mavuto.
Khamu Loipa Lidandaula Zochita za Yehova
4. Kodi Aisrayeli anadandaula motani m’chipululu?
4 Liwu la Chihebri lotanthauza ‘kung’ung’udza kapena kudandaula,’ lagwiritsidwa ntchito m’Baibulo pofotokoza zinthu zomwe zinachitika pa zaka 40 zimene Aisrayeli anali m’chipululu. Panthawi ina, Aisrayeli sanasangalale ndi mmene moyo wawo unalili ndipo anasonyeza zimenezi mwa kudandaula. Mwachitsanzo, patangopita milungu yochepa atalanditsidwa muukapolo ku Igupto, “khamu lonse la ana a Israyeli linadandaulira Mose ndi Aroni.” Aisrayeli anadandaula chifukwa cha chakudya, ndipo anati: “Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m’dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m’chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.”—Eksodo 16:1-3.
5. Pamene Aisrayeli ankadandaula, kodi ndani kwenikweni yemwe ankadandaulira?
5 Koma mosiyana ndi zomwe Aisrayeli ankanena, Yehova anawapatsa zonse zomwe ankafunikira m’chipululu, ndipo mwachikondi anawapatsa chakudya ndi madzi. Panalibe chodetsa nkhawa chilichonse choti Aisrayeli angafere ndi njala m’chipululu. Koma chifukwa chosakhala okhutira, anakokomeza vuto lawo ndipo anayamba kudandaula. Ngakhale kuti ankadandaulira Mose ndi Aroni, Yehova anaona kuti kwenikweni ankadandaulira Iye. Mose anauza Aisrayeli kuti: “Yehova adamva madandaulo anu amene mum’dandaulira nawo. Koma ife ndife chiyani? simulikudandaulira ife koma Yehova.”—Eksodo 16:4-8.
6, 7. Monga momwe lemba la Numeri 14:1-3 likusonyezera, kodi maganizo a Aisrayeli anali atasintha motani?
6 Sipanapite nthawi yaitali chichitikireni izi, Aisrayeli anadandaulanso. Mose anatumiza amuna khumi ndi awiri kuti akazonde Dziko Lolonjezedwa. Amuna khumi anabwerako ndi lipoti loipa. Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Ana onse a Israyeli anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nawo, Mwenzi tikadafa m’dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m’chipululu muno! Ndipo Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno [Kanani], kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chawo; kodi sikuli bwino tibwerere ku Aigupto?”—Numeri 14:1-3.
7 Maganizo a Aisrayeli anali atasinthiratu! Poyamba, kuyamikira kwawo chifukwa cha kumasulidwa ku Igupto ndi kupulumutsidwa pa Nyanja Yofiira kunawalimbikitsa kuimbira Yehova zitamando. (Eksodo 15:1-21) Koma chifukwa cha mavuto omwe ankakumana nawo m’chipululu ndiponso kuopa Akanani, kuyamikira konse kwa anthu a Mulungu kunatha, m’malo mwake anakhala ndi mzimu wosakhutira. M’malo moyamikira Mulungu chifukwa cha ufulu wawo, iwo molakwika anamuimba mlandu woti anawamana zinthu. Chotero, kudandaula kunasonyeza kuti sanayamikire zinthu zomwe Yehova anawapatsa. N’chifukwa chake ananena kuti: “Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa ine kufikira liti?”—Numeri 14:27; 21:5.
Kung’ung’udza M’nthawi ya Akristu Oyambirira
8, 9. Tchulani zitsanzo za kung’ung’udza zolembedwa m’Malemba Achigiriki Achikristu.
8 Zitsanzo za kudandaula zomwe tafotokozazi zinakhudza magulu a anthu amene zikuoneka kuti anasonyeza kusakhutira kwawo poyera. Koma nthawi imene Yesu Kristu anali ku Yerusalemu kudzachita Madyerero a Misasa mu 32 C.E., ‘kunali kung’ung’udza kwambiri za Iye m’makamu a anthu.’ (Yohane 7:12, 13, 32) Iwo ankanong’onezana za iye, ena ankanena kuti anali munthu wabwino ndipo ena ankati sanali munthu wabwino.
9 Panthawi inanso, Yesu ndi ophunzira ake anakacheza ku nyumba ya Levi, amene ankatchedwanso kuti Mateyu, wamsonkho. “Afarisi ndi alembi awo anang’ung’udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?” (Luka 5:27-30) Patapita nthawi ali ku Galileya, “Ayuda anang’ung’udza za [Yesu], chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.” Ngakhale ena omwe anali otsatira Yesu anakhumudwa ndi zimene ananena ndipo anayamba kung’ung’udza.—Yohane 6:41, 60, 61.
10, 11. N’chifukwa chiyani Ayuda olankhula Chigiriki anadandaula, ndipo akulu achikristu angapindule bwanji ndi mmene madandaulowo anasamaliridwira?
10 Kudandaula komwe kunachitika patangopita nthawi yochepa kuchoka pa Pentekoste 33 C.E., kunali ndi zotsatira zabwino. Ophunzira ambiri amene anangotembenuka kumene ochokera ku madera a kunja kwa Israyeli, ankacherezedwa bwino ndi okhulupirira anzawo a ku Yudeya. Koma panabuka mavuto okhudza kagawidwe ka zinthu zomwe zinalipo. Nkhaniyo imati: “Kunauka chidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.”—Machitidwe 6:1.
11 Odandaulawa sanali monga Aisrayeli m’chipululu. Aheleniste, kapena kuti Ayuda olankhula Chigiriki, sanasonyeze mwadyera kusasangalala kwawo ponena za mmene zinthu zinkayendera pa moyo wawo. Iwo anafotokoza za akazi ena amasiye omwe ankasowa thandizo. Ndiponso, odandaula amenewa, sanachite zinthu n’cholinga chofuna kukhala anthu ovutitsa ndi kudandaulira Yehova poyera. Iwo anauza atumwi madandaulo awo, ndipo atumwiwo anachitapo kanthu kuti zinthu zikonzedwe mwamsanga chifukwa madandaulo awo anali omveka. Atumwiwa anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu achikristu masiku ano. Abusa auzimu amenewa amasamala kwambiri kuti ‘asatseke makutu awo polira waumphawi.’—Miyambo 21:13; Machitidwe 6:2-6.
Samalani Kuti Kung’ung’udza Kungakuwonongeni
12, 13. (a) Fotokozani chitsanzo chosonyeza mmene kung’ung’udza kungatikhudzire. (b) Kodi n’chiyani chingachititse munthu kuyamba kudandaula?
12 Zitsanzo zambiri za m’Malemba zomwe takambirana zasonyeza kuti kale kung’ung’udza kunawononga zinthu kwambiri pakati pa anthu a Mulungu. Chotero, masiku anonso sitifunikira kunyalanyaza kuti kung’ung’udza kungatiwononge. Chitsanzo chotsatirachi chingatithandize kuona mmene kung’ung’udza kungatiwonongere pang’onopang’ono. Zitsulo zambiri zimachita dzimbiri. Ngati munyalanyaza zizindikiro zosonyeza kuti chitsulo chayamba kuchita dzimbiri, chitsulocho chingachite dzimbiri kwambiri moti simungachigwiritsenso ntchito. Galimoto zambiri zimatayidwa osati chifukwa choti injini yafa, koma chifukwa choti zitsulo zake zachita dzimbiri kwambiri moti kukwera galimoto zotero kungakhale koopsa. Kodi chitsanzochi chikugwirizana bwanji ndi nkhani ya kung’ung’udza?
13 Monga momwe zitsulo zina zimachitira dzimbiri, anthu opanda ungwiro ali ndi chizolowezi chodandaula. Tifunikira kukhala osamala kuti tithe kuona zizindikiro zilizonse za kung’ung’udza. Monga momwe chinyezi ndi mphepo yokhala ndi mchere imathandizira kuchita dzimbiri, mavuto amatichititsa kwambiri kuti tizidandaula. Kuvutika maganizo kungachititse munthu kuona zokhumudwitsa zazing’ono kukhala zinthu zazikulu. Pamene zinthu zikuipiraipira m’masiku otsiriza a dongosolo lino, zinthu zomwe zingatichititse kudandaula zikuwonjezeka. (2 Timoteo 3:1-5) Chotero, mtumiki wa Yehova angayambe kudandaula chifukwa cha zochita za mtumiki mnzake. Angayambe kudandaula pa zifukwa zochepa monga kusasangalala chifukwa cha zofooka za wina, luso lake, kapena mwayi wautumiki.
14, 15. N’chifukwa chiyani sitifunikira kulekerera chizolowezi chodandaula?
14 Kaya tili ndi zifukwa zotani zosasangalalira, ngati sitipewa chizolowezi chodandaula, chingatipangitse kuti tikhale ndi mzimu wosakhutira ndipo tingamangokhalira kung’ung’udza. Ndithudi, kung’ung’udza kungatiwononge pang’onopang’ono mwauzimu. Pamene Aisrayeli anadandaula za moyo wawo m’chipululu, iwo anafika mpaka poimba mlandu Yehova. (Eksodo 16:8) Zoterezi zisatichitikire!
15 Tingachepetse vuto loti chitsulo chichite dzimbiri mwa kuchipaka penti wosachita dzimbiri ndipo pamafunika kukonza mwamsanga malo aliwonse amene ayamba kuchita dzimbiri. Mofananamo, ngati tiona kuti tili ndi chizolowezi chodandaula, tingachithetse ngati mwamsanga tipemphera ndi kuyesetsa kuchitapo kanthu. Motani?
Onani Zinthu Mmene Yehova Amazionera
16. Ngati tili n’chizolowezi chodandaula, kodi tingachithetse bwanji?
16 Munthu akamang’ung’udza amangoganizira za iye yekha ndi mavuto ake ndipo amanyalanyaza madalitso amene tili nawo monga Mboni za Yehova. Ngati tili ndi chizolowezi chodandaula ndipo tikufuna kuchithetsa, tifunikira kumakumbukira madalitso amenewa. Mwachitsanzo, aliyense wa ife ali ndi mwayi wosangalatsa wodziwika ndi dzina la Yehova. (Yesaya 43:10) Tingakhale ndi ubwenzi wolimba ndi iye, ndipo timatha kulankhula ndi “Wakumva pemphero” ameneyu panthawi iliyonse. (Salmo 65:2; Yakobo 4:8) Moyo wathu umakhala n’cholinga chifukwa chakuti timamvetsa nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse ndipo timakumbukira kuti ndi mwayi wathu kukhala okhulupirika kwa Mulungu. (Miyambo 27:11) Tingatenge nawo mbali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu nthawi zonse. (Mateyu 24:14) Kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu kumatithandiza kukhala ndi chikumbumtima choyera. (Yohane 3:16) Amenewa ndi madalitso omwe timakhala nawo kaya tifunikira kupirira zinthu zotani.
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona zinthu ngati mmene Yehova amazionera, ngakhale titakhala ndi chifukwa chomveka chodandaulira?
17 Tiziyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera, osati chabe mmene timazionera. Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Salmo 25:4) Ngati tili ndi chifukwa chomveka chodandaulira, sikuti Yehova sakuchiona. Iye angathe kukonza zinthu nthawi yomweyo. Koma n’chifukwa chiyani nthawi zina amalola mavuto kupitiriza? Angachite zimenezi n’cholinga choti tikhale ndi makhalidwe abwino, monga kudekha, kupirira, chikhulupiriro ndi kuleza mtima.—Yakobo 1:2-4.
18, 19. Fotokozani chomwe chingachitike ngati tipirira zinthu zosokoneza popanda kudandaula.
18 Kupirira zinthu zosokoneza popanda kudandaula kumatithandiza kuwongolera umunthu wathu ndiponso anthu omwe akuona khalidwe lathu amasangalala. Mu 2003 gulu la Mboni za Yehova linachoka ku Germany paulendo wa pa basi kupita ku Hungary kuti likapezeke pamsonkhano. Woyendetsa basiyo sanali wa Mboni, ndipo sankafuna kuti akhale ndi Mboni masiku khumi. Koma pamapeto paulendo umenewu, anali atasinthiratu maganizo ake. Chifukwa chiyani?
19 Paulendo umenewu, zinthu zingapo zinasokonezeka. Koma Mbonizo sizinadandaule. Woyendetsa basiyo anati anthu amenewa anali abwino kuposa anthu onse omwe ananyamulapo. Ndipotu, analonjeza kuti nthawi imene Mboni zidzafike panyumba pake, adzazilowetsa m’nyumba ndi kumvetsera zolankhula zawo. Mbonizi zinapereka chitsanzo chabwino chifukwa ‘chochita zonse popanda kudandaula.’
Kukhululuka Kumalimbikitsa Umodzi
20. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukirana wina ndi mnzake?
20 Bwanji ngati tili ndi chifukwa chodandaulira ndi zochita za Mkristu mnzathu? Ngati nkhaniyo ndi yaikulu, tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo zopezeka m’mawu amene Yesu ananena olembedwa pa Mateyu 18:15-17. Koma zimenezi sizingakhale zofunikira nthawi zonse chifukwa madandaulo ambiri amakhala aang’ono. Bwanji osaona zimenezi monga mwayi wokhululukira ena? Paulo analemba kuti: “[Pitirizani] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:13, 14) Kodi timakhala okonzeka kukhululukira ena? Kodi Yehova alibe chifukwa chodandaulira ndi zochita zathu? Koma nthawi zonse amatisonyeza chifundo ndipo amatikhululukira.
21. Kodi anthu omwe amamvetsera kung’ung’udza kwathu angakhudzidwe bwanji?
21 Kaya tili ndi zifukwa zotani zodandaulira, kung’ung’udza sikungakonze zinthu. Mawu a Chihebri otanthauza kung’ung’udza angatanthauzenso kulankhula mosatulutsa mawu. N’zoona kuti sitimva bwino tikakhala ndi munthu wong’ung’udza ndipo timafuna kum’pewa. Tikamang’ung’udza kapena kudandaula, anthu omwe akutimvetsera angamve chimodzimodzi. Ndipotu, angamangike kwambiri moti angafune kutalikirana nafe. Kung’ung’udza poyera kungachititse chidwi munthu, koma sikungam’pangitse kutikonda.
22. Kodi mtsikana wina ananena chiyani chokhudza Mboni za Yehova?
22 Mtima wokhululukira ena umalimbikitsa umodzi, umene ndi chinthu chomwe anthu a Yehova amaona kukhala chofunika kwambiri. (Salmo 133:1-3) M’dziko lina ku Ulaya, mtsikana wina wa zaka 17 yemwe ndi Mkatolika analembera ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kufotokoza mmene amachitira chidwi ndi Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndi gulu lokhali limene anthu ake si ogawikana chifukwa cha chidani, umbombo, kusalolerana, dyera, kapena kusagwirizana.”
23. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
23 Kuyamikira madalitso onse auzimu omwe timalandira monga olambira Mulungu woona, Yehova, kudzatithandiza kulimbikitsa umodzi ndi kupewa kung’ung’udza pa zinthu zimene ena angatichitire. Nkhani yotsatira ifotokoza mmene makhalidwe amene Mulungu amatiphunzitsa kukhala nawo, angatithandizire kupewa kung’ung’udza komwe kuli koopsa kwambiri, kumene ndi kung’ung’udzira mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi kung’ung’udza kumaphatikizapo chiyani?
• Kodi mungafotokoze bwanji mmene kung’ung’udza kungakhudzire munthu?
• Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kuthetsa chizolowezi chong’ung’udza?
• Kodi kukhala okonzeka kukhululukira ena kungatithandize bwanji kupewa kung’ung’udza?
[Chithunzi patsamba 14]
Aisrayeli anadandaula zochita za Yehova
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi mumayesa kuona zinthu mmene Yehova amazionera?
[Zithunzi patsamba 18]
Kukhululuka kumalimbikitsa umodzi wachikristu