“Mphatso Yabwino Kwambiri”
ANANENA mawuwa ndi nduna yaikulu yakale ya dziko la Belgium pofotokoza za buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.a Munthu wina wa Mboni yemwe anayandikana naye nyumba anapita kukacheza ndi ndunayi ndipo anaipatsa bukuli. Kenako, ndunayi inalemba kalata yothokoza ndipo inati: “Kubwera kwanu kunandithandiza kwambiri, chinandisangalatsa zedi ndi mphatso yabwino kwambiri imene munandipatsa yomwe ndi buku longofotokoza za ‘Munthu Wamkulu’ basi.”
Nduna yakaleyi itawerenga bwinobwino bukuli inati: “Anthu atamawerenga Uthenga Wabwino ndi kutsatira mfundo za Yesu Khristu, dzikoli lingakhale labwino kwabasi. Ndiye kuti sitingafunikenso kukhala ndi nthambi yachitetezo ya bungwe la United Nations chifukwa sipangakhalenso zauchigawenga, ndipo ziwawa zingakhale mbiri yakale.” Ngakhale kuti ndunayi inkaona kuti izi sizingatheke, inayamikira kubwera kwa Mboniyo.
Kalatayo inapitiriza kuti: “Gulu lanu ndi la anthu amaganizo abwino chifukwa simumayembekezera kuti panopa zinthu zisintha kukhala bwino komanso simukayikira kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo.”
Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti ndi Mulungu yekha amene adzasinthe dzikoli kukhala labwino osati anthu ayi. Iwo amayesetsa kutsanzira munthu wamkulu yemwe ndi Yesu Khristu. Kodi Mboni za Yehova zakuyenderani posachedwapa? Tikukhulupirira kuti mungasangalale kukambirana nawo za munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Ndipo iwonso adzasangalala kukupatsani buku limene nduna yakale ija inasangalala nalo.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.