Chikondi cha Mulungu Chimaonekera M’chikondi cha Mayi
“Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wom’bala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.”—YESAYA 49:15.
SIZACHILENDO kuona mayi atanyamula mwana wake wakhanda mosonyeza kuti amam’konda kwambiri. Ndipo mayi wina dzina lake Pam anati: “Pamene ndinam’nyamula koyamba mwana wanga wakhanda, ndinayamba kum’konda kwambiri ndiponso ndinamva kuti ndili ndi udindo wom’samalira.”
Ngakhale kuti izi sizachilendo, ofufuza apeza kuti chikondi cha mayi n’chofunika zedi kuti mwana akule bwino. Chikalata china chofalitsidwa ndi nthambi yoona za matenda a maganizo ya Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse chinati: “Kafukufuku wasonyeza kuti ana amene amanyalanyazidwa ndiponso kusiyidwa ndi amayi awo amakhala osasangalala komanso amavutika maganizo kwambiri, moti sakhala ndi chiyembekezo chilichonse.” Ndipo chikalata chomwecho chinasonyeza kuti ana amene makolo awo amawakonda ndi kuwasamalira kuyambira ali makanda, amakhala anzeru kwambiri kuposa ana amene amanyalanyazidwa.
Ponena za kufunika kwa chikondi cha mayi, Alan Schore yemwe ndi katswiri wa matenda a zamaganizo pa yunivesite ya UCLA School of Medicine ku United States, anati: “Ubwenzi woyambirira umene umakhalapo pakati pa mayi ndi mwana umathandiza kwambiri kuti mwanayo akamakula azikhala pa ubwenzi ndi anthu ena.”
Koma n’zomvetsa chisoni kuti amayi ena amanyalanyaza ana awo ngakhale ‘kuwaiwala’ kumene, chifukwa cha kuvutika maganizo, matenda kapena mavuto ena. (Yesaya 49:15) Komabe, zimenezi sizichitika kawirikawiri. Ndipotu zimaoneka kuti mwachibadwa amayi amakonda ana awo. Ofufuza apeza kuti panthawi imene amayi akubereka, timadzi tinatake timachuluka kwambiri m’thupi mwawo. Timadzi timeneti timathandiza mayiyo pobereka ndiponso kuti thupi lake lizitha kupanga mkaka wa m’mawere. Akuti timadziti, timene timapezekanso m’thupi la abambo, n’timene timachititsa kuti amayi azikonda kwambiri ana awo.
N’chifukwa Chiyani Anthu Amakondana?
Anthu amene amalimbikitsa zoti anthufe tinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina amaphunzitsa zoti chikondi, monga chomwe chimakhalapo pakati pa mayi ndi mwana, chinangokhalapo mwangozi ndipo chimapitirirabe chifukwa choti n’chopindulitsa. Mwachitsanzo, magazini ina imati: “Mbali ya ubongo wathu yomwe inayambirira kusintha kuchoka ku ubongo wa nyama ndi yomwe imatithandiza kuti tizitha kukhala ndi makhalidwe osiyanasiyana monga kukwiya kapena kusangalala. Mbali imeneyi ndi imene imachititsa kuti mayi ndi mwana wake azikondana kwambiri.”—Mothering Magazine.
N’zoona kuti ofufuza apeza kuti mbali ya ubongo imeneyi imachititsa anthu kukhala ndi makhalidwe osiyanasiyana monga kukwiya kapena kusangalala. Komabe, kodi inuyo mungakhulupirire kuti chikondi chimene mayi amakhala nacho kwa mwana wake chinangokhalapo mwangozi chifukwa cha ubongo umene amati unachita kusintha mwangozi kuchoka ku ubongo wa nyama?
Tiyeni tionenso zina zimene zingakhale chifukwa chimene chimapangitsa kuti anthufe tizikondana. Baibulo limanena kuti anthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, kutanthauza kuti angathe kusonyeza makhalidwe a Mulungu. (Genesis 1:27) Khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Wopanda chikondi sadziwa Mulungu.” N’chifukwa chiyani anatero? “Chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Taonani kuti vesili silinanene kuti Mulungu ali ndi chikondi. M’malo mwake limati Mulungu ndiye chikondicho. Iye ndiye chimake cha chikondi.
Baibulo limanenanso kuti: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekeza zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha konse.” (1 Akorinto 13:4-8) Kodi ndi zomveka kukhulupirira kuti chikondi chimenechi chinangokhalapo mwangozi?
Kodi Inuyo Zimakukhudzani Bwanji?
Pamene mumawerenga lemba lonena za chikondi limene lili m’ndime yapitayi, kodi munalakalaka munthu wina atakusonyezani chikondi cha mtundu umenewu? N’kwachibadwa kumva choncho. Chifukwa chiyani? N’chifukwa choti ndife “mbadwa za Mulungu.” (Machitidwe 17:29) Tinalengedwa moti tizitha kukondana. Ndipo sitingakayikire kuti Mulungu amatikonda kwambiri. (Yohane 3:16; 1 Petulo 5:6, 7) Lemba limene lili kumayambiriro kwa nkhani ino limafotokoza kuti chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa ife n’chachikulu ndiponso chosatha kuposa chimene mayi amakhala nacho kwa mwana wake.
Komabe, mwina mungadzifunse kuti: ‘Ngati Mulungu ndi wanzeru, wamphamvu ndiponso wachikondi, n’chifukwa chiyani sakuthetsa mavuto? N’chifukwa chiyani amalola kuti ana azimwalira, anthu aziponderezana, ndiponso dziko liziwonongedwa ndi anthu osayendetsa bwino zinthu ndiponso adyera?’ Awatu ndi mafunso omveka ndipo ndi ofunika mayankho ogwira mtima.
Ngakhale kuti anthu ena amaganiza kuti n’zosatheka kupeza mayankho a mafunso ngati amenewa, n’zotheka ndithu kupeza mayankho ake ogwira mtima. Anthu mamiliyoni ambiri m’mayiko ochuluka apeza mayankhowo mwa kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ofalitsa magazini ino akukupemphani kuti inunso muchite chimodzimodzi. Mukayamba kudziwa zambiri zokhudza Mulungu mwa kuphunzira Mawu ake ndiponso kuona zinthu zimene analenga, mudzazindikira kuti iye si wosadziwika. Ndipo mudzakhala wotsimikiza kuti Mulungu “sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:27.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa ife n’chosatha kuposa chimene mayi amakhala nacho kwa mwana wake