Tizigonjera Abusa Achikondi Modzichepetsa
“Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera.”—AHEBERI 13:17.
1, 2. Kodi ndi malemba ati amene amasonyeza kuti Yehova ndi Yesu ndi Abusa achikondi?
YEHOVA MULUNGU ndi Mwana wake, Yesu Khristu, ndi Abusa achikondi. Yesaya analosera kuti: “Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira. . . . Iye adzadyetsa zoweta zake ngati m’busa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.”—Yesaya 40:10, 11.
2 Ulosi umenewu unakwaniritsidwa koyamba mu 537 B.C.E pamene Ayuda ena anabwerera kwawo. (2 Mbiri 36:22, 23) Unakwaniritsidwanso mu 1919 pamene otsalira a odzozedwa anamasulidwa ku “Babulo Wamkulu” ndi Yesu Khristu, Koresi Wamkulu. (Chivumbulutso 18:2; Yesaya 44:28) Yesu ndiye “mkono” umene Yehova amagwiritsa ntchito polamulira, kusonkhanitsa, kudyetsa ndi kuweta nkhosa mwachikondi. Yesu anati: “Ine ndine m’busa wabwino, nkhosa zanga ndimazidziwa, izonso zimandidziwa ine.”—Yohane 10:14.
3. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amadera nkhawa ndi mmene nkhosa zake zimasamalidwira?
3 Ulosi wa pa Yesaya 40:10, 11 umatsindika mfundo yakuti Yehova amaweta anthu ake mwachikondi. (Salmo 23:1-6) Yesu ali padziko lapansi, ankasamaliranso mwachikondi otsatira ake ndi anthu ena. (Mateyo 11:28-30; Maliko 6:34) Yehova ndi Yesu yemwe ankadana ndi nkhanza za abusa, kapena kuti atsogoleri, a Isiraeli, amene mopanda manyazi ankanyalanyaza ndi kupondereza nkhosa zawo. (Ezekieli 34:2-10; Mateyo 23:3, 4, 15) Yehova analonjeza kuti: “Ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta. Ndipo ndidzaziutsira m’busa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala m’busa wawo.” (Ezekieli 34:22, 23) Nthawi ya mapeto ino, Yesu Khristu, Davide Wamkulu, ndiye “m’busa mmodzi” amene Yehova wamusankha kuyang’anira atumiki Ake onse, Akhristu odzozedwa ndi “nkhosa zina,” padziko lapansi.—Yohane 10:16.
Yehova Wapereka Mphatso Kumpingo
4, 5. (a) Kodi Yehova wapereka mphatso yamtengo wapatali yotani kwa anthu ake padziko lapansi? (b) Kodi Yesu wapereka mphatso yotani kumpingo wake?
4 Poutsa Yesu Khristu kuti akhale “m’busa mmodzi” wa atumiki Ake padziko lapansi, Yehova anapereka mphatso yamtengo wapatali kumpingo wachikhristu. Lemba la Yesaya 55:4, polosera za mphatso imeneyi ya Mtsogoleri wakumwamba, limati: “Taonani, ndam’pereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.” Akhristu odzozedwa ndi a “khamu lalikulu” amasonkhanitsidwa kuchokera ku mayiko, mafuko, mitundu, ndi malilime onse. (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:9) Amapanga mpingo wa padziko lonse, kapena kuti “gulu limodzi,” lotsogoleredwa ndi “m’busa mmodzi,” Khristu Yesu.
5 Yesu nayenso wapereka mphatso yamtengo wapatali kumpingo wake padziko lapansi. Wapereka abusa aang’ono okhulupirika amene, potsatira Yehova ndi Yesu, amaweta nkhosa mwachikondi. Mtumwi Paulo anatchula mphatso imeneyi m’kalata yake kwa Akhristu a ku Efeso. Analemba kuti: “‘Atakwera kumwamba anagwira anthu ukapolo; anapereka mphatso za amuna.’ . . . Anapereka ena monga atumwi, ena monga aneneri, ena monga alaliki, ena monga abusa ndi aphunzitsi, kuti awongolere oyerawo, achite ntchito yotumikira, amange thupi la Khristu.”—Aefeso 4:8, 11, 12.
6. Kodi oyang’anira odzozedwa amene anali m’mabungwe a akulu anaimiriridwa ndi chiyani pa Chivumbulutso 1:16, 20, ndipo tingati chiyani za akulu a nkhosa zina?
6 “Mphatso za amuna” zimenezi ndi oyang’anira, kapena akulu, amene Yehova ndi Mwana wake amawaika ndi mzimu woyera kuti aziweta nkhosa mwachikondi. (Machitidwe 20:28, 29) Kale, amuna onse oyang’anira amenewa anali Akhristu odzozedwa. Pa Chivumbulutso 1:16, 20, amene anali m’mabungwe a akulu mumpingo wa odzozedwa anaimiriridwa ndi “nyenyezi” kapena “amithenga” m’dzanja lamanja la Khristu, kutanthauza kuti mabungwewo anali kulamuliridwa ndi iye. Komabe, nthawi ya mapeto ino, akulu ambiri mumipingo ndi a nkhosa zina chifukwa chakuti oyang’anira odzozedwa amene adakali padziko lapansi akucheperachepera. Popeza kuti amenewa amaikidwa ndi oimira Bungwe Lolamulira motsogoleredwa ndi mzimu woyera, tingati iwonso ali m’dzanja lamanja (kapena kuti, akutsogoleredwa) ndi Yesu Khristu, M’busa Wabwino. (Yesaya 61:5, 6) Tifunikira kugonjera akulu mumipingo pazonse chifukwa chakuti iwo amagonjera Khristu, Mutu wa mpingo.—Akolose 1:18.
Kumvera ndi Kugonjera
7. Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo otani a mmene tiyenera kuonera oyang’anira achikhristu?
7 Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, Abusa athu akumwamba, amafuna kuti tizimvera ndi kugonjera abusa aang’ono amene apatsidwa udindo mumpingo. (1 Petulo 5:5) Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu, amene alankhula mawu a Mulungu kwa inu, ndipo poonetsetsa mmene khalidwe lawo likukhalira, tsanzirani chikhulupiriro chawo. Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu. Teroni kuti achite ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.”—Aheberi 13:7, 17.
8. Kodi Paulo akutiuza ‘kuonetsetsa’ chiyani, ndipo tiyenera ‘kumvera’ motani?
8 Onani kuti Paulo akutiuza ‘kuonetsetsa’ mmene khalidwe labwino la akulu likukhalira ndi kutsanzira chitsanzo chawo cha chikhulupiriro. Kenako akutilangiza kumvera ndi kugonjera zimene amuna amenewa akutiuza. Katswiri wa Baibulo R. T. France anafotokoza kuti m’Chigiriki choyambirira, mawu amene pano anawamasulira kuti “muzimvera” si mawu amene nthawi zonse amatanthauza “kumvera, koma ndi mawu otanthauza ‘kutsimikiza,’ kusonyeza kuti munthu akuvomereza ndi mtima wonse utsogoleri wawo.” Sikuti timamvera akulu chabe chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amatiuza kutero koma chifukwa chakuti tatsimikiza kuti iwo amakonda zinthu za Ufumu ndiponso kuti amatifunira zabwino. Tikavomereza ndi mtima wonse utsogoleri wawo, timakhaladi osangalala.
9. Kuwonjezera pa kukhala omvera, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ‘ogonjera’?
9 Nanga bwanji ngati sitili otsimikiza kuti njira imene akulu akutiuza kutsatira pankhani inayake, si njira yabwino kwenikweni? Apa ndiye pofunika kugonjera. N’zosavuta kumvera malangizo amene tapatsidwa ngati tikuwamvetsa bwino ndi kuwavomereza. Koma timasonyezadi kuti ndife ogonjera ngati tilolera kuchita zimene atiuzazo ngakhale kuti sitikuzimvetsa bwino. Petulo, yemwe kenako anadzakhala mtumwi, anagonjera mwanjira imeneyi.—Luka 5:4, 5.
Zifukwa Zinayi Zokhalira ndi Mtima Wogonjera
10, 11. Kodi oyang’anira “alankhula mawu a Mulungu” m’njira yotani, kwa Akhristu anzawo m’nthawi ya atumwi ndi masiku ano?
10 Palemba la Aheberi 13:7, 17 limene taligwira mawu kale, mtumwi Paulo anapereka zifukwa zinayi zokhalira omvera ndi ogonjera kwa oyang’anira achikhristu. Chifukwa choyamba ndi chakuti “alankhula mawu a Mulungu” kwa ife. Kumbukirani kuti Yesu amapereka ku mpingo “mphatso za amuna” kuti “awongolere oyerawo.” (Aefeso 4:11, 12) Iye anawongolera maganizo ndi makhalidwe a Akhristu oyambirira pogwiritsa ntchito abusa aang’ono okhulupirika, amene ena a iwo anauziridwa kulembera mipingo kalata zosiyanasiyana. Anagwiritsa ntchito oyang’anira oikidwa ndi mzimu amenewo kutsogolera ndi kulimbikitsa Akhristu oyambirira.—1 Akorinto 16:15-18; 2 Timoteyo 2:2; Tito 1:5.
11 Masiku ano, Yesu akutitsogolera pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amene amaimiriridwa ndi Bungwe lake Lolamulira ndi akulu. (Mateyo 24:45) Chifukwa chofuna kulemekeza Yesu Khristu, “m’busa wamkulu,” timamvera malangizo a Paulo akuti: “Muzilemekeza aja amene akugwira ntchito zolimba pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye ndi kukulangizani.”—1 Petulo 5:4; 1 Atesalonika 5:12; 1 Timoteyo 5:17.
12. Kodi akulu “amayang’anira miyoyo” yathu motani?
12 Chifukwa chachiwiri chogonjera oyang’anira achikhristu ndi chakuti “iwo amayang’anira miyoyo” yathu. Akaona kuti penapake mtima wathu kapena khalidwe lathu lingaike moyo wathu wauzimu pachiswe, mwachangu amatilangiza pofuna kutiwongolera. (Agalatiya 6:1) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “amayang’anira” amatanthauza “kusagona tulo.” Katswiri wina wa Baibulo anati mawuwo “amanena za m’busa amene amakhala tcheru nthawi zonse.” Kuwonjezera pa kuyesetsa kwawo kukhala atcheru mwauzimu, akulu nthawi zina sagona tulo chifukwa chodera nkhawa moyo wathu wauzimu. Kodi simukuona kuti n’koyenera kukhala ndi mtima wogonjera abusa aang’ono achikondi, amene amayesetsa kusamalira nkhosa mwachikondi ngati Yesu Khristu, “m’busa wa nkhosa wamkuluyo”?—Aheberi 13:20.
13. Kodi oyang’anira ndi Akhristu onse adzayankha mlandu kwa ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?
13 Chifukwa chachitatu chokhalira ndi mtima wogonjera oyang’anira ndi chakuti iwo amatiyang’anira “monga anthu amene adzayankha mlandu.” Oyang’anirawo amakumbukira kuti iwo ndi abusa aang’ono, amene akutumikira pansi pa Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, Abusa akumwamba. (Ezekieli 34:22-24) Yehova ndiye Mwini nkhosa zimene ‘anazigula ndi magazi a Mwana wake wa iye mwini,’ ndipo amafuna kuti zizisamaliridwa “mwachikondi.” N’chifukwa chake oyang’anira adzayankha mlandu kwa Iye wokhudza mmene iwo akusamalira nkhosa Zake. (Machitidwe 20:28, 29) Choncho, tonsefe tidzayankha mlandu kwa Yehova chifukwa cha mmene timalabadirira malangizo ake. (Aroma 14:10-12) Tikamamvera akulu, timapereka umboni wakuti timagonjera Khristu, Mutu wa mpingo.—Akolose 2:19.
14. N’chiyani chimene chingachititse oyang’anira achikhristu kutumikira “modandaula,” ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
14 Paulo anapereka chifukwa chachinayi chogonjera oyang’anira achikhristu modzichepetsa. Analemba kuti: “Teroni kuti achite ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.” (Aheberi 13:17) Akulu achikhristu amasenza mtolo wolemera chifukwa cha udindo waukulu umene ali nawo wophunzitsa, kuweta, kutsogolera ntchito yolalikira, kusamalira banja ndiponso mavuto mumpingo. (2 Akorinto 11:28, 29) Tikapanda kuwagonjera, timangowawonjezera mtolo. Mapeto ake, iwo angayambe ‘kudandaula.’ Tikakhala ndi mtima wosagonjera, Yehova sasangalala ndipo zimenezi zingatiwononge. Koma tikamawapatsa ulemu woyenera ndi kuwagonjera, akulu amachita ntchito yawo mwachimwemwe, ndipo zimenezi zimalimbikitsa umodzi komanso anthu amasangalala kuchita ntchito yolalikira Ufumu.—Aroma 15:5, 6.
Kodi Tingagonjere Bwanji?
15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife omvera ndi ogonjera?
15 Pali zinthu zambiri zimene tingachite kuti tigonjere oyang’anira. Kodi akulu asintha nthawi kapena tsiku la misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda chifukwa cha kusintha kwa zinthu m’gawo lathu, zimene zingafune kuti ifenso tisinthe? Ngati atero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tigwirizane ndi dongosolo latsopanolo. Tikachita zimenezi, tidzalandira madalitso amene mwina sitinayembekezere. Kodi woyang’anira utumiki akuyendera Phunziro la Buku la Mpingo la kwathu? Tiyeni tiyesetse kulalikira nawo kwambiri mlungu umenewo. Kodi tapatsidwa nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu? Tisalephere kupezekapo ndi kukamba nkhani yathuyo. Kodi woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo walengeza kuti gulu lathu ndilo lidzayeretse m’Nyumba ya Ufumu? Tiyeni timuthandize, malinga ndi mmene thanzi lathu ndi mphamvu zathu zilili. Mwa njira zimenezi ndi zinanso zambiri, timasonyeza kuti ndife ogonjera kwa amuna amene Yehova ndi Mwana wake asankha kusamalira gulu la nkhosa.
16. Ngati mkulu sachita zinthu zimene walangizidwa, kodi n’chifukwa chiyani zimenezi sizitipatsa chifukwa chopandukira?
16 Nthawi zina, mwina mkulu sachita zinthu zimene gulu la kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira lanena. Akapitiriza zimenezi, adzayankha yekha mlandu kwa Yehova, “m’busa ndi woyang’anira miyoyo” yathu. (1 Petulo 2:25) Pajatu kulakwitsa kapena kulephera kuchita zinthu kwa akulu ena, sikutipatsa chifukwa chokhalira ndi mtima wosafuna kugonjera. Yehova sadalitsa anthu osamvera ndi opanduka.—Numeri 12:1, 2, 9-11.
Yehova Amadalitsa Mtima Wogonjera
17. Kodi oyang’anira athu tiyenera kuwaona bwanji?
17 Yehova Mulungu amadziwa kuti amuna amene waika kukhala oyang’anira ndi anthu opanda ungwiro. Ngakhale zili choncho, akuwagwiritsabe ntchito, ndipo mwa mzimu wake, Yehova akuweta anthu ake padziko lapansi. Tonse, akulu ndi ife tomwe ‘mphamvu yoposa yachibadwa imene tingakhale nayo, ndi yochokera kwa Mulungu, osati kwa ife.’ (2 Akorinto 4:7) Choncho tiyenera kuthokoza Yehova chifukwa cha zimene akuchita kudzera mwa oyang’anira athu okhulupirika, ndipo tiyenera kuwagonjera ndi mtima wonse.
18. Tikamagonjera oyang’anira, kodi kwenikweni timakhala tikuchita chiyani?
18 Oyang’anira amayesetsa kukhala ofanana ndi abusa abwino amene Yehova wasankha kuti ayang’anire gulu lake la nkhosa masiku otsiriza ano. Yehova wafotokoza abusa amenewo pa Yeremiya 3:15 kuti: “Ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.” Akulu akuchitadi ntchito yotamandika yophunzitsa ndi kuteteza nkhosa za Yehova. Tiyeni tipitirizebe kusonyeza mtima woyamikira khama lawo powamvera ndi kuwagonjera ndi mtima wonse. Potero, timasonyeza mtima woyamikiranso Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, Abusa athu akumwamba.
Kubwereza
• Kodi Yehova ndi Yesu Khristu achita chiyani kusonyeza kuti ndi Abusa achikondi?
• Kuwonjezera pa kukhala omvera, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ogonjera?
• Kodi tingachite chiyani posonyeza kuti ndife ogonjera?
[Chithunzi patsamba 27]
Akulu achikhristu amagonjera utsogoleri wa Khristu
[Zithunzi patsamba 29]
Pali zinthu zambiri zimene tingachite kuti tigonjere abusa amene Yehova waika