“Chirimikani, Ndipo Penyani Chipulumutso cha Yehova”
“Yehova ndi wanga; sindidzawopa; adzandichitanji munthu?”—SALMO 118:6.
1.Kodi anthu adzaona zinthu zoopsa kwambiri ziti?
POSACHEDWAPA anthu adzaona zinthu zoopsa kwambiri zimene sizinachitikepo. Yesu analosera za masiku athu ano pamene anachenjeza otsatira ake kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zoona, kupanda kufupikitsa masikuwo, palibe aliyense akanapulumuka; koma chifukwa cha osankhikawo, masikuwo adzafupikitsidwa.”—Mateyo 24:21, 22.
2.Kodi n’chiyani chaimitsa kaye chisautso chachikulu?
2 Angelo ndi amene aimitsa kaye chisautso chachikulu kuti chisachitike ngakhale kuti sitikuwaona. Koma mtumwi Yohane anali ndi mwayi woona chifukwa chake angelo aimitsa kaye chisautso chachikuluchi m’masomphenya amene Yesu anamuonetsa. Taonani mmene mtumwi wokalambayu anafotokozera masomphenyawo. Iye anati: “Ndinaona angelo anayi ataimirira ku ngodya zinayi za dziko lapansi, atagwira zolimba mphepo zinayi za dziko lapansi . . . Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa, ali ndi chosindikizira cha Mulungu wamoyo. Mokweza mawu, iye anafuula kwa angelo anayiwo . . . ‘Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titasindikiza akapolo a Mulungu wathu chisindikizo pamphumi pawo.’”—Chivumbulutso 7:1-3.
3.Kodi n’chiyani chidzayamba kuchitika pa chisautso chachikulu?
3 Kuikidwa chisindikizo komaliza kwa “akapolo [odzozedwa] a Mulungu” wathu kutha posachedwapa. Angelo anayiwo atsala pang’ono kusiya mphepo zowononga zimenezi. Kodi chidzayamba kuchitika n’chiyani akasiya mphepozi? Mngelo anayankha funso limeneli kuti: “Mofulumira ndi mwamphamvu chomwechi, mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi, ndipo sudzapezekanso.” (Chivumbulutso 18:21) Ndipo kumwamba kudzakhala chisangalalo chachikulu pamene “mzinda waukulu wa Babulo” womwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga udzawonongedwa.—Chivumbulutso 19:1, 2.
4.Kodi kutsogoloku kudzachitika zotani?
4 Kenako mitundu yonse ya padziko lonse idzagwirizana kuti ilimbane ndi anthu a Yehova. Koma kodi mitundu imeneyi idzasesadi Akhristu okhulupirika amenewa? Zingaonekedi choncho. Komabe dziwani kuti magulu ankhondo akumwamba amene ali ndi Khristu Yesu adzaonetsetsa kuti magulu a anthu amenewa awonongedwa. (Chivumbulutso 19:19-21) Pomaliza, Mdyerekezi ndi angelo ake adzaponyedwa kuphompho kumene sadzatha kuchita chilichonse. Ndipo sadzathanso kusocheretsa anthu chifukwa adzamangidwa kwa zaka 1,000. Imeneyi idzakhala nthawi ya mpumulo weniweni kwa khamu lalikulu lomwe lidzapulumuke.—Chivumbulutso 7:9, 10, 14; 20:1-3.
5.Kodi anthu amene adzakhalabe okhulupirika kwa Yehova adzasangalala motani?
5 Posachedwapa tidzaona zinthu zosangalatsa ndi zochititsa chidwi kwambiri zimene zidzasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Ndipo taganizirani izi: Tikakhala okhulupirika kwa Yehova ndi kuimabe ku mbali ya ulamuliro wake, tidzakhala ndi mwayi woyeretsa nawo dzina lake ndi kukwaniritsa nawo cholinga chake. Kodi si zoona kuti tidzasangalala kwambiri pochita nawo zimenezi?
6.Tikaona zimene zili pafupi kuchitika, kodi tikambirana chiyani?
6 Kodi takonzekera zinthu zofunika kwambiri zimenezi? Kodi timakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zopulumutsa? Kodi timakhulupirira kuti adzatithandiza pa nthawi yoyenera ndiponso m’njira yabwino? Poyankha mafunso amenewa, tiganizire zimene mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake a ku Roma kuti: “Zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Nkhani yokhudza mmene Yehova anapulumutsira Aisiraeli mu ukapolo wankhanza ku Iguputo ndi imodzi mwa zinthu zimene zinalembedwa kuti zitilangize, zititonthoze ndi kutipatsa chiyembekezo. Kuona bwinobwino nkhani yosangalatsa ya mmene Yehova anapulumutsira ana a Isiraeli, kuyenera kutilimbikitsa kwambiri pamene tikuyembekezera chisautso chachikulu chimene chayandikirachi.
Yehova Amapulumutsa Anthu Ake
7.Kodi ku Iguputo kunachitika zotani m’chaka cha 1513 B.C.E.?
7 Munali m’chaka cha 1513 B.C.E. ndipo Yehova anali atakantha kale Aiguputo ndi milili 9. Mlili wa 9 utachitika, Farao anauza Mose mokalipa kuti: “Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.” Ndipo Mose anayankha kuti: “Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu.”—Eksodo 10:28, 29.
8.Kodi Aisiraeli anauzidwa malangizo otani kuti apulumuke, ndipo chinachitika n’chiyani?
8 Tsopano Yehova anaululira Mose kuti patsala mlili wina umodzi woti ubwere pa Farao ndi Aiguputo onse. Pa tsiku la 14 la mwezi wa Abibu (Nisani), mwana aliyense woyamba kubadwa wa Aiguputo ndi wa nyama zomwe anayenera kufa. Koma zimenezi sizikanakhudza mabanja a Isiraeli ngati akanatsatira malangizo amene Mulungu anapereka kwa Mose. Iwo anafunika kupaka magazi a mwana wankhosa wamphongo pa mafelemu awiri a m’mbali ndi la pamwamba pa chitseko cha nyumba zawo ndipo iwo anafunika kusatuluka m’nyumbazo. Kodi chinachitika n’chiyani usiku umenewo? Mose akutiuza kuti: “Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m’dziko la Aiguputo.” Nthawi yomweyo Farao anaitana Mose ndi Aroni amvekere: “Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, . . . ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.” Aisiraeli sanazengereze ananyamuka, iwo analipo mwina oposa 3 miliyoni osawerengera anthu amene sanali Aisiraeli.—Eksodo 12:1-7, 29, 31, 37, 38.
9.Kodi Mulungu anawauza Aisiraeli kudzera njira iti pochoka ku Iguputo, ndipo n’chifukwa chiyani?
9 Njira yachidule kwa Aisiraeli inali yodzera ku nyanja ya Mediterranean kudutsa m’dziko la Afilisiti. Koma limeneli linali dziko la adani. Choncho, mwina pofuna kuteteza anthu ake ku nkhondo, Yehova anawauza kuti adutse njira ya kuchipululu ya ku Nyanja Yofiira. Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imati gululi linayenda mwa dongosolo ngakhale kuti anali anthuwo ambiri zedi.—Eksodo 13:17, 18.
“Penyani Chipulumutso cha Yehova”
10.Kodi Mulungu anauziranji Aisiraeli kugona pafupi ndi dera la Pihahiroti?
10 Kenako, zinthu zinasintha mwadzidzidzi. Yehova anauza Mose kuti: “Lankhula ndi anthu a Isiraeli, kuti abwerere m’mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja yamchere, patsogolo pa Baala-Zefoni.” Akutsatira malangizo amenewa, gululi linapezeka kuti latsekerezedwa pakati pa mapiri ndi Nyanja Yofiira. Zinaoneka ngati kuti analibe kothawira. Komabe, Yehova ankadziwa zimene anali kuchita. Iye anauza Mose kuti: “Ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”—Eksodo 14:1-4.
11.(a) Kodi Farao anachita chiyani, nanga Aisiraeli anatani? (b) Kodi Mose anati chiyani Aisiraeli atadandaula?
11 Farao ataona kuti analakwitsa kulola Aisiraeli kuchoka mu Iguputo, anawalondola msangamsanga ndi magaleta 600 a nkhondo osankhidwa bwino. Aisiraeli ataona gulu lankhondo la Aiguputowo, anachita mantha ndi kuyamba kulilira Mose kuti: “Kodi mwatichotsera kuti tikafe m’chipululu chifukwa panalibe manda m’Iguputo?” Mose pokhulupirira kuti Yehova awapulumutsa anayankha kuti: “Musawope, chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero. . . Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.”—Eksodo 14:5-14.
12.Kodi Yehova anapulumutsa bwanji anthu ake?
12 Zimene Mose ananena ndi zoonadi chifukwa Yehova mwiniyo anamenyera nkhondo Aisiraeli pogwiritsa ntchito angelo ake. Mngelo wa Yehova anachotsa mozizwitsa mtambo umene unali kuwatsogolera n’kuupititsa kumbuyo kwawo. Mtambo umenewu umathandiza Aisiraeli kuti aziona kuwala koma Aiguputo umawachititsa mdima. (Eksodo 13:21, 22; 14:19, 20) Pomvera malangizo a Mulungu, Mose tsopano anatambasula dzanja lake. Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’mawa usiku wonse . . . Ndipo ana a Isiraeli analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.” Nawo Aiguputo anapitiriza kuwalondola, koma Yehova anali ndi anthu ake. Iye anachititsa chipwirikiti pa gulu la Aiguputowo, ndiyeno anauza Mose kuti: “Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aiguputo, magareta awo, ndi apakavalo awo.” Gulu la nkhondo la Farao linawonongedweratu ndipo sanatsale ndi mmodzi yemwe.—Eksodo 14:21-28; Salmo 136:15.
Zimene Tikuphunzira pa Kupulumutsidwa kwa Aisiraeli
13.Kodi ana Aisiraeli anatani atapulumutsidwa?
13 Kodi kupulumutsidwa mozizwitsa kumeneku kunawakhudza bwanji Aisiraeli? Nthawi yomweyo Mose ndi ana Aisiraeli onse anayamba kuimba potamanda Yehova amvekere: “Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu . . . Yehova adzachita ufumu nthawi yomka muyaya.” (Eksodo 15:1, 18) Inde, chinthu choyamba chimene iwo anaganiza kuchita ndi kutamanda Mulungu. Panthawi imeneyi Yehova anasonyezadi kuti ndi woyenera kulamulira.
14.(a) Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova pa zimene anachitira Aisiraeli? (b) Kodi lemba la chaka chino n’loti chiyani?
14 Kodi nkhani yochititsa chidwi imeneyi tikupezapo malangizo, chitonthozo ndi chiyembekezo chotani? Ndithudi tikuona kuti Yehova ndi wokonzeka kutithandiza mavuto aliwonse amene anthu akefe tingakumane nawo. Akhoza kuthana ndi chilichonse chimene chingatipinge. Mwachitsanzo, Yehova anagawa Nyanja Yofiira ndi mphepo yamphamvu ya kum’mawa kuti Aisiraeli awoloke. Komanso Yehova anachititsa kuti Nyanja Yofiira yomweyo ikhale manda a gulu la nkhondo la Farao. Kuganizira nkhani imeneyi kungatipangitse kugwirizana ndi mawu a wamasalmo akuti: “Yehova ndi wanga; sindidzawopa; adzandichitanji munthu?” (Salmo 118:6) Tingatonthozedwenso ndi mawu a Paulo olembedwa pa Aroma 8:31 akuti: “Ngati Mulungu ali ku mbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?” Malemba ouziridwa amenewa akutithandiza kwambiri kuti tizidalira Yehova. Amatithandiza kuthetsa mantha ndi kukayikira kulikonse kumene tingakhale nako ndipo amatipatsa chiyembekezo. N’chifukwa chake lemba la chaka chino n’loyenera kwambiri. Likuti: “Chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova.”—Eksodo 14:13.
15.Kodi kumvera kunali kofunika bwanji kuti Aisiraeli apulumuke ku Iguputo, nanga n’kofunika bwanji masiku ano?
15 Kodi n’chiyaninso chimene tingaphunzire pa nkhani ya kuchoka kwa Aisiraeli ku Iguputo? Tikuphunzirapo kuti tiyenera kumvera zilizonse zimene Yehova watiuza mulimonse mmene zinthu zingakhalire. Aisiraeli anamvera malangizo onse a Pasika ndipo sanatuluke m’nyumba zawo usiku wa pa Nisani 14. Kenaka atachoka ku Iguputo, iwo anayenda “mwa dongosolo.” (Eksodo 13:18, Malembo Oyera) Masiku ano ndi kofunikanso kwambiri kutsatira malangizo amene timapatsidwa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyo 24:45) Tifunika kumvera mwatcheru kwambiri mawu a Mulungu amene amamveka kumbuyo kwathu kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo; potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Pamene chisautso chachikulu chikuyandikira kwambiri, n’kutheka kuti tizilandira malangizo ena omveka bwino. Kuti zinthu zidzatiyendere bwino m’masiku ovuta amenewo zidzadalira kumvera kwathu atumiki okhulupirika a Yehova amenewa.
16.Kodi tikuphunzirapo chiyani tikaona mmene Mulungu anachitira zinthu kuti apulumutse Aisiraeli?
16 Kumbukiraninso kuti Yehova anauza Aisiraeli kudutsa ku malo amene anaoneka ngati kuti atsekerezedwa pakati pa mapiri ndi Nyanja Yofiira. Zimene anauzidwazi zinaoneka ngati si zanzeru. Koma Yehova ndi amene ankayendetsa zinthu, ndipo zonse zinayenda bwino moti iye analemekezedwa ndipo anthu ake anapulumuka. Masiku anonso, mwina sitingadziwe chifukwa chimene gululi layendetsera zinthu m’njira inayake, koma tili ndi zifukwa zonse zokhulupirira malangizo amene Yehova amatipatsa kudzera mwa kapolo wokhulupirika. Nthawi zina adani athu angaoneke ngati akupambana. Koma ndi nzeru zathu zochepazi, sitingadziwe zonse zokhudza nkhaniyo. Komabe, Yehova ali ndi mphamvu zokonza zinthu panthawi yake, monga anachitira ndi ana Aisiraeli.—Miyambo 3:5.
Khulupirirani Yehova
17.N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira ngakhale pang’ono malangizo a Mulungu?
17 Tangoganizani chikhulupiriro chimene Aisiraeli anali nacho akamaganizira za mtambo umene unkawatsogolera masana uja ndi moto umene unkawatsogolera usiku? Zinali zoonekeratu kuti “mthenga wa Mulungu” woona anali kuwatsogolera pa ulendo wawo. (Eksodo 13:21, 22; 14:19) Masiku ano, tingakhulupirire kuti Yehova ali ndi anthu ake ndipo adzawatsogolera, kuwateteza ndi kuwapulumutsa. Tingadalire lonjezo lakuti: “[Yehova] sataya okondedwa; asungika kosatha.” (Salmo 37:28) Tisaiwale kuti magulu a angelo ndi amene akuthandiza atumiki a Mulungu masiku ano. Iwo angatithandize ‘kuchirimika, ndi kupenya chipulumutso cha Yehova.’—Eksodo 14:13.
18.N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kuvala zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu’?
18 Kodi n’chiyani chimene chingatithandize ‘kuchirimika’ m’njira ya choonadi? Kuvala zovala zankhondo zauzimu zimene Paulo analongosola m’kalata yake yopita kwa Aefeso. Onani kuti mtumwiyu akutilimbikitsa ‘kuvala zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.’ Kodi tikuvala zovala zonse zankhondo zauzimu zimenezi? Chaka chino, tingachite bwino kuti aliyense payekha aone ngati wavala bwinobwino zovala zonse zankhondo zauzimu zimenezi. Mdani wathu Satana Mdyerekezi amadziwa zofooka zathu ndipo amayesetsa kutigwira mwadzidzidzi kapena amalowera pambali imene tili ofooka. Ngakhale kuti ‘tikulimbana’ ndi makamu a mizimu yoipa, tingapambane ndi mphamvu za Yehova.—Aefeso 6:11-18; Miyambo 27:11.
19.Ngati tipirira, tidzakhala ndi mwayi wotani?
19 Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ngati inu mudzapirira, mudzapeza miyoyo yanu.” (Luka 21:19) Tikhaletu pakati pa anthu amene akupirira mavuto ena aliwonse amene akukumana nawo mokhulupirika. Tikatero Mulungu adzatikomera mtima ndipo ‘tidzachirimika, ndi kupenya chipulumutso cha Yehova.’
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ndi zinthu zochititsa chidwi ziti zimene zichitike posachedwapa?
• Kodi Yehova anasonyeza bwanji mphamvu zake zopulumutsa mu 1513 B.C.E.?
• Kodi mwatsimikiza kuchita chiyani m’tsogolomu?
[Mawu Otsindika patsamba 20]
Lemba la chakacha 2008 ndi lakuti: “Chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova.”—Eksodo 14:13.
[Chithunzi patsamba 17]
“Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza”
[Chithunzi patsamba 18]
Kuuma mtima kwa Farao kunabweretsa mavutoaakulu pa Iguputo
[Chithunzi patsamba 19]
Aisiraeli anapulumuka chifukwa chomvera malangizo onse amene Yehova anawapatsa