Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse
“Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.”—SAL. 16:8.
1. Kodi nkhani za m’Baibulo zimatithandiza motani?
M’MAWU a Yehova muli mbiri yochititsa chidwi ya zimene Mulungu wakhala akuchita ndi anthu. Mmenemo muli anthu ambiri amene anagwiritsidwa ntchito kukwaniritsa cholinga cha Mulungu. Ndipotu mawu ndi zochita zawo sizinalembedwe m’Baibulo ngati nkhani wamba zotisangalatsa. M’malo mwake, nkhani zimenezi zimatithandiza kuyandikira Mulungu.—Yak. 4:8.
2, 3. Kodi mawu a pa Salmo 16:8 akutanthauza chiyani?
2 Tonsefe timaphunzira zambiri pankhani za anthu odziwika bwino a m’Baibulo monga Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Davide, Estere, mtumwi Paulo ndi ena. Komanso tingapindule ndi nkhani za anthu omwe si odziwika kwambiri. Kusinkhasinkha nkhani za m’Babulo kungatithandize kuchita zimene wamasalmo anachita. Iye anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse: Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Sal. 16:8) Kodi mawuwa akutanthauza chiyani?
3 Kale msilikali anali kugwirira lupanga kudzanja lake lamanja. Chifukwa cha zimenezi, mbali ya kumanjayo inali yosatetezeka ndi chishango chomwe anali kunyamula ku dzanja lamanzere. Komabe, iye anali kukhala wotetezeka ngati msilikali mnzake akumenya nkhondo ataima chapafupi kudzanja lake lamanja. Ifenso tikamakumbukira Yehova ndi kuchita chifuniro chake nthawi zonse, adzatiteteza. Choncho tiyeni tione mmene nkhani za m’Baibulo zingalimbitsire chikhulupiriro chathu kuti ‘tiike Yehova patsogolo pathu nthawi zonse.’
Yehova Amayankha Mapemphero Athu
4. Perekani chitsanzo cha m’Malemba chosonyeza kuti Mulungu amayankha mapemphero.
4 Tikamaika Yehova patsogolo pathu, iye amayankha mapemphero athu. (Sal. 65:2; 66:19) Umboni wa zimenezi timaupeza m’nkhani ya mtumiki wamkulu wa Abulahamu, yemwe ayenera kuti anali Eliezere. Abulahamu anatumiza mtumiki wakeyu ku Mesopotamiya kuti akapezere Isake mkazi woopa Mulungu. Eliezere anapempha Mulungu kuti amutsogolere ndipo anazindikira kuti Mulungu wamutsogoleradi pamene Rebeka anamwetsa ngamila zake madzi. Chifukwa chakuti Eliezere anapemphera ndi mtima wonse, anapeza mkazi amene Isake anamukonda kwambiri. (Gen. 24:12-14, 67) N’zoona kuti ulendo wa mtumiki wa Abulahamu unali wapadera. Koma kodi ifenso sitiyenera kukhala ndi chikhulupiriro ngati iyeyo, chakuti Yehova amayankha mapemphero athu?
5. N’chifukwa chiyani tikunena kuti Yehova amayankha pemphero ngakhale litakhala lachidule ndi la mumtima?
5 Nthawi zina tingafunikire kupempha thandizo la Mulungu mwachidule. Tsiku lina, Mfumu Aritasasta ya Perisiya inaona kuti Nehemiya, yemwe anali woperekera chikho, anali wachisoni. Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ufunanji iwe? Pamenepo [Nehemiya] anapemphera kwa Mulungu wa Kumwamba.’ Apa n’zoonekeratu kuti sizikanatheka Nehemiya kupereka pemphero lalitali la mumtima. Koma Mulungu anayankhabe pemphero lake, chifukwa mfumuyo inathandiza Nehemiya kuti amange linga la Yerusalemu. (Werengani Nehemiya 2:1-8.) Zoonadi, Mulungu amayankha pemphero ngakhale litakhala lachidule ndi la mumtima.
6, 7. (a) Kodi Epafura anapereka chitsanzo chotani pankhani yopemphera? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera anzathu?
6 Timalimbikitsidwa “kupemphererana wina ndi mnzake” ngakhale kuti umboni wakuti mapemphero otero akuyankhidwa, suoneka nthawi yomweyo. (Yak. 5:16) Epafura, “mtumiki wokhulupirika wa Khristu,” anapempherera abale ake ndi mtima wonse. Polemba kalata ali ku Roma, Paulo anati: “Epafura, amene anachokera pakati panu [Akolose], kapolo wa Khristu Yesu, akuti moni kwa inu. Iye nthawi zonse amakupemphererani molimbika, kuti pomalizira pake mukhale athunthu ndi otsimikiza kotheratu m’chifuniro chonse cha Mulungu. Ndikum’chitiradi umboni kuti amadzipereka kwambiri chifukwa cha inu ndi a ku Laodikaya ndi a ku Herapoli.”—Akol. 1:7; 4:12, 13.
7 Mizinda ya Kolose, Laodikaya ndi Herapoli inali mu dera limodzi la ku Asia Minor. Ku Herapoli, Akhristu anali kukhala limodzi ndi anthu olambira mulungu wamkazi dzina lake Cybele. Nawonso Akhristu a ku Laodikaya akanatha kutengera khalidwe lokondetsa zinthu zakuthupi la anthu akumeneko. Ndiponso Akhristu a ku Kolose akanatha kusokonezeka ndi nzeru za anthu. (Akol. 2:8) N’chifukwa chake Epafura, yemwe anali wa ku Kolose, ‘anapempherera molimbika’ okhulupirira anzake a mumzindawo. Baibulo silinena kuti mapemphero a Epafura anayankhidwa, koma iye sanaleke kupempherera okhulupirira anzake. Ifenso tisaleke kupempherera anzathu. Ngakhale kuti ‘sitilowerera nkhani za ena,’ mwina tingakhale tikudziwa kuti chikhulupiriro cha wachibale wathu kapena mnzathu chikuyesedwa kwambiri. (1 Pet. 4:15) Apa ndiye pofunika kumupempherera koma patokha. Paulo anathandizidwa chifukwa cha mapembedzero a ena, ndipo mapemphero athu angathandizenso kwambiri.—2 Akor. 1:10, 11.
8. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti akulu a ku Efeso anali kudziwa kufunika kwa pemphero? (b) Kodi nkhani yopemphera kwa Mulungu tiziiona bwanji?
8 Kodi anthu ena amaona kuti ndife okonda kupemphera? Paulo atakumana ndi akulu a ku Efeso, “anagwada nawo pansi onsewo ndi kupemphera.” Atatero, “onse analira kwambiri pamenepo, ndipo anam’kumbatira Paulo ndi kum’psompsona mwachikondi. Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.” (Mac. 20:36-38) Sitikudziwa mayina a akulu onsewo, koma zikuonekeratu kuti iwo anali kudziwa kufunika kwa pemphero. Ifenso tiziona kuti ndi mwayi waukulu kupemphera kwa Mulungu ndipo ‘tizikweza manja athu okhulupirika m’mwamba’ ndi chikhulupiriro chakuti Atate wathu wakumwamba adzatiyankha.—1 Tim. 2:8.
Mverani Mulungu Pazonse
9, 10. (a) Kodi ana aakazi a Tselofekadi anapereka chitsanzo chotani? (b) Kodi Akhristu osakwatira angapindule bwanji ndi kumvera kwa ana aakazi a Tselofekadi?
9 Kukumbukira Yehova nthawi zonse kudzatithandiza kumumvera ndipo tidzalandira madalitso. (Deut. 28:13; 1 Sam. 15:22) Zimenezi zimafuna kuti tikhale ndi mtima womvera. Taganizirani mtima umene amayi asanu apachibale anali nawo. Amenewa anali ana aakazi a Tselofekadi, yemwe anakhalako m’nthawi ya Mose. Pamwambo wa Aisiraeli, ana aamuna ndi amene anali kulandira cholowa kwa bambo wawo. Tselofekadi anamwalira wopanda mwana wamwamuna, ndipo Yehova analamula kuti akazi asanu amenewa alandire cholowa chawo chonse koma anafunika kuchita chinthu chimodzi. Anafunika kukwatiwa ndi ana a Manase kuti cholowacho chikhalebe pa mtundu wawo.—Num. 27:1-8; 36:6-8.
10 Ana a Tselofekadi anali ndi chikhulupiriro chakuti zinthu zidzawayendera bwino akamvera Mulungu. Baibulo limati: “Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana aakazi a Tselofekadi anachita; popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Tselofekadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wawo. Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chawo chinakhala m’fuko la banja la atate wawo.” (Num. 36:10-12) Akazi omvera amenewo anachita zimene Yehova analamula. (Yos. 17:3, 4) Chifukwa cha chikhulupiriro ngati chimenechi, Akhristu osakwatira okhwima mwauzimu amamvera Mulungu mwa kukwatira kapena kukwatiwa “kokha mwa Ambuye.”—1 Akor. 7:39.
11, 12. Kodi Kalebi anasonyeza bwanji kuti anali kukhulupirira Mulungu?
11 Tiyenera kumvera Yehova pazonse monga mmene Kalebi Mwisiraeli anachitira. (Deut. 1:36) Aisiraeli atalanditsidwa ku Iguputo m’zaka za m’ma 1500 B.C.E., Mose anatuma amuna 12 kuti akazonde dziko la Kanani. Pa azondiwo, Kalebi ndi Yoswa ndi amene analimbikitsa anthu kukhulupirira Mulungu ndi mtima wonse kuti alowe m’dzikolo. (Num. 14:6-9) Patapita zaka pafupifupi 40, Yoswa ndi Kalebi anali adakali ndi moyo ndipo anali kutsatira Yehova ndi mtima wawo wonse, ndiponso Mulungu anagwiritsa ntchito Yoswa kutsogolera Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma zikuoneka kuti azondi 10 osakhulupirika aja anafa pa ulendo wazaka 40 wa Aisiraeli m’chipululu.—Num. 14:31-34.
12 Monga munthu amene anapulumuka pa ulendo wa Isiraeli m’chipululu ndipo tsopano ndi wokalamba, Kalebi anaima pamaso pa Yoswa ndi kunena kuti: “Ndinam’tsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.” (Werengani Yoswa 14:6-9.) Kalebi ali ndi zaka 85, anapempha kuti apatsidwe dera lamapiri limene Mulungu anamulonjeza. Anapempha deralo ngakhale kuti kunali adani awo m’mizinda yaikulu yokhala ndi malinga.—Yos. 14:10-15.
13. Kaya tikumane ndi mayesero otani, kodi tidzadalitsidwa ngati tikuchita chiyani?
13 Mofanana ndi Kalebi amene anali wokhulupirika ndi womvera, ifenso Mulungu adzatithandiza ‘tikamatsatira Yehova ndi mtima wathu wonse.’ Pokumana ndi mavuto aakulu, tidzadalitsidwa ngati ‘tikutsatira Yehova ndi mtima wathu wonse.’ Koma ndi zovuta kuchita zimenezi moyo wathu wonse ngati mmene Kalebi anachitira. Ngakhale kuti Mfumu Solomo inayamba bwino, akazi ake anapatutsa mtima wake ndipo atakalamba, anayamba kutumikira milungu yonyenga. Iye anasiya ‘kutsatira Yehova ndi mtima wake wonse monga Davide atate wake.’ (1 Maf. 11:4-6) Kaya tikumane ndi mayesero otani, tiyeni timvere Mulungu pazonse ndi kumuika patsogolo pathu nthawi zonse.
Khulupirirani Yehova Nthawi Zonse
14, 15. Kodi pankhani ya Naomi mwaphunzirapo chiyani za kufunika kokhulupirira Mulungu?
14 Tiyenera kukhulupirira Mulungu makamaka ngati tili ndi mtima wachisoni chifukwa chakuti zinthu zikuoneka kuti sizidzasintha m’tsogolo. Taganizirani za Naomi wokalamba. Mwamuna wake ndi ana ake aamuna awiri anamwalira. Atabwerera ku Yuda kuchokera ku Moabu, iye anadandaula kuti: “Musanditcha Naomi [kutanthauza “Kusangalatsa Kwanga”], munditche Mara [kutanthauza “Kuwawa”]; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu. Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa?”—Rute 1:20, 21.
15 Ngakhale kuti Naomi anali ndi chisoni, tikawerenga bwinobwino buku la Rute timapeza kuti iye anakhulupirirabe Yehova. Ndipo zinthu zinasintha kwambiri pamoyo wa Naomi. Mpongozi wake wamasiye Rute anakwatiwa ndi Boazi ndi kubereka mwana wamwamuna. Naomi anakhala mlezi wa mwanayo, ndipo nkhaniyo imati: “Akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Jese atate wa Davide.” (Rute 4:14-17) Naomi akadzaukitsidwa padziko lapansi, adzamva kuti Rute, yemwe adzakhalanso ndi moyo, anali kholo la Yesu, Mesiya. (Mat. 1:5, 6, 16) Mofanana ndi Naomi, sitingadziwe kuti mavuto amene tili nawo atithera bwanji. Choncho tiyeni nthawi zonse tizikhulupirira Mulungu monga mmene lemba la Miyambo 3:5, 6 limatiuzira, kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”
Dalirani Mzimu Woyera
16. Kodi mzimu woyera wa Mulungu unawathandiza bwanji akulu ena mu Isiraeli wakale?
16 Tikaika Yehova patsogolo pathu nthawi zonse, adzatitsogolera ndi mzimu wake woyera. (Agal. 5:16-18) Mzimu wa Mulungu unali pa akulu 70 amene anasankhidwa kuthandiza Mose “kusenza katundu wa anthu” a Isiraeli. Akulu amene anatchulidwa mayina ndi Elidadi ndi Medadi okha koma mzimuwo unathandiza akulu onsewo kuchita ntchito zawo. (Num. 11:13-29) Mosakayika, iwo anali odziwa ntchito yawo, oopa Mulungu, odalirika ndi okhulupirika mofanana ndi amuna amene anasankhidwa m’mbuyomo. (Eks. 18:21) Makhalidwe amenewa ndi amene akulu achikhristu ali nawo masiku ano.
17. Kodi mzimu woyera wa Yehova unagwira ntchito yotani pomanga chihema?
17 Mzimu woyera wa Yehova unathandiza kwambiri pantchito yomanga chihema m’chipululu. Yehova anasankha Bezaleli kukhala mmisiri wamkulu ndi womanga chihema ndipo analonjeza kuti ‘adzam’dzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m’ntchito zilizonse.’ (Eks. 31:3-5) Amuna ‘amtima waluso’ anagwira ntchito limodzi ndi Bezaleli ndi womuthandiza wake Oholiabu, pochita ntchito yabwino imeneyo. Ndiponso, mzimu wa Yehova unalimbikitsa anthu amtima wofunitsitsa kupereka zopereka mwaufulu. (Eks. 31:6; 35:5, 30-34) Mzimu womwewo umalimbikitsa atumiki amakono a Mulungu kuchita zonse zomwe angathe kuti apititse patsogolo zinthu za Ufumu. (Mat. 6:33) Mwina tingakhale ndi luso linalake, koma tiyenerabe kupempherera mzimu woyera ndi kuulola kutitsogolera. Tikatero tidzakwanitsa ntchito imene Yehova wapereka kwa anthu ake masiku ano.—Luka 11:13.
Khalani ndi Mtima Woopa Yehova Wamakamu Nthawi Zonse
18, 19. (a) Kodi mzimu woyera wa Mulungu umatipatsa mtima wotani? (b) Kodi inu mwaphunzirapo chiyani pachitsanzo cha Simiyoni ndi Anna?
18 Mzimu woyera umatipatsa mtima woopa Yehova umene umatithandiza kumuika patsogolo pathu nthawi zonse. Anthu akale a Mulungu anauzidwa kuti: “Yehova wa Makamu muzimuopa chifukwa iye ndi woyera.” (Yes. 8:13, Byington) M’zaka za zana loyamba, ku Yerusalemu kunali nkhalamba ziwiri zoopa Mulungu. Mayina awo anali Simiyoni ndi Anna. (Werengani Luka 2:25-38.) Simiyoni anakhulupirira ulosi wonena za Mesiya ndipo anali “kuyembekezera chipukutamisozi cha Isiraeli.” Mulungu anatsanulira mzimu woyera pa Simiyoni ndipo anamutsimikizira kuti sadzamwalira mpaka ataona Mesiya. Ndipo zimenezi zinachitikadi. Tsiku lina m’chaka cha 2 B.C.E., Mariya mayi wa Yesu ndi Yosefe bambo ake omulera, anabweretsa Yesuyo kukachisi. Atagwidwa ndi mzimu woyera, Simiyoni ananena mawu olosera za Mesiya ndi chisoni chimene Mariya adzakhala nacho. Ndipo Mariya anamvadi chisoni pamene Yesu anapachikidwa pa mtengo wozunzikirapo. Koma taganizirani mmene Simiyoni anasangalalira atanyamula “Khristu wa Yehova” m’manja mwake. Zoonadi, Simiyoni anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki a Mulungu amakono pankhani ya kuopa Mulungu.
19 Anna, mkazi wamasiye wa zaka 84 woopa Mulungu, “sanali kusowa pa kachisi.” Anali kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova usiku ndi usana ndipo anali “kusala kudya ndi kupereka mapembedzero.” Anna analipo pamene Yesu wakhanda anamubweretsa ku kachisi. Iye anathokoza kwambiri kuona mwana amene anali kudzakhala Mesiya. Inde, ‘anayamba kuyamika Mulungu, ndi kulankhula za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.’ Anna sakanachitira mwina koma kuuza anzake za uthenga wabwino umenewu. Mofanana ndi Simiyoni ndi Anna, Akhristu okalamba masiku ano amasangalala kwambiri kuti ukalamba suletsa munthu kutumikira Yehova monga Mboni yake.
20. Kaya ndife amsinkhu wotani, kodi tiyenera kuchita chiyani, ndipo chifukwa chiyani?
20 Kaya ndife amsinkhu wotani, tifunikira kuika Yehova patsogolo pathu nthawi zonse. Tikatero, iye adzatidalitsa chifukwa cha kudzichepetsa ndi kudzipereka kwathu pouza ena za ufumu wake ndi ntchito zake zodabwitsa. (Sal. 71:17, 18; 145:10-13) Koma kuti tilemekeze Yehova, tiyenera kukhala ndi makhalidwe abwino. Kodi tingaphunzire chiyani za makhalidwe amenewa m’nkhani zina za m’Baibulo?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amayankha mapemphero?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Mulungu pazonse?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yehova nthawi zonse ngakhale tili ndi mtima wachisoni?
• Kodi mzimu woyera wa Mulungu umawathandiza bwanji anthu ake?
[Chithunzi patsamba 4]
Pemphero la Nehemiya kwa Yehova linayankhidwa
[Chithunzi patsamba 5]
Kukumbukira mmene zinthu zinayendera ndi Naomi, kudzatithandiza kukhulupirira Yehova